Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Munagulidwa ndi Mtengo Wake Wapatali”

“Munagulidwa ndi Mtengo Wake Wapatali”

“Munagulidwa ndi Mtengo Wake Wapatali”

“Munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu.”​—1 AKORINTO 6:20.

1, 2. (a) Malinga ndi Chilamulo cha Mose, kodi akapolo achiisrayeli ankafunika kukhala nawo motani? (b) Kodi kapolo amene anali kukonda mbuye wake anali ndi ufulu wosankha kutani?

BUKU lakuti Holman Illustrated Bible Dictionary limanena kuti: “Kalekale ukapolo unali wofala kwambiri ndipo unali wovomerezeka kwa anthu ambiri.” Ndiyeno limawonjezera kuti: “Chuma cha mayiko a Egypt, Greece, ndi Rome chinkadalira ntchito za akapolo. M’zaka 100 zoyambirira za Chikristu, munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse ku Italy, ndiponso munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse m’mayiko ena anali kapolo.”

2 Ngakhale kuti ukapolo unali kuchitikanso m’Israyeli wakale, Chilamulo cha Mose chinali kuteteza akapolo achihebri. Mwachitsanzo, malinga ndi Chilamulo Mwisrayeli ankayenera kugwira ukapolo kwa zaka zosaposa zisanu ndi chimodzi. M’chaka cha chisanu ndi chiwiri, ankamulola ‘kutuluka mwaufulu chabe.’ Ndipo malamulo okhudza mmene anayenera kukhalira ndi akapolowo anali abwino kwabasi. Anasonyeza kuti akapolowo anafunika kukhala nawo mokoma mtima. Mwachitsanzo, Chilamulo cha Mose chinanena kuti: “Mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am’boole khutu lake ndi lisungulu; ndipo iye azim’gwirira ntchito masiku onse.”​—Eksodo 21:2-6; Levitiko 25:42, 43; Deuteronomo 15:12-18.

3. (a) Kodi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira anavomera ukapolo wotani? (b) N’chiyani chimene chimatilimbikitsa kutumikira Mulungu?

3 Dongosolo la ukapolo wodzifunirawo linali chithunzi cha ukapolo wa Akristu oona. Mwachitsanzo, olemba Baibulo Paulo, Yakobo, Petro ndi Yuda anadzitcha akapolo a Mulungu ndi a Kristu. (Tito 1:1; Yakobo 1:1; 2 Petro 1:1; Yuda 1) Paulo anakumbutsa Akristu a ku Tesalonika kuti iwo ‘anatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano awo, kuti atumikire Mulungu weniweni wamoyo.’ (1 Atesalonika 1:9) N’chiyani chomwe chinalimbikitsa Akristu amenewo kukhala akapolo a Mulungu mofunitsitsa? Tingafunsenso kuti, n’chiyani chimene chinali kulimbikitsa akapolo achiisrayeli aja kukana kuchoka mwaufulu mbuye wawo atawamasula? Kodi sichinali chifukwa chakuti anali kukonda mbuye wawoyo? Ukapolo wachikristu nawonso wagona pa kukonda Mulungu. Tikam’dziwa Mulungu woona ndi wamoyo ndi kum’konda, timalimbikitsika kum’tumikira “ndi mtima [wathu] wonse ndi moyo [wathu] wonse.” (Deuteronomo 10:12, 13) Koma kodi n’chiyani chomwe chimafunika kwa akapolo a Mulungu ndi a Kristu? Kodi zimenezi zimakhudza bwanji moyo wathu watsiku ndi tsiku?

“Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu”

4. Kodi timakhala bwanji akapolo a Mulungu ndi a Kristu?

4 Mawu akuti kapolo amatanthauza “munthu amene mwalamulo amakhala m’manja mwa munthu wina kapena anthu ena ndipo amayenera kuwamvera kotheratu.” Mwalamulo, ife tinakhala ake a Yehova pamene tinapereka miyoyo yathu kwa iye ndi kubatizidwa. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali.” (1 Akorinto 6:19, 20) Mtengo wapatali umenewo ndiwo nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu amativomereza kukhala atumiki ake chifukwa cha nsembe imeneyi, kaya ndife Akristu odzozedwa kapena anzawo omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi. (Aefeso 1:7; 2:13; Chivumbulutso 5:9) Chotero kuchokera pa ubatizo wathu, ‘tinakhala ake a Ambuye.’ (Aroma 14:8) Popeza kuti tinagulidwa ndi magazi a mtengo wapatali a Yesu Kristu, ndifenso akapolo ake ndipo tiyenera kusunga malamulo ake.​—1 Petro 1:18, 19.

5. Monga akapolo a Yehova, kodi tili ndi udindo waukulu uti, nanga tingaukwaniritse bwanji?

5 Akapolo amayenera kumvera mbuye wawo. Ife ukapolo wathu ndi wochita kudzifunira ndipo timasankha kukhala akapolo chifukwa chakuti timakonda Mbuye wathu. Lemba la 1 Yohane 5:3, limati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” Choncho ife timasonyeza chikondi chathu ndi kugonjera kwathu mwa kumvera Mulungu. Izi zimaonekera m’chilichonse chimene tikuchita. Paulo anati: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) M’moyo wathu watsiku ndi tsiku, tiyenera kusonyeza kuti ‘tikutumikira Ambuye,’ ngakhale m’zinthu zazing’ono.​—Aroma 12:11.

6. Kodi kukhala akapolo a Mulungu kumakhudza motani zosankha zimene timachita m’moyo? Perekani chitsanzo.

6 Mwachitsanzo, pamene tikusankha zochita tiyenera kuganizira mozama kwambiri za chifuniro cha Mbuye wathu wakumwamba, Yehova. (Malaki 1:6) Kufunitsitsa kwathu kumvera Mulungu kungayesedwe posankha zochita pankhani zovuta. Kodi tidzamvera malangizo ake m’malo mongotsatira zofuna za mtima wathu “wonyenga” ndi ‘wosachiritsikawu’? (Yeremiya 17:9) Melisa, yemwe ndi Mkristu wosakwatiwa, atangobatizidwa kumene, mnyamata wina ankafuna atakhala naye pachibwenzi. Mnyamata ameneyu ankaoneka kuti ndi munthu wabwino, ndipo anali atayamba kale kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe, mkulu anakambirana ndi Melisa ubwino wotsatira lamulo la Yehova lokhudza kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14) Melisa akuvomereza kuti: “Kutsatira malangizo amenewa sichinali chapafupi kwa ine. Komabe ndinatsimikiza mtima kumvera malangizo a Mulungu osapita m’mbaliwo, chifukwa chakuti ndinadzipereka kwa Iye kuti ndichite chifuniro chake.” Pokumbukira zomwe zinachitikazo, iye akuti: “Ndine wosangalala kwambiri kuti ndinamvera malangizowo. Posapita nthawi mnyamata uja anasiya kuphunzira. Ngati ndikanavomera kupalana naye ubwenzi, bwenzi pano nditakwatiwa ndi wosakhulupirira.”

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kumangofuna kukondweretsa anthu nthawi zonse? (b) Perekani chitsanzo cha mmene tingathetsere kuopa anthu.

7 Popeza ndife akapolo a Mulungu, sitiyeneranso kukhala akapolo a anthu. (1 Akorinto 7:23) N’zoona kuti aliyense wa ife amafuna kuti anthu azim’konda, koma tiyenera kukumbukira kuti Akristu ali ndi miyezo yosiyana ndi ena onse m’dzikoli. Paulo anafunsa kuti: “Kodi ndifuna kukondweretsa anthu?” Ndiyeno pamapeto pake iye anati: “Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Kristu.” (Agalatiya 1:10) Sitiyenera kugonjera anzathu amene akutikakamiza kuchita zofuna zawo pongofuna kuti tiwasangalatse. Nanga tingatani ngati tikukakamizika kutsanzira anzathu?

8 Ganizirani chitsanzo chotsatirachi cha Elena, mtsikana wachikristu wa ku Spain. Anzake ambiri a m’kalasi ankakonda kupereka magazi. Iwo ankadziwa kuti Elena sangapereke kapena kuikidwa magazi chifukwa ndi wa Mboni za Yehova. Mpata utapezeka woti afotokozere kalasi lonselo maganizo ake, Elena anadzipereka kukamba nkhani m’kalasimo. Elena anati: “Kunena mosabisa, ndinkachita mantha kwambiri. Koma ndinakonzekera bwino, mwakuti zotsatira zake zinali zodabwitsa. Ana asukulu anzangawo anayamba kundilemekeza, ndipo aphunzitsi anga anandiuza kuti anachita chidwi ndi ntchito imene ndinali kugwira. Koposa zonse, ndinali wokhutira chifukwa choikira kumbuyo dzina la Yehova ndipo ndinatha kufotokoza momveka bwino chikhulupiriro changa cha m’Malemba.” (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 15:28, 29) Inde, monga akapolo a Mulungu ndi a Kristu, ndife osiyana ndi ena onse. Komabe, kawirikawiri anthu adzatilemekeza ngati ndife okonzeka kuikira kumbuyo chikhulupiriro chathu mwaulemu.​—1 Petro 3:15.

9. Kodi tikuphunzira chiyani kwa mngelo amene anaonekera mtumwi Yohane?

9 Kukumbukira kuti ndife akapolo a Mulungu kungatithandizenso kukhala odzichepetsa. Nthawi inayake, mtumwi Yohane anachita chidwi kwambiri ndi masomphenya osangalatsa a Yerusalemu wakumwamba, mwakuti anagwa pamapazi a mngelo, amene anali mthenga wa Mulungu, kuti amulambire. Mngeloyo anamuuza kuti: “Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mawu a buku ili; lambira Mulungu.” (Chivumbulutso 22:8, 9) Apatu mngelo ameneyu anasonyeza chitsanzo chabwino kwabasi kwa akapolo onse a Mulungu! Akristu ena ali ndi maudindo apadera mumpingo. Ngakhale kuti izi zili choncho, Yesu anati: “Amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:26, 27) Monga otsatira a Yesu, tonsefe ndife akapolo.

“Tangochita Zimene Tayenera Kuzichita”

10. Perekani zitsanzo za m’Malemba zosonyeza kuti kawirikawiri sizinali zophweka kwa atumiki okhulupirika a Mulungu kuchita chifuniro chake.

10 Kawirikawiri sizophweka kwa anthu opanda ungwiro kuchita chifuniro cha Mulungu. Mneneri Mose ankafuna kukana pamene Yehova anam’tuma kukatulutsa ana a Israyeli mu ukapolo ku Igupto. (Eksodo 3:10, 11; 4:1, 10) Yona atatumidwa kukalengeza uthenga wa chiweruzo kwa anthu a ku Nineve, “ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova.” (Yona 1:2, 3) Baruki yemwe anali mlembi wa mneneri Yeremiya, ankanyinyirika kuti watopa. (Yeremiya 45:2, 3) Kodi tiyenera kuchitanji ngati zofuna zathu kapena zokonda zathu zikuwombana ndi kuchita chifuniro cha Mulungu? Yankho likupezeka mu fanizo limene Yesu ananena.

11, 12. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu lopezeka pa Luka 17:7-10. (b) Kodi tikuphunzira chiyani m’fanizo la Yesuli?

11 Yesu anafotokoza za kapolo amene anali kuthengo tsiku lonse kuweta nkhosa za mbuye wake. Kapoloyu anabwerera kunyumba, ali wotopa chifukwa cha ntchito yaikulu imene anaigwira maola khumi ndi awiri. Koma atafika kunyumbako, mbuye wake sanamuuze kuti akhale pansi ndi kulandira chakudya chokoma. M’malo mwake, mbuye wakeyo anati: “Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe.” Kapoloyo anafunikira kutumikira mbuye wakeyo choyamba, asanachite zofuna zake. Yesu anamaliza fanizoli ndi mawu akuti: “Chotero inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.”​—Luka 17:7-10.

12 Yesu sanapereke fanizo limeneli posonyeza kuti Yehova sayamikira zimene timachita mu utumiki wake ayi. Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Koma mfundo ya m’fanizo la Yesuli ndi yakuti kapolo sangathe kudzikondweretsa yekha kapena kumangochita zomusangalatsa. Pamene tinadzipereka kwa Mulungu ndi kusankha kukhala akapolo ake, tinavomereza kuti tidzaika chifuniro chake patsogolo pa zofuna zathu. Chotero tiyenera kuika chifuniro cha Mulungu patsogolo pa zofuna zathu.

13, 14. (a) Kodi tingafunike kunyalanyaza zofuna zathu m’mikhalidwe yotani? (b) N’chifukwa chiyani chifuniro cha Mulungu tifunika kuchiika patsogolo nthawi zonse?

13 Tingafunike kuyesetsa mwakhama kwambiri kuti tiziphunzira Mawu a Mulungu komanso zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” nthawi zonse. (Mateyu 24:45) Izi zingakhaledi choncho makamaka ngati kuwerenga kwathu n’kovutikira nthawi zonse kapena ngati chofalitsacho chikufotokoza “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Koma kodi zimenezi ziyenera kutilepheretsa kupatula nthawi yochita phunziro laumwini? Pangafunike kudzikakamiza kukhala pansi ndi kuphunzira nkhaniyo mwachifatse. Kodi n’zotheka kukulitsa chilakolako cha ‘chakudya chotafuna cha anthu akulu misinkhu,’ ngati tikulephera kudzikakamiza mwa njira imeneyi?​—Ahebri 5:14.

14 Nanga bwanji ngati timafika kunyumba tili otopa chifukwa chogwira ntchito tsiku lonse? Tingafunike kudzikoka ndithu kuti tikapezeke ku misonkhano yachikristu. Mwina mwachibadwa sitingakonde kwenikweni kumalalikira kwa anthu achilendo. Paulo nayenso anadziwa kuti nthawi zina tingafunike kulengeza uthenga wabwino motsutsana ndi kufuna kwathu. (1 Akorinto 9:17) Koma timachitabe zimenezi chifukwa chakuti Ambuye wathu wakumwamba Yehova, amenenso timam’konda, akutiuza kuti tizichita zimenezi. Ndipo kodi nthawi zonse sitimakhala okhutira ndi olimbikitsidwa tikachita khama kuphunzira, kupezeka pa misonkhano, ndi kulalikira?​—Salmo 1:1, 2; 122:1; 145:10-13.

Musayang’ane “za Kumbuyo”

15. Kodi Yesu anasonyeza motani chitsanzo cha kugonjera Mulungu?

15 Yesu Kristu anasonyeza mwapadera kwambiri kuti amagonjera Atate wake wakumwamba. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “ndinatsika kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 6:38) Atavutika maganizo m’munda wa Getsemane, Yesu anapemphera kuti: “Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.”​—Mateyu 26:39.

16, 17. (a) Kodi zinthu zimene tazisiya m’mbuyo tiyenera kuziona motani? (b) Sonyezani kuti Paulo anachita mwanzeru potaya ziyembekezo zake za m’dzikoli ndi ‘kuziyesa zapadzala.’

16 Yesu Kristu akufuna kuti tikhalebe okhulupirika pa chosankha chathu chokhala akapolo a Mulungu. Iye anati: “Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:62) Pamene tikutumikira Mulungu, sikoyenera m’pang’ono pomwe kumangoganizira zimene tasiya m’mbuyo nthawi zonse. M’malo mwake, tiziyamikira zomwe tapeza chifukwa chosankha kukhala akapolo a Mulungu. Polembera Afilipi, Paulo anati: “Ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.”​—Afilipi 3:8.

17 Taganizirani zinthu zonse zimene Paulo anaziyesa zapadzala ndi kuzisiya kuti apindule mwauzimu monga kapolo wa Mulungu. Sikuti anangosiya zosangalatsa zam’dziko zokha komanso analolera kutaya chiyembekezo chodzakhala mtsogoleri wachiyuda m’tsogolo. Ngati Paulo akanapitirizabe m’chipembedzo cha Chiyuda, akanatha kulandira udindo wofanana ndi wa Simeoni amene anali mwana wa Gamaliyeli mphunzitsi wa Paulo. (Machitidwe 22:3; Agalatiya 1:14) Simeoni anakhala mtsogoleri wa Afarisi ndipo anatsogolera Ayuda kuukira Aroma mu 66-70 C.E., ngakhale kuti anali kukayikakayika. Iye anaphedwa pa chipolowe chimenecho ndi Ayuda olimbikitsa kuukirako kapena asilikali achiroma.

18. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene kuchita zinthu zauzimu kumapindulitsira.

18 Mboni za Yehova zambiri zatsanzira chitsanzo cha Paulo chimenechi. Jean anati: “M’zaka zowerengeka chabe nditamaliza sukulu, ndinapeza ntchito kwa loya wotchuka mu London. Ndinali mlembi wake wamkulu ndipo ndinkasangalala ndi ntchito yanga. Ndinkalandira ndalama zambiri, koma mumtima mwangamu ndinkadziwa kuti ndingathe kuchita zambiri potumikira Yehova. Pamapeto pake, ndinalemba kalata yomudziwitsa kuti ndasiya ntchito ndipo ndinayamba kuchita upainiya. Ndikunyadira kwambiri kuti ndinachita zimenezi pafupifupi zaka 20 zapitazo. Utumiki wanga wanthawi zonse wandikhutiritsa kwambiri kuposa mmene zikanakhalira ngati ndikanapitiriza kugwira ntchito ya ulembi ija. Palibe chimene chimakhutiritsa kwambiri kuposa kuona mmene Mawu a Yehova amasinthira moyo wa munthu. N’zosangalatsa zedi kuthandiza munthu kusintha moyo wake. Zomwe timalandira kwa Yehova n’zochuluka kwabasi, sitingaziyerekezere ndi zomwe timam’patsa.”

19. Kodi tifunika kutsimikiza mtima kuchitanji, ndipo n’chifukwa chiyani?

19 M’kupita kwa nthawi zinthu zingasinthe m’moyo wathu. Koma, kudzipereka kwathu kwa Mulungu sikudzasintha. Ndifebe akapolo a Yehova, ndipo amatilola kusankha mmene tingagwiritsire ntchito moyenera nthawi yathu, mphamvu zathu, maluso athu ndiponso zinthu zina zofunika. Choncho zomwe tingasankhe kuchita pambali imeneyi zingasonyeze mmene chikondi chathu kwa Mulungu chilili. Zingasonyezenso kuti ndife ofunitsitsa kudzimana kufika pati. (Mateyu 6:33) Kodi sizoona kuti tifunika kutsimikiza mtima kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa, mulimonse mmene zinthu zilili kwa ife? Paulo analemba kuti: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chim’sowa.”​—2 Akorinto 8:12.

“Muli Nacho Chobala Chanu”

20, 21. (a) Kodi akapolo a Mulungu amabala chipatso chotani? (b) Kodi Yehova amapereka mphoto yotani kwa amene amam’patsa zabwino zawo zonse?

20 Kukhala akapolo a Mulungu sikolemetsa. M’malo mwake, timathawa ukapolo wopondereza umene umatichotsera chimwemwe chathu. Paulo analemba kuti: “Pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.” (Aroma 6:22) Tikamatumikira monga akapolo a Mulungu timabala chipatso cha chiyero chifukwa chakuti timapindula ndi makhalidwe athu oyera, kapena kuti kudzisunga. Komanso, tidzapeza moyo wosatha m’tsogolo.

21 Yehova ndi woolowa manja kwa akapolo ake. Tikayesetsa kuchita zonse zimene tingathe muutumiki wake, amatitsegulira “mazenera a kumwamba” ndi kutitsanulira ‘mdalitso wosowa nawo malo akuulandira.’ (Malaki 3:10) Zidzakhalatu zosangalatsa kwabasi kupitirizabe kutumikira monga akapolo a Yehova kwa muyaya.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani timakhala akapolo a Mulungu?

• Kodi timasonyeza bwanji kugonjera chifuniro cha Mulungu?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okonzeka kuika chifuniro cha Yehova patsogolo pa zofuna zathu?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera ‘kuyang’ana zinthu za kumbuyo’?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Dongosolo la ukapolo wodzifunira mu Israyeli linali chithunzi cha ukapolo wa Akristu

[Chithunzi patsamba 17]

Tikabatizidwa timakhala akapolo a Mulungu

[Zithunzi patsamba 17]

Akristu amaika chifuniro cha Mulungu patsogolo

[Chithunzi patsamba 18]

Mose ankafuna kukana utumiki umene anapatsidwa