Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muyezo wa “Pimu” Ukutsimikizira Kuti Baibulo ndi Lolondola Mogwirizana ndi Mbiri Yakale

Muyezo wa “Pimu” Ukutsimikizira Kuti Baibulo ndi Lolondola Mogwirizana ndi Mbiri Yakale

Muyezo wa “Pimu” Ukutsimikizira Kuti Baibulo ndi Lolondola Mogwirizana ndi Mbiri Yakale

MAWU akuti “pimu” amapezeka kamodzi kokha m’mabaibulo ambiri. M’masiku a Mfumu Sauli, Aisrayeli ankanoletsa zitsulo zawo kwa amisiri azitsulo achifilisti. Lemba la 1 Samueli 13:21, m’Baibulo la New World Translation limati: “Ndipo pimu anali malipiro onoletsera mapulawo, makasu, zipangizo za mano atatu, nkhwangwa ndi kusongoletsera zisonga zotosera ng’ombe.”

Kodi pimu chinali chiyani? Palibe amene ankadziwa yankho la funso limeneli mpakana m’chaka cha 1907, pamene ofukula m’mabwinja anapeza mwala woyamba woyezera wotchedwa pimu mu mzinda wakale wa Gezer. Omasulira Baibulo akale zinawavuta kumasulira mawu akuti “pimu.” Mwachitsanzo, Baibulo lakuti Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, pa 1 Samueli 13:21 limati: “Koma anali nawo matupa kukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano ndi nkhwangwazo; ndi kusongola zothwikira.”

Masiku ano akatswiri amaphunziro amadziwa kuti pimu unali muyezo wolemera pafupifupi magalamu 8, kapena pafupifupi sekeli limodzi, lomwe linali muyezo waukulu woyezera kulemera kwa zinthu m’Chihebri. Afilisti anali kulipiritsa Aisrayeli zidutswa za chitsulo cha siliva zolemera pimu imodzi, akawanolera zipangizo zawo. Anthu anasiya kugwiritsa ntchito masekeli poyeza kulemera kwa zinthu mu 607 B.C.E. pamene adani anagwetsa ufumu wa Yuda ndi likulu lake Yerusalemu. Nanga kodi muyezo wa pimu ukutsimikizira bwanji kuti Malemba Achihebri ndi olondola mogwirizana ndi mbiri yakale?

Akatswiri ena amaphunziro amanena kuti nkhani za m’Malemba Achihebri, kuphatikizapo buku la Samueli Woyamba, zinalembedwa m’kati mwa ulamuliro wa Agiriki ndi Aroma. Iwo amati nkhani zimenezi n’zaposachedwapa m’kati mwa zaka 200 ndi 100 zomalizira za m’ma B.C.E. Pachifukwa chimenechi, iwo amanena kuti “nkhani za m’Malemba Achihebri . . . ‘sizigwirizana ndi mbiri yakale,’ sizifotokoza mbiri yoona ya ‘Israyeli wa m’Baibulo’ kapena ‘Israyeli wakale.’ Amati Ayuda ndi Akristu amakono anangopeka nkhani zimenezi.”

Koma ponena za muyezo wa pimu wotchulidwa pa 1 Samueli 13:21, William G. Dever, katswiri wophunzira za m’mabwinja ndi chikhalidwe cha anthu ku Near East, anati: “N’zosatheka kuti olemba mabuku a m’nthawi ya ulamuliro wa Agiriki ndi Aroma ‘anangopeka’ zimenezi, chifukwa panthawiyo, zaka zambirimbiri zinali zitadutsa kuchokera pamene miyezo imeneyi inazimiririka ndi kuiwalika. Ndipotu mawu a m’Baibulo ochepawa . . . anali ovuta kuwamvetsa mpakana kudzafika kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1900 A.D. Imeneyi ndi nthawi yomwe anapeza zitsanzo zenizeni zoyambirira za zinthu zofukulidwa m’mabwinja, zolembedwa mawu a Chihebri akuti pîm.” Katswiriyu anapitiriza kuti: “Ngati nkhani zonse za m’Baibulo zili ‘nkhani zongopeka’ za m’nthawi ya ulamuliro wa Agiriki ndi Aroma, nanga nkhani imeneyi ikupezeka bwanji m’Baibulo la Chihebri? N’kutheka kuti wina anganene kuti nkhani ya pîm ‘si nkhani yaikulu ayi.’ Zimenezo n’zoona, koma monga momwe tikudziwira, ‘mbiri yakale yagona m’nkhani zing’onozing’onozo.’”

[Chithunzi patsamba 29]

Muyezo wa pimu unali wolemera pafupifupi sekeli limodzi