‘Ngati Mwala Wofiira Wamtengo Wapatali’
‘Ngati Mwala Wofiira Wamtengo Wapatali’
MTUMWI Yohane anaona masomphenya a mpando wachifumu waulemerero kumwamba. Wokhala pa mpando wachifumuwo, maonekedwe ake ankafanana ndi “mwala wa jaspi.” Iye ankaonekanso ngati “sardiyo [“mwala wofiira wamtengo wapatali, NW].” (Chivumbulutso 4:2, 3) Kodi miyala imeneyi inali yotani?
Imeneyi inali miyala yoonekera m’kati osati yongonyezimira pamwamba pokha. M’nthawi yakale, liwu lachigiriki lomwe analimasulira kuti “jaspi” anali kuligwiritsa ntchito kutanthauza miyala ya mitundu yosiyanasiyana, kuphatikizapo ngale zamtengo wapatali zomwe zinali zoonekera kwambiri m’kati. M’buku lakuti Word Pictures in the New Testament, A. T. Robertson anati: “Mosakayikira, ‘Mwala wa jaspi’ wotchulidwa pa Chivumbulutso 4:3, unali wosiyana ndi jaspi wathu wotchipa wamakonoyu.” Komanso, chakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, Yohane anafotokoza za mzinda wakumwamba wa Yerusalemu, iye anati: “Kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo.” (Chivumbulutso 21:10, 11) Zikuoneka kuti miyala imene Yohane anali kunena inali yosaonekera kwambiri m’kati.
Wokhala pa mpando wachifumu m’masomphenya a Yohane akuimira Yehova Mulungu, yemwe ndi waulemerero kwambiri m’chilengedwe chonse. Iye ndi wolungama ndi woyera koposa m’chilengedwe chonse. Mogwirizana ndi zimenezo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.” (1 Yohane 1:5) Chotero Yohane analimbikitsa okhulupirira anzake kuti ‘adziyeretse okha monga mmene Yehova alili woyera.’—1 Yohane 3:3.
Kodi tiyenera kuchitanji kuti Mulungu azitiona monga oyera? Chofunika kwambiri ndicho kukhala ndi chikhulupiriro kuti machimo athu angakhululukidwe kudzera m’mwazi umene Kristu anakhetsa. Tiyeneranso kupitiriza ‘kuyenda m’kuunika’ mwa kuphunzira Baibulo nthawi zonse ndi kumachita zinthu mogwirizana ndi ziphunzitso zakezo.—1 Yohane 1:7.