Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tisakhalenso ndi Moyo mwa Ife Tokha

Tisakhalenso ndi Moyo mwa Ife Tokha

Tisakhalenso ndi Moyo mwa Ife Tokha

“[Kristu] adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha.”​—2 AKORINTO 5:15.

1, 2. Kodi ndi lamulo liti la m’Malemba limene linalimbikitsa otsatira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira kuthana ndi kudzikonda?

UNALI usiku wotsiriza wa moyo wa Yesu padziko lapansi. Kunali kutangotsala maola owerengeka chabe kuti apereke moyo wake m’malo mwa onse okhulupirira mwa iye. Usiku umenewo, Yesu anauza atumwi ake okhulupirikawo zinthu zambiri zofunika. Mwa zina, anawapatsa lamulo lokhudza khalidwe limene otsatira ake adzadziwika nalo. Iye anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:34, 35.

2 Akristu oona ayenera kusonyezana chikondi chodzimana ndi kuika zofuna za okhulupirira anzawo patsogolo pa zofuna zawo. Ayenera kukhala ofunitsitsa ngakhale ‘kutaya moyo wawo chifukwa cha mabwenzi awo.’ (Yohane 15:13) Kodi Akristu oyambirirawo anachitanji atalandira lamulo latsopanoli? M’buku lake lotchuka lakuti Apology, Tertullian, wolemba mabuku wa m’zaka za m’ma 200, anagwira mawu olemba mabuku anzake omwe ananenapo za Akristu, kuti: ‘Onani mmene amakonderana; mmene alili okonzeka ngakhale kuferana wina ndi mnzake.’

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kuthetsa mtima wodzikonda? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana chiyani?

3 Nafenso tiyenera ‘kunyamulirana zothodwetsa, ndipo kotero tifitse chilamulo cha Kristu.’ (Agalatiya 6:2) Komatu kudzikonda ndi chimodzi mwa zopinga zikuluzikulu zimene zingatilepheretse kumvera lamulo la Kristu ndi ‘kukonda Ambuye Mulungu wathu ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse ndi kukonda mnzathu monga timadzikondera ife eni.’ (Mateyu 22:37-39) Popeza ndife opanda ungwiro, nthawi zambiri timakhala odzikonda. Kuwonjezera apo, tili ndi nkhawa za moyo watsiku ndi tsiku, tikulimbana ndi mpikisano wa kusukulu kapena kuntchito, ndiponso tikuyesetsa kupeza zosowa zathu. Zonsezi zimangokulitsa vuto lathu lachibadwa lija la mtima wodzikonda. Mtima wodzikonda umenewu sukutha ayi. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Masiku otsiriza . . . anthu adzakhala odzikonda okha.”​—2 Timoteo 3:1, 2.

4 Chakumapeto kwa utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anapatsa ophunzira ake mfundo zitatu zoti ziwathandize kuthetsa mtima wodzikonda. Kodi mfundo zake zinali zotani, ndipo ifeyo tingapindule bwanji ndi malangizo akewo?

Njira Yodalirika Yothetsera Kudzikonda

5. Kodi Yesu ananena chiyani kwa ophunzira ake pamene anali kulalikira kumpoto kwa Galileya, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zinawakhumudwitsa?

5 Yesu anali kulalikira pafupi ndi Kaisareya wa Filipi kumpoto kwa Galileya. N’kutheka kuti chigawo chabata ndi chochititsa chidwichi anali kuchiona ngati malo abwino opumulirako osati kokaphunzirira za kudzimana. Koma ali kumeneko, Yesu anayamba kuuza ophunzira akewo kuti “kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.” (Mateyu 16:21) Mawu amenewa ayenera kuti anawakhumudwitsa ophunzira a Yesuwo, chifukwa kwa nthawi yaitali iwo anali kuyembekezera kuti Mtsogoleri wawoyo adzakhazikitsa Ufumu wake padziko lapansi.​—Luka 19:11; Machitidwe 1:6.

6. N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula Petro mwamphamvu?

6 Nthawi yomweyo Petro “anam’tengera [Yesu] pambali, nayamba kum’dzudzula kuti, ‘Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi.’” Kodi Yesu anachitanji? “Anatembenuka nati kwa Petro, ‘Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa ine; ulibe zinthu za Mulungu m’maganizo mwako koma zinthu za anthu.’” Izi zikusonyezeratu kuti awiriwa anali ndi maganizo osiyana. Mofunitsitsa Yesu analandira ntchito yofuna kudzipereka imene Mulungu anam’patsa. Ntchito yomwe inali yoti pakangopita miyezi yowerengeka imudzetsera imfa pa mtengo wozunzikirapo. Petro anapatsa Yesu maganizo akuti akhale ndi moyo wofewa. Iye anati: “Dzichitireni chifundo.” Mosakayikira Petro anali ndi zolinga zabwino. Koma Yesu anam’dzudzulabe chifukwa chakuti panthawiyo Petro analola kutsogoleredwa ndi Satana. Petro ‘analibe zinthu za Mulungu m’maganizo mwake koma zinthu za anthu.’​—Mateyu 16:22, 23, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

7. Kodi Yesu analimbikitsa moyo wotani kwa otsatira ake pa Mateyu 16:24?

7 Mawu ofanana ndi amene Petro anauza Yesuwa timawamvanso masiku ano. Nthawi zambiri dzikoli limalimbikitsa anthu ‘kudzichitira chifundo’ kapena ‘kukhala moyo wofewerapo.’ Koma Yesu analimbikitsa maganizo osiyana kotheratu ndi amenewa. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu akufuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsate ine mosalekeza.” (Mateyu 16:24, NW) Buku lakuti The New Interpreter’s Bible, limati: “Sikuti mawu amenewa cholinga chake ndi kulimbikitsa anthu kukhala ophunzira, koma kulimbikitsa omwe anavomera kale chiitano cha Kristu kuganizira mozama za tanthauzo la kukhala wophunzira.” Okhulupirira ayenera kutsatira mfundo zitatu zomwe Yesu anatchula m’lemba limeneli. Tiyeni tikambirane mfundo iliyonse payokha.

8. Fotokozani tanthauzo la kudzikana wekha.

8 Mfundo yoyamba ndi yakuti tiyenera kudzikana tokha. Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “adzikane yekha” amasonyeza kukhala wofunitsitsa kukana maganizo odzikonda kapena odzifunira zabwino zokhazokha. Kudzikana tokha sikutanthauza kungonyalanyaza zosangalatsa zinazake mwa apo ndi apo. Komanso sikutanthauza kudzimana monyanyira kapena kudzikhaulitsa. Popeza kuti timapereka moyo wathu wonse ndi zonse zimene tili nazo kwa Yehova mofunitsitsa, ‘sitikhala a ife tokha.’ (1 Akorinto 6:19, 20) M’malo mokhala ndi moyo wodzikonda, timakhala ndi moyo wokonda kutumikira Mulungu. Kudzikana tokha kumatanthauza kukhala ofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu, ngakhale kuti zimenezi zingasemphane ndi zimene ifeyo patokha mwachibadwa tingakonde kuchita. Timasonyeza kuti tadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse mwa kupereka moyo wathu wonse kwa iye ndi kubatizidwa. Tikatero timayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwathuko moyo wathu wonse.

9. (a) Pamene Yesu anali padziko lapansi, kodi mtengo wozunzikirapo unkaimira chiyani? (b) Kodi timanyamula motani mtengo wathu wozunzikirapo?

9 Mfundo yachiwiri ndi yakuti tiyenera kunyamula mtengo wathu wozunzikirapo. M’zaka 100 zoyambirira, mtengo wozunzikirapo unkaimira kuvutika, kuchititsidwa manyazi, ndiponso imfa. Kawirikawiri, okhawo amene anali zigawenga, ndi omwe anali kuphedwa mwa kuwapachika pa mtengo wozunzikirapo, nthawi zina anali kungopachikapo mitembo yawo. Ndi mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti Mkristu ayenera kukhala wokonzeka kuzunzidwa, kunyozedwa, ngakhalenso kuphedwa kumene, chifukwa chakuti sali mbali ya dziko lapansi. (Yohane 15:18-20) Popeza kuti miyezo yathu yachikristu imatisiyanitsa ndi anthu a m’dzikoli, anthu amenewa ‘angatichitire mwano.’ (1 Petro 4:4) Izi zingachitike kusukulu, kuntchito kwathu, ngakhalenso m’banja mwathu. (Luka 9:23) Komabe, ndife ofunitsitsa kupirira pamene dzikoli likutinyoza chifukwa chakuti sitikukhalanso ndi moyo mwa ife tokha. Yesu ananena kuti: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu m’Mwamba.” (Mateyu 5:11, 12) Ndithudi, kuyanjidwa ndi Mulungu ndicho chinthu chofunika koposa.

10. Kodi n’chiyani chimene chimafunika potsatira Yesu mosalekeza?

10 Mfundo yachitatu ya Yesu Kristu ndi yakuti tiyenera kumutsata mosalekeza. Malinga n’kunena kwa buku lakuti An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine, mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti kutsata amatanthauza kukhala mnzake “woyenda naye limodzi.” Lemba la 1 Yohane 2:6 limati: “Iye wakunena kuti akhala mwa [Mulungu], ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo [Kristu].” Kodi Yesu anayenda motani? Yesu anali kukonda kwambiri Atate wake wakumwamba ndi ophunzira ake, chotero sanali wodzikonda. Paulo analemba kuti: “Kristunso sanadzikondweretsa yekha.” (Aroma 15:3) Yesu anaika patsogolo zosowa za ena mmalo mwa zosowa zake, ngakhale pamene anali wotopa kapena wanjala. (Marko 6:31-34) Yesu analinso kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Ufumu mwakhama kwambiri. Kodi sikoyenera kumutsanzira pamene tikuyesetsa mwakhama kukwaniritsa ntchito yathu ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwaphunzitsa, kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamulira’? (Mateyu 28:19, 20) M’zonse zimene anali kuchita, Kristu anatisiyira chitsanzo, choncho tiyenera ‘kulondola mapazi ake.’​—1 Petro 2:21.

11. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti tidzikane tokha, tinyamule mtengo wathu wozunzikirapo, ndiponso kutsatira Yesu Kristu mosalekeza?

11 M’pofunika kuti tidzikane tokha, tinyamule mtengo wathu wozunzikirapo ndiponso mosalekeza titsatire Kristu, yemwe ndi Chitsanzo chathu. Ngati tichita zimenezi tidzathetsa mtima wodzikonda, umene mosakayikira ungatilepheretse kusonyeza chikondi chodzimana. Komanso, Yesu anati: “Iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?”​—Mateyu 16:25, 26.

Sitingathe Kutumikira Ambuye Awiri

12, 13. (a) Kodi wolamulira wachinyamata amene anafunsa malangizo kwa Yesu ankafuna kudziwa chiyani? (b) Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa mnyamatayo, nanga n’chifukwa chiyani?

12 Patapita miyezi ingapo kuchokera pamene Yesu anatsindika kufunika koti ophunzira ake adzikane okha, wolamulira wachinyamata wachuma anam’fikira ndi kunena kuti: “Mphunzitsi, chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?” Yesu anamuuza kuti ayenera ‘kusunga malamulo’ nthawi zonse, ndipo kenako anatchula ena mwa malamulowo. Mnyamatayo ananena kuti: “Zonsezi ndinazisunga.” Zikuoneka kuti mnyamatayo ananena izi moona mtima ndipo anayesetsa mwakhama kutsatira Chilamulo. Choncho anafunsa kuti: “Ndisowanso chiyani?” Poyankha, Yesu anapatsa mnyamatayo mwayi wapadera kwambiri mwa kumuuza kuti: “Ngati ufuna kukhala wangwiro [“kukwaniritsa zonse,” New American Standard Bible] pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.”​—Mateyu 19:16-21.

13 Yesu anaona kuti mnyamata ameneyu angatumikire Yehova ndi mtima wonse ngati atachotsa chuma chakecho, chomwe chinali chododometsa chachikulu m’moyo wake. Wophunzira weniweni wa Kristu sangathe kutumikira ambuye awiri. ‘Sangathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.’ (Mateyu 6:24) Afunika kukhala ndi ‘diso la kumodzi’ lolunjika pa zinthu zauzimu. (Mateyu 6:22) Kutenga chuma chonse ndi kuchipereka kwa anthu osauka kungakhaledi kudzimana. Pouza wolamulira wachinyamata uja kuti apereke chuma chake chonse kwa ena, Yesu anapatsa wolamulirayo mwayi wamtengo wapatali wokundika chuma kumwamba. Chuma chimenechi chikanam’thandiza kupeza moyo wosatha ndiponso kum’patsa chiyembekezo cha m’tsogolo chodzalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba. Komatu mnyamatayu sanathe kudzikana yekha. “Anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.” (Mateyu 19:22) Komabe, otsatira ena a Yesu anachita zosiyana ndi zimenezo.

14. Kodi asodzi anayi anachitanji Yesu atawaitana kuti amutsate?

14 Pafupifupi zaka ziwiri izi zisanachitike, Yesu anapereka chiitano chofanana ndi chimenechi kwa asodzi anayi omwe ndi Petro, Andreya, Yakobo ndi Yohane. Panthawiyi, n’kuti awiri mwa amuna amenewa akusodza, ndipo awiri enawo anali kusoka maukonde awo. Yesu anawauza kuti: “Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Pambuyo pake anayi onsewo anasiya ntchito yawo yopha nsomba ndi kukhala otsatira a Yesu kwa moyo wawo wonse.​—Mateyu 4:18-22.

15. Kodi Mboni ya Yehova ina yamakono inadzimana motani kuti itsatire Yesu?

15 Akristu ambiri lerolino atsanzira chitsanzo cha asodzi anayiwo osati wolamulira wachinyamata wachuma uja. Pofuna kutumikira Yehova, iwo apewa kudzikundikira chuma ndi kudzipangira dzina m’dzikoli. Deborah ananena kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 22, ndinafunikira kusankha chochita pa nkhani yaikulu.” Ndiyeno anafotokoza kuti: “Ndinali nditaphunzira Baibulo kwa pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ndinkafuna kupereka moyo wanga kwa Yehova, koma achibale anga sankagwirizana nazo m’pang’ono pomwe. Popeza kuti anali ampondamatiki, ankaganiza kuti adzanyozeka kwabasi ngati ine nditakhala wa Mboni. Chotero anandipatsa maola 24 kuti ndisankhe ngati ndikufuna moyo wa mwanaalirenji kapena choonadi. Iwo ananeneratu kuti ndikapitiriza kugwirizana ndi Mboni, sadzandionanso ngati mbale wawo. Koma Yehova anandithandiza kusankha moyenera ndipo anandipatsa nyonga kuti ndichite mogwirizana ndi chosankha chimenecho. Ndakhala ndikuchita utumiki wanthawi zonse kwa zaka 42 tsopano, ndipo sindikunong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Mwa kukana moyo wodzikonda, wongofuna zosangalatsa, ndinathawa moyo wopanda tanthauzo ndi wosowa chimwemwe womwe ndikuuona mwa achibale angawo. Ine limodzi ndi mwamuna wanga, tathandiza anthu oposa 100 kuphunzira choonadi. Ana auzimu amenewa ndi amtengo wapatali kwa ine kuposa chuma chilichonse.” Ndi mmenenso mamiliyoni ena a Mboni za Yehova akuonera. Nanga inuyo mukuona bwanji?

16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitikukhalanso ndi moyo mwa ife tokha?

16 Mtima wofunitsitsa kusakhalanso ndi moyo mwa iwo okha, walimbikitsa Mboni za Yehova mazanamazana kutumikira monga apainiya, kapena kuti olengeza Ufumu anthawi zonse. Ena amene sangathe kuchita utumiki wanthawi zonse chifukwa cha zovuta zina, akulitsa mzimu wa upainiya ndipo ayesetsa kuthandiza nawo pa ntchito yolalikira Ufumu. Makolo nawonso amasonyeza mzimu wofananawo mwa kuthera nthawi yawo yochuluka kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu ndiponso amadzimana kuti akwaniritse udindo umenewu. Mwa njira inayake, tonsefe tingasonyeze kuti timaika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wathu.​—Mateyu 6:33.

Kodi Ndi Chikondi cha Ndani Chimene Chimatikakamiza?

17. N’chiyani chimatilimbikitsa kukhala odzimana?

17 Kusonyeza chikondi chodzimana sikophweka. Komano ganizirani chimene chimatikakamiza kuchita zimenezo. Paulo analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse . . . Ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) Chikondi cha Kristu n’chimene chimatikakamiza kusakhalanso ndi moyo mwa ife tokha. Chimatilimbikitsa kwabasi kukhala odzimana. Popeza kuti Yesu anatifera, kodi sitikuona kuti sitingachitire mwina koma kukhala ndi moyo mwa iye? Ndipotu mofunitsitsa tinapereka miyoyo yathu kwa Mulungu ndi kukhala ophunzira a Kristu, posonyeza kuyamikira chikondi chakuya chimene Mulungu ndi Kristu anatisonyeza.​—Yohane 3:16; 1 Yohane 4:10, 11.

18. N’chifukwa chiyani kudzimana kuli kopindulitsa?

18 Kodi kusakhalanso ndi moyo mwa ife tokha kuli ndi phindu lililonse? Mnyamata wachuma uja atakana chiitano cha Kristu ndi kuchoka, Petro anafunsa Yesu kuti: “Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?” (Mateyu 19:27) Petro ndi ophunzira enawo analidi atadzikana okha. Kodi mphoto yawo inali chiyani? Choyamba Yesu anawauza za mwayi umene adzakhala nawo wolamulira naye limodzi kumwamba. (Mateyu 19:28) Panthawi imodzimodziyo, Yesu anatchulanso madalitso omwe otsatira ake onse adzasangalala nawo. Iye anati: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi ino . . . ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha.” (Marko 10:29, 30) Timalandira zochuluka kuposa zimene tadzimana. Kodi atate athu, amayi athu, abale athu, alongo athu komanso ana athu auzimu si amtengo wapatali kuposa chilichonse chimene tasiya chifukwa cha Ufumu? Kodi ndani amene anali ndi moyo wopindulitsa kwambiri pakati pa Petro ndi wolamulira wachinyamata wachuma uja?

19. (a) Kodi chimwemwe chenicheni tingachipeze bwanji? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana zotani?

19 Mwa mawu ndi zochita zake, Yesu anasonyeza kuti kugawira ena ndi kuwatumikira n’zomwe zimadzetsa chimwemwe, osati kudzikonda. (Mateyu 20:28; Machitidwe 20:35) Tikapanda kukhalanso ndi moyo mwa ife tokha, ndiyeno n’kumatsatira Kristu mosalekeza, timakhutira nawo kwambiri moyo panopa, ndipo timakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’tsogolo. Inde, tikadzikana tokha, timakhala Ake a Yehova. Chotero timakhala akapolo a Mulungu. N’chifukwa chiyani ukapolo umenewu uli wopindulitsa? Kodi umakhudza motani zinthu zimene timasankha kuchita m’moyo? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tifunika kuthetsa mtima wathu wodzikonda?

• Kodi kudzikana tokha, kunyamula mtengo wathu wozunzikirapo, ndi kutsatira Yesu mosalekeza zimatanthauzanji?

• N’chiyani chimene chimatilimbikitsa kusakhalanso ndi moyo mwa ife tokha?

• N’chifukwa chiyani kukhala moyo wodzimana kuli kopindulitsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

“Dzichitireni chifundo, Ambuye”

[Chithunzi patsamba 13]

N’chiyani chomwe chinalepheretsa wolamulira wachinyamatayu kutsatira Yesu?

[Zithunzi patsamba 15]

Chikondi chimakakamiza Mboni za Yehova kukhala olengeza Ufumu achangu