Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Anthu Oyenerera M’madera a Kumidzi ku Australia

Kufunafuna Anthu Oyenerera M’madera a Kumidzi ku Australia

Olengeza Ufumu Akusimba

Kufunafuna Anthu Oyenerera M’madera a Kumidzi ku Australia

M’KATIKATI mwa dziko la Australia muli chigawo chachikulu kwambiri chimene chili ndi madera akumidzi. Ena mwa maderawa anali asanalalikidwepo kwa zaka 12. Motero Mboni za Yehova za mumzinda wa Darwin, womwe uli likulu la chigawo cha kumpoto kwa dzikoli, zinakonza ntchito ya masiku naini yofunafuna anthu oyenerera uthenga wabwino.​—Mateyu 10:11.

Anthuwa anakhala akukonzekera ntchitoyi kwa chaka chathunthu, ndipo anakonzeratu mapu a dera lalikulu masikweya kilomita oposa 800,000, pafupifupi kasanu ndi kawiri kuyerekezera ndi dziko la Malawi. Derali lili kutali kwambiri ndi madera ena ndipo kuti mumvetse mfundo imeneyi, ingoganizirani kuti misewu yambiri yochoka mumsewu waukulu kukafika ku mafamu oweterako ng’ombe a m’derali imakhala yaitali makilomita oposa 30. Komanso mafamu ena n’ngotalikirana mtunda wokwana mwina mpaka makilomita 300.

Mboni zokwana 145 zinadzipereka kukagwira nawo ntchitoyi. Ena anachokera kutali kwambiri, monga ku Tasmania. Ena anabwera pamagalimoto otha kuyenda mosavuta m’misewu ya matope atalongedzamo katundu yense woyenera ulendo wokagona panja. Analongedzamonso masipeyala ndiponso mafuta a galimoto. Anthu ena katundu wawo anamuika m’ngolo za magalimoto awo. Kuphatikizanso apo, anachita hayala maminibasi awiri a mipando yokwana anthu 22 kuti anyamule anthu amene analibe magalimoto otha kuyenda m’misewu ya matope. Anthu amene ankayenda m’maminibasiwo ankalalikira makamaka kwa anthu okhala m’matauni ang’onoang’ono a m’madera enaake.

Asananyamuke paulendowu, abalewo anakonza nkhani ndiponso zitsanzo za mmene angakalalikirire uthenga wabwino m’dera lachilendoli. Mwachitsanzo, kuti munthu alalikire bwinobwino m’midzi ya anthu amtundu wa Aborigine amafunika kuti azichita zinthu mogwirizana ndi mwambo wa anthuwa. Komanso anakambirana zoyenera kuchita kuti asawononge zachilengedwe.

Mbonizi zinakumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa. Mwachitsanzo, pamudzi wina wa anthu amtundu wa Aborigine, abale anakonza zokakamba nkhani ya onse yochokera m’Baibulo. Mfumukazi ya m’mudziwo inapita yokha kukauza anthu za nkhaniyi. Kenaka a Mboniwo anapereka mabuku 5 ndiponso timabuku 41 kwa anthu amene anabwera pamsonkhanopo. Pamudzi wina anapeza munthu wina wamtunduwu. Iyeyu anali ndi Baibulo lakelake la King James Version, koma linali lakale ndiponso long’ambikang’ambika. Atamufunsa ngati akudziwa dzina la Mulungu, iye anavomera ndipo anapisa m’jekete mwake n’kutulutsa magazini ina yakale ya Nsanja ya Olonda. Munthuyo anawerenga lemba lomwe linali m’magaziniyi la Marko 12:30, lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse.” Iye anati: “Lemba limeneli ndimalikonda kwambiri.” Atakambirana naye za m’Baibulo kwa nthawi yaitali, anam’patsa Baibulo latsopano ndiponso mabuku ena ofotokoza Baibulo.

Kufupi ndi ku Gulf of Carpentaria, mkulu woyang’anira famu ya ng’ombe ya maekala wani miliyoni anachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Atamusonyeza buku la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndiponso la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, * iye anafunsa ngati angapeze mabuku aliwonse a m’chinenero cha Kriol. Izi zinali zodabwitsa chifukwa ngakhale kuti anthu ambiri amtundu wa Aborigine amalankhula chinenero cha Kriol, ndi ochepa chabe amene amatha kuwerenga chinenerochi. Koma panapezeka kuti anthu onse 50 amene amagwira ntchito pa famupo amatha kuwerenga chinenerochi. Mkulu woyang’anira pamalopo anasangalala kulandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero cha Kriol, ndipo anapereka nambala yake ya telefoni kuti adzathe kumupezanso.

Pamasiku naini amene anakhala akulalikira mwakhama, anagawira mabaibulo 120, mabuku 770, magazini 705, ndiponso timabuku 1,965. Kuphatikizanso apo, anachita maulendo obwereza 720 ndiponso anachititsa maphunziro a Baibulo 215.

N’zoona kuti njala yauzimu ya anthu ambiri oyenerera uthenga wabwino amene amakhala m’madera osiyanasiyana otalikirana a m’chigawo chachikulu chimenechi inathetsedwa.​—Mateyu 5:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AUSTRALIA

CHIGAWO CHAKUMPOTO

Darwin

Gulf of Carpentaria

Sydney

TASMANIA