Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo, Tetezani Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali

Makolo, Tetezani Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali

Makolo, Tetezani Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali

“Nzeru itchinjiriza . . . isunga moyo wa eni ake.”​MLALIKI 7:12.

1. Kodi n’chifukwa chiyani makolo ayenera kuona kuti ana awo ndi mphatso?

MAKOLO amabereka mwana amene amakhala wofanana nawo maonekedwe ndiponso zochitika. Baibulo limati anawa ndi “cholandira [kapena kuti cholowa] cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Popeza kuti Yehova ndiye kwenikweni ali Wopatsa Moyo, makolo akakhala ndi mwana, ndiye kuti kwenikweni Yehova amakhala atangowaikiza mwanayo. (Salmo 36:9) Makolonu, kodi mphatso yanu yamtengo wapatali yochokera kwa Mulunguyi mumaiona bwanji?

2. Kodi Manowa anatani atamva kuti akhala ndi mwana?

2 Ndithu, mphatso yotereyi n’njoyenera kuilandira modzichepetsa ndiponso moyamikira. Izi n’zimene Mwiisrayeli wina dzina lake Manowa anachita zaka 3,000 zapitazo, mkazi wake atauzidwa ndi mngelo kuti abereka mwana. Atamva nkhani yabwinoyi Manowa anapemphera motere: “Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudam’tumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.” (Oweruza 13:8) Kodi makolo mungaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Manowachi?

Chifukwa Chake Kuthandizidwa ndi Mulungu Kukufunikira Panopa

3. N’chifukwa chiyani kuthandizidwa ndi Mulungu polera ana kuli kofunika kwambiri makamaka masiku ano?

3 Panopa, kusiyana ndi m’mbuyo monsemu, m’pamene makamaka makolo akufunikira kwambiri kuthandizidwa ndi Yehova polera ana awo. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti Satana Mdyerekezi ndi angelo ake anaponyedwa pansi pano kuchoka kumwamba. Baibulo limatichenjeza kuti: “Tsoka mtunda . . . chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kam’tsalira kanthawi.” (Chivumbulutso 12:7-9, 12) Baibulo limati “monga mkango wobuma,” Satana ‘akufunafuna wina am’likwire.’ (1 Petro 5:8) Nthawi zambiri mikango imasaka nyama zosavuta kugwira, makamaka zimene zidakali zazing’ono. Motero, mwanzeru, makolo achikristu amadalira malangizo a Yehova pofuna kuteteza ana awo. Kodi inuyo mwachitapo khama lotani kuti muteteze ana anu?

4. (a) Kodi makolo angachite zotani atadziwa kuti mkango ukuyendayenda m’dera limene akukhala? (b) Kodi ana amafunikira chiyani kuti atetezedwe?

4 Ngati mutadziwa kuti m’dera lanulo muli mkango umene ukuyendayenda, n’zosachita kufunsa kuti ana anu mungawateteze kwambiri. Satana n’chilombo cholusa. Iye amafuna kuwononga makhalidwe a anthu a Mulungu kuti Mulunguyo asiye kuwayanja. (Yobu 2:1-7; 1 Yohane 5:19) Ana n’ngosavuta kugwira. Kuti azembe misampha ya Mdyerekezi, ana ayenera kudziwa Yehova ndiponso kumumvera. Motero ayenera kuphunzira Baibulo. Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Chinanso n’chakuti, ana amafunikira nzeru, kapena kuti luso lomatha kumvetsetsa ndiponso kugwiritsira ntchito zimene akuphunzira. Popeza kuti “nzeru isunga moyo wa eni ake,” makolonu muyenera kuchinyiza choonadi m’mitima ya ana anu. (Mlaliki 7:12) Kodi mungachite bwanji zimenezi?

5. (a) Kodi munthu angaphunzitsidwe bwanji kukhala ndi nzeru? (b) Kodi buku la Miyambo limalongosola motani kufunika kwa nzeru?

5 Makolo, inuyo mungathe kumawawerengera ana anu Mawu a Mulungu ndipotu dziwani kuti muyenera kumatero. Komano kuti muthandize ana kumvera Yehova m’pofunikanso kuti anawo azimvetsetsa zimene mukuwauzazo. Mwachitsanzo, mwana angauzidwe kuti asamawoloke msewu asanayang’ane mbali zonse ziwiri. Koma pali ana ena amene samvera zimenezi. Kodi samvera chifukwa chiyani? N’kutheka kuti anawo sankawalongosolera kawirikawiri za kuopsa kogundidwa ndi galimoto, kapena sankawalongosolera zimenezi m’njira yoti anawo aonedi kuopsa kwake, n’kuthana ndi “utsiru” umene ungadzawachititse ngozi. Kuphunzitsa munthu kuti akhale ndi nzeru kumatenga nthawi, komanso kumafuna kuleza mtima kwambiri. Komatu nzeru n’zofunika kwambiri. Ponena za nzeru, Baibulo limati: “Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira n’ngodala.”​—Miyambo 3:13-18; 22:15.

Kuphunzitsa M’njira Yopatsa Nzeru

6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zambiri ana amachita zinthu mopanda nzeru? (b) Kodi ndi nkhondo yanji imene ikuchitika?

6 Nthawi zambiri ana amachita zinthu zolakwika, osati chifukwa choti sanaphunzitsidwe zoyenerera, koma chifukwa choti zimene anaphunzitsidwazo sizinawakhudze mtima. Mdyerekezi akumenya nkhondo yofuna kulanda mitima ya ana. Iye amatero poyesetsa kuwaipitsa maganizo ndi zinthu zoipa za m’dzikoli. Komanso poti anawa anatengera chibadwa chokonda zinthu zoipa, Mdyerekezi amatengeraponso mwayi pamenepa. (Genesis 8:21; Salmo 51:5) Makolo ayenera kuzindikira kuti ali pankhondo yeniyeni yolimbirana mitima ya ana awo.

7. Kodi n’chifukwa chiyani sizokwanira kungomuuza mwana kuti zakuti n’zoyenera koma zakuti n’zosayenera?

7 Nthawi zambiri makolo amangouza mwana kuti zakuti n’zoyenerera koma zakuti n’zosayenerera, ndipo akatero amaganiza kuti mwanayo watolapo kanthu. Angathe kumuuza mwanayo kuti kunama, kuba, kapena kugonana ndi aliyense amene sanakwatirane naye n’kulakwa. Komatu, mwanayo amafunikira kudziwa zifukwa zamphamvu zotsatirira mfundo zimenezi, osati chifukwa chongoti makolo ake anena choncho ayi. Amenewatu ndi malamulo a Yehova. Motero mwanayo ayenera kuphunzira kuti kumvera malamulo a Mulungu ndiko chinthu chanzeru.​—Miyambo 6:16-19; Ahebri 13:4.

8. Kodi ndi kuphunzitsa m’njira yotani kumene kungathandize ana kuchita zinthu mwanzeru?

8 Mwana wamng’ono tingamuthandize kuona kuti pali Mlengi wanzeru zakuya mosaneneka, pomuuza za zinthu monga chilengedwe chonse chovuta kufotokozachi, kuchuluka kwa mitundu ya zinthu zamoyo zosiyanasiyana, ndiponso kusinthasintha kwa nyengo pachaka. (Aroma 1:20; Ahebri 3:4) Kuphatikiza apo, mwanayo ayenera kuphunzitsidwa kuti Mulungu amam’konda ndipo wakonza njira yomupatsira iyeyo moyo wosatha kudzera mwa nsembe ya Mwana Wake, ndiponso kuti iyeyo angasangalatse Mulungu pomvera zimene Mulunguyo amanena. Tikatero n’zosakayikitsa kuti mwanayo angayambe kutumikira Yehova, ngakhale pamene Mdyerekezi akuyesa kumuletsa kutero.​—Miyambo 22:6; 27:11; Yohane 3:16.

9. (a) Kodi kuphunzitsa kopulumutsa moyo kumafunika chiyani? (b) Kodi abambo akulangizidwa chiyani, ndipo kodi ayenera kutani kuti akwaniritse zimenezi?

9 Kuphunzitsa kumene kumateteza mwana ndi kumulimbikitsa kuchita zinthu zabwino kumafunika nthawi, kuikirapo mtima, ndiponso kukonzekera bwino. Kumafunanso kuti makolo azikhala ndi mtima wofuna kutsatira malangizo a Mulungu. Baibulo limati: “Atate inu, . . . muwalere [ana anu] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mawu akuti “chilangizo,” mu Chigiriki choyambirira amatanthauza kuti “kuikamo maganizo.” Motero, kwenikweni lembali likulimbikitsa abambo kuika maganizo a Yehova m’maganizo mwa ana awo. Ndithu, zimenezi zingawateteze kwambiri anawo. Mukachinyiza maganizo a Mulungu m’maganizo a ana anu, anawo amatetezedwa ku makhalidwe oipa.

Muziphunzitsa Ana Chifukwa Chowakonda

10. Kuti mwana wanu mumulangize bwino, kodi muyenera kudziwa chiyani?

10 Komabe, kuti mukwanitse kulera bwino ana, muyenera kumachita zinthu chifukwa chowakonda. Kulankhulana bwino kungakuthandizeni kwambiri pankhani imeneyi. Dziwani zinthu zimene mwana wanu akukumana nazo m’moyo komanso dziwani maganizo ake. Pezani njira yom’chititsa mwana wanuyo kukhala womasuka kunena bwinobwino zakukhosi kwake. Nthawi zina mungadzidzimuke kwambiri kumva zimene mwanayo akukuuzani. Samalani kuti musachite zinthu mothamanga magazi. M’malo mwake, mvetserani mosonyeza kuti mukumumvetsa.

11. Kodi makolo angaike bwanji maganizo a Mulungu m’maganizo a mwana?

11 N’zoona kuti mwina ana anu munawawerengerapo malemba a m’Baibulo onena za malamulo a Mulungu oletsa kugonana ndi munthu amene sanakwatirane naye, ndipo mwina munatero kangapo konse. (1 Akorinto 6:18; Aefeso 5:5) Zimenezi ziyenera kuti zinathandiza ana anuwo kumvetsa zinthu zimene Yehova amasangalala nazo ndi zimene sasangalala nazo. Komano mukangotero basi sindiye kuti mwaika maganizo a Yehova m’maganizo mwa anawo. Ana amafuna kuwathandiza kuti athe kuona kufunikira kwa malamulo a Yehova. Ayenera kukhutira kuti malamulo ake n’ngolondola komanso n’ngabwino ndiponso kuti kumvera malamulowa n’koyenerera ndipo kumasonyeza kuti munthuwe uli ndi chikondi. Ngati mutawathandiza anawo kumvetsetsa Malemba mpaka kufika pozindikira kaganizidwe ka Mulungu, ndiye kuti mwakwanitsadi kuika maganizo ake m’maganizo awo.

12. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuona nkhani ya kugonana m’njira yoyenera?

12 Pokambirana za kugonana, mungafunse kuti, “Kodi ukuganiza kuti kumvera lamulo la Yehova lakuti osagonana ndi munthu aliyense usanakwatirane naye kungachititse kuti munthu asamasangalale?” Akayankha, mufunseni kuti alongosole bwinobwino yankho lakelo. Mulongosolereni za mphatso yodabwitsa yobereka ana imene Mulungu anapereka ndipo kenaka mungamufunse kuti: “Kodi iweyo ukuganiza kuti Mulungu amene amatikonda chonchiyu angapange malamulo otimanitsa zabwino m’moyo? Kapena kodi ukuona kuti malamulo ake amatipatsa chimwemwe ndiponso amatiteteza?” (Salmo 119:1, 2; Yesaya 48:17) Dziwani zimene mwana wanuyo akuganiza pankhani imeneyi. Ndiyeno mungapereke zitsanzo zosonyeza mavuto amene amabwera chifukwa chogonana ndi munthu amene sunakwatirane naye. (2 Samueli 13:1-33) Pokambirana ndi mwana wanuyo m’njira yakuti amvetsetse ndiponso kuti akhutire kuti maganizo a Mulungu n’ngoyeneradi kuwatsatira, mungamuthandize kwambiri kuika maganizo a Mulungu m’maganizo ake. Komabe, pali zinthu zinanso zimene mungachite.

13. Kodi n’chiyani makamaka chimene mwana ayenera kumvetsetsa kuti athe kumamvera Yehova?

13 Ndi chinthu chanzeru kumuphunzitsa mwana wanuyo zimene zimachitika munthu akapanda kumvera Yehova komanso kumuphunzitsa mmene Yehova amakhudzidwira ndi zochita zathu. Musonyezeni zimene Baibulo limanena, zosonyeza kuti tingathe kum’pweteketsa mtima Yehova tikapanda kuchita zimene akufuna. (Salmo 78:41) Kenaka mungamufunse kuti, “N’chifukwa chiyani iweyo sufuna kum’pweketsa mtima Yehova?” ndipo longosolani kuti: “Satana, yemwe ali mdani wa Mulungu, amanena kuti anthufe timatumikira Yehova pazifukwa zongotikomera ifeyo koma osati chifukwa choti timamukonda Yehovayo.” Kenaka longosolani kuti pochita zinthu mokhulupirika, Yobu anasangalatsa mtima wa Mulungu, motero anatsutsa bodza la Satanali. (Yobu 1:9-11; 27:5) Mwana wanu ayenera kumvetsetsa mfundo yakuti angathe kusangalatsa kapena kukwiyitsa Yehova malingana ndi zochita zake. (Miyambo 27:11) Ana angaphunzitsidwe zimenezi ndiponso zinthu zina zambiri zofunika kwabasi pogwiritsira ntchito buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. *

Zotsatirapo Zosangalatsa

14, 15. (a) Kodi ndi maphunziro otani a m’buku la Mphunzitsi amene alimbikitsa ana? (b) Kodi ndi zinthu zabwino zotani zimene mwapeza pogwiritsira ntchito bukuli? (Onaninso bokosi lomwe lili patsamba 18 ndi 19.)

14 Agogo ena aamuna ku Croatia amene amawerenga buku la Mphunzitsi pamodzi ndi mdzukulu wawo wamwamuna wa zaka seveni analemba kuti mwanayo anawauza nkhani yotsatirayi: “Amayi anandituma, koma ndinakana. Kenaka ndinakumbukira mutu wakuti ‘Kumvera Kudzakuteteza,’ motero ndinabwerera n’kukawauza kuti ndichita zimene anditumazo.” Mwamuna wina ndi mkazi wake, omwe amakhala ku Florida, m’dziko la America ananena izi pofotokoza za mutu wakuti “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza.” Iwo anati: “Mutu umenewu uli ndi mafunso amene amathandiza ana kunena za mumtima mwawo ndi kuvomereza zolakwa zimene sakanavomereza.”

15 Buku la Mphunzitsi lili ndi zithunzi zopitirira 230, ndipo pansi pa chithunzi chilichonse, kapena gulu la zithunzi pali mawu olongosola zithunzizo. Mayi wina ananena izi poyamikira: “Nthawi zambiri mwana wanga amangoti maso dwii kuyang’ana chithunzi chinachake ndipo safuna kutsegula tsamba lina. Zithunzi zake n’zokongola komanso zithunzizo pazokha zimaphunzitsa anawo chinachake kapenanso kuwachititsa kufunsa mafunso. Ataona chithunzi chimene chili ndi mwana akuonera wailesi ya kanema m’chipinda chamdima, mwana wanga anafunsa kuti, ‘Amama, kodi uyuyu akutani apapa?’ Ndipo anafunsa mosonyeza kuti akudziwa kuti mwanayo akuchita zinazake zosayenera.” Mawu a pansi pa chithunzichi amati: “Kodi ndani amene amaona zonse zimene timachita?”

Maphunziro Ofunika Masiku Ano

16. Kodi ana masiku ano amafunika kuwaphunzitsa nkhani yofunika yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

16 Ana amafunika kudziwa njira yoyenera ndi yosayenera yogwiritsira ntchito maliseche awo. Komano nthawi zambiri nkhani imeneyi imavuta kukambirana. Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala ananena kuti panthawi imene iyeyo anali mwana, anthu ankaona kuti mawu aliwonse otchula za maliseche n’ngotukwana. Ndiye pankhani yophunzitsa ana ake, iye anati: “Ndiyenera kuyesetsa kuthetsa manyazi angawa.” Komatu dziwani kuti ana athu satetezeka ifeyo tikamachita manyazi kukambirana nawo nkhani ya kugonana. Kunja kuno kuli achidyamakanda amene amapezerera ana osadziwa zinthu. Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso limalongosola nkhaniyi mosachititsa manyazi komanso mwaulemu. Kuwafotokozera ana nkhani ya kugonana si kuwasokoneza ayi, komano kusawauza nkhaniyi n’kumene kungawasokonezedi.

17. Kodi buku la Mphunzitsi limathandiza bwanji makolo kuphunzitsa ana awo nkhani ya kugonana?

17 M’mutu 10, pokambirana za angelo oipa amene anabwera padziko lapansi n’kubala ana, bukuli limafunsa mwanayo funso lakuti, “Kodi umadziwapo chiyani za kugonana?” Bukuli limayankha funsoli m’njira yosavuta kumvetsa komanso yosachititsa manyazi. Kenaka, mutu 32 umalongosola mmene ana angatetezedwere kwa achidyamakanda. Talandira makalata ambiri onena kuti kuphunzitsa ana zimenezi n’kofunika kwambiri. Mayi wina analemba kuti: “Mlungu watha, ineyo ndi mwana wanga wamwamuna, Javan, tinapita kwa dokotala wa ana, ndipo dokotalayo anandifunsa ngati mwana wanga ndinakambirana naye nkhani ya kugwiritsira ntchito maliseche m’njira yoyenerera. Dokotalayo anachita chidwi kwambiri nditamuuza kuti tinakambirana nkhaniyi pogwiritsira ntchito buku lathu latsopanoli.”

18. Kodi buku la Mphunzitsi limalongosola motani nkhani ya kulambira zizindikiro za dziko, monga mbendera?

18 Mutu wina umanena za nkhani ya m’Baibulo ya anyamata atatu achihebri, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anakana kugwadira fano loimira boma la Babulo. (Danieli 3:1-30) Anthu ena sangaone kugwirizana kulikonse pakati pa kulambira fano ndi kuchitira sawatcha mbendera, monga mmene anasonyezera m’buku la Mphunzitsi. Komabe, taonani zimene wolemba mabuku wina dzina lake Edward Gaffney ananena poyankha mafunso a atolankhani a magazini ya U.S. Catholic. Iye analongosola kuti mwana wake wamkazi atapita kusukulu tsiku loyamba anadzamuuza kuti “kusukuluko waphunzirako pemphero latsopano.” Iye anamufunsa mwanayo kuti anene pempherolo. Popitiriza nkhaniyi, Gaffney anati: “Iye anaika dzanja lake pamtima n’kuyamba kunena kuti, ‘Ndikulumbira kuti ndidzalemekeza mbendera ya dziko lathu . . . ’ Nthawi yomweyo ndinazindikira mfundo yofunika. Mfundo yakuti a Mboni za Yehova aja amanena zoona. M’masukulu mwathumu ana akuphunzitsidwa adakali aang’ono kwambiri kuti azilambira dziko lawo, ndipo akuphunzitsidwa kukhala okhulupirika ku dziko lawo popanda malire aliwonse.”

M’poyeneradi Khama

19. Kodi kuphunzitsa ana kumabweretsa mphoto zotani?

19 Ndithudi, muyenera kuchita khama kwambiri pophunzitsa ana anu. Mayi wina wa ku Kansas, ku United States analira misozi yachimwemwe atalandira kalata yochokera kwa mwana wake wamwamuna. Iye analemba kuti: “Ndimaona kuti ndili ndi mwayi kwabasi kuti munandilera bwino kwambiri moti ndine munthu wamaganizo olongosoka. Inuyo ndi bambo munagwira ntchito kwambiri, zikomo.” (Miyambo 31:28) Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso lingathandize makolo ambiri kuphunzitsa ana awo n’cholinga choti awateteze anawo, omwe ndi cholowa chamtengo wapatali kwambiri.

20. Kodi makolo sayenera kuiwala chiyani nthawi zonse, ndipo kodi zimenezi ziyenera kuwakhudza motani?

20 Ana athu amafunikira kuti tiziyesetsa kwambiri kukhala nawo nthawi yaitali, kuchita nawo chidwi kwambiri, ndiponso kuwaikirapo mtima kwambiri. Ana amakhala aang’ono kwa kanthawi kochepa chabe. Yesetsani kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kukhala nawo ndi kuwathandiza. Simudzanong’oneza bondo chifukwa chochita zimenezi. Ndipo anawo adzafika pomakukondani kwambiri. Nthawi zonse musamaiwale kuti ana anuwo ndi mphatso imene Mulungu anakupatsani. Ndithu, ana ndi cholowa chamtengo wapatali kwambiri. (Salmo 127:3-5) Motero muziwasamalira mosonyeza kuti mukudziwa zimenezi komanso mokhala ngati kuti Mulungu akuona mmene mukuwalerera, ndipotu zoona zake n’zakuti Mulungu akuonadi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Onani mutu 40, wakuti “Zimene Tingachite Kuti Tikondweretse Mulungu.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani makolo akufunika kuteteza ana makamaka panopa?

• Kodi ndi kuphunzitsa m’njira yotani kumene kumapatsa nzeru?

• Kodi ndi zinthu zotani zofunika kukambirana ndi ana anu masiku ano?

• Kodi buku la Mphunzitsi lathandiza bwanji makolo kuphunzitsa ana awo?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 18, 19]

Buku la Aliyense

Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso analilemba kuti lithandize makolo kapena achikulire ena kuti aziwerenga ndi kukambirana ndi ana awo zimene Yesu Kristu anaphunzitsa. Komatu anthu achikulire amene awerenga bukuli pawokha ayamikira kwambiri zimene aphunziramo.

Bambo wina wa ku Texas, ku United States, anati: “Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso limalongosola zinthu mosavuta kumvetsa, motero limatilimbikitsa ngakhale titakhala achikulire a zaka 76, monga ndilili inemu. Zikomo kwambiri. Ndikuthokoza monga munthu amene wakhala akutumikira Yehova kuyambira ali mwana.”

Wowerenga wina wa ku London, ku England anati: “Ndithu, zithunzi zokongola za m’bukuli zikopa kwambiri makolo ndiponso ana. Bukuli lili ndi mafunso ochititsa chidwi ndipo analikonza bwino kwabasi, komanso n’zosangalatsa kwambiri kuona kuti limafotokoza nkhani zovuta kukambirana, mwachitsanzo nkhani ya pa mutu 32, wakuti “Mmene Yesu Anatetezedwera.’” Iye anamaliza motere: “Inde, bukuli kwenikweni analembera ana a Mboni za Yehova, komabe ndikuona kuti aphunzitsi ndiponso anthu ena angasangalale kwambiri atakhala nalo. Ndikhala ndikuligwiritsira ntchito kwambiri masiku akubwerawa.”

Mayi wina wa ku Massachusetts, ku United States anatchulapo za zithunzi zambirimbiri ndipo iye anati zithunzi zimenezi “anazikonza moganizira kwambiri.” Iye anati: “Ndinaona kuti ngakhale kuti bukuli anakonzera ana, zimene analongosolamo zingathandizenso anthu aakulufe kuganizira za ubwenzi wathu ndi Yehova.”

Mayi wina wa ku Maine ku United States anati: “Eee, ndagoma! Buku limeneli si pano ayi! Si kuti ndi buku la ana aang’ono okha ayi, koma ndi la ana a Mulungu tonsefe. Lachita kundifika pamtima penipeni ndipo landiimitsa mutu kwinaku n’kundikhazika mtima pansi komanso n’kundipatsa mtendere. Ndayamba kumukonda kwambiri Yehova ngati Atate wanga. Wandichotsera zowawa zanga za m’mbuyo monsemu ndipo cholinga chake wachimveketsa bwino kwambiri.” Mayiyu anamaliza motere: “Ndikuuza aliyense kuti, ‘Ndithu, bukuli muliwerenge basi.’”

Mayi wina wa mumzinda wa Kyoto, ku Japan, analongosola kuti pamene anali kuwerenga bukuli ndi zidzukulu zake, zidzukuluzo zinkamufunsa mafunso, monga akuti: “‘Kodi mwana uyuyu akutani apapa? Mtsikana uyuyu walakwa chiyani kuti am’kalipire? Nanga amayi awawa akutani? Nangano mkango uwuwu ukutani?’ Bukuli limaphunzitsa zinthu zimene timachita nazo chidwi, motero ndimalikonda kwambiri kuposa buku lina lililonse limene ndingalipeze ku laibulale.”

Bambo wina wa mumzinda wa Calgary, ku Canada, anati atangolandira bukuli, anayamba kuliwerenga pamodzi ndi mwana wake wamkazi wa zaka sikisi ndiponso mwana wake wamwamuna wa zaka naini. Bamboyu anati: “Posakhalitsa ndinaona kuti zinthu zinayamba kuyenda bwino kwambiri. Ana angawo anayamba kumvetsera mwatcheru ndiponso kuyankha mafunso mochokera pansi pamtima. Anayamba kuona kuti iwowo ali ndi mbali yawo pa phunzirolo. Chinanso, phunziroli linawapatsa mwayi wolongosola zakukhosi kwawo. Anawa anayamba kusangalala kwambiri, ndipo wamkaziyo ananena kuti akufuna aziphunzira buku latsopanoli usiku uliwonse.”

Tsiku lina atamaliza kuphunzira bukuli, bamboyo anati: “Ndinakambirana ndi mwana wanga wamwamuna kwa maola ambiri za Yehova ndiponso zolinga zake. Iye anandifunsa mafunso ambiri okhudza nkhani za m’bukuli. Ndinatuluka misozi mwanayu atanditsanzika kuti akukagona kenaka n’kundifunsa kuti: ‘Ababa, mungalole kuti tidzachitenso zimenezi? Ndili ndi mafunso ambiri, ndipo ndikufuna kudziwa chilichonse chokhudza Yehova.’”

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi makolo mungaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Manowa?

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi ananu mungaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Ahebri atatuwa?

[Zithunzi patsamba 17]

Zithunzi ndiponso mawu olongosola zithunzizo m’buku la “Mphunzitsi” n’ngothandiza kwambiri

Kodi Hananiya akuuza Petro bodza lotani?

Kodi ndani amene amaona zonse zimene timachita?