Mwana Wamasiye Wosowa Wom’samala Apeza Atate Womukonda
Mbiri ya Moyo Wanga
Mwana Wamasiye Wosowa Wom’samala Apeza Atate Womukonda
YOSIMBIDWA NDI DIMITRIS SIDIROPOULOS
Msilikali wamkulu anandikakamiza kunyamula mfuti kwinaku akunena mokalipa kuti: “Tiye, tenga mfutiyi uwombere.” Koma ndinam’kanira mwaulemu. Kenaka iye anayamba kuwombera, ndipo zipolopolozo zinangotsala pang’ono kunditsepula phewa moti asilikali amene anali kuonerera zimenezi anagwidwa nthumanzi kwambiri. Ndinkangoona kuti ndifa basi. Komabe mwamwayi ndinapulumuka. Imeneyitu siinali nthawi yoyamba kuti ndipulumukire m’kamwa mwa mbuzi.
BANJA lathu linali la anthu a fuko linalake laling’ono lomwe linkakhala kufupi ndi ku Kayseri, ku Cappadocia, m’dziko la Turkey. Zikuoneka kuti anthu ena a m’dera limeneli anayamba Chikristu m’zaka 100 zoyambirira. (Machitidwe 2:9) Komabe, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, zinthu zinali zitasintha kwambiri.
Ndinathawa Nkhondo Kenaka Ndinakhala Wamasiye
Patangotha miyezi ingapo ineyo nditabadwa mu 1922, nkhondo ya pakati pa mafuko inachititsa kuti banja lathu lithawire ku Greece. Chifukwa cha mantha makolo anga sanatenge china chilichonse kupatulapo mwana wawone, amene panthawiyi ndinali ndi miyezi ingapo chabe. Atavutika mosaneneka, anafika m’mudzi wa Kiria kufupi ndi mzinda wa Drama, kumpoto kwa Greece ndipo apa n’kuti ali paumphawi wadzaoneni ndiponso atafookeratu.
Ndili ndi zaka zinayi, ndipo mng’ono wanga atabadwa kale, bambo anatisiya. Anali ndi zaka 27 zokha basi, koma mavuto a panthawiyi anali atawafooleratu. Mayi nawo anakumana ndi nsautso zosaneneka moti posakhalitsa, nawonso anamwalira. Ineyo ndi mng’ono wanga uja anatisiya paumphawi
wadzaoneni. Tinatumizidwa ku nyumba zosiyanasiyana zosungirako ana amasiye, ndipo pamene ndinali ndi zaka 12, ndinatumizidwa ku nyumba ina yotere ku Thessalonica, kumene ndinayamba kuphunzira umakaniki.Pamene ndinali kukhala moyo wozunzika m’nyumba za ana amasiye, sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthu ena amavutika kwambiri m’moyo ndipo zinthu siziwayendera mwachilungamo. Ndinkadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu zomvetsa chisoni zoterezi zizichitika. Pa maphunziro athu a zachipembedzo, ankatiphunzitsa kuti Mulungu n’ngwamphamvu zonse, koma sankatilongosolera bwinobwino kuti zoipazi zachuluka chonchi chifukwa chiyani. Panali mawu ena otchuka onena kuti tchalitchi chabwino kwambiri ndi cha Greek Orthodox. Nthawi ina ndinafunsa kuti: “Ngati tchalitchi cha Orthodox chili chabwino kwambiri, n’chifukwa chiyani anthu onse sanalowe tchalitchi chimenechi?” Koma sanandiyankhe zomveka.
Komabe mphunzitsi wathu ankalemekeza kwambiri Baibulo, ndipo ankatiuza mogogomezera kwambiri kuti Baibulo ndi buku lopatulika. Mkulu woyang’anira nyumba yosungako ana amasiyeyo anali ndi mtima womwewo, koma sindinkadziwa kuti n’chifukwa chiyani sankachita nawo mapemphero a pasukulupo. Nditafunsa, ndinauzidwa kuti iyeyo anaphunzirapo ndi Mboni za Yehova, koma sindinkadziwapo chilichonse chokhudza gulu la chipembedzo limeneli.
Ndinamaliza maphunziro anga ku Thessalonica ndili ndi zaka 17. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba, ndipo dziko la Greece linayamba kulamulidwa ndi boma la chipani cha Nazi. Anthu anayamba kufa ndi njala m’misewu. Poopa kufa, ndinathawira kumidzi n’kuyamba kugwira ntchito yaulebala, ya malipiro ochepa kwambiri.
Baibulo Linayankha Mafunso Anga
Nditabwerera ku Thessalonica mu April 1945, ndinalandira mlendo, yemwe anali mchemwali wake wa mnzanga wina wakale, amene ndinakhala naye m’nyumba zingapo za ana amasiye. Mlendoyu dzina lake anali Paschalia ndipo anandiuza kuti mlongo wakeyo anasowa motero amafuna kundifunsa ngati mwina ndikudziwa kumene ali. Tikukambirana anandiuza kuti iyeyo ndi wa Mboni za Yehova ndipo anandifotokozera kuti Mulungu amaganizira anthu.
Posagwirizana ndi zimenezi, ndinamutsutsa pa mfundo zambiri. Mwachitsanzo, ndinamufunsa kuti ngati amaganiziradi anthu, nanga n’chifukwa chiyani ineyo ndinakula movutika? N’chifukwa chiyani ndinakhala mwana wamasiye? Mulunguyo amakhala ali kuti panthawi imene tikumufuna kwambiri? Poyankha, iye anandifunsa kuti: “Kodi iweyo ukunenetsa kuti Mulungu ndi amene amachititsa zovuta zonsezi?” Anatenga Baibulo lake n’kundisonyeza kuti Mulungu sachititsa anthu kuvutika. Anandithandizanso kuona kuti Mlengi amakonda anthu ndipo posachedwa adzakonza zinthu. Anawerenga malemba monga Yesaya 35:5-7 ndiponso Chivumbulutso 21:3, 4, n’kundisonyeza kuti posachedwapa, nkhondo, mavuto, matenda, ndiponso imfa zidzatha, ndipo anthu okhulupirika adzakhala padziko lapansi kwamuyaya.
Ndinapeza Banja Londithandiza
Ndinamva kuti mlongo wake wa Paschalia uja anaphedwa pamene ankamenyana ndi zigawenga. Kenaka ndinapita kwawo kukapepesa maliro, koma m’malo mwake iwowo ndi amene anandilimbikitsa pondiwerengera Malemba. Panthawi ina ndinapitakonso kuti ndikamve mawu ena olimbikitsa ochokera m’Baibulo, ndipo posakhalitsa ndinalowa nawo m’kagulu kakang’ono ka a Mboni za Yehova kamene kankakumana mwachinsinsi n’kumaphunzira ndiponso kulambira. Ngakhale kuti a Mboni anali oletsedwa, ineyo ndinatsimikiza mtima kupitiriza kusonkhana nawo.
Gulu la Akristu odzichepetsali, linali lokondana ngati banja, ndipo chikondi choterechi n’chimene ineyo ndinali kusowa. Iwowa anandithandiza kwambiri mwauzimu ndipotu ndinkafunikira kwambiri thandizo lotere. Anthuwa anakhala anzanga ondiganizira amene anali ofunitsitsa kundithandiza ndiponso kundilimbikitsa. (2 Akorinto 7:5-7) Chofunika kwambiri chinali chakuti zimenezi zinandithandiza kuyamba kugwirizana kwambiri ndi Yehova, amene ndinali nditayamba kumuona ngati Atate wanga wokondedwa wakumwamba. Makhalidwe ake monga chikondi, chifundo, ndiponso kuganizira kwambiri ena, ndinawakonda kwambiri. (Salmo 23:1-6) Tsopano ndinali nditapezadi banja lauzimu ndiponso Atate wondikonda. Zinandikhudza mtima kwambiri. Posakhalitsa ndinafika podzipereka kwa Yehova, ndipo ndinabatizidwa mu September 1945.
Kupita kumisonkhano yachikristu kunandithandiza kudziwa zambiri komanso kunalimbikitsa kwambiri chikhulupiriro changa. Popeza kuti panalibe njira ina yoyendera, angapo mwa ife nthawi zambiri tinkayenda mtunda wa makilomita asanu kuchokera pamudzi wathu kupita ku malo amsonkhano, ndipo paulendowu tinkakambirana nkhani zauzimu zosaiwalika. Kumapeto kwa chaka cha 1945, nditamva za mwayi wofalitsa uthenga wabwino nthawi zonse, ndinayamba kuchita upainiya. Ndinafunikira kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova, popeza kuti posakhalitsa ndinadzakumana ndi chiyeso choopsa cha chikhulupiriro ndiponso kukhulupirika.
Cholinga Chawo Polimbana Nafe Chinalephereka
Nthawi zambiri apolisi ankangotulukira pa malo athu amsonkhano atatenga mfuti. Popeza kuti nkhondo ya pakati pa mafuko inali ili m’kati ku Greece, dziko lathu linali mu ulamuliro wa asilikali. Magulu ankhondo anamenyana koopsa. Potengerapo mwayi pa zimenezi, abusa ananamiza aboma n’kuwachititsa kukhulupirira kuti ifeyo tinali anthu andale za Chikomyunizimu ndipo anawachititsa kuti atizunze kwadzaoneni.
Pa zaka ziwiri zokha, anatimanga kambirimbiri, ndipo nthawi sikisi anatipatsa chilango chokhala m’ndende kwa miyezi yosachepera inayi. Komano, ndendezo zinali zodzaza kale ndi akaidi omangidwa pa zifukwa zandale, motero ifeyo anatitulutsa. Tinagwiritsira ntchito mwayi wosayembekezekawu kupitiriza kulalikira, koma posakhalitsa anatimanganso, ndipo mlungu umodzi wokhawu anatimanga katatu. Tinkadziwa kuti abale athu ambiri anawaponya ku zilumba zachipululu. Kodi chikhulupiriro changa chinali cholimba moti n’kukwanitsa kupirira chiyeso chotere?
Zinthu zinafika povuta kwambiri atandiuza kuti ndizikaonekera kupolisi tsiku lililonse mpaka mlandu wanga udzathe. Pofuna kuti aziona zochitika zanga, aboma ananditumiza ku Evosmos, kufupi ndi ku Thessalonica, kumene kunali siteshoni ya apolisi. Ndinachita lendi nyumba ina pafupi ndi siteshoniyo, ndipo kuti ndizipezako ndalama, ndinayamba kugwira ntchito yoyendayenda yomapukuta mapoto komanso mafelempani a kopa kuti awale. Pamene ndinkachita upainiya m’midzi yapafupi, ntchito imeneyi inandithandiza kupita mosavuta m’nyumba za anthu popanda kukayikitsa apolisi. Motero, anthu ambiri ndithu anamva uthenga wabwino n’kuchitapo kanthu. Pa anthu amenewa, anthu oposa teni anafika podzipereka kwa Yehova.
Ndinatsekeredwa M’ndende Eyiti pa Zaka Teni
Ndinkapita kukaonekera kupolisi mpaka kumapeto kwa chaka cha 1949, ndipo kenaka ndinabwerera ku Thessalonica, ndili wofunitsitsa kwambiri kupitiriza utumiki wa nthawi zonse. Panthawi imene ndinali kuganiza kuti mavuto anga tsopano atha, mu 1950, anandiitana mosayembekezereka kuti ndikayambe usilikali. Monga Mkristu, sindinafune kulowerera m’zandale, motero ndinatsimikiza mtima ‘kusaphunzira nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Apa m’pamene panayambira ukabwerebwere wanga kundende ndipo unandipititsa m’ndende zina zotchuka kwambiri ku Greece.
Zonsezi zinayambira mumzinda wa Drama. Pa milungu yoyambirira imene ndinakhala m’ndende kumeneku, anthu amene anali atangowalemba kumene usilikali anayamba kuwaphunzitsa chandamale. Tsiku lina ananditenga n’kundipititsa pamalo amene amaphunzirira kuwombera. M’modzi wa akuluakulu a asilikali anandikakamiza kunyamula mfuti n’kundiuza kuti ndiwombere. Nditakana anayamba kuwombera mondiphonya. Asilikali anzake ataona kuti sindigonjera zofuna zawo, anayamba kundimenya ngati akumenya chithumba. Anayatsa ndudu n’kumanditentha nazo
m’manja. Kenaka ananditsekera m’chipinda chandekha. Zimenezi zinachitika kwa masiku atatu. Ululu wa zilonda za moto wa ndudu zija unali wosasimbika, ndipo kwa zaka zambiri manja anga akhala ndi zipsera za zilonda zimenezi.Asanandipititse ku khoti la asilikali, anandisamutsira ku kampu ya asilikali ku Iráklion, ku Crete. Kumeneko, pofuna kuti ndisiye kutumikira Mulungu mokhulupirika, anandimenya koopsa. Poopa kuti ndigonjera, ndinapemphera kwambiri, ndipo ndinapempha Atate wanga wakumwamba kuti andilimbikitse. Mawu a Yeremiya 1:19 anandibwerera m’maganizo. Mawu ake ndi akuti: “Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.” Mtima wanga unakhala pansi chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.” Ndinamvetsetsadi kuti kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse n’chinthu chanzeru.—Afilipi 4:6, 7; Miyambo 3:5.
Kenaka atazenga mlandu wanga, anandiweruza kuti ndikakhale m’ndende kwa moyo wanga wonse. Anthu ankaona kuti Mboni za Yehova ndi “adani a dziko” oopsa kwambiri. Ndinayamba kugwira ukaidi wa moyo wanga wonse pa ndende ya Itsedin, yomwe inali kunja kwa mzinda wa Canea, ndipo ananditsekera m’chipinda chandekha. Ndende ya ku Itsedin, kwenikweni inali chinyumba cha mfumu chamakedzana, ndipo m’chipinda chimene anandiikamo munali makoswe adzaoneni. Ndinkadzikulunga thupi lonse m’kasanza ka bulangete kuti makoswewo asamandikhudze thupi akamandikwerakwera. Kenaka chibayo chinanditengetsa kwabasi. Dokotala ananena kuti ndiyenera kumakhala padzuwa, motero ndinatha kukambirana ndi akaidi ambiri amene anali pabwalo la m’kati mwa chinyumba chandendecho. Komabe matenda anga anaipiraipira, ndipo nditatuluka magazi kwambiri m’mapapo mwanga, anandipititsa kuchipatala cha Iráklion.
Apanso, banja langa lauzimu la Akristu anzanga linandithandiza. (Akolose 4:11) Abale a ku Iráklion ankandiyendera kawirikawiri, ndipo ankandilimbikitsa. Ndinawauza kuti ndikufunikira mabuku kuti ndizitha kulalikira kwa anthu ochita chidwi. Anandibweretsera sutukesi yokhala ndi kathumba kobisika kamene ndimabisamo mabukuwo bwinobwino. Ndinali wosangalala kwambiri kuti panthawi yonse imene ndinakhala ku ndendezo, ndinathandiza anthu mwina okwana sikisi kukhala Akristu oona.
Kenaka nkhondo yachiweniweni ija itatha chilango changa anachichepetsa kuti ndingokhala m’ndende zaka teni. Zaka zotsalazi ndinagwira ukaidi m’ndende za ku Rethimno, Genti Koule ndiponso Cassandra. Nditakhala zaka pafupifupi teni m’ndende zokwana eyiti, ndinatulutsidwa, ndipo ndinabwerera ku Thessalonica, kumene abale anga Achikristu anandilandira ndi manja awiri.
Ndinapita Patsogolo Mwauzimu Mothandizidwa ndi Abale
Panthawiyi a Mboni a ku Greece anali ndi ufulu ndithu wopembedza. Nthawi yomweyo ineyo ndinagwiritsira ntchito mwayi umenewu kupitiriza utumiki wa nthawi zonse. Posakhalitsa ndinalandiranso dalitso lina. Ndinadziwana ndi mlongo wina wokhulupirika, dzina lake Katina ndipo iyeyo ankakonda Yehova komanso ankachita khama kwambiri pa ntchito yolalikira. Tinakwatirana mu October 1959. Mabala a umasiye wanga anapola kwambiri mwana wathu wamkazi Agape atabadwa komanso chifukwa chokhala ndi banja langalanga. Koposa zonsezi, banja lathu linali lokhutira kutumikira motetezedwa ndi Atate wathu wachikondi Yehova.—Salmo 5:11.
Chifukwa cha mavuto a zachuma, ndinakakamizika kusiya upainiya, koma ndinali kumuthandiza mkazi wanga kupitiriza kuchita utumiki wa nthawi zonse. Chinthu chachikulu kwambiri pa moyo wanga wachikristu chinachitika mu 1969 pamene ku Nuremberg, m’dziko la Germany kunachitika msonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova. Pokonzekera kupita kumsonkhanowu, ndinasayina fomu yokonzetsera pasipoti. Ndiyeno nthawi ina mkazi wanga atapita ku siteshoni ya polisi kukafunsa kuti n’chifukwa chiyani patha miyezi iwiri koma pasipoti yanga siinatulukebe, wapolisi wina anam’tulutsira chimpukutu cha mapepala n’kunena kuti: “Kodi mukufuna tikonze pasipoti ya mkulu uyu kuti akatembenuze anthu ku Germany? Iwalaniko zimenezo! Ndi munthu woopsa ameneyu.”
Mothandizidwa ndi Yehova ndiponso abale ena, anandiika pa pasipoti ya gulu ndipo ndinatha kukachita nawo msonkhano wosangalatsawo. Pamsonkhanowo panafika anthu oposa 150,000, ndipo ineyo ndinatha kuona mosavuta kuti mzimu wa Yehova unali kutsogolera ndiponso kugwirizanitsa banja la padziko lonse lauzimu limeneli. Patsogolo pake m’moyo wanga, ndinadzafika poona kwambiri kufunika kwa ubale wachikristu umenewu.
M’chaka cha 1977, mkazi wanga wokondedwa ndi wokhulupirika anamwalira. Ndinayesetsa kwambiri kulera mwana wanga wamkazi mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, koma sikuti ndinali ndekha ayi. Apanso banja langa lauzimu linandithandiza kwambiri. Sindidzaiwala mmene abale anandithandizira panthawi yovuta imeneyi. Ena ankadzakhala nane kunyumba kwathu kuti andithandize kulera mwana uja. Sindidzaiwala chikondi chawo chololera kuvutikira ena.—Yohane 13:34, 35.
Agape atakula anakwatiwa ndi mbale, dzina lake Elias. Iwo ali ndi ana aamuna anayi, ndipo onse ali m’choonadi. Posachedwapa ndavutika kangapo konse chifukwa cha matenda a sitoloko ndipo m’thupi mwanga simulinso bwino ayi. Mwana wanga wamkazi ndi banja lake amandisamalira bwino kwambiri. Ngakhale kuti thanzi langa silili bwino, ndine wosangalala pazifukwa zambiri. Ndimakumbukira nthawi ina pamene ku Thessalonica konse kunali abale pafupifupi 100 okha, amene ankasonkhana m’nyumba zawo mobisa. Panopo, m’derali muli Mboni zakhama pafupifupi faifi sauzande. (Yesaya 60:22) Pa misonkhano ikuluikulu, abale achinyamata amandifunsa kuti: “Kodi mukukumbukira nthawi ija munkabweretsa magazini kunyumba kwathu?” Ngakhale kuti nthawi zina makolo awo sankawerenga magaziniwo, anawo ankawerenga, ndipo anapita patsogolo mwauzimu.
Ndikamaona mmene gulu la Yehova lakulira, ndimaona kuti sindinavutike pachabe. Nthawi zonse ndimauza zidzukulu zanga ndiponso achinyamata ena kuti azikumbukira Atate wawo wakumwamba paunyamata wawo, ndipo iye sadzawaleka. (Mlaliki 12:1) Yehova anakwaniritsa mawu ake, ndipo kwa ineyo anakhala “Atate wa ana amasiye.” (Salmo 68:5) Ngakhale kuti ndinali mwana wamasiye wosowa wondisamalira, pamapeto pake ndinapeza Atate wondikonda.
[Chithunzi patsamba 22]
Ndikugwira ntchito yophika m’ndende ya mumzinda wa Drama
[Chithunzi patsamba 23]
Ndili ndi Katina pa tsiku la ukwati wathu, mu 1959
[Chithunzi patsamba 23]
Uwu ndi msonkhano wochitikira kutchire la pafupi ndi Thessalonica, chakumapeto kwa m’ma 1960
[Chithunzi patsamba 24]
Tili pamodzi ndi mwana wathu, mu 1967