Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Yehova Akhale Mulungu Wanu

Zimene Mungachite Kuti Yehova Akhale Mulungu Wanu

Zimene Mungachite Kuti Yehova Akhale Mulungu Wanu

M’NTHAWI za m’Baibulo, panali anthu ena amene ankagwirizana kwambiri ndi Yehova moti Baibulo limanena kuti iye anali Mulungu wawo. Mwachitsanzo, m’Malemba, Yehova amatchulidwa kuti “Mulungu wa Abrahamu,” “Mulungu wa Davide,” ndiponso “Mulungu wa Eliya.”​—Genesis 31:42; 2 Mafumu 2:14; 20:5.

Kodi anthu amenewa anatani kuti afike pogwirizana chonchi ndi Mulungu? Kodi tingaphunzire zotani kwa iwowo zomwe zingatithandize kuti nafenso tikhale ndi ubwenzi wotere ndi Mlengi ndiponso kuti ubwenziwo ukhalebe wolimba?

Abrahamu “Anakhulupirira Yehova”

Abrahamu anali munthu woyamba amene Baibulo limati anakhulupirira Yehova. Chikhulupiriro chinali khalidwe lalikulu kwambiri la Abrahamu limene linachititsa kuti Mulungu amuyanje. Ndipotu, Abrahamu ankakondedwa kwambiri ndi Yehova moti patsogolo pake Mlengiyu anamuuza Mose kuti Iye ndi “Mulungu wa Abrahamu” ndiponso wa mwana wake, Isake, ndi chidzukulu chake, Yakobo.​—Genesis 15:6; Eksodo 3:6.

Kodi Abrahamu anatani kuti akhale ndi chikhulupiriro choterechi mwa Mulungu? Choyamba n’chakuti, Abrahamu anamanga chikhulupiriro chake pa maziko olimba. N’kutheka kuti Semu ndiye anaphunzitsa Abrahamu njira za Yehova. Semu anali mwana wa Nowa, amene anaona ndi maso mmene Mulungu amapulumutsira ndipo iyeyu anali umboni wooneka ndi maso wakuti Yehova “anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.” (2 Petro 2:5) Abrahamu ayenera kuti anaphunzitsidwa ndi Semu kuti Yehova akalonjeza chinthu amachikwaniritsa popanda kukayika. Mulimonsemo, Abrahamu payekha atalonjezedwa ndi Mulungu, anasangalala ndipo pamoyo wake wonse sankakayikira ngakhale pang’ono zoti lonjezolo lidzakwaniritsidwa.

Poti chikhulupiriro cha Abrahamu chinali kale ndi maziko olimba, iye anachilimbitsa mwa ntchito zake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka ku malo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.” (Ahebri 11:8) Kumvera kumeneku kunalimbitsanso chikhulupiriro cha Abrahamu, ndipo pankhaniyi mtumwi Yakobo analemba kuti: “Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro.”​—Yakobo 2:22.

Komanso Yehova analola kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chiyesedwe ndipo zimenezi zinachititsa kuti chifike polimba kwambiri. Paulo anapitiriza kunena kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake.” Kuyesedwa kumakonza ndi kulimbitsa chikhulupiriro, ndipo zimenezi zimachititsa kuti chikhulupirirocho chifike pokhala ‘chamtengo wake woposa wa golidi.’​—Ahebri 11:17; 1 Petro 1:7.

Ngakhale kuti Abrahamu sanakhale ndi moyo n’kuona zonse zimene Mulungu analonjeza, iye anali wosangalala kuona anthu ena akutsatira chitsanzo chake. Baibulo limatchulapo za chitsanzo chabwino cha mkazi wake Sara ndiponso anthu ena atatu a m’banja mwake, Isake, Yakobo, ndi Yosefe, pokhala ndi chikhulupiriro chachikulu.​—Ahebri 11:11, 20-22.

Mmene Tingakhalire ndi Chikhulupiriro Monga cha Abrahamu

Chikhulupiriro n’chofunika kwa aliyense amene amafuna kuti Yehova akhale Mulungu wake. “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa [Mulungu],” analemba choncho Paulo. (Ahebri 11:6) Kodi mtumiki wa Mulungu masiku ano angatani kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba changati cha Abrahamu?

Monga Abrahamu, chikhulupiriro chathu chiyenera kukhazikika pa maziko olimba. Njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi ndiyo kuwerenga nthawi zonse Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo. Kuwerenga Baibulo ndiponso kusinkhasinkha zimene tikuwerenga kungatithandize kukhala otsimikiza kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Motero timalimbikitsidwa kusintha moyo wathu kuti ugwirizane ndi zinthu zimenezi, zomwe zili zotsimikizika. Chikhulupiriro chathu chimalimbikitsidwanso tikamamvera Mulungu, monga kuchita nawo utumiki wa kumunda ndiponso kupezeka pa misonkhano yachikristu.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Ahebri 10:24, 25.

Mosakayikira, chikhulupiriro chathu chimayesedwa ndipo mwina chimayesedwa ndi anthu olimbana nafe, kaya matenda aakulu, imfa ya munthu amene tinali kumukonda, kapenanso zinthu zina. Kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova pamene tikuyesedwa kumalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndipo kumachititsa kuti chikhale chamtengo wapatali kuposa golide. Kaya tikhala ndi moyo mpaka kuona malonjezo onse a Mulungu kapena ayi, chikhulupiriro chathu chingatithandizebe kuyandikira kwa Yehova. Komanso, chitsanzo chathu chingalimbikitse anthu ena kutsanzira chikhulupiriro chathu. (Ahebri 13:7) Zimenezi n’zimene zinamuchitikira Ralph, amene anaona ndiponso kutsanzira chikhulupiriro cha makolo ake. Iye analongosola kuti:

“Ndisanachoke pakhomo pa makolo anga, iwo ankalimbikitsa tonse m’banja mwathu kuti tizidzuka m’mawa n’kuwerenga Baibulo pamodzi. Motero tinatha kuwerenga Baibulo lonse.” Ralph amawerengabe Baibulo m’mawa uliwonse, ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti tsiku aziliyamba bwino. Mlungu uliwonse Ralph ankalowa muutumiki wa kumunda pamodzi ndi abambo ake. Ralph anati: “Apa m’pamene ndinaphunzira kuchita maulendo obwereza ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo.” Panopo, Ralph amatumikira mongodzipereka pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Ulaya. Iyitu ndi mphoto yabwino kwambri imene anapata chifukwa cha chikhulupiriro cha makolo ake.

Munthu wa Pamtima pa Yehova

Davide anabadwa zaka pafupifupi 900 pambuyo pa Abrahamu, ndipo iye ndi munthu wodziwika kwambiri pa gulu la atumiki a Yehova otchulidwa m’Malemba. Ponena za chifukwa chimene Yehova anasankhira Davide kuti adzakhale Mfumu ya m’tsogolo, Samueli anati: “Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake.” Yehova ndi Davide ankagwirizana kwambiri moti patsogolo pake, mneneri Yesaya akulankhula ndi Mfumu Hezekiya, ananena mawu akuti: “Yehova, Mulungu wa Davide kholo lako.”​—1 Samueli 13:14; 2 Mafumu 20:5; Yesaya 38:5.

Ngakhale kuti Davide anali munthu wa pamtima pa Yehova, nthawi zina iyeyu analekerera zilakolako zake kumuchititsa zoipa. Katatu konse iye anachita zolakwa zazikulu: Analola kuti likasa la chipangano linyamulidwe m’njira yosayenera popita ku Yerusalemu; anachita chigololo ndi Batiseba ndi kuchita chiwembu chopha mwamuna wake Uriya; komanso anawerengera anthu ku Israyeli ndi Yuda mosalamulidwa ndi Yehova. Panthawi zonsezi, Davide ananyalanyaza Lamulo la Mulungu.​—2 Samueli 6:2-10; 11:2-27; 24:1-9.

Komabe Davide atauzidwa za machimo ake, iye anavomereza kuti anali wolakwa ndipo sanaimbe mlandu anthu ena. Iye anavomereza kuti nkhani ya kunyamula Likasa sanaiyendetse bwino, ndipo ananenanso kuti “sitinam’funafuna [Yehova] monga mwa chiweruzo.” Mneneri Natani atavumbula zoti Davide anachita chigololo, Davideyo anayankha kuti: “Ndinachimwira Yehova.” Ndipo Davide atadziwa kuti anachita zopusa powerenga anthu, iye anavomereza kuti “Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita.” Davide analapa machimo ake ndipo anapitirizabe kugwirizana ndi Yehova.​—1 Mbiri 15:13; 2 Samueli 12:13; 24:10.

Tikalakwa

Tikamayesetsa kuchita zinthu zoti Yehova akhale Mulungu wathu, tingalimbikitsidwe kwambiri ndi chitsanzo cha Davide. Ngati munthu wa pamtima pa Yehova anachita machimo aakulu motere, ifenso sitiyenera kufooka ngati tikuyesetsa kuchita zabwino komabe n’kupezeka kuti pena talakwitsa, ngakhale pa zinthu zazikulu. (Mlaliki 7:20) Tingalimbikitsidwe podziwa kuti Davide atalapa, machimo ake anakhululukidwa. Zimenezi n’zimene zinam’chitikira Uwe * zaka zingapo zapitazo.

Uwe anali mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova. Panthawi ina, iye anatengeka ndi chilakolako choipa ndipo anachita chigololo. Poyamba, Uwe anayesa kubisa nkhaniyi monga mmene Mfumu Davide anachitiranso, poganiza kuti Yehova anyalanyaza tchimo lakelo. Komabe chikumbumtima chake chinayamba kum’pweteka kwambiri moti anaulula tchimo lakelo kwa mkulu mnzake ndipo akulu anam’thandiza kuti apulumuke ngozi yauzimuyi.

Uwe analapa machimo ake ndipo anapitiriza kuyandikira kwa Yehova ndiponso mpingo. Iye anayamikira kwambiri thandizo limene analandira moti patatha milungu ingapo izi zitachitika, iye analemba kalata kwa akulu, yothokoza moona mtima chifukwa chomuthandiza. Iye analemba kuti: “Mwandithandiza kuchotsa chitonzo pa dzina la Yehova.” Uwe anayambanso kugwirizana ndi Yehova ndipo patsogolo pake anadzaikidwanso kukhala mtumiki mumpingo womwewo.

“Munthu Wakumva Zomwe Tizimva Ife”

Eliya, amene anakhalako pambuyo pa Davide, anali mmodzi wa aneneri odziwika kwambiri a ku Israyeli. Eliya ankalimbikitsa chipembedzo choona panthawi imene zinthu zinaipa kwambiri pankhani ya chilungamo ndiponso makhalidwe, ndipo iye anadzipereka kwa Yehova mosabwerera m’mbuyo. N’zosadabwitsa kuti Elisa, amene analowa m’malo mwake, nthawi inayake anafika potcha Yehova kuti “Mulungu wa Eliya.”​—2 Mafumu 2:14.

Komabe, Eliya sikuti anali munthu winawake wodabwitsa ayi. Yakobo analemba kuti: “Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5:17) Mwachitsanzo, Eliya atagonjetseratu anthu onse olambira Baala, Mfumukazi Yezebeli inafuna kumupha. Kodi Eliya anatani? Iye anachita mantha ndipo anathawira kuchipululu. Kumeneko, anakhala pansi pamtengo watsanya, ndipo anadandaula motere: “Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.” Eliya sankafunanso kukhala mneneri koma ankaona kuti ndi bwino kungofa basi.​—1 Mafumu 19:4.

Komabe, Yehova anasonyeza kuti ankamvetsa mmene Eliya anali kumvera. Motero anamulimbikitsa, n’kumutsimikizira kuti sanali yekha, chifukwa panalinso anthu ena amene anali okhulupirika pa kulambira koona. Komanso, Yehova ankamukhulupirirabe Eliya ndipo anali ndi ntchito yoti Eliya achite.​—1 Mafumu 19:5-18.

Sikuti posokonezeka maganizo chonchi, Eliya anali kusonyeza kuti wasiya kuyanjidwa ndi Mulungu ayi. Patatha zaka 1,000, Kristu Yesu atasandulika pamaso pa Petro, Yakobo ndi Yohane, kodi Yehova anasankha kuti m’masomphenyawa muoneke ndani ali pamodzi ndi Yesu? Mose ndi Eliya. (Mateyu 17:1-9) N’zoonekeratu kuti Yehova ankamuona Eliya ngati mneneri wachitsanzo chabwino kwambiri. Ngakhale kuti Eliya anali chabe “munthu wakumva zomwezi tizimva ife,” Mulungu anayamikira ntchito yake pochita khama kubwezeretsa kulambira koona ndiponso poyeretsa dzina Lake.

Kulimbana ndi Nkhawa Zathu

Atumiki a Yehova masiku ano amalefuka ndiponso amakhala ndi nkhawa nthawi zina. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Eliya anamvaponso chimodzimodzi. Ndipotu n’zolimbikitsa kwabasi kudziwa kuti monga mmene Yehova anachitira pomumvetsa Eliya, amatimvetsanso ifeyo tikamavutika maganizo m’njira imeneyi.​—Salmo 103:14.

Tikudziwa kuti timakonda Mulungu komanso anthu anzathu ndipo timafuna kuchita ntchito ya Yehova yolalikira za uthenga wabwino wa Ufumu. Komano tingakhumudwe kuona kuti anthu sakumvera tikamawalalikira kapenanso tingade nkhawa adani a kulambira koona akamatiopseza. Komabe Yehova amathandiza atumiki ake masiku ano kuti apitirize ntchito yawo monga mmene anathandizira Eliya. Taonani chitsanzo cha Herbert ndi Gertrud.

Herbert ndi Gertrud anabatizidwa m’chaka cha 1952 kukhala Mboni za Yehova ku Leipzig, m’dziko limene kale linkadziwika kuti German Democratic Republic. Panthawiyo zinthu sizinali bwino kwa anthu otumikira Mulungu, chifukwa chakuti ntchito yawo yolalikira inali yoletsedwa. Kodi Herbert ankaiona bwanji nkhani yolalikira kunyumba ndi nyumba?

Iye anati: “Nthawi zina tinkakhala ndi nkhawa kwambiri. Tikamayenda khomo ndi khomo, tinkada nkhawa poganizira kuti aboma angathe kungotulukira n’kutimanga.” Kodi n’chiyani chimene chinathandiza Herbert ndiponso anzake ena kuthana ndi manthawo? Herbert anati: “Tinkawerenga kwambiri Baibulo. Ndipo Yehova anatipatsa mphamvu zopitirizira ntchito yathu yolalikira.” M’ntchito yake yolalikira, Herbert anakumana ndi zinthu zambiri zolimbikitsa ndiponso zosangalatsa.

Nthawi ina Herbert anapezana ndi mayi wina wachikulire amene anachita chidwi ndi Baibulo. Herbert anapitanso kwa mayiyo patatha masiku angapo, ndipo anapezako mnyamata yemwe anamvetsera zomwe ankakambiranazo. Patatha mphindi zingapo Herbert anaona chinthu chinachake chimene chinamunyumwitsa. Pampando wina pakona pa chipindacho panali chipewa chapolisi. Chipewachi chinali cha mnyamatayo, ndipo zinaonekeratu kuti iyeyu anali wapolisi ndiponso kuti, mosachitira mwina, Herbert amumanga.

Mnyamatayo ananena mwamphamvu kuti: “Ndiwe wa Mboni za Yehova eti? Tandionetsa chiphaso chako.” Herbert anapereka chiphasocho. Kenaka panachitika zosayembekezereka. Mayi uja anayang’ana wapolisiyo n’kumuchenjeza kuti: “Munthu wa Mulungu ameneyu chikamuonekera chinachake, iweyo sindidzakulolanso kuponda pakhomo panga pano.”

Mnyamatayo anachita kaye jegaa, kenaka anam’bwezera Herbert chiphaso chija, n’kumulola kuti apite. Pambuyo pake Herbert anauzidwa kuti wapolisiyo anali chibwenzi cha mwana wamkazi wa mayiyo. N’zoonekeratu kuti iyeyu anaona kuti ndi bwino kupitiriza chibwenzi chake ndi mtsikanayo kusiyana ndi kukam’tsekera Herbert.

Yehova Akhale Mulungu Wathu

Kodi zochitika zimenezi zingatiphunzitse chiyani? Monga Abrahamu, tiyenera kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova. Monga Davide, tikalakwa tiyenera kulapa moona mtima kuti Yehova atikhululukire. Ndipo monga Eliya, tiyenera kudalira Yehova kuti atipatse mphamvu tikakhala ndi nkhawa. Pochita zimenezi, Yehova angathe kukhala Mulungu wathu panopo komanso mpakana kalekale, popeza kuti iye ndi “Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupira.”​—1 Timoteo 4:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Dzinali talisintha.

[Zithunzi patsamba 25]

Kumvera kunalimbitsa chikhulupiriro cha Abrahamu

[Chithunzi patsamba 26]

Monga Davide tiyenera kulapa tikachimwa

[Chithunzi patsamba 28]

Yehova anamvetsa mmene Eliya ankamvera, ndipo amamvetsanso mmene ifeyo timamvera