Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Lolani Kuti Mawu a Mulungu Aunike Njira Yanu

Lolani Kuti Mawu a Mulungu Aunike Njira Yanu

Lolani Kuti Mawu a Mulungu Aunike Njira Yanu

“Mawu anu ndiwo . . . kuunika kwa panjira panga.”​—SALMO 119:105.

1, 2. Kodi mawu a Yehova angaunike njira yathu ngati titachita chiyani?

MAWU a Yehova angaunike njira yathu tikalola kuti zimenezo zichitike. Kuti tipindule ndi kuunika kwauzimu kumeneko, tiyenera kumaphunzira Mawu olembedwa a Mulungu mwakhama ndi kumagwiritsa ntchito malangizo ake. Pokhapokha ngati titachita zimenezi m’pamene tingagwirizane ndi wamasalmo amene anati: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”​—Salmo 119:105.

2 Tsopano tiyeni tikambirane Salmo 119:89-176. M’mavesi amenewa mulitu mfundo zochuluka, zomwe anazindandalika m’zigawo 11. Mfundo zimenezi zingatithandize kupitiriza kuyenda m’njira ya kumoyo wosatha.​—Mateyu 7:13, 14.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukonda Mawu a Mulungu?

3. Kodi Salmo 119:89, 90 likusonyeza bwanji kuti tingakhulupirire mawu a Mulungu?

3 Kukonda mawu a Yehova kumam’chititsa munthu kukhala wolimba mwauzimu. (Salmo 119:89-96) Wamasalmo anaimba kuti: “Mawu anu aikika kumwamba, kosatha, Yehova. . . . Munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.” (Salmo 119:89, 90) Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zimayenda m’njira zawo mwadongosolo, ndipo dziko lapansi linakhazikika pamaziko ake kwamuyaya. Zonsezi zinatheka ndi mawu a Mulungu kapena kuti ‘malemba ake a kuthambo.’ (Yobu 38:31-33; Salmo 104:5) Tingakhulupirire mawu onse otuluka m’kamwa mwa Yehova. Zimene Yehova ananena ‘zidzakula’ kapena kuti zidzapambana pokwaniritsa chifuno chake.​—Yesaya 55:8-11.

4. Kodi kukonda mawu a Mulungu kumathandiza bwanji atumiki ake amene akuzunzika?

4 ‘Chilamulo cha Mulungu chikadapanda kukhala chikondweretso chake’, wamasalmo ‘akadatayika m’kuzunzika kwake.’ (Salmo 119:92) Sikuti iye anali kuzunzidwa ndi alendo ayi, anali Aisrayeli oswa malamulo amene anali kudana naye. (Levitiko 19:17) Komatu zimenezi sanafooke nazo chifukwa ankakonda chilamulo cha Mulungu chimene chinam’limbikitsa. Mtumwi Paulo anakumana ndi zoopsa ku Korinto pakati pa “abale onyenga.” Mwina ena a iwo anali “atumwi oposatu” omwe ankafuna kumutola zifukwa. (2 Akorinto 11:5, 12-14, 26) Koma Paulo anatetezeka mwauzimu chifukwa ankakonda mawu a Mulungu. Ife timakonda abale athu chifukwa chakuti timakonda Mawu olembedwa a Yehova ndipo timagwiritsa ntchito zimene mawuwo amanena. (1 Yohane 3:15) Ngakhale dzikoli lizidana nafe sitiiwala malangizo alionse a Mulungu. Timapitiriza kuchita chifuniro chake mokondana komanso mogwirizana ndi abale athu pamene tikuyembekezera kudzatumikira Yehova mokondwa kwamuyaya.​—Salmo 119:93.

5. Kodi Mfumu Asa anafunafuna Yehova motani?

5 Posonyeza kudzipereka kwathu kwa Yehova, tingapemphere kuti: “Ine ndine wanu, ndipulumutseni pakuti ndinafuna malangizo anu.” (Salmo 119:94) Mfumu Asa anafunafuna Mulungu ndipo anathetsa mpatuko mu Yuda. Pa msonkhano waukulu womwe unachitika m’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa (mu 963 B.C.E.), anthu okhala mu Yuda ‘analowa chipangano chakufuna Yehova.’ Mulungu analola kuti iwo ‘amupeze’ ndipo anapitiriza ‘kuwapumulitsa pozungulirapo.’ (2 Mbiri 15:10-15) Chitsanzo chimenechi chiyenera kulimbikitsa aliyense amene wasiyana ndi mpingo wachikristu kuti ayambirenso kufunafuna Mulungu. Iye adzadalitsa ndi kuteteza onse amene ayambiranso kuyanjana ndi anthu ake.

6. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisavulale mwauzimu?

6 Mawu a Yehova amatipatsa nzeru zimene zimatiteteza kuti tisavulale mwauzimu. (Salmo 119:97-104) Malamulo a Mulungu amatithandiza kukhala anzeru kwambiri kuposa adani athu. Kumvera zikumbutso zake kumatipatsa luntha, ndipo ‘timazindikira kuposa okalamba chifukwa timasunga malangizo ake.’ (Salmo 119:98-100) Ngati mawu a Yehova ‘amazunadi koposa uchi m’kamwa mwathu,’ tidzadana ndi “mayendedwe onse achinyengo” ndiponso tidzawapewa. (Salmo 119:103, 104) Zimenezi zidzatiteteza kuti tisavulale mwauzimu pamene tikukumana ndi anthu odzikuza, oopsa ndiponso osaopa Mulungu masiku otsiriza ano.​—2 Timoteo 3:1-5.

Nyali ya ku Mapazi Athu

7, 8. Kodi tifunika kuchita chiyani mogwirizana ndi Salmo 119:105?

7 Mawu a Mulungu ndiwo gwero limodzi lodalirika la kuunika kwauzimu. (Salmo 119:105-112) Kaya ndife Akristu odzozedwa kapena anzawo a “nkhosa zina,” tonsefe timanena motsimikiza kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Yohane 10:16; Salmo 119:105) Mawu a Mulungu ali ngati nyali younikira njira yathu, kuti tisapunthwe ndi kugwa mwauzimu. (Miyambo 6:23) Komabe, aliyense payekha ayenera kulola mawu a Yehova kuti akhale nyali ya kumapazi ake.

8 Tiyenera kukhala osasunthika monga mmene wolemba Salmo 119 analili. Anali wotsimikiza mtima kusapatuka pa malangizo a Mulungu. Iye anati : “Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu [a Yehova] olungama.” (Salmo 119:106) Sitiyenera kuchepetsa phindu la kuphunzira Baibulo nthawi zonse ndi kutenga nawo mbali m’misonkhano yachikristu.

9, 10. Kodi tikudziwa bwanji kuti anthu odzipereka kwa Yehova ‘angasochere m’malangizo ake,’ koma kodi zimenezi tingazipewe bwanji?

9 Wamasalmo ‘sanasochere m’malangizo a Mulungu,’ komatu n’zotheka munthu wodzipereka kwa Yehova kusochera. (Salmo 119:110) Mfumu Solomo anasochera, ngakhale kuti anali wochokera mu mtundu wodzipereka kwa Yehova ndiponso ngakhale kuti kuchiyambi kwa ulamuliro wake ankachita zinthu mogwirizana ndi nzeru zimene Mulungu anam’patsa. “Ngakhale iye, akazi achilendo anam’chimwitsa” mwa kumukopa kuyamba kulambira milungu yonyenga.​—Nehemiya 13:26; 1 Mafumu 11:1-6.

10 “Msodzi,” Satana, amatchera misampha yambirimbiri. (Salmo 91:3) Mwachitsanzo, munthu amene kale tinali kulambira naye limodzi angayese kutisocheretsa, mwa kutichotsa panjira ya kuunika kwauzimu ndi kutipititsa ku mdima wampatuko. Pakati pa Akristu ku Tiyatira, panali “mkazi Yezebeli.” N’kutheka kuti mkazi ameneyu anali gulu la azimayi amene anali kuphunzitsa ena kupembedza mafano ndi kuchita dama. Yesu sanalekerere khalidwe loipali, ndipo nafenso tisalilekerere. (Chivumbulutso 2:18-22; Yuda 3, 4) Chotero tizipempherera thandizo la Yehova kuti tisasochere ndi kulekana nawo malangizo ake, koma kuti tipitirize kuyenda m’kuunika kwa Mawu a Mulungu.​—Salmo 119:111, 112.

Mawu a Mulungu Amatichirikiza

11. Malinga ndi Salmo 119:119, kodi Mulungu amawaona motani anthu oipa?

11 Mulungu adzatichirikiza tikapanda kupatuka pa malemba ake. (Salmo 119:113-120) Anthu a “mitima iwiri” sitigwirizana nawo, mofanana ndi Yesu amene sagwirizana ndi anthu ofunda odzitcha Akristu masiku ano. (Salmo 119:113; Chivumbulutso 3:16) Popeza kuti timatumikira Yehova ndi mtima wonse, iye ndiye ‘pobisala pathu’ ndipo adzatichirikiza. ‘Onse osochera m’malemba ake,’ mwa kuyamba kuchita chinyengo ndi mabodza adzawataya. (Salmo 119:114, 117, 118; Miyambo 3:32) Anthu oipa amenewo amawaona ngati “mphala” kapena kuti zinyansi zimene amazichotsa poyenga zitsulo ngati siliva ndi golide. (Salmo 119:119; Miyambo 17:3) Tiyeni tizisonyeza nthawi zonse kuti timakonda zikumbutso za Mulungu, chifukwatu tikapanda kutero tidzaunjikidwa limodzi ndi anthu oipa pa mulu wa zinyansi nthawi ya chiwonongeko.

12. N’chifukwa chiyani kuopa Yehova kuli kofunika?

12 “Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu [Yehova],” anatero wamasalmo. (Salmo 119:120) Ngati tikufuna kuti Mulungu atichirikize monga atumiki ake, tiyenera kumuopa moyenera. Mantha amenewa amaonekera tikamapewa zinthu zimene amadana nazo. Kuopa Yehova ndi kumupatsa ulemu kunathandiza Yobu kukhala moyo wolungama. (Yobu 1:1; 23:15) Kuopa Mulungu kungatithandize kupitirizabe kuyenda m’njira imene Mulungu amayanja mosasamala kanthu za zinthu zimene tingafunike kupirira. Komabe, kuti tithe kupirira tifunika kumapemphera ndi chikhulupiriro kuchokera pansi pa mtima.​—Yakobo 5:15.

Pempherani ndi Chikhulupiriro

13-15. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chikhulupiriro kuti mapemphero athu adzayankhidwa? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati tikusowa chonena m’pemphero? (c) Fotokozani mmene Salmo 119:121-128 lingagwirizanire ndi ‘zobuula zathu zosatheka kuneneka’ m’pemphero.

13 Tikhoza kupemphera ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu adzachitapo kanthu. (Salmo 119:121-128) Mofanana ndi wamasalmoyu, ndife otsimikiza kuti mapemphero athu adzayankhidwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti timakonda malamulo a Mulungu “koposa golidi, inde golidi woyengeka.” Komanso, ‘malangizo onse a Mulungu onena zonse’ timawaona kuti n’ngolunjika.​—Salmo 119:127, 128.

14 Yehova amamva mapemphero athu chifukwa chakuti timapemphera ndi chikhulupiriro komanso timatsatira malangizo ake mosamala. (Salmo 65:2) Nanga bwanji ngati nthawi zina timakumana ndi mavuto othetsa nzeru mwakuti timasowa chonena m’pemphero? Zikatero ‘mzimu mwini umatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.’ (Aroma 8:26, 27) Panthawi imeneyi, Mulungu amatenga mapemphero opezeka m’Mawu ake monga mapemphero amene angakwaniritse zofuna zathuzo.

15 M’Malemba muli mapemphero ambiri ndi maganizo omwe angagwirizane ndi ‘zobuula zathu zosatheka kuneneka.’ Mwachitsanzo, taganizirani Salmo 119:121-128. Mmene salmo limeneli likufotokozera zinthu, zingagwirizane ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Mwachitsanzo, ngati tikuopa kuchitiridwa chinyengo, tingapemphe thandizo la Mulungu monga momwe wamasalmoyu anachitira. (Mavesi 121-123) Mwina tikufuna kusankha chochita pankhani yovuta. Pamenepo tingapemphere kuti mzimu wa Yehova utithandize kukumbukira ndi kugwiritsa ntchito zikumbutso zake. (Mavesi 124, 125) Ngakhale kuti ‘timadana nazo njira zonse zonyenga,’ tingafunikebe kupempha Mulungu kuti achitepo kanthu kuti tisagonje pa chiyeso ndi kuswa malamulo ake. (Mavesi 126-128) Ngati timawerenga Baibulo tsiku lililonse, tingakumbukire malemba othandiza ngati amenewa pamene tikupemphera kwa Yehova.

Zikumbutso za Yehova Zimatithandiza

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani timafunikira zikumbutso za Mulungu, ndipo tiziziona motani? (b) Kodi ena angamatione motani, koma kodi n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri?

16 Ngati tikufuna kuti Mulungu azimva mapemphero athu ndiponso kuti atiyanje, tiyenera kumvera zikumbutso zake. (Salmo 119:129-136) Popeza sitichedwa kuiwala, timafunikira zikumbutso zodabwitsa za Yehova zimene zimatikumbutsa malangizo ndi malamulo ake. Inde, timayamikira kuunika kwauzimu kumene kumawala pakakhala kamvedwe katsopano kalikonse ka mawu a Mulungu. (Salmo 119:129, 130) Komanso tikuyamikira kuti Yehova ‘wawalitsira nkhope yake pa ife’ posonyeza kuti akutiyanja, ngakhale kuti ‘maso athu akutsitsa mitsinje ya madzi’ chifukwa choti ena akuswa chilamulo chake.​—Salmo 119:135, 136; Numeri 6:25.

17 Mosakayikira, Mulungu adzapitiriza kutiyanja ngati titsatira zikumbutso zake zolungama. (Salmo 119:137-144) Monga atumiki a Yehova, tikuvomereza kuti n’koyenera kuti azitikumbutsa zikumbutso zake ndi kuzikhazikitsa monga malamulo oti tiwatsatire. (Salmo 119:138) Popeza kuti wamasalmoyu ankamvera malamulo a Mulungu, n’chifukwa chiyani ananena kuti: “Wamng’ono ine, ndi wopepulidwa”? (Salmo 119:141) Zikuoneka kuti anali kufotokoza mmene adani ake ankamuonera. Ena angatinyoze chifukwa chakuti tikutsatira chilungamo mosasunthika. Komabe, chofunika kwambiri n’chakuti Yehova azitiyanja chifukwa chotsatira zikumbutso zake zolungama pamoyo wathu.

Kukhala Otetezeka Ndiponso Pamtendere

18, 19. Kodi tikamamvera zikumbutso za Mulungu zotsatira zake zimakhala zotani?

18 Kumvera zikumbutso za Mulungu kumatithandiza kuyandikira kwa iye. (Salmo 119:145-152) Chifukwa chakuti timalabadira zikumbutso za Yehova, timakhala omasuka kuitanira pa iye ndi mtima wonse, ndipo timadziwa kuti atimvera. Tingathe kugalamuka m’mamawa “kusanache” ndi kupempha thandizo. Imeneyi ndi nthawi yabwinodi kupemphera. (Salmo 119:145-147) Mulungu alinso pafupi ndi ife chifukwa chakuti timapewa khalidwe lotayirira ndipo timaona mawu ake monga choonadi, monganso mmene Yesu anachitira. (Salmo 119:150, 151; Yohane 17:17) Ubwenzi wathu ndi Yehova umatithandiza m’dziko lamavutoli ndipo udzatithandiza pa nkhondo yake yaikulu ya Armagedo.​—Chivumbulutso 7:9, 14; 16:13-16.

19 Chifukwa choti timalemekeza kwambiri mawu a Mulungu, ndife otetezekadi. (Salmo 119:153-160) ‘Sitinapatukane nazo mboni zake’ kapena kuti zikumbutso zake, monga mmene anthu oipa achitira. Timakonda malangizo a Mulungu chotero ndife otetezeka chifukwa cha chifundo chake. (Salmo 119:157-159) Zikumbutso za Yehova zimatithandiza kukumbukira zimene iye amafuna kwa ife pa nkhani iliyonse. Koma malangizo a Mulungu amatiuza zochita, ndipo timavomereza ndi mtima wonse kuti Mlengi wathu ndiye ayenera kutipatsa malangizo. Popeza tikudziwa kuti ‘chiwerengero cha mawu a Mulungu ndicho choonadi,’ ndiponso kuti patokha sitingathe kulongosola mapazi athu, timatsatira malangizo a Mulungu mosangalala.​—Salmo 119:160; Yeremiya 10:23.

20. N’chifukwa chiyani tili ndi “mtendere wambiri”?

20 Timapeza mtendere wochuluka chifukwa chokonda chilamulo cha Yehova. (Salmo 119:161-168) Chizunzo sichimatichotsera “mtendere wa Mulungu” wosayerekezeka umenewu. (Afilipi 4:6, 7) Timayamikira kwambiri ziweruzo za Yehova mwakuti timamulemekeza nthawi zonse, inde “kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi.” (Salmo 119:161-164) Wamasalmo anaimba kuti: “Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa,” kapena kuti chopunthwitsa. (Salmo 119:165) Ngati ifeyo patokha timakonda ndi kusunga chilamulo cha Yehova, sitidzapunthwa mwauzimu ndi zimene winawake wachita kapena chifukwa cha nkhani ina iliyonse.

21. Ndi zitsanzo za m’Malemba ziti zimene zikusonyeza kuti sitiyenera kupunthwa ngati mumpingo mwabuka mavuto?

21 Baibulo limatchula anthu ambiri omwe sanalole chilichonse kukhala chopunthwitsa chosatha kwa iwo. Mwachitsanzo, mwamuna wachikristu Gayo sanapunthwe ndi makhalidwe osaopa Mulungu a Diotrefe, m’malo mwake anapitirizabe ‘kuyenda m’choonadi.’ (3 Yohane 1-3, 9, 10) Paulo anadandaulira akazi achikristu Euodiya ndi Suntuke kuti “alingirire ndi mtima umodzi,” mwachionekere chifukwa chakuti akazi amenewa anali atasemphana maganizo. Zikuoneka kuti anathandizidwa kuthetsa vuto lawolo ndipo anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. (Afilipi 4:2, 3) Choncho tisapunthwe ngati mumpingo mwabuka mavuto alionse. Tiyeni tiike maganizo athu onse pa kusunga malangizo a Yehova, ndi kukumbukira kuti ‘njira zathu zonse zili pamaso pake.’ (Salmo 119:168; Miyambo 15:3) Tikatero palibe chimene chidzasokoneze ‘mtendere wathu wambiriwu.’

22. (a) Kodi tingapeze dalitso lotani tikamamvera Mulungu? (b) Kodi anthu ena amene anachoka mu mpingo wachikristu tiziwaona motani?

22 Ngati timvera Yehova nthawi zonse, tidzakhala ndi mwayi wopitirizabe kumulemekeza. (Salmo 119:169-176) Tikamatsatira malemba a Mulungu pamoyo wathu, timakhala otetezeka mwauzimu komanso ‘milomo yathu imapitiriza kulemekeza’ Yehova. (Salmo 119:169-171, 174) Palibenso dalitso lalikulu loposa limeneli lomwe tingakhale nalo m’masiku otsiriza ano. Wamasalmo ankafuna atakhalabe ndi moyo n’kumalemekeza Yehova, koma m’njira imene sinatchulidwe, iye ‘anasochera ngati nkhosa yotayika.’ (Salmo 119:175, 176) Ena amene achoka mu mpingo wachikristu angakhale akukondabe Mulungu ndipo angamafune kumulemekeza. Chotero tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuthandiza anthu amenewa kuti abwerere m’malo otetezeka mwauzimu, n’kupeza chimwemwe potamanda Yehova limodzi ndi anthu ake.​—Ahebri 13:15; 1 Petro 5:6, 7.

Kuunika Kosatha Panjira Yathu

23, 24. Kodi mwapindula chiyani pophunzira Salmo 119?

23 Salmo 119 lingatipindulitse m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, lingatithandize kudalira kwambiri Mulungu, chifukwa chakuti salmo limeneli likusonyeza kuti chimwemwe chenicheni tingachipeze mwa ‘kuyenda m’chilamulo cha Yehova.’ (Salmo 119:1) Wamasalmo akutikumbutsa kuti ‘chiwerengero cha mawu a Mulungu ndicho choonadi.’ (Salmo 119:160) Zimenezitu ziyenera kutithandiza kuwonjezera kuyamikira kwathu Mawu onse olembedwa a Mulungu. Kusinkhasinkha Salmo 119 kuyenera kutilimbikitsa kuphunzira Malemba mwakhama. Mobwerezabwereza wamasalmo anapempha Mulungu kuti: “Ndiphunzitseni malemba anu.” (Salmo 119:12, 68, 135) Anachondereranso kuti: “Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.” (Salmo 119:66) Nafenso tiyenera kupemphera chimodzimodzi.

24 Ziphunzitso za Mulungu zimathandiza munthu kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mobwerezabwereza wamasalmo anadzitcha mtumiki wa Mulungu. Ndipotu anauza Yehova mawu okhudza mtima akuti: “Ine ndine wanu.” (Salmo 119:17, 65, 94, 122, 125; Aroma 14:8) Ndi mwayitu wamtengo wapatali kutumikira ndi kulemekeza Yehova monga mmodzi wa Mboni zake. (Salmo 119:7) Kodi mukutumikira Mulungu mokondwera monga wolengeza Ufumu? Ngati mukutero, mosakayika konse Yehova adzapitiriza kukuchirikizani ndi kukudalitsani mu ntchito yapadera imeneyi ngati nthawi zonse mumakhulupirira mawu ake ndi kulola kuti mawu akewo aunike njira yanu.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda mawu a Mulungu?

• Kodi mawu a Mulungu amatichirikiza motani?

• Kodi zikumbutso za Yehova zimatithandiza m’njira ziti?

• N’chifukwa chiyani anthu a Yehova ali otetezeka komanso ali pamtendere?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Mawu a Mulungu ndiwo gwero limodzi la kuunika kwauzimu

[Chithunzi patsamba 17]

Ngati timakonda zikumbutso za Yehova, sadzationa ngati ‘zinyansi’

[Zithunzi patsamba 18]

Ngati timawerenga Baibulo tsiku lililonse, pamene tikupemphera tingakumbukire mwamsanga malemba othandiza