Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anachita Zazikulu

Anachita Zazikulu

Anachita Zazikulu

KODI mumakumana ndi mavuto kuntchito, kusukulu, m’banja, chifukwa cha chikhulupiriro chanu, kapena chifukwa choti chipembedzo chanu n’choletsedwa ndi Boma? Musataye mtima. Mboni za Yehova zambiri zakumanapo ndi mavuto otero, koma zinatha kuchitabe zinthu zazikulu kwambiri. Mwachitsanzo, taonani zimene anachita Erna Ludolph.

Erna anabadwa mu 1908 ku Lübeck, m’dziko la Germany. Iye yekha ndiye anali kutumikira Yehova m’banja mwawo. Hitler atayamba kulamulira mu 1933, Mboni za Yehova zinayamba kuvutitsidwa. Kuntchito, anzake a Erna anayamba kudana naye chifukwa chokana kuchita sawatcha ya Hitler. Chifukwa cha izi, iye anamangidwa ndi achipani cha Nazi. Anakhala m’ndende zosiyanasiyana zokwana eyiti ndiponso m’ndende zozunzirako anthu za Hamburg-Fuhlsbüttel, Moringen, Lichtenburg, ndi Ravensbrück. Ali m’ndende ya Ravensbrück, panachitika chinachake chomwe chinam’patsa mwayi wochita zazikulu.

Wantchito Wabwino Koposa

Pulofesa Friedrich Holtz ndi akazi wake Alice anali kukhala mu mzinda wa Berlin. Iwo sanali achipani cha Nazi ndipo sankagwirizana ndi zochita za chipanichi. Koma iwo anali achibale a mmodzi mwa akuluakulu a gulu la apolisi la SS, yemwe ankayang’anira akaidi ena m’ndende zozunzirako anthu. Ndiye pamene a Holtz ndi akazi awo anali kufuna wantchito, mkulu wa SS uja anawalola kuti akasankhe mkaidi wamkazi. Choncho, m’mwezi wa March 1943, mayi Holtz anapita ku Ravensbrück kukasankha wantchito. Kodi anasankha ndani? Anasankha Erna Ludolph. Erna anayamba kukhala ndi banja la a Holtz ndipo anali kukhala naye bwino. Nkhondo itatha, banjalo limodzi ndi Erna anasamukira ku mzinda wa Halle m’mphepete mwa mtsinje wa Saale. Kumeneko Erna anavutitsidwanso ndi akuluakulu a boma la Sosholizimu la East Germany. Mu 1957 banja la a Holtz analithamangitsa m’dzikolo ndipo linapita ku West Germany limodzi ndi Erna. Kumeneko, Erna tsopano anali ndi ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi chikhulupiriro chake.

Kodi Erna anachita zazikulu m’njira yotani? Chifukwa cha khalidwe lake labwino ndiponso kulalikira mwaluso uthenga wa m’Baibulo, mayi Holtz ndi ana awo asanu anakhala Mboni za Yehova zobatizidwa. Kuwonjezera apo, adzukulu 11 a mayi Holtz nawonso ndi Mboni. Awiri mwa adzukuluwo akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Selters m’dziko la Germany. Mwana wamkazi wa mayi Holtz dzina lake Susanne anati: “Banja lathu lili m’choonadi makamaka chifukwa cha chitsanzo cha Erna.” Kupirira kwa Erna kunapindula kwambiri. Nanga bwanji za inu? Ngati mutapirira mokhulupirika pa mavuto aakulu, mungadzapindule mofanana ndi Erna. Inde, khalidwe labwino ndi kulalikira mwaluso kungakuthandizeni kuchita zazikulu. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Pamene nkhaniyi inali kukonzedwa, Erna Ludolph anamwalira ali ndi zaka 96, ali wokhulupirikabe.

[Chithunzi patsamba 31]

Erna Ludolph (wakhala pampandoyo) ndi a m’banja la a Holtz