Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiphunzitso cha Kuuka kwa Akufa Chimakukhudzani

Chiphunzitso cha Kuuka kwa Akufa Chimakukhudzani

Chiphunzitso cha Kuuka kwa Akufa Chimakukhudzani

“Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—MACHITIDWE 24:15.

1. Kodi zinatani kuti nkhani ya kuuka kwa akufa ivute pamaso pa Sanihedirini?

ATATSIRIZA ulendo wake wachitatu wa umishonale mu 56 C.E., mtumwi Paulo anapita ku Yerusalemu. Ali kumeneko, Aroma anamumanga ndipo anam’patsa mwayi wokaonekera ku khoti lalikulu la Chiyuda, la Sanihedirini. (Machitidwe 22:29, 30) Paulo anaona kuti ena mwa anthu a m’khotili anali Asaduki ndipo ena anali Afarisi. Magulu awiriwa ankasiyana maganizo kwambiri pa mfundo imodzi. Asaduki ankatsutsa zoti kudzakhala kuuka kwa akufa; koma Afarisi ankavomerezana nazo. Posonyeza mmene iyeyo ankaonera nkhaniyi, Paulo anati: “Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.” Ponena zimenezi, Paulo anasokonezeratu khotilo!​—Machitidwe 23:6-9.

2. Kodi n’chifukwa chiyani Paulo anali wokonzeka kunena zifukwa zimene iyeyo amakhulupirira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?

2 Zaka zambiri m’mbuyo mwake, ali panjira kupita ku Damasiko, Paulo anaona masomphenya n’kumva mawu a Yesu. Paulo anafunsa Yesuyo kuti: “Ndidzachita chiyani, Ambuye?” Ndipo Yesu anayankha kuti: “Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.” Ku Damasiko, Paulo anakapezana ndi Hananiya, wophunzira wachikristu yemwe anali wothandiza kwambiri. Iyeyu anamulongosolera kuti: “Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo [Yesu woukitsidwa], numve mawu otuluka mkamwa mwake.” (Machitidwe 22:6-16) Motero n’zosadabwitsa kuti Paulo anali wokonzeka kunena zifukwa zimene iyeyo amakhulupirira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.​—1 Petro 3:15.

Kulengeza za Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa

3, 4. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti anali wosasunthika pouza ena za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, ndipo kodi chitsanzo chakechi chingatiphunzitse chiyani?

3 Pambuyo pake, Paulo anakaonekera pamaso pa kazembe Felike. Pamenepa, Tertulo, wodziwa kulankhula pagulu, amene anayala mlandu wonse umene Ayuda ankamuimba Paulo, ananena kuti Paulo anali m’tsogoleri wa gulu lampatuko ndiponso kuti n’ngoukira boma. Panthawi yake yolankhula, Paulo ananena mosazengereza kuti: “Monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu.” Kenaka, ponena chinatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga, Paulo anapitiriza kuti: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 23:23, 24; 24:1-8, 14, 15.

4 Patatha zaka ziwiri, Porkiyo Festo, amene analowa m’malo mwa Felike, anaitana mfumu Herode Agripa kuti athandizane kumuzenga mlandu Paulo. Festo analongosola kuti anthu oimba mlandu Paulo ankatsutsana naye pa mfundo yoti ‘munthu wina, dzina lake Yesu, amene adafa . . . ali moyo.’ Ponena mbali yake, Paulo anafunsa kuti: “Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa?” Kenaka anatinso: “Pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang’ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika; kuti Kristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.” (Machitidwe 24:27; 25:13-22; 26:8, 22, 23) Ndithu, Paulo anali wosasunthika pouza ena za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Monga Paulo, ifenso tingathe kulalikira molimba mtima zoti kudzakhala kuuka kwa akufa. Koma kodi tingayembekezere kukumana ndi zotani tikamaphunzitsa anthu zimenezi? N’zosakayikitsa kuti sizingasiyane ndi zimene Paulo anakumana nazo.

5, 6. (a) Kodi anthu amene anamva atumwi akufotokoza za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa anaitenga motani nkhaniyi? (b)  Kodi n’chiyani chili chofunika kwambiri tikamauza ena chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?

5 Taganizirani zimene Paulo anakumana nazo m’mbuyo mwake, paulendo wachiwiri wa umishonale (cha m’ma 49 mpaka 52 C.E.) pamene anapita ku Atene. Iye anakambirana ndi anthu amene ankakhulupirira milungu yambirimbiri, ndipo anawalimbikitsa kuti aganizire za cholinga cha Mulungu chodzaweruza dziko lonse lapansi mwachilungamo kudzera mwa munthu amene Iye waika. Munthu ameneyu sanali wina ayi, koma Yesu. Paulo analongosola kuti Mulungu anatsimikizira mfundo imeneyi poukitsa Yesu. Kodi anthuwo anatani atamva zimenezi? Baibulo limati: “Pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.”​—Machitidwe 17:29-32.

6 Zimenezi n’zofanana ndi zimene Petro ndi Yohane anakumana nazo patatha nthawi yochepa phwando la Pentekoste la mu 33 C.E. litachitika. Apanso Asaduki ndiwo makamaka anautsa mapiri pachigwa. Lemba la Machitidwe 4:1-4 limalongosola nkhaniyi motere: “Mmene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa kukachisi ndi Asaduki anadzako, ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.” Komabe ena anasangalala nazo. “Ambiri a iwo amene adamva mawu anakhulupira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.” Motero, tikamauza anthu za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, tiyenera kuyembekeza kuti anthuwo nkhaniyi aziitenga m’njira yosiyanasiyana. Motero, m’pofunikadi kumafotokoza za chikhulupiriro chathu pa chiyembekezo chimenechi.

Chikhulupiriro ndi Kuuka kwa Akufa

7, 8. (a) Malingana ndi zimene zili m’kalata yopita ku mpingo wa ku Korinto wa m’zaka 100 zoyambirira, kodi zingatheke bwanji kuti chikhulupiriro chikhale chachabe? (b) Kodi kumvetsetsa chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kumalekanitsa bwanji Akristu oona ndi onyenga?

7 Ena amene anakhala Akristu m’zaka 100 zoyambirira anavutika kuvomereza chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Ena mwa anthu amenewa anali a mu mpingo wa ku Korinto. Paulo anawalembera kuti: “Ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo.” Kenaka, Paulo anatsimikizira mfundo yoonayi ponena kuti Kristu ataukitsidwa anaoneka “kwa abale oposa mazana asanu,” ndipo Paulo anati ambiri mwa iwo anali ndi moyo panthawiyo. (1 Akorinto 15:3-8) Iye anafotokozanso kuti: “Ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.”​—1 Akorinto 15:12-14.

8 Inde, chiphunzitso cha kuuka kwa akufa n’chofunika kwambiri moti chikhulupiriro cha Chikristu sichingakhale ndi phindu lililonse ngati chiphunzitsochi chitakhala kuti si chenichenidi. Inde, kumvetsetsa chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kumasiyanitsa Akristu oona ndi onyenga. (Genesis 3:4; Ezekieli 18:4) Motero, Paulo anaika chiyembekezo cha kuuka kwa akufa m’gulu la “mawu a chiyambidwe” a Chikristu. Tiyeni tiyesetse ‘kupitiriza kutsata ukulu msinkhu.’ Paulo analimbikitsa kuti: “Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.”​—Ahebri 6:1-3.

Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa

9, 10. Kodi Baibulo limatanthauzanji likamanena za kuuka kwa akufa?

9 Kuti tilimbikitse chikhulupiriro chathu m’chiyembekezo cha kuuka kwa akufa tiyeni tiganizirenso mafunso monga akuti: Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena za kuuka kwa akufa? Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimaonetsa bwanji kukula kwa chikondi cha Yehova? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kukonda Mulungu kwambiri komanso atithandiza kuphunzitsa ena za chiyembekezochi.​—2 Timoteo 2:2; Yakobo 4:8.

10 Mawu akuti “kuuka kwa akufa” amamasulira mawu a Chigiriki omwe kwenikweni amatanthauza “kuimanso chilili.” Kodi mawu amenewa amasonyezanso chiyani? Baibulo limati chiyembekezo cha kuuka kwa akufa ndicho kutsimikiza mtima kuti munthu wakufa angathe kukhalanso ndi moyo. Baibulo limasonyezanso kuti munthuyo amaukanso ndi thupi lamunthu apo ayi lauzimu, malingana ndi chiyembekezo cha munthuyo, kaya n’chodzakhala padziko lapansi kapena chopita kumwamba. Timachita kusowa chonena tikaganizira za chikondi, nzeru, ndiponso mphamvu za Yehova zokwaniritsira chiyembekezo chimenechi.

11. Kodi atumiki odzozedwa a Mulungu anapatsidwa chiyembekezo chotani pankhani ya kuuka kwa akufa?

11 Poukitsidwa, Yesu ndi abale ake odzozedwa amakhala ndi matupi auzimu oyenererana ndi kukatumikira kumwamba. (1 Akorinto 15:35-38, 42-53) Onsewa adzatumikira monga olamulira mu Ufumu wa Mesiya, umene udzabweretse Paradaiso padziko lapansi. Odzozedwa ndiwo ansembe achifumu omwe ali pansi pa Yesu, Mkulu wa Ansembe. M’dziko latsopano la chilungamo, odzozedwa adzapatsa anthu onse madalitso a nsembe ya dipo ya Kristu. (Ahebri 7:25, 26; 9:24; 1 Petro 2:9; Chivumbulutso 22:1, 2) Pakali pano anthu odzozedwa amene akanali ndi moyo padziko pano amayesetsa kukhalabe ovomerezeka kwa Mulungu. Akamwalira adzalandira mphotho yawo poukitsidwa n’kukakhala ndi moyo wosafa wauzimu kumwamba. (1 Akorinto 15:51, 52; 2 Akorinto 5:1-3, 6-8, 10; Chivumbulutso 14:13) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake.” (Aroma 6:5) Nangano bwanji za anthu amene adzakhalenso padziko lapansi akadzaukitsidwa? Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingawathandize bwanji kukonda Mulungu? Tingaphunzire zinthu zambiri pankhaniyi poona chitsanzo cha Abrahamu.

Nkhani ya Kuuka kwa Akufa ndi Kukhala Paubwenzi ndi Yehova

12, 13. Kodi Abrahamu anali ndi maziko amphamvu otani okhalira ndi chikhulupiriro cha kuuka kwa akufa?

12 Abrahamu, amene Baibulo limati anali “bwenzi la Mulungu,” anali munthu wa chikhulupiriro chachikulu kwambiri. (Yakobo 2:23) Paulo anatchulapo katatu za chikhulupiriro cha Abrahamuyu pagulu la amuna ndi akazi achikhulupiriro omwe iye anawatchula mu chaputala 11 cha Ahebri. (Ahebri 11:8, 9, 17) Kachitatuko Paulo ananena za chikhulupiriro chimene Abrahamu anasonyeza pomvera Mulungu n’kukonzekera kupereka nsembe mwana wake Isake. Abrahamu sankakayika ngakhale pang’ono kuti Yehova anatsimikizira lonjezo la mbewu yodzera mwa Isake. Ngakhale Isake akanafa poperekedwa nsembe, Abrahamu anadziwa “kuti Mulungu n’ngokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa.”

13 Malingana ndi mmene zinthu zinachitikira, Yehova anaona kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinali cholimba kwambiri, motero anapereka chiweto kuti ndicho chikhale nsembe m’malo mwa Isake. Komabe, zimene zinam’chitikira Isake zinali kuphiphiritsira kuuka kwa akufa, monga mmene Paulo analongosolera, kuti : “Kuchokera komwe [Abrahamu], pachiphiphiritso, anam’landiranso [Isake].” (Ahebri 11:19) Kuphatikizanso apo, Abrahamu anali kale ndi maziko amphamvu kwambiri a chikhulupiriro cha kuuka kwa akufa. Ankadziwa bwino lomwe kuti Yehova ndiye anaukitsanso mphamvu yake yobereka pamene iyeyo ndi mkazi wake Sara, anakhala pamodzi ali okalamba n’kubereka mwana wawo, Isake.​—Genesis 18:10-14; 21:1-3; Aroma 4:19-21.

14. (a) Malingana ndi lemba la Ahebri 11:9, 10, kodi Abrahamu anadikira chiyani? (b) Kodi n’chiyani chiyenera kudzam’chitikira kaye Abrahamu kuti adzalandire madalitso a Ufumu m’dziko latsopano? (c) Kodi tingatani kuti tilandire madalitso a Ufumu?

14 Paulo analongosola kuti Abrahamu anali mlendo ndiponso munthu wokhala m’mahema yemwe “analindirira mudzi wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:9, 10) Umenewu sunali mudzi kapena kuti mzinda weniweni monga mzinda wa Yerusalemu, womwe kunali kachisi wa Mulungu. Ayi, uwu unali mzinda wophiphiritsira. Unali Ufumu wakumwamba wa Mulungu wokhala ndi Kristu Yesu ndiponso olamulira anzake 144,000. Anthu 144,000 amenewa, muulemerero wawo wa kumwamba amatchulidwanso kuti “mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano,” “mkwatibwi” wa Kristu. (Chivumbulutso 21:2) M’chaka cha 1914, Yehova anaika Yesu kukhala Mfumu ya Umesiya ya Ufumu wa kumwambawu ndipo anamuuza kuti alamulire pakati pa adani ake. (Salmo 110:1, 2; Chivumbulutso 11:15) Kuti Abrahamu, “bwenzi la Mulungu” uja adzalandire madalitso a ulamuliro wa Ufumuwu, ayenera kudzauka n’kukhalanso ndi moyo. Moteronso, kuti ifeyo tidzalandire madalitso a Ufumuwu, tiyenera kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu, kaya monga a khamu lalikulu la opulumuka pa Armagedo kapena monga oukitsidwa kwa akufa. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komano kodi maziko a chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’ngotani?

Chikondi cha Mulungu Ndicho Maziko a Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa

15, 16. (a) Kodi ulosi woyamba m’Baibulo umaika motani maziko a chiyembekezo chathu cha kuuka kwa akufa? (b) Kodi kukhulupirira za kuuka kwa akufa kungatithandize bwanji kuti tizim’konda kwambiri Yehova?

15 Kukhala paubwenzi wabwino ndi Atate wathu wachikondi wakumwamba, kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha Abrahamu, ndiponso kumvera malamulo a Mulungu kumatipatsa mwayi woti Yehova atione ngati olungama ndiponso ngati mabwenzi ake. Zimenezi zimatipatsa mwayi wodzapindula nawo ndi zimene Ufumuwu udzachite. Inde, ulosi woyamba kulembedwa m’Mawu a Mulungu, wa pa Genesis 3:15, umakhazikitsa maziko a chiyembekezo cha kuuka kwa akufa ndiponso maziko a ubwenzi ndi Mulungu. Ulosiwu sikuti umangonena za kulalira, kapena kuti kuphwanya mutu wa Satana kokha, koma umanenanso za kuvulaza chitendene cha Mbewu ya mkazi wa Mulungu. Kufa kwa Yesu pa mtengo kunali kuvulaza chitendene kophiphiritsira. Kuukitsidwa kwake pa tsiku lachitatu kunapoletsa chilonda chimenecho n’kulambula njira yodzathanirana ndi ‘amene ali nayo mphamvu ya imfa, ndiye Mdierekezi.’​—Ahebri 2:14.

16 Paulo akutikumbutsa kuti “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Kuyamikira chisomo chimenechi kumatithandiza kukondadi kwambiri Yesu ndiponso Atate wathu wachikondi wakumwamba.​—2 Akorinto 5:14, 15.

17. (a) Kodi Yobu ananena kuti anali ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi lemba la Yobu 14:15 limatidziwitsa chiyani za Yehova, ndipo kodi inuyo mukumva bwanji podziwa zimenezi?

17 Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika amene anakhalapo Chikristu chisanayambe, nayenso ankakhulupirira kuti kudzakhala kuuka kwa akufa. Iyeyu anavutika kwadzaoneni chifukwa cha zimene Satana anam’chitira. Mosiyana ndi anzake onamizira aja, amene sanatchulepo za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, Yobu anadzilimbitsa ndi chiyembekezo chimenechi ndipo anafunsa kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Yobu anadziyankha yekha kuti: ‘Ndidzayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.’ Kenaka ananena mawu awa kwa Mulungu wake, Yehova: ‘Mudzaitana, ndipo ndidzakuyankhani.’ Posonyeza mmene Mlengi wathu wachikondi amamvera, Yobu anati: ‘Mudzakhumba ntchito ya manja anu.’ (Yobu 14:14, 15) Inde, Yehova amayembekezera mwachidwi nthawi imene anthu okhulupirika adzauke pa kuuka kwa akufa n’kukhalanso amoyo. Zimenezi zimatithandiza kuti tiyandikane naye kwambiri pamene tikusinkhasinkha za chikondi ndiponso chisomo chimene amatisonyeza ngakhale kuti ndife opanda ungwiro.​—Aroma 5:21; Yakobo 4:8.

18, 19. (a) Kodi pali chiyembekezo chotani choti Danieli adzakhalanso ndi moyo? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana mfundo zotani?

18 Mneneri Danieli, amene mngelo wa Mulungu anamutchula kuti “wokondedwatu,” anakhala kwa nthawi yaitali akutumikira Mulungu mokhulupirika. (Danieli 10:11, 19) Iyeyu anakhulupirikabe kwambiri kwa Yehova kuchokera pamene anatengedwa kupita ku ukapolo mu 617 B.C.E. mpaka pamene anamwalira patatha nthawi ndithu chionereni masomphenya m’chaka cha 536 B.C.E., chomwe chinali chaka chachitatu cha ulamuliro wa Koresi, mfumu ya Perisiya. (Danieli 1:1; 10:1) Panthawi inayake pa chaka chachitatuchi cha ulamuliro wa Koresi, Danieli anaona masomphenya a mzera wa maulamuliro a dziko lonse amene adzathere pa chisautso chachikulu chikubweracho. (Danieli 11:1–12:13) Popeza kuti sanathe kumvetsa bwinobwino masomphenyawo, Danieli anafunsa mngelo amene anatumidwa kudzamusonyeza masomphenyawo kuti: “Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi n’chiyani?” Poyankha, mngeloyu anatchulapo za “nthawi ya chitsiriziro” pamene “aphunzitsi ndiwo adzazindikira.” Nangano Danieliyo tsogolo lake lidzakhala lotani? Mngeloyo anati: “Udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” (Danieli 12:8-10, 13) Danieli adzauka “pa kuuka kwa olungama,” mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu.​—Luka 14:14.

19 Tikukhala pamapeto penipeni pa masiku otsiriza ndipo tayandikira kwambiri chiyambi cha Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu kusiyana ndi mmene zinthu zinalili titangoyamba kumene kukhulupirira Mulungu. Motero tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzakhalapo m’dziko latsopano kuti ndidzakhale limodzi ndi anthu monga Abrahamu, Yobu, Danieli, ndiponso amuna komanso akazi ena okhulupirika?’ Tingadzakhalepo ngati tikuyesetsa kuti tisatalikirane ndi Yehova ndiponso kuyesetsa kumvera malamulo ake. M’nkhani yotsatirayi, tikambirana mfundo zinanso zokhudza chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kuti tithe kudziwa omwe adzaukitsidwe.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi anthu anachita zotani pamene Paulo analengeza za chiyembekezo chake cha kuuka kwa akufa?

• Kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimasiyanitsa Akristu oona ndi onyenga?

• Kodi timadziwa bwanji kuti Abrahamu, Yobu, ndi Danieli ankakhulupirira za kuuka kwa akufa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Paulo anaonekera pamaso pa kazembe Felike n’kulalikira molimba mtima za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi n’chifukwa chiyani Abrahamu ankakhulupirira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?

[Chithunzi patsamba 12]

Yobu analimba mtima chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa

[Chithunzi patsamba 12]

Danieli adzauka n’kukhalanso ndi moyo panthawi ya kuuka kwa olungama