Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa N’chosangalatsa
Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa N’chosangalatsa
CHIKHULUPIRIRO cha kuuka kwa akufa n’chofala. Buku loyera la Chisilamu, la Korani, lili ndi chaputala chathunthu chongofotokoza za kuuka kwa akufa. Mbali ina ya Sura 75 imanena kuti: “Ndikulumbirira tsiku lachimaliziro. . . . Kodi munthu akuganiza kuti . . . sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake? . . . Akufunsa (mwa chipongwe): ‘Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?’ . . . Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa?”—Sura 75:1-6, 40.
Buku la The New Encyclopædia Britannica, limati: “Malinga ndi chikhulupiriro cha anthu a chipembedzo cha Zoroastrianism, zoipa zonse zidzagonjetsedwa, kudzakhala kuuka kwa akufa, kudzakhala chiweruzo chotsiriza, ndipo dzikoli lidzakonzedwanso kuti olungama akhalemo.”
Buku la Encyclopaedia Judaica limanena kuti kuuka kwa akufa ndi “chikhulupiriro choti akufa adzauka ndi matupi awo n’kudzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.” Buku lomwelo limanenanso kuti chikhulupiriro chimene Chiyuda chimavomereza, choti munthu ali ndi mzimu womwe sufa, n’chovuta kumvetsa. Bukuli limavomereza kuti: “Kunena mwachidule, zikhulupiriro ziwirizi, choti akufa adzauka ndi choti munthu ali ndi mzimu womwe sufa, n’zotsutsana.”
Chihindu chimaphunzitsa kuti munthu amamwalira n’kumabadwanso nthawi zambirimbiri. Ngati zimenezi zili zoona ndiye kuti munthu ayenera kukhala ndi mzimu umene sufa iyeyo akamwalira. Buku loyera la Chihindu, la Bhagavad Gita, limati: “Mzimu, womwe umadzadza thupi lonse, sufa. Palibe amene angathe kuwononga mzimu chifukwa mzimu suwonongeka.”
Chibuda chimasiyana ndi Chihindu poti sichivomereza zoti munthu ali ndi mzimu womwe sufa. Komabe, masiku ano Abuda ambiri a ku Far East amakhulupirira kuti mzimu sufa koma umangosamuka. *
Kusokoneza Chiphunzitso cha Kuuka kwa Akufa
Nthawi zambiri pa miyambo ya maliro a Matchalitchi Achikristu amatchulapo mawu osonyeza kuti mzimu umakhalabe ndi moyo munthu akafa komanso mawu osonyeza kuti anthu akufa adzaukitsidwa. Mwachitsanzo, abusa a Angilikani nthawi zambiri amanena mawu akuti: “Popeza mbale wathu . . . wachoka m’moyo uno, tiliika thupi lake m’nthaka; dothi kudothi; phulusa kuphulusa; pfumbi kupfumbi. Chikhulupiriro chathu chonse chili m’chifundo cha Atate wathu wakumwamba, ndi m’kupambana kwa Mwana wake Yesu Kristu Ambuye wathu, amene adafa naikidwa m’manda, naukanso kwa akufa chifukwa chathu, ndipo tsopano ali moyo ndi Mfumu kunthaŵi zosatha.”—Mapemphero ndi Nyimbo za Eklezia.
Mawu amenewa angachititse munthu kudzifunsa kuti kodi Baibulo limaphunzitsa kuti akufa adzauka kapena kuti anthu ali ndi mzimu wosatheka
kufa? Komabe, onani mawu amene ananena pulofesa wina wachipolotesitanti wa ku France dzina lake Oscar Cullmann. M’buku lake lakuti Immortality of the Soul or Resurrection of the Dead? iye analemba kuti: “Pali kusiyana kwakukulu pakati pa chikhulupiriro cha Chikristu choti akufa adzauka ndi chikhulupiriro cha Agiriki chakuti mzimu sufa. . . . Ngakhale kuti Chikristu chinadzayamba kugwirizanitsa zikhulupiriro ziwirizi, ndipo masiku ano Akristu ambiri amasokoneza kwambiri zikhulupirirozi, sindikuona chifukwa chilichonse chobisira mfundo imene ineyo ndiponso akatswiri ambiri a maphunziro a Baibulo amaona kuti n’njoona. . . . Mfundo yake n’njakuti m’mabuku onse a Chipangano Chatsopano chikhulupiriro chimene amachigogomezera ndicho cha kuuka kwa akufa. . . . Mmenemo amati munthu yense wathunthu, amene wafadi mbali ina iliyonse, amaukitsidwa polengedwanso ndi Mulungu.”Motero n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amasokonezeka pankhani ya imfa ndiponso kuuka kwa akufa. Kuti tisasokonezeke motere, tiyenera kuona zimene Baibulo limanena, chifukwa Baibulo limanena zinthu zoona zimene Yehova Mulungu, Mlengi wa anthu, anavumbula. M’Baibulo munalembedwa nkhani zingapo za kuuka kwa akufa. Tiyeni tione nkhani zinayi zoterezi ndi kuona mmene zingatitsegulire m’maso pankhaniyi.
“Akazi Analandira Akufa Awo mwa Kuuka kwa Akufa”
M’kalata yake yopita kwa Ayuda amene anali atayamba Chikristu, mtumwi Paulo ananena kuti akazi achikhulupiriro “analandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa.” (Ahebri 11:35) Mmodzi wa akazi amenewa ankakhala ku tauni ya ku Foinike ya Zarefati, kufupi ndi Sidoni m’gombe la nyanja ya Mediterranean. Uyu anali mayi wamasiye amene analandira Eliya, mneneri wa Mulungu, n’kumam’patsa chakudya ngakhale panthawi imene kunali njala yadzaoneni. N’zomvetsa chisoni kuti mwana wa mayiyu anadwala n’kumwalira. Nthawi yomweyo Eliya anamunyamula n’kupita naye m’chipinda chosanja chimene Eliyayo ankakhalamo. Kenaka anadandaulira Yehova kuti abwezeretse moyo wa mnyamatayo. Ndiye panachitika chinthu chozizwitsa, motero mnyamatayo ‘anakhalanso moyo.’ Eliya anapita ndi mwanayo kwa mayi wake n’kumuuza kuti: “Taona, mwana wako ali moyo.” Kodi mayiyo anatani? Mosangalala, iye anati: “Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mawu a Yehova ali mkamwa mwanuwo n’ngoona.”—1 Mafumu 17:22-24.
M’dera lina la kummwera kwa Zarefati, pamtunda wa makilomita pafupifupi 100, munkakhala munthu wina ndi mkazi wake omwe anasamalira mneneri Elisa, yemwe analowa m’malo mwa Eliya. Iwowa anali anthu owolowa m’manja kwambiri. Mkaziyo anali wodziwika kwambiri m’tauni yakwawo ya Sunemu. Iyeyu ndi mwamuna wake anagwirizana zom’patsa malo ogona Elisa m’chipinda chosanja cha m’nyumba yawo. Chisoni chawo choti anali opanda ana chinatheratu pamene mkaziyo anadzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo atasinkhuka, nthawi zambiri ankapita kumunda pamodzi bambo ake komanso anthu okakolola dzinthu. Koma tsiku lina panachitika zoopsa. Mwana uja anadandaula kuti mutu ukumupweteka kwabasi. Motero munthu wina anathamangira naye kunyumba. Mayi ake anamuika pamwendo, komabe patapita nthawi mwanayo anamwalira. Mayiyo anasowa pogwira
motero anaganiza zokapeza thandizo kwa Elisa. Ndiye anatengana ndi munthu wina n’kuyamba ulendo wa kumpoto chakumadzulo, polowera ku phiri la Karimeli, kumene Elisa anali kukhala.Mneneriyo atamva nkhaniyi anatumiza Gehazi, mtumiki wake, kuti atsogole, ndipo anakapeza kuti mnyamatayo analidi atamwalira. Elisa ndi mayiyo ankabwera pambuyo pake, koma kodi chinachitika n’chiyani atafika ku Sunemu? Nkhani ya pa 2 Mafumu 4:32-37 imati: “Ndipo pamene Elisa analowa m’nyumba, taonani, mwanayo n’ngwakufa, adam’goneka pakama pake. Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova. Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda. Pamenepo anabwera nayenda m’nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake. Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunemu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ake, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wake, natuluka.”
Monga mayi wamasiye wa ku Zarefati, mayi wa ku Sunemu ankadziwa kuti zimene zinachitikazo, zinachitika mwa mphamvu ya Mulungu. Amayi awiri onsewa anali osangalala kwambiri pamene Mulungu anaukitsa ana awo okondedwa.
Kuuka kwa Akufa M’nthawi ya Utumiki wa Yesu
Patatha zaka pafupifupi 900, munthu wina anaukitsidwa pafupi ndi Sunemu chakumpoto kwake, kunja kwa mudzi wa Nayini. Pamene Yesu Kristu ndi ophunzira ake anali paulendo wochoka ku Kapernao, atayandikira pa chipata cha Nayini, anakumana ndi gulu la anthu atanyamula maliro, ndipo Yesu anaona mayi wamasiye amene anaferedwa mwana wake m’modzi yekhayo. Yesu anamuuza mayiyu kuti asiye kulira. Luka, yemwe anali dokotala, analongosola motere zimene zinachitika: “Ndipo [Yesu] anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akum’nyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anam’pereka kwa amake.” (Luka 7:14, 15) Anthu amene anaona chozizwitsa chimenechi anatamanda Mulungu. Nkhani ya kuuka kwa wakufa ameneyu inafalikira chakummwera mpaka ku Yudeya ndiponso m’madera ozungulira derali. N’zochititsa chidwi kuti ophunzira a Yohane Mbatizi anamva nkhaniyi n’kukamuuza Yohane. Zitatero, Yohane anawatuma kuti akamufunse Yesuyo ngati Iyeyo ndiye anali Mesiya amene anthu ankamuyembekezera. Ndiyeno Yesu anakawauza kuti: “Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.”—Luka 7:22.
Yohane 11:39) Komatu, ngakhale kuti mtembo wa Lazaro unali utawonongeka, Yesu sanalephere kumuukitsa. Yesu atalamula, “womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo.” Zimene adani a Yesu anachita pambuyo pa zimenezi, zimatsimikizira kuti amene anaukitsidwayo analidi Lazaro.—Yohane 11:43, 44; 12:1, 9-11.
Nkhani yodziwika kwambiri ya anthu amene Yesu anawaukitsa ndi yokhudza mnzake wapamtima kwambiri, Lazaro. Chinachitika n’chakuti Lazaro atamwalira, Yesu anafika mochedwa kwawo kwa Lazaroyo. Motero pamene Yesu amafika ku Betaniyako, n’kuti patatha masiku anayi Lazaro atamwalira. Yesu atalangiza anthu kuti achotse mwala wotseka polowera mandawo, Marita analetsa ponena kuti: “Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi.” (Kodi nkhani zinayi za kuuka kwa akufa zimenezi zikutithandiza kuona chiyani? Zikutithandiza kuona kuti aliyense wakufayo anaukitsidwa n’kukhala mmene analili kale. Anthu onsewo anatha kudziwidwa ngakhale ndi achibale awo a pafupi kwambiri. Palibe aliyense mwa anthu oukitsidwawa amene ananenapo chilichonse chokhudza mmene zinthu zinalili panthawi yochepa imene anali atafayo. Palibe aliyense amene ananenapo zoti anapita ku dziko linalake. Ndipo zikuoneka kuti onse anauka ali ndi thanzi labwino. Kwa iwowo, zinali ngati kuti anagona kwa kanthawi kenaka n’kudzuka, monga mmene Yesu anasonyezera. (Yohane 11:11) Komabe, m’tsogolo mwake anthuwa anadzafanso.
Chiyembekezo Chodzaonananso ndi Okondedwa Athu N’chosangalatsa
Patatha nthawi yochepa chabe Owen tam’tchula m’nkhani yoyamba uja atamwalira momvetsa chisoni, bambo ake anapita kunyumba ya mnzawo wina wa chapafupi. Ndiye anaona kuti patebulo panali kapepala koitanira anthu ku nkhani ya anthu onse yokonzedwa ndi Mboni za Yehova. Mutu wa nkhaniyo wakuti, “Kodi Akufa Ali Kuti?,” unawachititsa chidwi kwambiri. Funso limeneli ndi lomwe linali kuwavutitsa m’mbuyo monsemo. Motero anapita kukamvetsera nkhaniyo ndipo mfundo zake za m’Baibulo zinawalimbikitsadi kwambiri. Anaphunzirapo kuti anthu akufa savutika. Sapsa ndi moto ku helo ndiponso satengedwa kupita kumwamba ndi Mulungu kuti akakhale angelo, m’malo mwake, akufa, kuphatikizapo Owen, amakhala m’manda kudikirira nthawi youkitsidwa.—Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4.
Kodi banja lanu lakumanapo ndi zovuta? Kodi inuyo, mofanana ndi bambo a Owen, mumadzifunsa kuti okondedwa anu amene anamwalira ali kuti ndiponso kuti kodi mungathe kudzaonana nawonso? Ngati n’choncho, tikukupemphani kuti muone mfundo zinanso zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kuuka kwa akufa. Mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi anthu akufawo adzauka liti? Nanga ndani kwenikweni amene adzaukitsidwe?’ Werengani nkhani zotsatirazi kuti mudziwe mayankho atsatanetsatane a mafunso amenewa ndi mafunso enanso.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1997 tsamba 4 mpaka 5, ndiponso buku la Mankind’s Search for God, tsamba 150 mpaka 154, lomwe limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 5]
Yehova anapatsa Elisa mphamvu zoukitsa mwana wamwamuna wa mayi wa ku Sunemu
[Chithunzi patsamba 5]
Eliya anapempha Yehova kuti abwezeretse moyo wa kamnyamata
[Chithunzi patsamba 6]
Yesu anaukitsa mwana wamwamuna wa mayi wamasiye wa ku Nayini
[Chithunzi patsamba 7]
Kuuka kwa akufa kudzachititsa kuti anthu akumanenso ndi achibale awo okondedwa