Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa Mumachiona Motani?

Kodi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa Mumachiona Motani?

Kodi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa Mumachiona Motani?

“Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.”​—SALMO 145:16

1-3. Kodi anthu ena ali ndi chiyembekezo chotani cha m’tsogolo? Perekani chitsanzo.

TSIKU lina mumzinda wa Manchester, ku England, mwana wina wa zaka naini, dzina lake Christopher, m’mawa wonse anakhalira kuyenda khomo ndi khomo polalikira za Mawu a Mulungu pamodzi ndi mchimwene wake, amalume ake, azakhali ake, ndiponso asuweni ake awiri. Magazini yathu ina ya Galamukani!, inalongosola motere zimene zinachitika: “Masana ake, anthu onsewa anatengana kukaona malo ku tauni ya Blackpool, yomwe ili m’mphepete mwa nyanja, chakufupi ndi kwawoko. N’zomvetsa chisoni kuti anthu 6 onsewa anali m’gulu la anthu 12 amene anafa pangozi ya galimoto ndipo anachita kufera pompo. Ponena za ngoziyi apolisi anati ‘anthuwa anafa chipere.’”

2 Usiku wa tsiku loti ngoziyi ichitika mawa, banjali linapita ku Phunziro la Buku la Mpingo, kumene anakambirana nkhani ya imfa. Bambo a Christopher anati: “Christopher anali mwana woganiza kwambiri. Pa phunziroli ananena mfundo zomveka bwino zokhudza dziko latsopano ndiponso chiyembekezo chake. Kenaka tikukambirana choncho, Christopher ananena mawu akuti: ‘Ubwino wokhala wa Mboni za Yehova ndi woti, ngakhale kuti inde imfa imawawa, ifeyo timadziwa kuti tidzaonananso m’tsogolo padziko pompano.’ Tonse amene tinali pamenepo sitimaganizako n’komwe zoti mawu amenewa adzakhala osaiwalika.” *

3 M’mbuyo mwake, mu 1940, munthu wina wa Mboni wa ku Austria, dzina lake Franz anauzidwa kuti anyongedwa chifukwa chokana kuphwanya malamulo a Yehova. Franz ali kundende ina ya ku Berlin, analembera mayi ake kalata, kuti: “Ndikudziwa kuti ndikanati ndivomere [zokhala msilikali], ndikanachita tchimo loyenera imfa. Sindingalole m’pang’ono pomwe kuchita tchimo ngati limeneli. Chifukwatu nditatero sindingadzaukitsidwe. . . . Ndiyeno amayi, ndiponso abale anga nonsenu, dziwani kuti lero ndauzidwa chilango changa, ndipo musachite mantha ayi, chilango chake ndi kunyongedwa, ndipo andinyonga mawa m’mawa. Ndikulimba mtima podziwa kuti Mulungu ali nane, monga mmene anachitira Akristu ena onse oona a m’mbuyomo. . . . Ngati mutalimbika mpaka imfa, tidzakumananso pa kuuka kwa akufa. . . . Tsalani bwino, tidzaonananso nthawi imeneyo.” *

4. Kodi nkhani zimene zasimbidwazi zakukhudzani mtima motani, ndipo kodi tsopano tikambirana chiyani?

4 Christopher ndiponso Franz ankaona kuti chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chofunika kwambiri. Ankaona kuti n’chenicheni. Ndithu, nkhani zimenezi zimatikhudza mtima kwambiri. Kuti tiyambe kukonda ndiponso kuyamikira kwambiri Yehova komanso kuti tilimbitse chiyembekezo chathu cha kuuka kwa akufa, tiyeni tikambirane zifukwa zimene Mulungu adzaukitsire akufa ndiponso mmene nkhaniyi iyenera kutikhudzira ifeyo patokhapatokha.

Masomphenya a Kuuka kwa Anthu Odzakhala Padziko

5, 6. Kodi masomphenya amene mtumwi Yohane analemba pa Chivumbulutso 20:12, 13 amatithandiza kudziwa zotani?

5 M’masomphenya osonyeza zinthu zochitika mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu Yesu, mtumwi Yohane anaona kuuka kwa akufa kwa anthu odzakhala padziko lapansi. Iye analongosola kuti: “Ndinaona akufa, akulu ndi ang’ono. . . . Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo.” (Chivumbulutso 20:12, 13) Zilibe kanthu kuti ndi anthu apamwamba motani, kaya ndi ‘aakulu’ kapena ‘aang’ono,’ anthu onse otsekeredwa mu Hade (Sheol), kapena kuti manda a anthu onse akufa, adzamasulidwa. Anthu amene anafera panyanja adzauka n’kukhalanso ndi moyo. Zinthu zosangalatsazi zili mbali ya chifuno cha Yehova.

6 Ulamuliro wa Kristu wa zaka 1,000 ukadzayamba, udzamanga kaye Satana n’kumuponyera kuphompho. Palibe woukitsidwa aliyense kapena aliyense wopulumuka chisautso chachikulu amene adzasocheretsedwe ndi Satana panthawi ya ulamuliro umenewu, chifukwa panthawiyi Satana adzakhala wopanda mphamvu. (Chivumbulutso 20:1-3) Mwina mungaone kuti zaka 1,000 ndi nthawi yaitali kwambiri, koma kwenikweni, Yehova amangoziona “ngati tsiku limodzi.”​—2 Petro 3:8.

7. Kodi maziko a chiweruzo pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu adzakhala chiyani?

7 Malingana ndi masomphenyawo, nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu idzakhala nthawi ya chiweruzo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinaona akufa, akulu ndi ang’ono alinkuima ku mpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo. . . . Ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.” (Chivumbulutso 20:12, 13) Onani kuti maziko a chiweruzo chimenechi si zochita za munthuyo asanamwalire ayi. (Aroma 6:7) Koma ndi zolembedwa mu “mabuku” amene adzatsegulidwewo. Zochita za munthu pambuyo poti waphunzira zimene zili m’mabukuwo n’zimene zidzakhale maziko olembera dzina lake mu ‘buku la moyo.’

“Kuuka kwa Moyo” Kapena “Kuuka kwa Kuweruza”

8. Kodi oukitsidwa adzakumana ndi zinthu ziwiri ziti mogwirizana ndi zochita zawo?

8 Kumayambiriro a masomphenya ake, Yohane analongosola kuti anaona Yesu ali ndi “zofungulira [zotsegulira] za imfa ndi Hade.” (Chivumbulutso 1:18) Yesu ali ndi ntchito yopatsidwa ndi Yehova yokhala “Mkulu wa moyo,” ndipo anapatsidwa mphamvu zoweruza “amoyo ndi akufa.” (Machitidwe 3:15; 2 Timoteo 4:1) Kodi adzachita bwanji zimenezi? Adzatero poukitsanso anthu amene ali mtulo ta imfa. Yesu anauza gulu lalikulu la anthu amene anali kuwalalikira, kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” Ndipo anapitiriza kuti: “Amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:28-30) Motero, kodi amuna ndi akazi a kale ali ndi chiyembekezo chotani?

9. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene mosakayikira ambiri oukitsidwa adzaphunzire? (b) Kodi ndi ntchito yaikulu yotani imene idzachitidwe?

9 Anthu a kale okhulupirika akadzaukitsidwa, posakhalitsa adzazindikira kuti malonjezo amene anawakhulupirira akwaniritsidwa. Ndithu, iwowa adzakhala ndi chidwi kwambiri chofuna kudziwa kuti Mbewu ya mkazi wa Mulungu, yotchulidwa muulosi woyamba wa m’Baibulo pa Genesis 3:15, ndi ndani. Adzasangalala kwambiri kumva kuti Yesu, Mesiya wolonjezedwayo, anakhulupirika mpaka kufa kwake, motero anapereka moyo wake kukhala nsembe ya dipo. (Mateyu 20:28) Anthu amene adzawalandire poukitsidwapo adzasangalala kwambiri powathandiza kumvetsetsa kuti nsembe ya dipoyi imasonyeza chisomo ndiponso chifundo cha Yehova. Oukitsidwawo akadzaona zimene Ufumu wa Mulungu ukuchita pokwaniritsa chifuno cha Yehova padziko lapansi, n’zosakayikitsa kuti adzachita kusowa mawu pom’tamanda Yehova. Adzakhala ndi mwayi wonse wosonyeza kuti amakonda Atate wawo wakumwamba ndiponso Mwana wake. Munthu aliyense amene adzakhalepo panthawiyi adzasangalala pochita nawo ntchito yaikulu yophunzitsa anthu mabiliyoni ochoka kumanda, amenenso adzafunike kuvomereza nsembe ya dipo imene Mulungu anakonza.

10, 11. (a) Kodi Zaka 1,000 zidzawapatsa mwayi wotani anthu onse a padziko lapansi? (b) Kodi zimenezi ziyenera kutikhudza motani?

10 Abrahamu akadzaukitsidwa adzalimbikitsidwa kwambiri pokhala mu ulamuliro wa “mudzi” uja umene anali kuuyembekezera kwambiri. (Ahebri 11:10) Yobu wokhulupirika uja adzakhala ndi chimwemwe chodzadza tsaya akadzamva kuti zimene anachita pamoyo wake zinalimbikitsa atumiki ena a Yehova amene anakumana ndi ziyeso zofuna kuwalepheretsa kukhala okhulupirika. Ndipotu Danieli mtima udzakhala dyokodyoko kufuna kudziwa mmene maulosi amene iye anauziridwa kulemba anakwaniritsidwira.

11 Inde, anthu amene adzakhale ndi moyo m’dziko latsopano lolungamalo, kaya adzachita kuukitsidwa, kaya adzapulumuka pa chisautso chachikulu, onse adzakhala ndi zinthu zambiri zoti aziphunzire pa nkhani ya chifuno cha Yehova chokhudza dziko lapansi ndi anthu okhalamo. Ndithu, chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha n’kumatamanda Yehova kwamuyaya chidzachititsa kuti ntchito yophunzitsa anthu ya Zaka 1,000 imeneyi idzakhale yokoma kwabasi. Komabe, chofunika kwambiri chidzakhala zochita zathu patokhapatokha pamene tikuphunzira zinthu za m’mabuku aja. Kodi tizidzatsatira zimene tikuphunzirazo? Kodi tizidzasinkhasinkha ndi kumvera malangizo otikonzekeretsa kulimbana ndi Satana akadzapatsidwa mpata wotsiriza woyesa kutisocheretsa kuti tisiye choonadi?

12. Kodi n’chiyani chidzathandize kuti aliyense adzathe kukwanitsa kuchita nawo mokwanira ntchito yophunzitsa ndiponso yosintha dzikoli kukhala paradaiso?

12 Sitiyeneranso kuiwala madalitso ambiri amene adzakhalepo chifukwa cha zipatso za nsembe ya dipo ya Kristu. Anthu amene adzaukitsidwe sadzakhala ndi matenda kapena zilema tili nazo masiku anozi. (Yesaya 33:24) Chifukwa chokhala athanzi ndiponso chifukwa choyembekezera kudzakhala ndi thanzi langwiro, anthu onse okhala m’dziko latsopanoli adzachita nawo mokwanira ntchito yowaphunzitsa anthu mabiliyoni omwe adzaukitsidwe za njira ya kumoyo. Anthuwa adzakhalanso ndi ntchito yaikulu koposa ntchito ina iliyonse imene anthu anachitapo padziko pano. Ntchito yake idzakhala yosandutsa dziko lonseli kukhala paradaiso, ndipo motero Yehova adzatamandidwa.

13, 14. Kodi Satana adzam’masuliranji pa kuyesa kotsiriza, ndipo kodi zimenezi zidzatikhudza motani ifeyo patokhapatokha?

13 Satana akadzatulutsidwa m’chiphompho pa kuyesa kotsiriza, iye adzayesanso kusocheretsa anthu. Malingana ndi lemba la Chivumbulutso 20:7-9, ‘mitundu yosocheretsedwa,’ kapena kuti magulu onse a anthu amene adzatsatire Satana, adzawaweruza kuti awonongedwe. ‘Udzatsika moto wakumwamba n’kudzawanyeketsa.’ Anthu amene anaukitsidwa pa nthawi ya Zaka 1,000 zija, komano n’kudzawonongedwa panthawiyi, kuuka kwawoko kudzakhala kuuka kwa kuweruza. Komano anzawo amene adzakhulupirike adzalandira mphatso ya moyo wosatha. Amenewa kuuka kwawo kudzakhaladi “kuuka kwa moyo.”​—Yohane 5:29.

14 Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingatilimbikitse bwanji ngakhale panopo? Ndiyeno kodi tiyenera kutani kuti madalitso a kuuka kwa akufawa asadzatiphonye?

Zinthu Zoyenera Kuphunzirapo Panopo

15. Kodi kukhulupirira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kungatithandize bwanji panopo?

15 N’kutheka kuti munthu wina amene mumamukonda anamwalira posachedwapa motero mudakali achisoni kwambiri chifukwa cha zosautsa zosasimbikazi. Mosiyana ndi anthu amene sadziwa choonadi, chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimakukhazikani mtima m’malo ndiponso kukulimbitsani mtima. Paulo anawapepesa motere Atesalonika: “Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13) Kodi mumatha kudziona muli m’dziko latsopano mukuona akufa akuukitsidwa? Limbani mtima panopo posinkhasinkha za chiyembekezo chodzakumananso ndi okondedwa anu.

16. Kodi n’kutheka kuti inuyo mudzamva bwanji pa kuuka kwa akufa?

16 N’kutheka kuti pakali pano mukuvutika ndi zovuta zina, monga matenda, zomwe zinabwera chifukwa cha kugalukira kwa Adamu. Musalole kuti zimenezi zikudwalitseni kwambiri maganizo moti mpaka kuiwalako za chiyembekezo chosangalatsa choti inuyo panokha ngati mutafa mudzaukitsidwa n’kukhala ndi thanzi labwino ndi thupi lamphamvu m’dziko latsopano. Panthawiyo, mukadzatsegula maso n’kuona anthu okuyembekezerani, chimwemwe chawo chikuchita kusefukira poona kuti mwaukitsidwa, simudzalephera kuthokoza Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwake kwachikondi.

17, 18. Kodi ndi zinthu ziwiri zofunika zotani zimene tikuphunzirapo zoyenera kuzikumbukira?

17 Pakali pano, tiyeni tionepo zinthu ziwiri zimene tikuphunzirapo, zomwe sitiyenera kuziiwala. Chinthu choyamba ndicho kufunika kotumikira Yehova mwamtima wonse panopa. Potsanzira Mbuye wathu, Kristu Yesu, moyo wathu wololera kuvutikira ena umasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso anthu ena. Moyo kapena ufulu wathu ukasokonezeka chifukwa cha kuvutitsidwa kapena kuzunzidwa, timayenera kutsimikiza mtima kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba, zivute zitani. Ngati anthu olimbana nafe atatiopseza kuti atipha, chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimatilimbikitsa kukhulupirikabe kwa Yehova ndiponso Ufumu wake. Inde, khama lathu pantchito yolalikira za Ufumuwu ndiponso kupanga ophunzira limatipatsa chiyembekezo chodzalandira madalitso osatha amene Yehova akufuna kudzapatsa anthu olungama.

18 Chinthu chachiwiri chimene tiyenera kuphunzirapo n’chokhudza zimene tiyenera kuchita tikamakumana ndi ziyeso chifukwa cha kupanda ungwiroku. Chifukwa chodziwa za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa ndiponso chifukwa choyamikira chisomo cha Yehova sitibwerera m’mbuyo ngakhale pang’ono pa chikhulupiriro chathu cholimba. Yohane anachenjeza kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2:15-17) Zokopa za m’dzikoli, monga chuma, sizingatitenge mtima tikaziyerekezera ndi “moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:17-19) Tikamayesedwa kuchita zachiwerewere, tingakane kwamtuwagalu. Tikudziwa kuti ngati titafa Armagedo isanachitike, khalidwe lokhumudwitsa Yehova lingatichititse kukhala m’gulu la anthu amene palibe chiyembekezo chilichonse choti adzaukitsidwa.

19. Kodi ndi mwayi wosaneneka wotani umene sitiyenera kuuiwala?

19 Chachikulu kwambiri n’chakuti tisaiwale mwayi wosaneneka wokondweretsa mtima wa Yehova panopo ndiponso kwa moyo wosatha. (Miyambo 27:11) Kukhala okhulupirika mpaka mapeto a moyo wathu kapena mpaka mapeto a dongosolo loipa lino kumam’sonyeza Yehova kuti ifeyo tili mbali yake pa nkhani yakuti ndani ali wolamulira woyenera wa chilengedwe chonse. Ndiyetu si mmene tidzasangalalire kukhala m’Paradaiso padziko lapansi, kaya populumuka chisautso chachikulu kapena poukitsidwa mozizwitsa.

Kukwaniritsa Zokhumba Zathu

20, 21. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukhalabe okhulupirika ngakhale titapanda kudziwa mayankho a mafunso enaake okhudza kuuka kwa akufa? Fotokozani.

20 Zimene takambirana pa nkhani ya kuuka kwa akufazi sizikuyankha mafunso onse. Mwachitsanzo, kodi Yehova adzayendetsa bwanji nkhani ya anthu amene anamwalira ali okwatira kapena okwatiwa? (Luka 20:34, 35) Kodi anthu adzaukira m’madera amene anafera? Kodi adzaukira kufupi ndi azibale awo? N’zoona kuti pali mafunso enanso ambiri okhudza mmene zinthu zidzayendere pa kuuka kwa akufa. Komabe, tiyenera kukumbukira mawu a Yeremiya akuti: “Yehova akhalira wabwino om’lindirira, ndi moyo wom’funafuna. N’kokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” (Maliro 3:25, 26) Panthawi imene Yehova waika, tidzadziwa mayankho okhutiritsa a mafunso onsewa. Kodi n’chifukwa chiyani sitingakayikire kuti tidzatero?

21 Taganizirani mozama mawu awa a wamasalmo m’nyimbo yake yonena za Yehova: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:16) Tikamakula, zokhumba zathu zimasintha. Zinthu zimene tinkakhumba tili ana si zimene timalakalaka panopa. Moyo timauona mogwirizana ndi zimene takumana nazo pa moyo wathu ndiponso zimene timayembekezera. Komabe, zinthu zilizonse zoyenerera zimene tizidzakhumba m’dziko latsopano, Yehova adzatipatsa mosakayika.

22. Kodi tili ndi zifukwa zomveka zotani zotamandira Yehova?

22 Panopo, chinthu chofunika kuti tonsefe tizichiganizira kwambiri ndicho kukhala okhulupirika. “Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.” (1 Akorinto 4:2) Tonsefe tili ndi udindo pa uthenga wabwino wosangalatsa wa Ufumu wa Mulungu. Kufalitsa uthenga wabwino umenewu mwakhama kwa anthu onse amene timakumana nawo kumatithandiza kukhalabe m’njira yopita ku moyo. Nthawi zonse osamaiwala kuti “yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” (Mlaliki 9:11) Polimbana ndi nkhawa zobwera chifukwa cha zovuta zilizonse zosayembekezeka, osamaiwala ngakhale pang’ono za chiyembekezo chosangalatsa cha kuuka kwa akufa. Ngati mukuona kuti inuyo mudzakhala mutafa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu usanayambe, limbani mtima chifukwa ndithu mudzaukitsidwa. Nthawi yoikika ya Yehova ikadzakwana, nanunso mudzanena mawu amene Yobu ananena kwa Mlengi akuti: ‘Mudzaitana, ndipo ndidzakuyankhani.’ Atamandike Yehova, amene akulakalaka kuukitsa anthu onse omwe ali m’chikumbumtima chake.​—Yobu 14:15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani Galamukani! ya Chingelezi ya July 8, 1988, tsamba 10, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 3 Zachokera m’buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 662, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi m’Zaka 1,000 anthu adzaweruzidwa pa maziko otani?

• N’chifukwa chiyani ena kuuka kwawo kudzakhale “kuuka kwa moyo” pamene ena kudzakhale “kuuka kwa kuweruza”?

• Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingatilimbitse mtima bwanji panopo?

• Kodi mawu a pa Salmo 145:16 amatithandiza bwanji kusavutika ndi mafunso okhudza kuuka kwa akufa amene sitikudziwa mayankho ake?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi kukhulupirira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kungatithandize bwanji panopo?