Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupindula ndi Tsiku Lililonse

Kupindula ndi Tsiku Lililonse

Kupindula ndi Tsiku Lililonse

“MUTIDZIWITSE kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” (Salmo 90:12) Limeneli ndi pemphero limene Mose, yemwe analemba nawo Baibulo, anapemphera modzichepetsa. Kodi iye anali kupempha chiyani kwenikweni? Kodi nafenso tingapemphere motere?

Mu vesi 10, Mose anadandaula ndi kufupika kwa moyo wa munthu. Nthawi inanso, iye analemba mawu a Yobu amene anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Apa zikuonekeratu kuti mtima unali kum’pweteka Mose akaganizira kufupika kwa moyo wopanda ungwiro wa munthu. Choncho, tsiku lililonse la moyo wake linali lamtengo wapatali kwa iye. Popemphera motere kwa Mulungu, Mose anasonyeza kuti anali kufunitsitsa kuti, m’masiku otsala a moyo wake, iye akhale ndi moyo mokondweretsa Mlengi wake. Kodi ifenso sitiyenera kuyesetsa kuchita zaphindu ndi masiku a moyo wathu? Tiyenera kutero ngati tikufuna kuti Mulungu azikondwera nafe.

Palinso mfundo ina imene inalimbikitsa Mose ndi Yobu kufuna kukhala moyo mokondweretsa Mulungu, ndipo mfundoyi iyenera kutilimbikitsa nafenso. Anthu awiriwa anali kuyembekezera mphoto yodzakhala ndi moyo wabwino m’tsogolo padziko lapansi. (Yobu 14:14, 15; Ahebri 11:26) Panthawiyo palibe munthu amene ntchito zake zabwino zidzathere panjira chifukwa cha imfa. Cholinga cha Mlengi wathu n’chakuti anthu okhulupirika adzakhale ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 21:3, 4) Nanunso mungathe kuyamba kuyembekezera zimenezi ngati ‘muwerenga masiku anu, kuti mukhale nawo mtima wanzeru.’