Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani Paulo analemba kuti mkazi wachikristu “adzapulumutsidwa mwa kubala mwana”?​—1 Timoteo 2:15.

Kodi nkhani imene mukupezeka lembali ikusonyeza kuti Paulo anali kutanthauza chiyani? Mwa mphamvu ya mzimu woyera, iye anali kupereka malangizo pa ntchito ya akazi achikristu mu mpingo. Iye anati: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” (1 Timoteo 2:9, 10) Apa Paulo anali kulimbikitsa alongo ake achikristu kukhala ndi malire pa kavalidwe, kuvala moyenera, ndi ‘kudziveka’ ntchito zabwino.

Kenako Paulo anafotokoza dongosolo la utsogoleri mu mpingo. Iye anati: “Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.” (1 Timoteo 2:12; 1 Akorinto 11:3) Anafotokoza maziko a dongosolo limeneli ponena kuti Adamu sananyengedwe ndi Satana, koma Hava “ponyengedwa analowa m’kulakwa.” Kodi akazi achikristu angatetezedwe bwanji ku tchimo la Hava? Paulo anayankha kuti: “Koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.” (1 Timoteo 2:14, 15) Kodi Paulo anatanthauzanji ponena mawu amenewa?

Anthu ena omasulira Baibulo amamasulira mawuwa kuti mkazi adzapulumuka pokhapokha akakhala ndi ana. Koma uku si kumasulira molondola mawu a Paulowa. Malemba ambiri amasonyeza kuti munthu adzapulumuka mwa kudziwa Yehova, kukhulupirira Yesu, kukhala ndi chikhulupiriro, ndi kusonyeza ntchito za chikhulupirirocho. (Yohane 17:3; Machitidwe 16:30, 31; Aroma 10:10; Yakobo 2:26) Komanso Paulo sanali kutanthauza kuti akazi okhulupirira sadzakumana ndi vuto lililonse pobereka. Akazi okhulupirira ndi osakhulupirira omwe aberekapo popanda vuto lililonse. Komanso n’zomvetsa chisoni kuti akazi ena okhulupirira ndi osakhulupirira omwe amwalirapo pobereka.​—Genesis 35:16-18.

Malangizo ena amene Paulo anapereka pambuyo kwa akazi m’kalata yomweyi akutithandiza kumvetsa zimene anali kutanthauza. Anachenjeza za akazi amasiye ena achitsikana amene anali ‘aulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso olankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.’ Kodi uphungu wake kwa akazi amenewa unali wotani? Iye anapitiriza kuti: “Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang’ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira.”​—1 Timoteo 5:13, 14.

Paulo anali kugogomezera mbali yofunika imene akazi ali nayo m’banja. Pokhala wotanganidwa ndi zochitika monga ‘kubereka ana ndi kusamalira banja,’ mkazi amene “akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso,” sangakhale ndi khalidwe losalimbikitsa ena. Moyo wake wauzimu “udzapulumutsidwa,” kapena kuti udzatetezeka. (1 Timoteo 2:15) Kukhala ndi moyo wotere kungathandize akazi ambiri achitsikana kupewa misampha ya Satana.

Mawu amenewa, omwe Paulo analembera Timoteo, akutikumbutsa ife tonse amuna ndi akazi kugwiritsa ntchito nthawi yathu pochita zinthu zopindulitsa. Mawu a Mulungu amalangiza Akristu onse kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru.”​—Aefeso 5:15.