Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
ZITHUNZI za Paradaiso, ngati chimene chili pachikuto cha magazini ino, n’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu amene ali paumphawi. Anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, anali kukhala m’paradaiso. Munda wa Edene ndiwo unali mudzi wawo. (Genesis 2:7-23) Ngakhale kuti Paradaiso ameneyo anatayika, sikuti tikuganizira zinthu zosatheka tikamakhulupirira za paradaiso wa m’tsogolo, kapena kuti dziko latsopano lopanda umphawi. Chikhulupiriro chimenechi chagona pa malonjezo otsimikizika opezeka m’Baibulo.
Ganizirani lonjezo limene Yesu Kristu anapereka patsiku limene anaphedwa. Mmodzi mwa anthu ochita zoipa amene anaphedwa limodzi ndi Yesu anasonyeza chikhulupiriro chakuti Mulungu angathetse mavuto amene anthu akukumana nawo. Iye anati: “Yesu, ndikumbukireni mmene mulowa Ufumu wanu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti wochita zoipayo anali ndi chikhulupiro kuti Yesu adzalamulira monga Mfumu komanso kuti akufa adzaukitsidwa. Yesu anayankha kuti: “Indetu, ndinena ndi iwe, lero lino udzakhala ndine m’Paradaiso.”—Luka 23:42, 43.
Ponena za awo amene adzakhale m’Paradaiso, Baibulo limati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake.” (Yesaya 65:21) Inde, “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”—Mika 4:4.
Koma n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti umphawi ukhalepo lerolino? Kodi Mulungu amawathandiza motani anthu omwe ali paumphawi? Kodi umphawi umenewu udzatha liti?
N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Umphawi?
Paradaiso amene Adamu ndi Hava analimo anatayika chifukwa cha kupanduka kwawo motsogoleredwa ndi mngelo woipa, Satana Mdyerekezi. Polankhula kudzera mwa njoka, Satana ananyenga Hava ndi kum’chititsa kuswa lamulo la Mulungu loletsa kudya chipatso cha mtengo winawake. Hava anakhulupirira bodza la Satana lakuti moyo wawo ungakhale wosangalatsa ngati atamadzilamulira okha m’malo momvera Mulungu. Hava atapereka chipatso choletsedwacho kwa Adamu, mwamuna wakeyo anadya, ndipo mwakutero anakana Mulungu pofuna kukondweretsa mkazi wake.—Genesis 3:1-6; 1 Timoteo 2:14.
Moyenerera banja lopandukali analipitikitsa m’Paradaiso, ndipo zitatero anafunika kuvutika kuti apeze chakudya. Kuchokera panthawiyo, Yehova walola kuti Satana alamulire anthu ochimwa, ndipo zotsatira za kusamvera Mulungu zaonekera. Mbiri ya anthu yasonyezeratu kuti anthu sangadzetse Yeremiya 10:23) M’malo mwake, pali mavuto osaneneka kuphatikizapo umphawi chifukwa chakuti anthu akana ulamuliro wa Mulungu ndipo asankha kudzilamulira okha.—Mlaliki 8:9.
Paradaiso pa dziko lapansi. (Komabe, sikuti anthu osauka alibiretu thandizo m’dziko lamavutoli. Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, ali ndi malangizo omwe angawathandize.
“Musadere Nkhawa”
Polankhula ndi khamu la anthu, kuphatikizapo osauka ambiri, Yesu anati: “Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? . . . Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:26-33.
Munthu sayenera kuba chifukwa chakuti ndi wosauka. (Miyambo 6:30, 31) Ngati aika Mulungu patsogolo m’moyo wake, iye adzam’patsa zosowa zake. Ganizirani zimene zinachitikira Tukiso, mwamuna wa ku Lesotho, kummwera kwa Africa. M’chaka cha 1998, asilikali achilendo analowa m’dziko la Lesotho kukaletsa zipolowe zoukira boma. Chifukwa cha nkhondo imeneyo, anthu anaphwanya masitolo ndi kubamo katundu, ena anachotsedwa ntchito ndipo kunali njala yosaneneka.
Tukiso ankakhala m’dera la anthu osauka kwambiri mu mzinda waukulu wa m’dzikoli. Anthu ambiri oyandikana nawo ankaswa masitolo ndi kubamo katundu kuti apeze zosowa zawo. Tsiku lina Tukiso atafika kunyumba yake, anapeza kuti Maseiso, mkazi amene anali kukhala naye, ali ndi katundu wambiri amene anaba m’sitolo. Tukiso anati: “Pita nazo panja zinthu zimenezi,” ndiyeno anafotokoza kuti malamulo a Mulungu amaletsa kuba. Maseiso anamvera. Anthu oyandikana nawo anawaseka ndipo anatenga chakudya chakubacho.
Tukiso anachita zimenezi chifukwa cha zimene anaphunzira m’Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi anafa ndi njala chifukwa chomvera malamulo a Mulungu? Ayi. Patapita nthawi, akulu a mpingo wa Mboni za Yehova umene Tukiso anali kusonkhana nawo, anafufuza kumene iye anali kukhala ndipo anapita kukam’patsa chakudya. Ndiponso Mboni za Yehova m’dziko loyandikana nalo la South Africa zinatumiza thandizo la chakudya choposa matani awiri kwa abale ndi alongo awo achikristu ku Lesotho. Maseiso anachita chidwi ndi Tukiso chifukwa cha kumvera kwake Mulungu komanso anachita chidwi ndi mmene mpingo unawathandizira mwachikondi. Nayenso anayamba kuphunzira Baibulo.
Pambuyo pake, awiriwa anakwatirana mwalamulo, zimene zinawathandiza kukhala oyenerera kubatizidwa monga Mboni za Yehova. Mpaka pano akutumikirabe Mulungu mokhulupirika.Yehova Mulungu amasamalira osauka. (Onani bokosi lakuti “Kodi Mulungu Amawaona Bwanji Anthu Osauka?”) Mwachikondi wapanga dongosolo lothandizira anthu ngati Tukiso ndi Maseiso kuti aphunzire za iye. Ndipo m’Mawu ake, wapereka malangizo othandiza pa moyo watsiku ndi tsiku.
Makonzedwe Abwino Kwambiri
Nthawi zonse Mboni za Yehova zimayesetsa kutsanzira Mulungu mwa kudera nkhawa anthu aumphawi. (Agalatiya 2:10) Kawirikawiri m’dziko mukagwa tsoka limene lakhudza Akristu oona, Mboni zimawatumizira thandizo loyenerera. Chofunika koposa n’chakuti, Mboni zimaderanso nkhawa zosowa zauzimu za aliyense, kuphatikizapo anthu osauka. (Mateyu 9:36-38) M’zaka 60 zapitazi, atumiki ambirimbiri ophunzitsidwa bwino adzipereka kukatumikira monga amishonale m’mayiko ena. Mwachitsanzo, amene anaphunzitsa Tukiso ndi Maseiso kuti akhale ophunzira a Yesu anali amishonale ochokera ku Finland, omwe anachita kuphunzira chinenero cha Chisutu. (Mateyu 28:19, 20) Ntchito yaumishonale imeneyi nthawi zambiri imafuna kudzimana, kuchoka pa moyo wofewa m’dziko lolemera ndi kupita kudziko losauka.
Akristu oona saba kuti akhale ndi moyo. M’malo mwake, ali ndi chikhulupiriro kuti Yehova Mulungu angathe kuwapatsa zosowa zawo. (Ahebri 13:5, 6) Njira imodzi imene Yehova amathandizira anthu ake ndi kudzera m’gulu la pa dziko lonse la opembedza ake, omwe amathandizana.
Njira ina imene Yehova amathandizira anthu osauka ndiyo kuwapatsa malangizo othandiza Aefeso 4:28) Anthu ambiri amene ali paulova ayesetsa kudzipezera zochita. Amagwira ntchito mwakhama, monga kulima ndiwo zamasamba. Baibulo limathandizanso anthu osauka kuti azisamala ndalama mwa kuwaphunzitsa kupewa zizolowezi zoipa, monga kumwa mowa kwambiri.—Aefeso 5:18.
pa moyo watsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, Baibulo limalamula kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.” (Kodi Tidzakhala Liti M’dziko Lopanda Umphawi?
Baibulo likusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a ulamuliro wa Satana. (2 Timoteo 3:1) Posachedwapa, Yehova Mulungu adzatumiza Yesu Kristu kudzaweruza anthu. Kodi chidzachitika n’chiyani panthawiyo? Yesu anapereka yankho m’fanizo linalake. Iye anati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pachimpando cha kuwala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.”—Mateyu 25:31-33.
Nkhosa za m’fanizoli ndi anthu amene akugonjera ufumu wa Yesu. Yesu anawayerekezera ndi nkhosa chifukwa chakuti amam’tsatira monga Mbusa wawo. (Yohane 10:16) Onga nkhosa amenewa adzapeza moyo mu ulamuliro wolungama wa Yesu. Moyo umenewo udzakhala wosangalatsa kwambiri m’dziko latsopano lopanda umphawi. Anthu onga mbuzi, amene akukana ulamuliro wa Yesu, adzawonongedwa kotheratu.—Mateyu 25:46.
Ufumu wa Mulungu udzathetsa zoipa zonse. Panthawiyo sikudzakhalanso umphawi. M’malo mwake, dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu okondana komanso osamala za wina ndi mnzake. Tikaona ubale wa pa dziko lonse wa Mboni za Yehova, timatsimikiza kuti n’zothekadi kudzakhala m’dziko latsopano loterolo, chifukwatu Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 6, 7]
KODI MULUNGU AMAWAONA BWANJI ANTHU OSAUKA?
Ponena za Mlengi wa anthu, Baibulo limati “ndiye wakupatsa anjala chakudya.” (Salmo 146:7) Lili ndi mavesi oposa 100 omwe amasonyeza kuti Mulungu amaganizira anthu osauka.
Mwachitsanzo, Yehova atapereka Chilamulo chake ku mtundu wakale wa Israyeli, analamula alimi achiisrayeli kuti asamakolole zonse za m’mphepete mwa minda yawo. Sanayenera kukunkha zipatso za azitona kapena mphesa zotsalira mumtengo. Malamulo amenewa anasonyeza kuti Mulungu amakonda alendo, ana amasiye, akazi amasiye ndi anthu ena ovutika.—Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 24:19-21.
Komanso, Mulungu analamula Aisrayeli kuti: “Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo; ndi mkwiyo wanga [udzayaka], ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe.” (Eksodo 22:22-24) N’zomvetsa chisoni kuti Aisrayeli ambiri olemera sanamvere mawu amenewo. Chifukwa cha cholakwa chimenechi ndi zolakwa zina, Yehova Mulungu anachenjeza Aisrayeli kudzera mwa aneneri ake osiyanasiyana. (Yesaya 10:1, 2; Yeremiya 5:28; Amosi 4:1-3) Pambuyo pake, Mulungu analola Asuri ndipo kenako Ababulo kugonjetsa Aisrayeli, ndipo Aisrayeli ambiri anaphedwa. Omwe anapulumuka anawatengera ku ukapolo m’dziko lachilendo.
Mwana wokondedwa wa Mulungu, Yesu Kristu, analinso kuganizira anthu osauka potsanzira Atate wake. Pofotokoza cholinga cha utumiki wake, Yesu anati: “Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino.” (Luka 4:18) Izi sizikutanthauza kuti Yesu ankalunjika osauka okha pa utumiki wakewo. Mwachikondi, anali kuthandizanso anthu olemera. Komabe pochita zimenezi, kawirikawiri Yesu ankasonyeza kuti akudera nkhawa anthu osauka. Mwachitsanzo, analangiza wolamulira wina wolemera kuti: “Gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m’Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.”—Luka 14:1, 12-14; 18:18, 22; 19:1-10.
Yehova Mulungu ndi Mwana wake amasamala kwambiri za anthu osauka. (Marko 12:41-44; Yakobo 2:1-6) Posonyeza kuti amasamaladi za osauka, Yehova akukumbukira mamiliyoni a anthu osauka omwe anamwalira. Onsewa adzaukitsidwa ndipo adzakhala m’dziko latsopano lopanda umphawi.—Machitidwe 24:15.
[Zithunzi]
Ubale wa pa dziko lonse wa Mboni za Yehova umasonyeza kuti dziko latsopano n’lotheka
[Chithunzi patsamba 5]
Tukiso ndi Maseiso limodzi ndi mmishonale yemwe anaphunzitsa Tukiso Baibulo
[Chithunzi patsamba 5]
Maseiso, pakhomo la nyumba yake limodzi ndi mmishonale amene anam’phunzitsa Baibulo