Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja Odziwa Mulungu Amalimba

Mabanja Odziwa Mulungu Amalimba

“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”

Mabanja Odziwa Mulungu Amalimba

MWAMUNA wina ndi mkazi wake ku Argentina anadulirana nyumba yawo mwa kumanga khoma pakati. Anasemphana maganizo kwambiri, moti anali kudana kwabasi.

N’zomvetsa chisoni kuti m’mabanja ambiri zinthu zili chimodzimodzi ndi mmene zinalili m’banja limeneli. M’mabanja ambiri okwatiranawo amangokhalira kumenyana, ndi osakhulupirika kwa wina ndi mnzake ndipo amadana kwadzaoneni. Izi n’zomvetsa chisoni, chifukwa banja analiyambitsa ndi Mulungu iyemwini. (Genesis 1:27, 28; 2:23, 24) Mphatso imeneyi yochokera kwa Mulungu ndi malo abwino osonyezera chikondi chakuya. (Rute 1:9) Mwa kukwaniritsa maudindo amene Mulungu anawapatsa, anthu a m’banja amalemekeza Yehova ndipo amadzetsa chimwemwe kwa wina ndi mnzake. *

Popeza kuti Mulungu ndiye anayambitsa banja, maganizo athu a kayendetsedwe ka banja ayenera kugwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Mawu ake amatipatsa malangizo othandiza kwambiri kuti mabanja aziyenda bwino, makamaka ngati pabuka mavuto. Ponena za udindo wa mwamuna m’banja, Baibulo limati: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” Mwamuna akamakwaniritsa mfundo yofunikayi, mkazi nayenso ‘amaopa mwamuna’ wake monyadira, kapena kuti amam’patsa ulemu waukulu.​—Aefeso 5:25-29, 33.

Pofotokoza mmene makolo ayenera kukhalira ndi ana awo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Zimenezi zimathandiza kuti onse m’banjamo azikondana, zomwe zimachititsa kuti ana azimvera makolo awo mosavuta.​—Aefeso 6:1.

Mfundo zimene tatchulazi ndi zitsanzo za malangizo a m’Baibulo othandiza pa moyo wa banja. M’mabanja ambiri anthu akukhala mosangalala, chifukwa akutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino. Chitsanzo ndi cha banja la ku Argentina lomwe talitchula lija. Ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwa miyezi itatu, onse anayamba kugwiritsa ntchito malangizo anzeru a m’Baibulo mu ukwati wawo. Aliyense anayesetsa mwakhama kuti azilankhula bwino ndi mnzake, kuti azimvetsa zosowa za wina, ndiponso kuti azikhululukira mnzake. (Miyambo 15:22; 1 Petro 3:7; 4:8) Anaphunzira kulamulira mkwiyo wawo ndi kudalira Mulungu kuti aziwathandiza zinthu zikasokonekera. (Akolose 3:19) Posakhalitsa, anagwetsa khoma limene anamanga m’nyumba mwawo lija.

Mulungu Angalimbitse Banja

Kudziwa miyezo ya Mulungu ndi kuigwiritsa ntchito kungathandize banja kupirira mavuto. Zimenezi n’zofunika, chifukwa chakuti ulosi unaneneratu kuti m’masiku athu ano mabanja adzaukiridwa mwankhanza. Paulo ananeneratu kuti makhalidwe ndi zochita za anthu zidzaipiraipira. Iye ananena kuti “masiku otsiriza” adzatchuka ndi kusakhulupirika, kusowa kwa “chikondi chachibadwidwe” ndi kusamvera makolo, ngakhale pakati pa anthu okhala ndi “maonekedwe a chipembedzo.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Kuyesa kukondweretsa Mulungu kungatithandize kuthana ndi makhalidwe owononga banja amenewa. Mabanja ambiri aona kuti kugwiritsa ntchito malangizo auzimu kwawathandiza kuthana ndi mavuto ambiri amene amakumana nawo. Ngati anthu a m’banja akufuna kukhalabe paubwenzi ndi Mulungu, ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino ndi kuzindikira kuti “akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” Kutsatira zimenezi n’kofunika kuposa kuchita china chilichonse. (Salmo 127:1) Anthu amene akuyesetsa kuti moyo wabanja lawo ukhale wachimwemwe, zinthu zimawayendera bwino kwambiri akaika Mulungu patsogolo m’banjamo.​—Aefeso 3:14, 15.

Munthu wina wa ku Hawaii, dzina lake Dennis, anaona kuti zimenezi n’zoonadi. Ngakhale kuti ankadzitcha Mkristu, ankakonda kulankhula mwachipongwe ndi kuchita ndewu. Pambuyo pogwira ntchito yausilikali, anawonjezera kuchita ndewu ndi nkhanza. Iye anati: “Ndinkachita ndewu nthawi zonse. Sindinkadera nkhawa za moyo wanga ndipo sindinkaopa kufa. Ndinapitiriza kulankhula mwachipongwe ndi kuchita ndewu. Mkazi wanga, amene anali wa Mboni za Yehova, ankandilimbikitsa kuphunzira Baibulo.”

Dennis ankakana thandizo la mkazi wake limenelo. Komabe, khalidwe lachikristu la mkazi wakeyo linam’thandiza kusintha maganizo. Tsiku lina Dennis anapita kumsonkhano wachikristu limodzi ndi mkazi wake ndi ana ake. Kenako, Dennis anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo anapita patsogolo mochititsa chidwi. Anasiya kusuta fodya, chomwe chinali chizolowezi chake kwa zaka 28. Anasiyanso kucheza ndi mabwenzi omwe anali kuchita zimene iye ankafuna kusiya. Pothokoza Yehova, Dennis anati: “Moyo wa banja langa wasintha. Timapitira limodzi kumisonkhano ndi kulowa mu utumiki monga banja. Ana anga awiri anasiya kuchita nane mantha, chifukwa ndinaphunzira kulamulira mkwiyo wanga ndipo ndinasiya kulankhula mawu achipongwe. Tinayamba kucheza bwinobwino ndi kumakambirana nkhani za m’Baibulo. Ndikanapanda kuphunzira choonadi cha m’Baibulo, sibwenzi ndili moyo lerolino, chifukwa ndinali wamtima wapachala kwabasi.”

Mabanja angapeze chimwemwe ngati atayesetsa mwakhama kuchita chifuniro cha Yehova. Zochitika zasonyeza kuti ngakhale munthu mmodzi yekha m’banja atamatsatira mfundo za m’Baibulo, zinthu zimakhalako bwino kusiyana ndi m’banja lomwe mulibe aliyense wotsatira mfundo za m’Baibulo. Kulimbitsa banja mwauzimu ndi ntchito yaikulu yofuna luso ndi nthawi. Koma mabanja omwe akuyesetsa kuchita zimenezi ndi otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lawo lolimbitsa mabanja awo mwauzimu. Anganene monga momwe wamasalmo ananenera kuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, mwezi wa May ndi June.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Mulungu amatcha dzina “fuko lonse,” kapena kuti banja lililonse, “la m’mwamba ndi la padziko.” ​—AEFESO 3:15

[Bokosi patsamba 8]

YEHOVA AMAONA BANJA KUKHALA LA MTENGO WAPATALI

“Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.”​—Genesis 1:28.

“Wodala yense wakuopa Yehova . . . Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m’mbali za nyumba yako.”​—Salmo 128:1, 3.