Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
N’chifukwa chiyani Davide ndi Bateseba sanaphedwe atachita chigololo, m’malo mwake mwana wawo woyamba ndiye anamwalira?
Chilamulo cha Mose chinanena mosapita m’mbali kuti: “Akam’peza munthu ali kugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israyeli.” (Deuteronomo 22:22) Yehova Mulungu akanalola kuti mlandu wa Davide ndi Bateseba uweruzidwe ndi anthu motsatira Chilamulo, ochita chigololowo akanaphedwa. Popeza kuti oweruza aumunthu sangadziwe zimene zili mumtima, iwo akanaweruza malinga ndi zimene ochimwawo anachita zomwe zinali ndi umboni wotsimikizika. Malinga ndi Chilamulo, wochita chigololo ankamuweruza kuti aphedwe. Oweruza achiisrayeli sanali kuloledwa kukhululukira munthu wochita tchimo limeneli.
Komabe, Mulungu woona amadziwa zimene zili mumtima ndipo amakhululukira machimo akaona kuti pali chifukwa chabwino chokhululukira. Popeza kuti wochimwa pankhaniyi anali Davide, amene Mulungu anachita naye pangano la Ufumu, Yehova anasankha kuweruza yekha nkhani imeneyi mwapadera. (2 Samueli 7:12-16) “Woweruza wa dziko lonse lapansi” ali ndi ufulu wosankha kuchita zimenezi.—Genesis 18:25.
Kodi Yehova anaonanji pamene anali kuyesa mtima wa Davide? Pa Salmo 51, timawu tapamwamba timanena kuti salmo limeneli limasonyeza mmene Davide anamverera “mmene anam’dzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba.” Lemba la Salmo 51:1-4 limati: “Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu.” Yehova ayenera kuti anaona kudzimvera chisoni kotereku mumtima wa Davide monga umboni wakuti analapadi moona mtima, ndipo anaona kuti panali chifukwa chabwino chowachitira chifundo olakwawo. Komanso, Davide anali munthu wachifundo, ndipo Yehova amachitira chifundo anthu achifundo. (1 Samueli 24:4-7; Mateyu 5:7; Yakobo 2:13) Chotero Davide atavomereza tchimo lake, Natani anamuuza kuti: “Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.”—2 Samueli 12:13.
Komabe Davide ndi Bateseba sakanatha kupewa zotsatira zonse za tchimo lawolo. Natani anauza Davide kuti: “Popeza pa kuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.” Mwana wawoyo anadwala ndi kumwalira ngakhale kuti Davide anasala kudya ndi kulira masiku asanu ndi awiri.—2 Samueli 12:14-18.
Ena samvetsa chifukwa chake mwanayo anafa, poona zimene lemba la Deuteronomo 24:16 limanena kuti: “Ana asaphedwere atate.” Koma tikumbukire kuti ngati anthu akanaweruza mlandu umenewu, makolowo limodzi ndi mwana wosabadwayo akanaphedwa. Kumwalira kwa mwanayo kuyenera kuti kunathandiza Davide kuzindikira mokwanira mmene tchimo limene anachita ndi Bateseba linanyansira Yehova. Tikhale otsimikiza kuti Yehova anaweruza nkhaniyi mwachilungamo, pakuti “njira yake ili yangwiro.”—2 Samueli 22:31.
[Chithunzi patsamba 31]
Davide analapadi moona mtima