Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mari Mzinda Wakale Wotchuka wa M’chipululu

Mari Mzinda Wakale Wotchuka wa M’chipululu

Mari Mzinda Wakale Wotchuka wa M’chipululu

ANDRÉ PARROT, katswiri wa ku France wofukula zinthu zakale m’mabwinja, anati: “Nditafika m’chipinda changa chogona usiku umenewo, ndinali wosangalala kwambiri chifukwa ine ndi anzanga tinali kukondwerera mwayi umene tinakhala nawo.” Mu January 1934, ku Tell Hariri, pafupi ndi tauni yaing’ono ya Abu Kemali imene ili m’mphepete mwa mtsinje wa Firate ku Suriya, a Parrot ndi gulu lawo anafukula chiboliboli cholembedwa mawu akuti: “Lamugi-Mari, mfumu ya Mari, mkulu wa ansembe wa Enelili.” Anasangalala kwambiri ndi chiboliboli chimene anafukulachi.

Uku kunali kupezeka kwa mzinda wa Mari. Kwa ophunzira Baibulo, kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi kupezeka kwa mzinda umenewu?

Kodi Chochititsa Chidwi N’chiyani ndi Mzinda wa Mari?

Zinadziwika kuchokera m’zolembedwa zamakedzana kuti kunali mzinda wotchedwa Mari, koma kwa nthawi yaitali kumene mzindawu unali sikunali kudziwika. Malinga ndi zimene ananena alembi a ku Sumeri, mzinda wa Mari unali likulu la ufumu womwe nthawi inayake unali kulamulira Mesopotamiya yense. Popeza kuti mzinda wa Mari unali m’mphepete mwa mtsinje wa Firate, unamangidwa pamalo abwino kwambiri pamene amalonda a ku Persian Gulf anali kukumana ndi amalonda a ku Asuri, Mesopotamiya, Anatolia, ndi mayiko a m’mbali mwa nyanja ya Mediterranean. Zinthu zomwe zinali zosowa kwambiri ku Mesopotamiya, monga matabwa, zitsulo ndi miyala, zinkadutsa mu mzinda umenewu. Msonkho wa katundu ameneyu unalemeretsa kwambiri mzinda wa Mari, ndipo zimenezi zinachititsa kuti mzindawu ukhale wamphamvu kwambiri m’deralo. Koma Sarigoni wa ku Akadi atagonjetsa dziko la Suriya, kutchuka kumeneku kunatha.

Kwa zaka ngati 300 kuchokera pamene Sarigoni anagonjetsa Suriya, mzinda wa Mari unalamulidwa ndi akazembe ankhondo osiyanasiyana. Mu ulamuliro wa akazembe amenewa, mzindawu unatukukanso pachuma. Koma podzafika nthawi ya Zimiri-Limu, wolamulira womalizira wa mzindawu, n’kuti mzinda wa Mari utayamba kuchepa mphamvu. Zimiri-Limu anayesa kulimbitsa ufumu wake mwa kugonjetsa mizinda ina, kuchita mapangano amtendere ndi kukwatitsa ana ake kwa mafumu ena. Koma cha m’ma 1760 B.C.E., Mfumu Hammurabi ya Babulo inagonjetsa ndi kuwononga mzindawu. Kumeneku kunali kutha kwa mzinda umene a Parrot anautcha “umodzi mwa mizinda yotukuka kwambiri yamakedzana.”

Pamene asilikali a Hammurabi anali kuwononga mzinda wa Mari, mosadziwa anathandiza kwambiri akatswiri ofukula zinthu zakale ndi olemba mbiri amasiku ano. Pogumula makoma a njerwa zosawotcha, m’malo ena anakwirira nyumba zina mamita 5 kupita pansi, ndipo zimenezi zinachititsa kuti zitetezeke kwa nthawi yaitali. Ofukula zinthu zakale afukula mabwinja a akachisi ndi nyumba zachifumu, komanso zinthu zina zakale ndi zolembalemba zambirimbiri zomwe zawathandiza kudziwa za chitukuko chimene chinalipo kalelo.

N’chifukwa chiyani mabwinja a Mari ali ochititsa chidwi kwa ife? Ganizirani za nthawi imene kholo lakale Abrahamu linali ndi moyo. Abrahamu anabadwa m’chaka cha 2018 B.C.E., patatha zaka 352 kuchokera nthawi ya Chigumula chachikulu. Mbadwo wake unali wa nambala 10 kuchokera pa Nowa. Atalamulidwa ndi Mulungu, Abrahamu anachoka mumzinda wakwawo wa Uri, ndi kupita ku Harana. M’chaka cha 1943 B.C.E., Abrahamu ali ndi zaka 75 zakubadwa, anachoka ku Harana ndi kupita m’dziko la Kanani. “Ulendo wa Abrahamu wochoka ku Uri kupita ku Yerusalemu [mu Kanani] unachitika panthawi imene mzinda wa Mari unalipo,” anatero Paolo Matthiae, katswiri wofukula zinthu zakale wa ku Italy. Choncho, kupezeka kwa mzinda wa Mari n’kopindulitsa chifukwa kungatipatse chithunzi cha mmene dziko linalili panthawi ya moyo wa Abrahamu, mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. *​—Genesis 11:10–12:4.

Kodi Mabwinjawo Amavumbula Zotani?

Chipembedzo chinali champhamvu mu mzinda wa Mari monga momwe zinalili m’madera ena ku Mesopotamiya. Kutumikira milungu unali udindo wa munthu aliyense. Posankha zochita pa nkhani yaikulu, nthawi zonse ankafunsira kwa milungu. Ofukula zinthu zakale anapeza mabwinja a akachisi asanu ndi mmodzi. Ena mwa iwo ndi Kachisi wa Mikango (ena amaganiza kuti kachisi ameneyu ndi wa Dagani, amene m’Baibulo amatchedwa Dagoni), malo opatulika a Ishitara, mulungu wamkazi wa mphamvu zobereka, komanso malo opatulika a mulungu dzuwa wotchedwa Shamashi. Kalelo mu akachisi onsewa munali chiboliboli cha mulungu, ndipo anthu ankapereka nsembe ndi kupemphera kwa fano limenelo. Anthu amene anali kupembedza milungu imeneyi ankatenga ziboliboli zomwetulira za nkhope zawo zooneka ngati zikupemphera, ndipo ankaziyika m’mabenchi m’malo opatulikawo. Iwo ankachita zimenezi chifukwa anali kukhulupirira kuti chibolibolicho chinkapitiriza kupembedza mwiniwakeyo akachoka. A Parrot ananena kuti: “Mofanana ndi makandulo amene amagwiritsidwa ntchito m’chipembedzo cha Katolika masiku ano, ziboliboli za nkhope ya munthu wopembedzayo kwenikweni zinali mlowam’malo wa wokhulupirirayo.”

Chinthu chochititsa chidwi kwambiri chomwe anafukula m’mabwinja a Tell Hariri chinali zotsalira za nyumba yaikulu yachifumu. Nyumba imeneyi inkadziwika ndi dzina la Mfumu Zimiri-Limu, munthu wotsiriza kukhalamo. Louis-Hugues Vincent, yemwe ndi katswiri wa ku France wofukula zinthu zakale, anaitcha “nyumba yokongola zedi pa nyumba zonse za Kum’mawa kalelo.” Nyumba imeneyi inali yaikulu maekala oposa asanu ndi limodzi, ndipo inali ndi zipinda komanso mabwalo am’kati pafupifupi 300. Ngakhale kalelo, nyumba yachifumu imeneyi inali chimodzi mwa zinthu zodabwitsa pa dziko lonse. Pothirira ndemanga, m’buku lake lakuti Ancient Iraq, Georges Roux anati: “Inalidi yotchuka kwambiri, mwakuti Mfumu ya mzinda wa Ugarit, womwe uli m’mbali mwa nyanja ku Suriya, sanazengereze kutumiza mwana wake wamwamuna kumeneko, mtunda wa makilomita 600, kuti akangoona chabe ‘nyumba ya Zimiri-Limu.’”

Asanafike pabwalo lalikulu la nyumba yachifumuyo, alendo ankalowa kum’panda kudzera pakhomo limodzi lomwe linali ndi zipilala mbali zonse. Akakhala pa mpando wake wachifumu womwe unali pachiundo, Zimiri-Limu, mfumu yomaliza ya Mari, anali kusamalira nkhani zokhudza asilikali, zamalonda, ndi mgwirizano wa dziko lake ndi mayiko ena. Analinso kuweruza milandu, ndi kulandira alendo ndi akazembe a mayiko ena. Nyumbayi inali ndi zipinda zogona alendo omwe kawirikawiri mfumu inali kuwachereza mwa kuwakonzera phwando lalikulu. Zakudya zake zinali nyama ya ng’ombe, ya nkhosa, ya mphoyo, nsomba ndi nkhuku. Zonsezi ankachita kuwotcha, kukazinga, kapena kuphika, ndipo msuzi wake unali wa adyo ndi zokometsera zina. Pankakhalanso ndiwo zamasamba zosiyanasiyana ndi tchizi cha mitundumitundu. Ndiye zotsitsira zake zinali zipatso zothyoledwa kumene, zoumitsa, kapena zopaka shuga, ndi makeke ophikidwa mochititsa kaso. Kenako alendowo ankawapatsa mowa kapena vinyo kuti aziziritse kukhosi.

Malowa anali aukhondo kwambiri. Ofukula mabwinja anapeza zipinda mmene munali zosambiramo zikuluzikulu zadothi ndi zimbudzi za m’nyumba. Pansi ndi mmunsi mwa khoma la zipinda zimenezi munali motetezedwa bwino ndi phula. Madzi oipa ankadutsa m’ngalande zomanga ndi njerwa, ndipo pakali pano mapaipi adothi otetezedwa ndi phula akugwirabe ntchito pambuyo pa zaka pafupifupi 3,500. Atatu mwa akazi a mfumu atagwidwa ndi matenda oopsa, anawapatsa malangizo okhwima kwambiri. Mkazi wodwalayo anafunika kumuchotsa pagulu la anzake ndi kumubindikiritsa. “Aliyense sankayenera kumwera kapu yake, kudya naye limodzi kapena kukhala pa mpando wake.”

Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zimene Zinalembedwa pa Miyala Yomwe Anaipeza Kumeneko?

A Parrot ndi gulu lawo lija anafukula miyala pafupifupi 20,000 yolembedwa m’chinenero cha Chiakadi. Miyala imeneyi inali makalata ndiponso nkhani za kayendetsedwe ka boma ndi chuma. Mwa zonsezi, zomwe azisindikiza kukhala mabuku lerolino n’zochepa chabe. Komabe, zili m’mavoliyumu 28. Kodi n’zofunika motani? Mkulu woyang’anira ntchito yofukula mabwinja a Mari, Jean-Claude Margueron, anati: “Tisanapeze miyala yolembedwayi ku Mari, sitinkadziwa chilichonse chokhudza mbiri, chikhalidwe, ndi mmene moyo watsiku ndi tsiku wa anthu a ku Mesopotamiya ndi ku Suriya unalili chitangotha chaka cha 2000 B.C.E. Kupezeka kwa miyala imeneyi kwathandiza kwambiri kulemba mabuku ochuluka ofotokoza mbiri ya nthawi imeneyo.” Monga mmene a Parrot ananenera, miyala imeneyi “inavumbula zinthu zofanana modabwitsa za anthu amene akutchulidwa mmenemo ndi zimene Chipangano Chakale chimatiuza zokhudza nthawi ya Makolo akale.”

Miyala imeneyi yomwe inapezeka ku Mari ikuthandizanso kumvetsa ndime zina za m’Baibulo. Mwachitsanzo, miyalayi ikusonyeza kuti “chizolowezi chachikulu cha mafumu panthawi imeneyo,” chinali kulanda akazi a mfumu imene amenyana nayo. Chotero malangizo amene Ahitofeli wopanduka uja anauza Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide, kuti akagone ndi akazi aang’ono a atate wake sanali achilendo.​—2 Samueli 16:21, 22.

Kuchokera m’chaka cha 1933, ntchito yofukula mabwinja a ku Tell Hariri yachitika maulendo 41. Koma padakali pano, mwa maekala onse 270 a mabwinja a Mari, angofufuza maekala okwana 20 okha. Mosakayikira adzapezanso zinthu zina zosangalatsa ku Mari, mzinda wakale wotchuka wa m’chipululu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 N’kuthekanso kuti Yerusalemu atawonongedwa mu 607 B.C.E., Ayuda omwe anali kupita ku ukapolo ku Babulo anadutsa m’mphepete mwa mabwinja a mzinda wa Mari.

[Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Persian Gulf

Uri

MESOPOTAMIYA

Firate

MARI

ASURI

Harana

ANATOLIA

KANANI

Yerusalemu

Nyanja ya Mediterranean (Nyanja Yaikulu)

[Chithunzi patsamba 11]

Pa mwala uwu, Mfumu Iyahaduni-Limu ya Mari inanena modzikuza za ntchito yake yomanga

[Chithunzi patsamba 11]

Kupezeka kwa chiboliboli ichi cha Lamugi-Mari kunathandiza kuti mzinda wa Mari udziwike bwino pomwe unali

[Chithunzi patsamba 12]

Ebihu-Ili, nduna mu ufumu wa Mari, akupemphera

[Chithunzi patsamba 12]

Chiundo cha m’nyumba yachifumu, mwinamwake pamene anaimikapo fano la mulungu wamkazi

[Chithunzi patsamba 12]

Makoma a njerwa zosawotcha a mabwinja a Mari

[Chithunzi patsamba 12]

Malo osambira m’nyumba yachifumu

[Chithunzi patsamba 13]

Mwala wakale pamene Naramu-Sini analembapo za mmene anagonjetsera mzinda wa Mari

[Chithunzi patsamba 13]

Miyala yolembedwa pafupifupi 20,000 inapezeka m’mabwinja a nyumba yachifumu

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

© Mission archéologique française de Tell Hariri-Mari (Syrie)

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Document: Musée du Louvre, Paris; statue: © Mission archéologique française de Tell Hariri-Mari (Syrie)

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Statue: Musée du Louvre, Paris; podium and bathroom: © Mission archéologique française de Tell Hariri-Mari (Syrie)

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Victory stele: Musée du Louvre, Paris; palace ruins: © Mission archéologique française de Tell Hariri-Mari (Syrie)