Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Njira za Yehova

Phunzirani Njira za Yehova

Phunzirani Njira za Yehova

“Mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni.”​—EKSODO 33:13.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani Mose anapha Mwaigupto atamuona akuzunza Mhebri? (b) Kuti akhale woyenerera kutumikira Yehova, kodi Mose anafunikira kuphunzira chiyani?

MOSE anakulira m’banja la Farao ndipo anaphunzitsidwa nzeru zimene olamulira a ku Igupto ankaziona kuti ndi zapamwamba. Komabe, Mose ankadziwa kuti sanali Mwaigupto. Ankadziwa kuti makolo ake anali Ahebri. Ali ndi zaka 40, anapita kukayendera abale ake, ana a Israyeli. Mose sanangokhala ataona Mwaigupto akuzunza Mhebri. Anapha Mwaiguptoyo. Mose anasankha kukhala kumbali ya anthu a Yehova ndipo anali kuganiza kuti Mulungu akumugwiritsa ntchito populumutsa abale akewo. (Machitidwe 7:21-25; Ahebri 11:24, 25) Nkhani imeneyi itadziwika, banja lachifumu ku Igupto linaona Mose monga wopanduka, chotero Mose anathawa pofuna kupulumutsa moyo wake. (Eksodo 2:11-15) Kuti Mose agwiritsidwe ntchito ndi Mulungu, anafunikira kudziwa bwino njira za Yehova. Kodi Mose anali woti akhoza kuphunzira?​—Salmo 25:9.

2 Kwa zaka 40 zotsatira, Mose anali kukhala m’dziko lachilendo ndipo anali mbusa. M’malo mokhumudwa ndi abale ake achihebri omwe anali kuoneka ngati sakulabadira za iye, Mose anagonjera zimene Mulungu analola. Ngakhale kuti kwa zaka zambiri palibe amene anazindikira kudzipereka kwa Mose, iye analola kuumbidwa ndi Yehova. Motsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, osati pofuna kudzitamandira, iye patapita nthawi analemba mawu otsatirawa: “Munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Yehova anagwiritsa ntchito Mose mwapadera kwambiri. Ifenso tikafuna chifatso, Yehova adzatidalitsa.​—Zefaniya 2:3.

Anapatsidwa Ntchito

3, 4. (a) Kodi Mose anapatsidwa ntchito yotani ndi Yehova? (b) Kodi Mose anapatsidwa thandizo lotani?

3 Tsiku lina mngelo woimira Yehova analankhula ndi Mose pafupi ndi Phiri la Horebe m’dera la Sinai. Mose anauzidwa kuti: “Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m’Aigupto, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zawo; ndipo ndatsikira kuwalanditsa m’manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” (Eksodo 3:2, 7, 8) Mogwirizana ndi mawu amenewa, Mulungu anali ndi ntchito yoti Mose agwire, koma anafunika kuigwira mmene Yehova akufunira.

4 Mngelo wa Yehova anapitiriza kuti: “Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israyeli m’Aigupto.” Mose anachita mantha. Anaona ngati sangakwanitse ntchito imeneyi, ndipo n’zoona kuti payekha sakanakwanitsa. Komabe, Yehova anatsimikizira Mose kuti: “Ine ndidzakhala ndi iwe.” (Eksodo 3:10-12) Yehova anapatsa Mose mphamvu zochita zozizwitsa kuti ukhale umboni wakuti anatumidwadi ndi Mulungu. Pa ulendowu Mose anafunika kutsagana ndi mbale wake Aroni, kuti akhale womulankhulira. Yehova akanawaphunzitsa zoti akanene ndi kuchita. (Eksodo 4:1-17) Kodi Mose akanagwira ntchito imeneyi mokhulupirika?

5. N’chifukwa chiyani zochita za Aisrayeli zinali zothetsa nzeru kwa Mose?

5 Poyambirira, amuna akulu a Israyeli anakhulupirira Mose ndi Aroni. (Eksodo 4:29-31) Koma posakhalitsa, “akapitawo a ana a Israyeli” anaimba mlandu Mose ndi mbale wake kuti ‘akuwanyansitsa’ pamaso pa Farao ndi antchito ake. (Eksodo 5:19-21; 6:9) Pamene Aisrayeli anali kuchoka m’dziko la Igupto, anachita mantha ataona magaleta a Aigupto akuwatsatira. Popeza kuti kutsogolo kwawo kunali Nyanja Yofiira, ndipo kumbuyo kwawo kunali kubwera magaleta ankhondo, Aisrayeli analibe kothawira ndipo anaimba mlandu Mose. Kodi mukanakhala inu mukanatani? Ngakhale kuti Aisrayeliwo analibe ngalawa, pomvera malangizo a Yehova, Mose analimbikitsa anthuwo kulongedza katundu wawo ndi kupitiriza ulendo. Kenako Mulungu anapatula madzi a Nyanja Yofiira, ndipo Aisrayeli anadutsa pouma.​—Eksodo 14:1-22.

Nkhani Yofunika Kwambiri Kuposa Chipulumutso

6. Kodi Yehova anagogomeza chiyani pamene anali kupatsa Mose ntchito yoti achite?

6 Potumiza Mose kuti akapulumutse Aisrayeli, Yehova anagogomeza kufunika kwa dzina la Mulungu. Kulemekeza dzina limenelo ndi mwiniwake wa dzinalo kunali kofunika. Mose atafunsa za dzina la Mulungu, Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine yemwe ndili Ine.” Komanso, Mose anafunikira kuuza ana a Israyeli kuti: “Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu.” Yehova anawonjezera kuti: “Ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.” (Eksodo 3:13-15) Kwa atumiki ake padziko lonse lapansi, Mulungu akudziwikabe ndi dzina lakuti Yehova.​—Yesaya 12:4, 5; 43:10-12.

7. Kodi Mulungu analimbikitsa Mose kuchita chiyani mosasamala kanthu za kudzitukumula kwa Farao?

7 Mose ndi Aroni anaonekera pamaso pa Farao ndi kupereka uthenga wawo m’dzina la Yehova. Koma modzitukumula Farao anati: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindim’dziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.” (Eksodo 5:1, 2) Farao anasonyeza kuuma mtima ndiponso anali kuchita zinthu mwachinyengo, koma Yehova analimbikitsa Mose kupita mobwerezabwereza kukamuuza uthenga. (Eksodo 7:14-16, 20-23; 8:1, 2, 20) Zinali zoonekeratu kwa Mose kuti Farao waipidwa. Kodi kupitanso kukalankhula naye kukanathandiza chilichonse? Aisrayeli anali ofunitsitsa kupulumutsidwa. Koma Farao anali kukana kwa mtu wa galu. Kodi inuyo mukanatani?

8. Kodi njira imene Yehova anachitira ndi Farao inali yopindulitsa motani, nanga kodi zochitika zimenezo ziyenera kutikhudza motani?

8 Mose anapita kukapereka uthenga winanso wakuti: ‘Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.’ Mulungu ananenanso kuti: “Ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uwonongeke pa dziko lapansi. Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.” (Eksodo 9:13-16) Mwa kupereka chiweruzo kwa Farao wouma mtimayo, Yehova anafuna kusonyeza mphamvu zake kuti likhale chenjezo kwa onse omunyoza. Amenewa anaphatikizapo Satana Mdyerekezi, amene pambuyo pake Yesu Kristu anamutcha “mkulu wa dziko lapansi.” (Yohane 14:30; Aroma 9:17-24) Monga mmene ulosi unanenera, dzina la Yehova linalengezedwa pa dziko lonse. Kuleza mtima kwake kunathandiza kuti Aisrayeli komanso namtindi wa anthu ena osiyanasiyana amene anagwirizana nawo polambira Mulungu apulumuke. (Eksodo 9:20, 21; 12:37, 38) Kuchokera panthawiyo, anthu enanso mamiliyoni ambiri omwe agwirizana ndi chipembedzo choona apindula ndi ntchito yolengeza dzina la Yehova.

Kutsogolera Anthu Ovuta

9. Kodi anthu a mtundu wa Mose enieniwo anasonyeza motani kusalemekeza Yehova?

9 Ahebri ankadziwa dzina la Mulungu. Mose anagwiritsa ntchito dzina limeneli polankhula nawo, koma iwo sanasonyeze ulemu woyenera kwa mwini dzinalo. Yehova atangopulumutsa kumene Aisrayeli mozizwitsa kuchoka ku Igupto, n’chiyani chimene anthuwo anachita atalephera kupeza mwamsanga madzi akumwa? Anang’ung’udza motsutsana ndi Mose. Kenako anadandaula ndi chakudya. Mose anawachenjeza kuti kung’ung’udza kwawoko sanali kung’ung’udzira iyeyo ndi Aroni koma Yehova. (Eksodo 15:22-24; 16:2-12) Pa Phiri la Sinai, Yehova anapereka Chilamulo kwa Aisrayeli, ndipo panthawiyo panachitikanso zinthu zozizwitsa. Komabe, mosamvera anthu anapanga fano la mwana wang’ombe wagolide ndi kulilambira, ndipo amenewo ankati ndi “madyerero a Yehova.”​—Eksodo 32:1-9.

10. N’chifukwa chiyani pempho la Mose lopezeka pa Eksodo 33:13 lili lapadera kwambiri kwa oyang’anira achikristu lerolino?

10 Kodi Mose akanachita bwanji ndi anthu omwe Yehova iyemwini anawatcha ouma khosi? Mose anapempha Yehova kuti: “Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu.” (Eksodo 33:13) Poyang’anira Mboni za Yehova zamakono, oyang’anira achikristu amaweta gulu la nkhosa lodzichepetsa kwambiri kuposa mtundu wa Israyeli. Komabe, nawonso amapemphera kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Kudziwa njira za Yehova kumathandiza oyang’anira kuthana ndi mavuto m’njira yogwirizana ndi Mawu a Mulungu komanso umunthu wake.

Zimene Yehova Amayembekezera kwa Anthu Ake

11. Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Mose, nanga n’chifukwa chiyani ifeyo tikufuna kudziwa malangizo amenewa?

11 Zimene Yehova anali kuyembekezera kwa anthu ake anazitchula pa Phiri la Sinai m’mawu apakamwa. Pambuyo pake, Mose analandira Malamulo Khumi olembedwa pa miyala iwiri. Mose atatsika m’phiri, anaona Aisrayeli akulambira fano la mwana wa ng’ombe, ndipo mokwiya anaponya pansi miyala iwiri ija ndipo inasweka. Yehova analembanso Malamulo Khumiwo pa miyala imene Mose anasema. (Eksodo 32:19; 34:1) Malamulo amenewa sanasinthe kuchokera pamene anaperekedwa. Mose anafunikira kuwatsatira. Mulungu anauzanso Mose momveka bwino za umunthu Wake, ndipo mwa kutero anasonyeza Mose mmene ayenera kuchitira zinthu monga woimira Yehova. Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose, komabe m’zimene Yehova anauza Mose timapezamo mfundo zikuluzikulu zomwe sizinasinthe ndipo zikugwirabe ntchito kwa onse opembedza Yehova. (Aroma 6:14; 13:8-10) Tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi.

12. Kodi Aisrayeli anayenera kukhudzidwa bwanji ndi mfundo yakuti iwo anafunikira kupembedza Yehova yekha?

12 Pembedzani Yehova yekha. Mtundu wa Israyeli unadzimvera wokha Yehova akunena kuti amafuna kuti iwo azipembedza iye yekha. (Eksodo 20:2-5) Aisrayeli anali ataona umboni wochuluka wosonyeza kuti Yehova ndi Mulungu woona. (Deuteronomo 4:33-35) Yehova ananena mosapita m’mbali kuti mosasamala kanthu zimene mitundu ina ikuchita, iye sadzalekerera mtundu uliwonse wa kupembedza mafano kapena kukhulupirira mizimu pakati pa anthu ake. Kudzipereka kwawo kwa iye sikunayenera kungokhala kwa mwambo chabe ayi. Onse anafunikira kukonda Yehova ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi mphamvu zawo zonse. (Deuteronomo 6:5, 6) Zimenezi zinalinso kukhudza kalankhulidwe kawo, khalidwe lawo, inde mbali iliyonse ya moyo wawo watsiku ndi tsiku. (Levitiko 20:27; 24:15, 16; 26:1) Yesu Kristu nayenso ananena mosapita m’mbali kuti Yehova amafuna kuti tizipembedza iye yekha basi.​—Marko 12:28-30; Luka 4:8.

13. N’chifukwa chiyani Aisrayeli anafunikira kumvera Mulungu zivute zitani, nanga n’chiyani chimene chiyenera kutilimbikitsa kumumvera? (Mlaliki 12:13)

13 Mverani malamulo a Yehova zivute zitani. Anthu a mu Israyeli anafunikira kukumbutsidwa kuti pamene anachita pangano ndi Yehova, analumbira kuti adzamumvera zivute zitani. Munthu aliyense payekha anali ndi ufulu wochuluka, koma pa nkhani zokhudzana ndi malamulo amene Yehova anawapatsa, anafunikira kumvera malamulowo zivute zitani. Mwa kuchita zimenezo akanasonyeza kuti amakondadi Mulungu, ndipo iwowo ndi ana awo akanapindula chifukwa zonse zimene Yehova anali kufuna zinali zoti zipindulitse iwowo.​—Eksodo 19:5-8; Deuteronomo 5:27-33; 11:22, 23.

14. Kodi Mulungu anagogomeza motani kwa Aisrayeli kufunika koika patsogolo zinthu zauzimu?

14 Ikani zinthu zauzimu patsogolo. Mtundu wa Israyeli sunayenera kulola zinthu zakuthupi kuwachotsera chidwi chawo pa zinthu zauzimu. Aisrayeli sanafunikire kutanganidwa ndi zinthu wamba pa moyo wawo. Yehova anapatula nthawi mlungu uliwonse kuti ikhale yopatulika, nthawi imene anafunikira kuigwiritsa ntchito pa zinthu zokhazo zokhudzana ndi kupembedza Mulungu woona. (Eksodo 35:1-3; Numeri 15:32-36) Chaka chilichonse, anali kupatulanso nthawi ina yochitira misonkhano inanso yopatulika. (Levitiko 23:4-44) Misonkhano imeneyi inali kuwapatsa mpata wokambirana ntchito zodabwitsa za Yehova, kukumbutsidwa njira zake, ndi kusonyeza kuyamikira kwawo Mulungu chifukwa cha zabwino zonse zimene wawachitira. Anthu akasonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova, ankakulitsa mantha ndi chikondi chawo pa Mulungu ndipo zinali kuwathandiza kuyenda m’njira zake. (Deuteronomo 10:12, 13) Mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’malangizo amenewo zimapindulitsa atumiki a Yehova lerolino.​—Ahebri 10:24, 25.

Kumvetsa Makhalidwe a Yehova

15. (a) N’chifukwa chiyani kumvetsa makhalidwe a Yehova kunali kopindulitsa kwa Mose? (b) Ndi mafunso ati amene angatithandize kuganizira mozama za khalidwe lililonse palokha mwa makhalidwe onse a Yehova?

15 Kumvetsa makhalidwe a Yehova kunathandizanso Mose kutsogolera bwino anthu. Lemba la Eksodo 34:5-7 limanena kuti Mulungu anadutsa pamaso pa Mose, nafuula kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi.” Ganizirani mawu amenewa mofatsa. Dzifunseni kuti: ‘Kodi lililonse mwa makhalidwe amenewa likutanthauzanji? Kodi Yehova analisonyeza motani? Kodi oyang’anira achikristu angasonyeze motani khalidwe limeneli? Kodi khalidwe lililonse palokha liyenera kukhudza motani zochita za aliyense wa ife?’ Onani zitsanzo zochepa chabe zotsatirazi.

16. Kodi chifundo cha Mulungu chimaphatikizapo chiyani?

16 Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo.” Kuwonjezera pa mfundo yakuti nthawi zina amafewetsako chilango, chifundo cha Yehova chimaphatikizapo chisoni chachikulu. Chimam’pangitsa Mulungu kuchitapo kanthu kuti athandize anthu ake. Umboni wa zimenezi ndi wakuti Mulungu anapatsa Aisrayeli zosowa zawo zakuthupi ndi zauzimu pa ulendo wawo wopita ku Dziko Lolonjezedwa. (Deuteronomo 1:30-33; 8:4) Munthu akalakwa, mwa chifundo Yehova anali kumukhululukira. Anthu ake akalewo anawasonyeza chifundo. Atumiki ake amakono ayeneratu kukomerana mtima wina ndi mnzake.​—Mateyu 9:13; 18:21-35.

17. Kodi kumvetsetsa kwathu chisomo cha Yehova kungalimbikitse motani kupembedza koona?

17 Chifundo cha Yehova chimayendera limodzi ndi chisomo. Dikishonale ina ya Chichewa imati “chisomo” ndi mkhalidwe wopeza kapena kukhala ndi chinthu chabwino mosavuta. Ndiyeno siyanitsani tanthauzo limeneli ndi malemba amene amanena za Yehova kuti ndi wachisomo. Baibulo limasonyeza kuti chisomo cha Yehova chimaphatikizapo kusamalira mwachikondi osauka omwe ali pakati pa anthu ake. (Eksodo 22:26, 27) M’dziko lililonse, alendo komanso anthu ena zinthu zingathe kuwavuta penapake. Pophunzitsa anthu ake kukhala opanda tsankho ndi kuti azisonyeza chifundo kwa anthu oterewa, Yehova anawakumbutsa kuti nawonso anali alendo ku Igupto. (Deuteronomo 24:17-22) Bwanji nanga ifeyo monga anthu a Mulungu masiku ano? Kuchitirana mwachisomo kumatithandiza kukhala ogwirizana ndipo zimakokera ena kudzapembedza Yehova.​—Machitidwe 10:34, 35; Chivumbulutso 7:9, 10.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anaphunzitsa Aisrayeli kuti azipewa pochita zinthu ndi anthu a mitundu ina?

18 Komabe, kuchitira chifundo anthu a mtundu wina sikunayenera kuphimba chikondi chimene Aisrayeli anali nacho pa Yehova ndi miyezo yake ya makhalidwe abwino. Choncho, Aisrayeli anaphunzitsidwa kusayenda m’njira za mitundu yowazungulira, monga kutengera miyambo yawo yachipembedzo ndi makhalidwe awo oipa. (Eksodo 34:11-16; Deuteronomo 7:1-4) Zimenezi zikugwiranso ntchito kwa ife masiku ano. Tiyenera kukhala anthu oyera, popeza Yehova Mulungu wathu ndi woyera.​—1 Petro 1:15, 16.

19. Kodi kumvetsetsa mmene Yehova amaonera tchimo kungateteze motani anthu ake?

19 Pofuna kuti Mose amvetse njira za Mulungu, Yehova anafotokoza momveka bwino kuti ngakhale kuti sagwirizana ndi tchimo, iye ndi wosakwiya msanga. Amapereka mpata wokwanira kuti anthu aphunzire zofuna zake ndi kuchita mogwirizana ndi zofuna zakezo. Munthu akalapa, Yehova amam’khululukira machimowo, koma salephera kupereka chilango choyenera pa machimo aakulu. Anachenjeza Mose kuti mibadwo ya m’tsogolo idzakhudzidwa ndi zabwino kapena zoipa zomwe Aisrayeliwo anali kuchita. Kumvetsa ndi kuyamikira njira za Yehova kungathandize anthu a Mulungu kupewa kuimba Mulungu mlandu pa mavuto omwe awayambitsa okha kapena kupewa kuganiza kuti Mulungu akuchedwa.

20. N’chiyani chingatithandize kuchita moyenera ndi okhulupirira anzathu ndi ena amene timakumana nawo mu utumiki wathu? (Salmo 86:11)

20 Ngati mukufuna kudziwa Yehova ndi njira zake mozama, pitirizani kufufuza ndi kusinkhasinkha pamene mukuwerenga Baibulo. Phunzirani mozama mbali zosiyanasiyana zochititsa chidwi za umunthu wa Yehova. Mwapemphero, ganizirani mmene mungatsanzirire Mulungu ndipo gwirizanitsani mokwanira moyo wanu ndi zifuno zake. Zimenezi zidzakuthandizani kupewa kulakwitsa zinthu, zidzakuthandizani kuchita zinthu moyenera ndi okhulupirira anzanu, ndiponso mudzatha kuthandiza ena kudziwa ndi kukonda Mulungu wathu wamkulu.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi chifatso chinali chofunika motani kwa Mose, nanga n’chifukwa chiyani chili chofunika kwa ifeyo?

• Kodi kuuza Farao mawu a Yehova mobwerezabwereza kunali kopindulitsa motani?

• Kodi ndi mfundo zapamwamba ziti zimene Mose anaphunzitsidwa zimenenso zikugwira ntchito kwa ife?

• Kodi tingazamitse motani kumvetsa kwathu makhalidwe a Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Mokhulupirika Mose anapereka uthenga wa Yehova kwa Farao

[Chithunzi patsamba 23]

Yehova anauza Mose zofuna zake

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Sinkhasinkhani makhalidwe a Yehova