Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ugwireni Mtima Pokumana ndi Zoipa’

‘Ugwireni Mtima Pokumana ndi Zoipa’

‘Ugwireni Mtima Pokumana ndi Zoipa’

“Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse, . . . wougwira mtima pokumana ndi zoipa.”​—2 TIMOTEO 2:24, NW.

1. Pamene tikugwira ntchito yachikristu, n’chifukwa chiyani nthawi zina timakumana ndi anthu achipongwe?

KODI mumatani mukamanyozedwa ndi anthu amene sagwirizana nanu kapena amene sagwirizana ndi chipembedzo chanu? Pofotokoza za masiku otsiriza, mtumwi Paulo ananeneratu kuti anthu adzakhala “amwano, . . . akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali.” (2 Timoteo 3:1-5, 12) Mungakumane ndi anthu oterewa mu utumiki wanu kapena pamene mukuchita zinthu zina.

2. Kodi ndi malemba ati omwe angatithandize kuchita mwanzeru ndi anthu amene akutilankhula mwachipongwe?

2 Sikuti aliyense wolankhula mwamwano alibe chidwi ndi zinthu zabwino ayi. Anthu akakumana ndi mavuto othetsa nzeru, kapena akakhumudwa ndi zinazake, angalankhule mwachipongwe kwa wina aliyense amene ali pafupi. (Mlaliki 7:7) Ambiri amachita zimenezi chifukwa chakuti akukhala komanso kugwira ntchito ndi anthu okonda kulankhula mwachipongwe. Izi sizikutanthauza kuti ife monga Akristu titengere kulankhula kotereku, koma zimatithandiza kumvetsa chifukwa chake ena amalankhula choncho. Kodi tizitani ngati ena akutilankhula mwachipongwe? Lemba la Miyambo 19:11 limati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.” Ndipo lemba la Aroma 12:17, 18 likutilangiza kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”

3. Kodi kukonda mtendere kukukhudzana motani ndi uthenga umene timalalikira?

3 Ngati ndifedi okonda mtendere, khalidwe lathu lidzasonyeza zimenezi. Zidzaonekera m’zimene tikunena ndi kuchita, ngakhalenso pankhope pathu ndi kamvekedwe ka mawu athu. (Miyambo 17:27) Potumiza atumwi ake kukalalikira, Yesu anawalangiza kuti: “Polowa m’nyumba muwalankhule [“muyionetse ndi kunena kuti: Mtendere ukhale ndi nyumbayi,” Malembo Oyera]. Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.” (Mateyu 10:12, 13) Uthenga umene timalengeza ndi uthenga wabwino. Baibulo limautcha “Uthenga Wabwino wa mtendere,” “Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu,” ndi “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Aefeso 6:15; Machitidwe 20:24; Mateyu 24:14) Cholinga chathu si kudzudzula zikhulupiriro za munthu wina kapena kukangana naye pa zimene amakhulupirira, koma kugawana naye uthenga wabwino wochokera m’Mawu a Mulungu.

4. Kodi munganene chiyani mwininyumba akakuuzani kuti “Ayi sindikufuna,” inu musananene n’komwe chimene mwabwerera?

4 Asanamvetsere n’komwe, mwininyumba anganene kuti, “Ayi sindikufuna.” Kawirikawiri zingathandize kunena kuti, “Ndimangofuna kuwerenga nanu mwachidule lemba limodzi ili la m’Baibulo.” N’kutheka kuti sangakane zimenezi. Nthawi zina, tingafunike kunena kuti: “Ndimangofuna kukuuzani za nthawi imene kupanda chilungamo sikudzakhalako ndipo anthu onse adzaphunzira kukondana.” Ngati mwininyumba sakuonetsa chidwi chofuna kumva zambiri, mungawonjezere kuti: “Koma mwina sindinakupezeni pa nthawi yabwino.” Kodi mwininyumba akapanda kutilandira mwa mtendere, tiganize kuti ‘sali woyenerera’? Mulimonse mmene mwininyumba angachitire, kumbukirani malangizo a m’Baibulo akuti muyenera “kukhala wodekha kwa onse, . . . wougwira mtima pokumana ndi zoipa.”​—2 Timoteo 2:24, NW.

Wachipongwe Koma Wosochera

5, 6. Kodi Saulo ankawachitira zotani otsatira a Yesu, nanga n’chifukwa chiyani ankachita zimenezi?

5 M’zaka 100 zoyambirira, munthu wotchedwa Saulo anatchuka chifukwa cholankhula mwachipongwe, ndiponso khalidwe lake la uchigawenga. Baibulo limanena kuti sanaleke “kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha.” (Machitidwe 9:1, 2) Patapita nthawi anavomereza kuti anali “wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe.” (1 Timoteo 1:13) N’kutheka kuti ena mwa achibale ake anali kale Akristu, koma pofotokoza mmene ankachitira ndi otsatira Kristu, iye anati: “Pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.” (Machitidwe 23:16; 26:11; Aroma 16:7, 11) Palibe umboni wosonyeza kuti pamene Saulo anali kuchita zimenezi, ophunzirawo anayesa kutsutsana naye.

6 N’chifukwa chiyani Saulo ankachita zimenezi? Patapita zaka, iye analemba kuti: “Ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.” (1 Timoteo 1:13) Iye anali Mfarisi, wophunzitsidwa “monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo.” (Machitidwe 22:3) Zikuoneka kuti mphunzitsi wa Saulo Gamaliyeli anali wololera, koma mkulu wa ansembe Kayafa, amene anadzagwirizana ndi Saulo anali waliuma. Kayafa ndi amene anali kutsogolera pokonza chiwembu chofuna kupha Yesu Kristu. (Mateyu 26:3, 4, 63-66; Machitidwe 5:34-39) Pambuyo pake, Kayafa anaonetsetsa kuti atumwi a Yesu akwapulidwa, ndipo anawalamula mwamphamvu kuti aleke kulalikira m’dzina la Yesu. Kayafa ndi amene anali kutsogolera bwalo la Sanihedirini pamene anali kuweruza mlandu wa Stefano. Panthawiyi, aliyense m’bwaloli anali wokwiya ndipo anam’tenga Stefano ndi kukam’ponya miyala. (Machitidwe 5:27, 28, 40; 7:1-60) Saulo anali kuonerera pamene Stefano anali kuponyedwa miyala, ndipo Kayafa anamulamula kuti amange otsatira a Yesu ku Damasiko pofuna kuletsa ntchito yawo. (Machitidwe 8:1; 9:1, 2) Popeza anali kulimbikitsidwa ndi Kayafa, Saulo ankaganiza kuti zimene anali kuchitazo unali umboni wakuti anali ndi changu potumikira Mulungu, koma zoona zake n’zakuti analibe chikhulupiriro chenicheni. (Machitidwe 22:3-5) Zotsatira zake, Saulo analephera kuzindikira kuti Yesu anali Mesiya weniweni. Koma Yesu woukitsidwa atalankhula naye mozizwitsa panjira yopita ku Damasiko, Saulo anazindikira kuopsa kwa zimene anali kuchitazo.​—Machitidwe 9:3-6.

7. Kodi chinachitikira Saulo n’chiyani atakumana ndi Yesu panjira yopita ku Damasiko?

7 Zitangochitika zimenezi, wophunzira Ananiya anatumidwa kukalalikira Saulo. Kodi inuyo mukanalola kukalalikira munthu woteroyo? Ananiya anachita mantha, komabe analankhula ndi Saulo mokoma mtima. Saulo anali atasintha chifukwa chokumana ndi Yesu mozizwitsa panjira yopita ku Damasiko. (Machitidwe 9:10-22) Pambuyo pake anadziwika monga mtumwi Paulo, mmishonale wachikristu wachangu.

Wofatsa Koma Wolimba Mtima

8. Kodi Yesu anasonyeza motani mmene Atate wake amaonera anthu ochita zinthu zoipa?

8 Yesu anali wolengeza Ufumu wachangu amene anali wofatsa koma wolimba mtima akakhala ndi anthu. (Mateyu 11:29) Anasonyeza mtima wa Atate wake wa kumwamba, amene akulimbikitsa oipa kuti asiye njira zawo zoipazo. (Yesaya 55:6, 7) Polankhula ndi anthu ochimwa, Yesu ankatha kuzindikira ngati wochimwayo wasintha, ndipo anthu oterewa ankawalimbikitsa. (Luka 7:37-50; 19:2-10) M’malo moweruza ena chifukwa cha maonekedwe okha, Yesu anali kutsanzira chifundo, kuleza mtima, ndi kupirira kwa Atate wake ndi cholinga chobweza wochimwayo kuti alape. (Aroma 2:4) Yehova akufuna kuti anthu onse alape ndi kupulumutsidwa.​—1 Timoteo 2:3, 4.

9. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kukwaniritsidwa kwa lemba la Yesaya 42:1-4 mwa Yesu?

9 Pofotokoza mmene Yehova anali kuonera Yesu Kristu, Mateyu, mlembi wa Uthenga Wabwino, anagwira mawu aulosi akuti: “Taona mnyamata wanga, amene ndinam’sankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja. Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake m’makwalala; bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.” (Mateyu 12:17-21; Yesaya 42:1-4) Mogwirizana ndi mawu aulosi amenewa, Yesu sanachitepo mkangano ndi wina aliyense. Iye anali kulankhula choonadi mokhutiritsa anthu oona mtima, ngakhale pamene zinthu zavuta.​—Yohane 7:32, 40, 45, 46.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani Yesu analalikira kwa ena mwa Afarisi, ngakhale kuti Afarisi anali kum’tsutsa kwambiri? (b) Kodi nthawi zina Yesu ankawayankha bwanji anthu otsutsa, koma kodi sanali kuchita chiyani?

10 Mu utumiki wake, Yesu analankhula ndi Afarisi ambiri. Ngakhale kuti ena a iwo ankafuna kumukola m’mawu ake, Yesu sanaganize kuti Afarisi onse ali ndi zolinga zoipa. Zikuoneka kuti Simoni, yemwenso anali Mfarisi wotsutsa, ankafuna kumudziwa bwino Yesu, choncho anamuitanira kunyumba kwake kuti akadye naye. Yesu anavomera ndipo anachitira umboni kwa amene analipo pa chakudyacho. (Luka 7:36-50) Panthawi ina, Mfarisi wina wotchuka, dzina lake Nikodemo anapita kwa Yesu mwachinsinsi usiku. Yesu sanam’dzudzule chifukwa choyembekezera mdima. M’malo mwake, analalikira kwa Nikodemo za chikondi chimene Mulungu anasonyeza potumiza Mwana wake kuti adzatsegule njira ya chipulumutso kwa onse okhulupirira. Mokoma mtima, Yesu anamuuzanso kufunika kogonjera makonzedwe a Mulungu. (Yohane 3:1-21) Nthawi inayake, Nikodemo anaikira Yesu kumbuyo pamene Afarisi ena ankanyoza lipoti labwino lonena za Yesu.​—Yohane 7:46-51.

11 Yesu ankadziwa bwino chinyengo cha anthu ofuna kumutchera msampha. Iye sanalole kuti otsutsawo amulowetse m’mikangano yopanda pake. Komabe, pamene kunali koyenera anali kuwayankha mwachidule koma mwamphamvu, mwa kuwauza mfundo ya choonadi, kuwapatsa fanizo, kapena kugwira lemba. (Mateyu 12:38-42; 15:1-9; 16:1-4) Nthawi zina, Yesu sanali kuyankha n’komwe akaona kuti kuyankha sikupindula chilichonse.​—Marko 15:2-5; Luka 22:67-70.

12. Kodi Yesu ankatha bwanji kuthandiza anthu, ngakhale pamene anamuzazira?

12 Nthawi zina, anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa anali kulankhula Yesu mozaza. Zimenezi zikachitika, iye anali kuugwira mtima ndipo ankathandiza anthu otero pogwiritsa ntchito mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu. (Marko 1:23-28; 5:2-8, 15) Mofananamo, anthu ena akakwiya nafe ndi kutizazira mu utumiki wathu, tifunika kuugwira mtima, ndi kuyesetsa kulankhula nawo mokoma mtima ndi mosamala.​—Akolose 4:6.

Kuugwira Mtima M’banja

13. N’chifukwa chiyani nthawi zina anthu amatsutsa wa m’banja mwawo amene wayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova?

13 Kawirikawiri zimaonekera m’banja kuti otsatira a Yesu afunika kumaugwira mtima. Munthu amene choonadi cha m’Baibulo chamufikadi pa mtima amafunitsitsa kuti zikhalenso chimodzimodzi ndi banja lake. Koma monga Yesu ananenera, anthu a m’banja lathu angadane nafe. (Mateyu 10:32-37; Yohane 15:20, 21) Izi zingachitike pa zifukwa zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, n’zoona kuti ziphunzitso za m’Baibulo zingatithandize kukhala oona mtima, osamalira bwino maudindo athu, ndiponso aulemu. Koma Malemba amatiphunzitsanso kuti mulimonse mmene zingakhalire, udindo wathu waukulu wagona pa kumvera Mlengi wathu. (Mlaliki 12:1, 13; Machitidwe 5:29) Wina m’banja lathu angakwiye nafe chifukwa cha kukhulupirika kwathu kwa Yehova, poona ngati kukhulupirika kwathuko kukumuchotsera mphamvu zimene ali nazo m’banjamo. Pothana ndi vuto limeneli, m’pofunikatu kwambiri kutsatira chitsanzo cha Yesu cha kuugwira mtima.​—1 Petro 2:21-23; 3:1, 2.

14-16. N’chiyani chimene chinachititsa kuti ena omwe kale ankatsutsa a m’banja mwawo asinthe?

14 Ambiri amene akutumikira Yehova panopa ankatsutsidwa kwambiri ndi anzawo a mu ukwati kapena anthu ena a m’banja mwawo, chifukwa cha kusinthika kwawo atayamba kuphunzira Baibulo. N’kutheka kuti otsutsawo anamva ndemanga zabodza zokhudza Mboni za Yehova, ndipo mwina ankaopa kuti zimenezo zidzadzetsa mavuto m’banjamo. N’chiyani chinawachititsa kusintha maganizo? Nthawi zambiri, chinawathandiza kusintha ndi chitsanzo chabwino cha wokhulupirirayo. Nthawi zina chitsutso cha m’banja chimachepa ngati wokhulupirirayo akugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo nthawi zonse, monga kupezeka pamisonkhano yachikristu ndi kulowa mu utumiki, kwinaku akusamalira maudindo ake a m’banja ndi kuugwira mtima pamene ena akumunenera chipongwe.​—1 Petro 2:12.

15 Munthu wotsutsa angakane kumvetsera mfundo iliyonse ya m’Baibulo chifukwa cha malingaliro ake olakwika kapena kunyada. Zinali choncho ndi mwamuna wina wa ku United States amene ananena kuti amakonda kwambiri dziko lake. Nthawi inayake, mkazi wake atapita kumsonkhano waukulu, anatenga zovala zake zonse ndi kuchoka panyumba. Panthawi ina, anatenga mfuti ndi kuchoka ndipo anaopseza kuti akukadzipha. Iye ankati chimene chinali kumuchititsa khalidwe lake losayenerali ndi chipembedzo cha mkazi wake. Koma mkaziyo anayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo. Patapita zaka 20 mkaziyu ali wa Mboni za Yehova, mwamuna wakeyo anakhalanso Mboni. Ku Albania mkazi wina anali wokwiya chifukwa mwana wake wamkazi anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kubatizidwa. Maulendo khumi ndi awiri, mayiwo anang’amba Baibulo la mwana wawoyo. Koma tsiku lina anatsegula Baibulo latsopano limene mwana wawoyo analisiya patebulo. Zinangochitika kuti lemba limene anatsegula linali la Mateyu 10:36, ndipo mayiwo anazindikira kuti zimene lembali likunena ndi zimene iwo akuchita. Komabe, podera nkhawa mwana wawo, mayiwo anam’perekeza kukakwera bwato pamene anali kupita ku msonkhano waukulu ku Italy limodzi ndi Mboni zina. Mayiwo ataona chikondi chimene gululo linali kusonyezana, kukumbatirana ndi kumwetulirana kwawo, komanso atamva kuseka kwawo kwachimwemwe, maganizo awo anayamba kusintha. Posapita nthawi zitachitika zimenezi, anavomera kuphunzira Baibulo. Lerolino akuyesetsa kuthandiza ena omwe poyamba amatsutsa.

16 Nthawi inayake, mwamuna wina amene anali ndi mpeni anaopseza mkazi wake ndi kumulalatira kwambiri mkaziyo atangotsala pang’ono kufika pa Nyumba ya Ufumu. Modekha mkaziyo anayankha kuti: “Tiyeni tilowe m’Nyumba ya Ufumuyi, mukadzionere nokha zimene zimachitika mmenemo.” Iye anavomera, ndipo patapita nthawi anakhala mkulu wachikristu.

17. Ndi malangizo a m’Malemba ati omwe angathandize ngati anthu asemphana maganizo m’banja lachikristu?

17 Ngakhale aliyense m’banja lanu atakhala Mkristu, nthawi zina zinthu zingavute m’banjamo ndipo anthu angalankhulane mawu opweteka chifukwa cha kupanda ungwiro. N’zochititsa chidwi kuti Akristu a ku Efeso wakale anawalangiza kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.” (Aefeso 4:31) Zikuoneka kuti Akristu a ku Efeso ankachita zosayenerazi chifukwa cha mmene zinthu zinalili kwawoko, chifukwa cha kupanda ungwiro kwawo, ndipo nthawi zina chifukwa cha moyo wawo wakale. N’chiyani chikanawathandiza kusintha? Anafunika kuti ‘akonzeke, ndi kukhala atsopano mu mzimu wa mtima wawo.’ (Aefeso 4:23) Chimene chikanawathandiza kusonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu pa moyo wawo mokulira kwambiri ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, kusinkhasinkha mmene mawuwo akukhudzira moyo wawo, kusonkhana ndi Akristu anzawo, ndi kupemphera moona mtima. Anafunika kuphunzira ‘kukhalirana okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana okha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira iwo.’ (Aefeso 4:32) Mosasamala kanthu zimene ena angatichitire, tifunika kuugwira mtima, kukhala achifundo, okoma mtima, ndi okhululukira. Inde, ‘tisabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa.’ (Aroma 12:17, 18) Nthawi zonse ndi bwino kusonyeza chikondi chenicheni potsanzira Mulungu.​—1 Yohane 4:8.

Malangizo kwa Akristu Onse

18. N’chifukwa chiyani malangizo a pa 2 Timoteo 2:24 anali a panthawi yake kwa mkulu ku Efeso wakale, nanga angapindulitse motani Akristu onse?

18 Malangizo oti ‘tiziugwira mtima pokumana ndi zoipa’ akupita kwa Akristu onse. (2 Timoteo 2:24, NW) Koma poyambapo anapita kwa Timoteo, ndipo analidi ofunika kwa iye kuti akwaniritse bwino udindo wake monga mkulu ku Efeso. Ena mu mpingo kumeneko ankalankhula mosapsatira pofotokoza maganizo awo ndipo ankaphunzitsa chiphunzitso cholakwika. Chifukwa chosamvetsa bwino cholinga cha Chilamulo cha Mose, sanazindikire kufunika kwa chikhulupiriro, chikondi, ndi chikumbumtima chabwino. Kunyada kwawo kunayambitsa mikangano ndi kutsutsana pa mawu, ndipo sanathe kuzindikira mfundo yofunika ya ziphunzitso za Kristu ndi kufunika kokhala odzipereka kwa Mulungu. Kuti athetse vuto limeneli, Timoteo anafunika kuima molimbika pa choonadi cha m’Malemba, koma panthawi imodzimodziyo kuchita mokoma mtima ndi abale akewo. Mofanana ndi akulu masiku ano, Timoteo anadziwa kuti gulu la nkhosalo silinali lake komanso kuti anafunika kuchita ndi ena m’njira yolimbikitsa chikondi chachikristu ndi umodzi.​—Aefeso 4:1-3; 1 Timoteo 1:3-11; 5:1, 2; 6:3-5.

19. N’chifukwa chiyani ‘kufuna chifatso’ kuli kofunika kwa tonsefe?

19 Mulungu akulimbikitsa anthu ake ‘kufuna chifatso.’ (Zefaniya 2:3) Mawu achihebri omwe anawamasulira kuti “chifatso” amatanthauza mtima umene umathandiza munthu kupirira zowawa moleza mtima, popanda kukhumudwa kapena kubwezera choipa. Tiyeni tipemphe moona mtima kwa Yehova kuti atithandize kuugwira mtima ndi kumuimira moyenera, ngakhale pamene zinthu zavuta.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Ndi malemba ati amene angakuthandizeni ena akakulankhulani mwachipongwe?

• N’chifukwa chiyani Saulo ankachita chipongwe?

• Kodi chitsanzo cha Yesu chikutithandiza bwanji kuchita zinthu moyenera ndi anthu onse?

• Kodi kulankhula modekha m’banja lathu kungatipindulitse motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Ngakhale kuti Saulo anali ndi mbiri yoipa, Ananiya analankhula naye mokoma mtima

[Chithunzi patsamba 29]

Chitsutso cha m’banja chingachepe Mkristu akamasamalira maudindo ake mokhulupirika

[Chithunzi patsamba 30]

Akristu amalimbikitsa chikondi ndi mgwirizano