Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumacheza Nawo Okondedwa Anu?

Kodi Mumacheza Nawo Okondedwa Anu?

Kodi Mumacheza Nawo Okondedwa Anu?

NYUZIPEPALA ina ya ku Poland, yotuluka mlungu uliwonse yotchedwa Polityka, inati: “Masiku ano anthufe tayamba kuiwala mmene tingachezere bwino ndi okondedwa athu.” Ku United States, akuti anthu okwatirana amacheza zenizeni kwa mphindi sikisi zokha basi patsiku. Akatswiri ena amaona kuti theka la mabanja amene amapatukana kapenanso kusudzulana amatero chifukwa cha kusachezera limodzi.

Nanga bwanji pankhani ya kucheza ndi ana awo? Lipoti lili pamwambali linati nthawi zambiri, “kucheza kwake kumangokhala kwa mafunso basi, monga akuti: Wayenda bwanji kusukulu? Kapenanso kuti: Anzako ali bwanji?” Ndiyeno lipotili linafunsa kuti: “Kodi choncho ana athu angaphunzire bwanji kugwirizana ndi anthu?”

Popeza kuti m’pofunika khama kuti munthu adziwe kucheza bwino ndi anzake, kodi tingatani kuti tizitha kutero? Wophunzira Yakobo anatiuza malangizo ofunikira akuti: “Munthu ali yense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” (Yakobo 1:19) Inde, kuti tithe kucheza molimbikitsana, tiyenera kumvetsera mwatcheru ndipo tisamafulumire kuwadula mawu anzathu kapena kunena maganizo athu tisanamvetsere bwinobwino nkhani yonse. Pewani kukonda kutsutsa anzanu, chifukwa mukatero macheza anuwo sangapite patali ayi. Yesutu ankafunsa mafunso mochenjera, osati kuti apanikize amene akuwafunsawo, koma kuti iwowo anene zimene zili mumtima mwawo ndi kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi iye.​—Miyambo 20:5; Mateyu 16:13-17; 17:24-27.

Mfundo zabwino za m’Baibulo zimakuphunzitsani kuyesetsa kucheza ndiponso kulankhula ndi okondedwa anu. Mukamatero mungakhale paubwenzi woti ungathe kukhala kwa zaka zambiri, mwinanso kosatha.