Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Atamva kuti Petro, yemwe anali atamangidwa, ali pakhomo, n’chifukwa chiyani ophunzira ananena kuti: “Ndiye mngelo wake”?​—Machitidwe 12:15.

Ophunzira ayenera kuti anaganiza molakwika kuti pakhomopo panafika mngelo wa Petro. Tatiyeni tione nkhani yonse imene mukupezeka mawu amenewa.

Petro anali atamangidwa ndi Herode, yemwe anali atapha Yakobo. Motero, mpake kuti ophunzirawo ankaganiza kuti Petro naye aphedwa. Petro anamangidwa unyolo ndipo ankayang’aniridwa ndi asilikali anayi panthawi iliyonse. Asilikaliwo ankasinthana kanayi tsiku lililonse ndipo analipo magulu anayi. Kenaka tsiku lina usiku, Petro anamasulidwa mozizwitsa n’kutulutsidwa m’ndendeyo ndi mngelo. Mapeto ake, Petro atazindikira zimene zinali kuchitika, anati: “Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m’dzanja la Herode.”​—Machitidwe 12:1-11.

Nthawi yomweyo Petro anapita kunyumba ya Mariya, mayi ake a Yohane Marko, kumene kunali kutasonkhana ophunzira ambiri. Atagogoda pakhomo lolowera pachipata cha nyumbayi, mtsikana wantchito, dzina lake Roda ndi amene anapita kuti akatsegule. Mtsikanayo atangozindikira mawu a Petro anathamanga kukadziwitsa anthu ena, asanam’tsegulire n’komwe Petroyo. Poyamba ophunzirawo sanakhulupirire kuti Petro anali pakhomopo. M’malo mwake iwo anaganiza molakwa kuti: “Ndiye mngelo wake.”​—Machitidwe 12:12-15.

Kodi ophunzirawo ankakhulupirira kuti Petro anali ataphedwa ndipo kuti mzimu wake ndi umene unali pakhomo la chipatapo? Ayi, sakanakhulupirira zimenezi, chifukwa ophunzira a Yesuwa ankadziwa zoona zake za anthu akufa zimene Malemba amanena, zakuti iwo “sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5, 10) Nangano kodi ophunzirawa anali kutanthauza chiyani ponena kuti: “Ndiye mngelo wake”?

Ophunzira a Yesu ankadziwa kuti m’mbuyo monsemo, angelo ankathandiza anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, Yakobo ananenapo kuti ‘mthenga [kapena kuti mngelo] anandiombola ine ku zoipa zonse.’ (Genesis 48:16) Ndipo nthawi ina Yesu anatenga mwana n’kuuza ophunzira ake kuti: “Yang’anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.”​—Mateyu 18:10.

N’zochititsa chidwi kuti Baibulo la Young’s Literal Translation of the Holy Bible limamasulira mawu akuti aggelos (“mngelo”) omwe ali m’lembali kuti “mthenga.” Zikuoneka kuti Ayuda ena ankakhulupirira kuti mtumiki aliyense wa Mulungu anali ndi mngelo wakewake, amene kwenikweni anali “mngelo wom’teteza.” Inde, zimenezi sikuti kwenikweni zimaphunzitsidwa m’Mawu a Mulungu. Komabe, n’zotheka kuti pamene ophunzirawo ananena kuti, “ndiye mngelo wake,” ankaganiza kuti pakhomopo panafika mngelo wa Petro.