Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ananu, Tamandani Yehova!

Ananu, Tamandani Yehova!

Ananu, Tamandani Yehova!

“Lemekezani [“Tamandani,” NW] Yehova kuchokera ku dziko lapansi, . . . Anyamata ndiponso anamwali.”​—SALMO 148:7, 12.

1, 2. (a) Kodi ana ambiri amadziwa za malire otani amene makolo awo amawaikira? (b) N’chifukwa chiyani ana sayenera kunyansidwa ndi malire amene makolo awo amawaikira?

KAWIRIKAWIRI ana osinkhukirapo amadziwa bwino zimene saloledwa kuchita. Ambiri angathe kukuuzani bwinobwino kuti akadzafika zaka zakutizakuti, aziloledwa kulumpha msewu okha, kusapita msanga kokagona, kapena kuyendetsa galimoto. Nthawi zina, mwana angaone ngati pa zambiri zimene amapempha mofunitsitsa, yankho limangokhala lakuti, “Dikira ukuleko kaye.”

2 Ananu, dziwani kuti makolo anu amaona kuti ndi chinthu chanzeru kukuikirani malire oterowo, pofuna kukutetezani. Inunso mumadziwa kuti Yehova amakondwera mukamamvera makolo anu. (Akolose 3:20) Kodi mumaona ngati moyo wanu weniweni usanayambe? Kodi ndi zinthu zonse zofunika zimene amakuletsani mpaka mudzakule? Zimenezo sizoona konse! Panopo pali ntchito imene ikuchitika yofunika kwambiri kuposa ufulu uliwonse umene mungakhale mukuuyembekezera. Kodi ananu ndinu ololedwa kugwira nawo ntchito imeneyo? Simuli ololedwa chabe, komanso Mulungu Wam’mwambamwamba mwiniyo akukupemphani kuti mugwire nawo ntchitoyo!

3. Ndi mwayi uti umene Yehova wapereka kwa ana, ndipo ndi mafunso ati amene tiwapende tsopano?

3 Kodi tikunena za ntchito yanji? Taonani lemba la mutu wa nkhani ino. Mawu ake akuti: “Lemekezani [“tamandani”] Yehova kuchokera ku dziko lapansi, . . . Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana.” (Salmo 148:7, 12) Umenewu ndi mwayi wanu waukulu kwambiri, inde, mwayi wa kutamanda Yehova. Monga wachichepere, kodi simungakonde kugwira nawo ntchito imeneyi? Ambiri akutero. Kuti muone chifukwa chake kuli kofunika kukhala ndi maganizo amenewo, tiyeni tipende mafunso atatu. Loyamba, n’chifukwa chiyani muyenera kutamanda Yehova? Lachiwiri, kodi mungachite chiyani kuti mum’tamande mogwira mtima? Lachitatu, kodi muyenera kuyamba liti kutamanda Yehova?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kutamanda Yehova?

4, 5. (a) Malinga n’kunena kwa Salmo la 148, kodi ifeyo timaziposa motani zinazo? (b) Kodi zolengedwa zimene sizitha kulankhula kapena kuganiza zimathabe motani kutamanda Yehova?

4 Chifukwa choposa zonse chotamandira Yehova n’chakuti iye ndi Mlengi wathu? Salmo la 148 limatithandiza kulunjikitsa maganizo anthu pa mfundo imeneyi. Tangoganizani! Kodi mungamve bwanji mutapeza khamu la anthu amene akuimba mwanthetemya nyimbo yokoma ndi yokhudza mtima? Bwanji ngati nkhani imene akuimba m’nyimboyo mumaidziwa kuti ndi yoona, ndipo akutchula mfundo zimene mukudziwa kuti n’zofunika, zosangalatsa, komanso zolimbikitsa? Kodi simungalakalake mutaiphunzira nyimboyo ndi kuimba nawo? Ambiri tingatero. Eya, Salmo la 148 limasonyeza kuti mukhoza kuchita zosangalatsa kuposa pamenepo. Salmo limeneli limalongosola za makamu, amene onse akulemekeza Yehova mogwirizana. Komabe, pamene mukuwerenga salmolo mungazindikire chinthu china chodabwitsa. N’chiyani chimenecho?

5 Makamu ambiri omwe akutchulidwa mu Salmo 148 kuti akum’lemekeza Yehova satha kulankhula kapena kuganiza. Mwachitsanzo, timawerenga za dzuwa, mwezi, nyenyezi, mphepo, mapiri, ndi zitunda kuti zimalemekeza Yehova. Kodi zachilengedwe zimenezi zopanda moyo zingathe bwanji kuchita zimenezo? (Mavesi 389) Kwenikweni, zimatero m’njira imene imachitiranso mitengo, zolengedwa za m’nyanja, ndi zinyama. (Mavesi 7910) Kodi munaonapo maonekedwe okongola a kulowa kwa dzuwa, kapena mwezi wathunthu ukudutsa kumwamba kodzala nyenyezi? Kodi munayamba mwasekapo poona mmene nyama zina zikusewerera, kapena kusangalatsidwa ndi kukongola kwa malo? Ngati munatero ndiye kuti ‘munamvapo’ chilengedwe chikuimba nyimbo yachitamando. Zonse zimene Yehova analenga zimatikumbutsa kuti iye ndi Mlengi wamphamvu, kuti palibe wina m’chilengedwe chonse angakhale wamphamvu, wanzeru, kapena wachikondi mofanana naye.​—Aroma 1:20; Chivumbulutso 4:11.

6, 7. (a) Kodi Salmo la 148 limanena za zolengedwa zanzeru ziti kuti zimalemekeza Yehova? (b) N’chifukwa chiyani sitingachitire mwina koma kum’tamanda Yehova? Fotokozani fanizo.

6 Salmo la 148 limanenanso kuti zolengedwa zanzeru nazonso zimalemekeza Yehova. Vesi 2, limanena za “makamu” a Yehova akumwamba, amene ndi angelo, kuti amalemekeza Mulungu. M’vesi 11, anthu amphamvu ndi audindo, ngati mafumu ndi oweruza, akupemphedwa kuti agwirizane nawo m’kulemekezako. Ngati angelo amphamvuwo amasangalala ndi kutamanda Yehova, kodi munthu wamba ndani kuti aganize zoti sangafunikire kutero? Ndiyeno m’mavesi 12 ndi 13, achicheperenu mukupemphedwa kuti inunso mum’lemekeze Yehova. Kodi mtima wanu ukufunadi kutero?

7 Taganizirani chitsanzo ichi. Tinene kuti munali ndi mnzanu wa luso linalake lapadera kwambiri, kaya ndi m’masewero, zojambulajambula, kapena kuimba. Kodi mukanauzako achibale anu kapena anzanu za iye? Mosakayika konse. Inde, tikhoza kuchita chimodzimodzi tikadziwa zonse zimene Yehova anachita. Mwachitsanzo, Salmo 19:1, 2 limanena kuti nyenyezi zakumwamba ‘zichulukitsa mawu.’ Koma ife, tikaganizira zinthu zodabwitsa zimene Yehova wachita, sitingachitire mwina koma kuuzako ena za Mulungu wathu.

8, 9. Kodi ndi zifukwa ziti zimene Yehova amafunira kuti tim’tamande?

8 Chifukwa china chachikulu chotamandira Yehova n’chakuti iye amafuna kuti tizitero. Chifukwa chiyani? Kodi n’chifukwa chakuti moyo wake umadalira anthu kum’tamanda? Ayi. Anthufe nthawi zina moyo wathu ungadalire anthu ena kutitamanda, koma Yehova ndi wokwezeka kuposa ife. (Yesaya 55:8) Palibe chosatsimikizirika ponena za iye kapena makhalidwe ake. (Yesaya 45:5) Komabe, iye amafuna kuti ife tim’tamande ndipo amakondwera tikamatero. Chifukwa chiyani? Taganizirani zifukwa ziwiri zotsatirazi. Choyamba, iye amadziwa kuti moyo wathu umadalira kum’tamanda iye. Iye anatilenga ndi chibadwa chofuna zauzimu, chofuna kupembedza. (Mateyu 5:3) Choncho, Yehova akamationa tikuchita zinthu zauzimu amasangalala kwambiri, ngati mmene makolo anu amasangalalira akamakuonani mukudya chakudya chopatsa thanzi.​—Yohane 4:34.

9 Chachiwiri, Yehova amadziwa kuti anthu ena moyo wawo umadalira kuti atimve ifeyo tikumutamanda. Mtumwi Paulo analembera Timoteo wachinyamatayo kuti: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Inde, pamene muphunzitsa ena za Yehova Mulungu, kumene ndiko kum’tamanda, iwonso angafike podziwa Yehova. Akadziwa za iye zingawathandize kudzapulumuka ndi kupeza moyo wosatha.​—Yohane 17:3.

10. N’chifukwa chiyani mtima wathu umafunitsitsa kutamanda Mulungu?

10 Palinso chifukwa china chom’tamandira Yehova. Kumbukirani chitsanzo chija cha mnzanu waluso. Ngati inuyo mungamve ena akunena zabodza zokhudza mnzanuyo, akumaipitsa dzina lake, kodi sindiye pamene mungafune kum’tamanda kwambiri? Ndi mmene zilili kwa Yehova. Anthu amam’nenera zoipa zambiri padziko lapansi. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) Choncho amene amam’konda sangachitire mwina koma kunena zoona za iye, kuti akonze chithunzi cholakwikacho. Kodi inunso mungakonde kusonyeza kuti Yehova mumam’konda ndi kum’yamikira? Kodi mungakonde kusonyeza kuti mumafuna iye kukhala Wolamulira wanu, osati mdani wake wamkulu uja, Satana? Mukhoza kuchita zonsezo mwa kutamanda Yehova. Koma funso n’lakuti, kodi mungam’tamande motani?

Mmene Ana Ena Anatamandira Yehova

11. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zosonyeza kuti achichepere akhoza kum’tamanda Yehova mogwira mtima?

11 Baibulo limasonyeza kuti achichepere kawirikawiri amatamanda Yehova mogwira mtima ndithu. Mwachitsanzo, panali mtsikana wachiisrayeli amene Aaramu anam’tengera kwawo ngati kapolo. Iye molimba mtima anachitira umboni za Elisa mneneri wa Yehova kwa dona wake. Mawu ake anapangitsa kuti pachitike chozizwitsa, ndipo umboni wamphamvu unaperekedwa. (2 Mafumu 5:1-17) Yesunso anachitira umboni molimba mtima ali mwana. Pa zochitika zonse ali wachichepere zimene zikanalembedwa m’Malemba, Yehova anasankhapo chimodzi. Chochitikacho n’chakuti, pamene Yesu anali ndi zaka 12, molimba mtima anafunsa mafunso aphunzitsi achipembedzo pakachisi ku Yerusalemu. Iwo anazizwa naye chifukwa cha kuzindikira kwake njira za Yehova.​—Luka 2:46-49.

12, 13. (a) Kodi Yesu anachita chiyani m’kachisi imfa yake itayandikira, ndipo anthuwo analabadira motani? (b) Kodi Yesu anakhudzidwa motani ndi mawu otamanda a ana?

12 Yesu atakula, analimbikitsanso ana kutamanda Yehova. Mwachitsanzo, imfa yake itayandikira, Yesu anali kupezeka pakachisi ku Yerusalemu. Baibulo limati anachita “zozizwitsa” kumeneko. Anathamangitsa anthu omwe anasandutsa malo opatulikawo kukhala ngati phanga la achifwamba. Anachiritsanso akhungu ndi olemala. Aliyense kumeneko, makamaka atsogoleri achipembedzo, anayenera kukhudzika mtima ndi kutamanda Yehova ndi Mwana wake, Mesiyayo. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, ambiri panthawiyo sanawatamande. Iwo anadziwa kuti Yesu anatumidwa ndi Mulungu, koma anaopa atsogoleri achipembedzo. Komabe, panali kagulu kena kamene kanalankhula mopanda mantha. Mukudziwa kuti kanali kagulu kati? Baibulo limati: “Ansembe aakulu ndi alembi, mmene anaona zozizwitsa zomwe iye [Yesu] anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima, nanena kwa iye [Yesu], Mulinkumva kodi chimene alikunena awa?”​—Mateyu 21:15, 16; Yohane 12:42.

13 Ansembewo anayembekezera kuti Yesu auza anawo omwe anali kum’tamanda kuti akhale chete. Kodi n’zimene anachita? Kutalitali! Powayankha ansembewo, Yesu anati: “Inde: simunawerenga kodi, M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?” Mwachionekere, Yesu limodzi ndi Atate wake anakondwera ndi mawu otamanda a anawo. Ana amenewo anachita zimene achikulire onse kumeneko anayenera kuchita. Ngakhale anali ana, m’maganizo mwawo mfundo imeneyo inali yoonekera bwino lomwe. Iwo anali ataona mwamuna ameneyu akuchita zinthu zozizwitsa, akulankhula molimba mtima ndi mwa chikhulupiriro, ndi kusonyeza chikondi champhamvu kwa Mulungu ndi anthu ake. Iye analidi “Mwana wa Davide” wolonjezedwa ndiponso Mesiya, mogwirizana ndi zomwe mwiniwakeyo anali kunena. Monga dalitso la chikhulupiriro chawo, anawo anakhala ndi mwayi wokwaniritsa ulosi.​—Salmo 8:2.

14. Kodi mphatso zimene achichepere ali nazo zingawathandize motani kutamandira Mulungu?

14 Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zitsanzo zimenezi? Tingaphunzirepo mfundo yakuti ana ang’onoang’ononso akhoza kutamanda Yehova mogwira mtima. Iwo kawirikawiri amakhala ndi mphatso yoona choonadi mmene chakhalira ndiponso mosavuta. Amalankhula za chikhulupiriro chawo ndi mtima wonse komanso mwachangu. Alinso ndi mphatso yotchulidwa pa Miyambo 20:29 kuti: “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo.” Inde, achicheperenu muli ndi nyonga, zimene ndi chuma chenicheni chotamandira Yehova. Koma kodi mphatso zimenezi mungazigwiritse ntchito motani?

Kodi Mungamutamande Motani Yehova?

15. Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kutamanda Yehova mochokera mu mtima?

15 Kutamanda Yehova zenizeni kumayambira mu mtima. N’zosatheka kutamanda Yehova mochokera mu mtima ngati mukuchita zimenezo chabe chifukwa chakuti ena akufuna kuti mutero. Kumbukirani kuti lamulo lalikulu pa malamulo onse ndi lakuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Kodi kuphunzira kwanu Mawu ake kwakuthandizani kum’dziwa bwinobwino Yehova? Zotsatira za kuphunzira koteroko n’zakuti mumafika pom’konda Yehova. Njira yachibadwa yosonyezera chikondicho ndi mwa kum’tamanda. Mukakhala ndi cholinga chabwino ndiponso cholimba, mumam’tamanda Yehova mosangalala.

16, 17. Kodi khalidwe la munthu lingathandize motani pa kutamanda Yehova? Fotokozani chitsanzo.

16 Tsopano, musanaganize n’komwe zimene muyenera kunena, ganizirani zimene muyenera kuchita. Kodi mukuganiza kuti mtsikana wachiisrayeli uja wa m’masiku a Elisa akanakhala wamwano, wopanda ulemu, kapena wosaona mtima, Aaramu amene anam’tenga ukapolo aja akanamvetsera zimene ananena za mneneri wa Yehova? N’zokayikitsa. Mofananamo, anthu amamvetsera msanga ngati aona kuti ndinu waulemu, woona mtima, ndi wa khalidwe labwino. (Aroma 2:21) Taganizirani chitsanzo chotsatirachi.

17 Mtsikana wina wazaka 11 wa ku Portugal anali kuumirizidwa ku sukulu kuti achite nawo maholide osemphana ndi chikumbumtima chake chophunzira Baibulo. Iye anafotokozera mphunzitsi wake mwaulemu chimene anakanira, koma mphunzitsiyo anamuseka. M’kupita kwa masiku, mphunzitsi uja anayesanso mobwerezabwereza kuti achititse manyazi mtsikanayo, akumatonza chipembedzo chake. Komabe, mtsikanayo anakhalabe waulemu. Patapita zaka, mlongo wachitsikanayo anakhala mpainiya wokhazikika, mtumiki wa nthawi zonse. Pamsonkhano wachigawo, anakaonerera anthu obatizidwa ndipo anazindikirapo mmodzi. Ha! anangoona ndi mphunzitsi wake uja. Atakumbatirana ndi misozi, mzimayi wachikulireyo anauza wachitsikanayo kuti sanaiwale konse za khalidwe lake laulemu panthawi imene anali wophunzira wake. Mboni inafika pakhomo pake, ndipo mphunzitsiyo anaifotokozera za khalidwe la mtsikana wina yemwe anali wophunzira wake pasukulu. Kenako phunziro la Baibulo linayambika, ndipo mzimayiyo analandira choonadi cha m’Baibulo. Inde, khalidwe lanu lingakhale njira yamphamvu yotamandira Yehova!

18. Kodi wachichepere angachite chiyani ngati akudodoma kuyambitsa makambirano okhudza Baibulo ndi Yehova Mulungu?

18 Kodi nthawi zina zimakuvutani kuyambitsa makambirano ndi ena ku sukulu okhudza chikhulupiriro chanu? Si muli nokha amene mumamva choncho. Komabe, mukhoza kupangitsa anthu ena kukufunsani za chikhulupiriro chanu. Mwachitsanzo, ngati malamulo amalola ndipo n’zololeka pasukulu panu, bwanji osanyamulako mabuku ophunzirira Baibulo ndi kumawawerenga nthawi yopuma masana, kapena panthawi zina pamene kuli kololeka kutero? Anzanu apasukulu angakufunseni za zimene mukuwerenga. Powayankha ndi kuwauza zimene zakusangalatsani m’nkhaniyo kapena bukulo, mungangoona kuti muli kale m’kati mwa makambirano osangalatsa. Kumbukirani kufunsa mafunso, kuti mudziwe zimene ophunzira anzanu amakhulupirira. Mvetserani mwaulemu, ndipo afotokozereni zimene mumaphunzira m’Baibulo. Monga zikusonyezera zokumana nazo za pa tsamba 29, achichepere ambiri akutamanda Mulungu ku sukulu. Zimenezi zimawapatsa chisangalalo chachikulu ndipo zimathandiza ambiri kum’dziwa Yehova.

19. Kodi achichepere angasule bwanji luso lawo mu ulaliki wa khomo ndi khomo?

19 Ulaliki wa khomo ndi khomo ndiyo njira yogwira mtima koposa yom’tamandira Yehova. Ngati simunayambe ulaliki umenewo, bwanji osakhala ndi cholinga chimenecho? Ngati mumatenga nawo mbali kale, kodi pali zolinga zinanso zimene mungadziikire? Mwachitsanzo, m’malo momanena mawu amodzimodzi pakhomo lililonse, yesani kupeza njira zina zosulira luso lanu. Mungafunse makolo anu kapena ena ozolowera kuti akupatseni maganizo othandiza. Phunzirani kugwiritsa ntchito Baibulo kwambiri, kupanga maulendo obwereza ogwira mtima, ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo. (1 Timoteo 4:15) Mukawonjezera kum’tamanda Yehova mwa njira zimenezi, mudzasulanso luso lanu kwambiri, ndipo utumiki wanu mudzasangalala nawo koposa.

Kodi Muyenera Kuyamba Liti Kutamanda Yehova?

20. N’chifukwa chiyani achichepere sayenera kuona kuti akali aang’ono kuti atamande Yehova?

20 Pa mafunso atatu m’nkhani ino, yankho la funso lomalizirali ndilo losavuta. Taonani yankho lachindunji la m’Baibulo: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 12:1) Inde, nthawi yoyamba kutamanda Yehova ndi panopo. Mungafulumire kunena kuti: “Ndikali wamng’ono kuti nditumikire Yehova. Sindikudziwa chilichonse. Ndidikire kaye ndikuleko.” Sindinu woyamba kukhala ndi maganizo amenewo. Mwachitsanzo, Yeremiya akali wamng’ono anauza Yehova kuti: “Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithayi kunena pakuti ndili mwana.” Koma Yehova anam’tsimikizira kuti asachite mantha m’pang’ono pomwe. (Yeremiya 1:6, 7) Ifenso n’chimodzimodzi. Sitiyenera kuopa chilichonse potamanda Yehova. Palibe choipa chimene chingatigwere chimene Yehova sangachotse kotheratu.​—Salmo 118:6.

21, 22. N’chifukwa chiyani achichepere otamanda Yehova akuyerekezedwa ndi mame, ndipo kuyerekezako n’kolimbikitsa chifukwa chiyani?

21 Choncho, tikukulimbikitsani ananu, musazengereze kum’tamanda Yehova! Pamene mukali aang’ono, ndiyo nthawi yabwino koposa yogwira nawo ntchito yofunika kwambri yomwe ikuchitika padziko lapansi lerolino. Mukatero, mudzakhala nawo m’gulu losangalatsa kwambiri, banja la m’chilengedwe chonse la otamanda Yehova. Yehova adzakondwa kwambiri ngati inunso mukhala nawo m’banja limeneli. Taonani mawu ouziridwawa amene wamasalmo ananena kwa Yehova: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M’moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nawo mame a ubwana wanu.”​—Salmo 110:3.

22 Mame onyezimira ndi kuwala kwa dzuwa la m’mawa amaoneka okongola kwabasi, si choncho kodi? Nyezinyezi wakeyo amasangalatsa zedi ndipo mamewo sawerengeka. Ndi mmenetu Yehova amakuonerani ananu amene mumam’tamanda mokhulupirika m’masiku ovuta ano. Mwachionekere, kusankha kwanu kum’tumikira kumakondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Choncho, ananu, chitani chilichonse chotheka kuti mutamande Yehova!

Kodi Mungayankhe Kuti Chiyani?

• Kodi zifukwa zina zofunika zotamandira Yehova ndi ziti?

• Kodi pali zitsanzo zotani za m’Baibulo zosonyeza kuti achichepere angathe kutamanda Yehova mogwira mtima?

• Kodi ana angatamande Yehova motani masiku ano?

• Kodi ana ayenera kuyamba liti kutamanda Yehova, ndipo chifukwa chiyani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 25]

Ngati mungakhale ndi mnzanu waluso lapadera, kodi simungamauzeko ena za luso lakelo?

[Chithunzi patsamba 27]

Ophunzira anzanu angafune kudziwa za chikhulupiriro chanu

[Chithunzi patsamba 28]

Ngati mungafune kusula luso lanu la kulalikira, funsirani maganizo kwa Mboni yozolowera