Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Dziko Limene Kale Chikristu Chinali Kuyenda Bwino

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Dziko Limene Kale Chikristu Chinali Kuyenda Bwino

Ntchito Yolalikira Ikupita Patsogolo ku Dziko Limene Kale Chikristu Chinali Kuyenda Bwino

ITALY ndi chilumba chooneka ngati nsapato pa nyanja ya Mediterranean. Chilumbachi chakhala malo amene akhudza kwambiri zochitika zachipembedzo ndiponso zachikhalidwe m’mbiri yadziko. Chilumba chimenechi chimakopa alendo ambirimbiri obwera kudzaona malo. Anthu amakopeka ndi kukongola kwa malo ake osiyanasiyana, zojambula zake zotchuka, ndiponso maphikidwe a zakudya zokhesa dovu. Pa chilumba chimenechinso maphunziro a Baibulo akuyenda bwino.

Mwina Chikristu Choona chinayamba kufika ku Roma pamene Ayuda ndi anthu olowa chiyuda amene anakhala Akristu pa Pentekoste 33 C.E., anabwerera kwawo kuchokera ku Yerusalemu. Mzinda wa Roma umenewu unali likulu la ulamuliro wa mphamvu padziko lonse. Pafupifupi 59 C.E., mtumwi Paulo anapita ku Italy kwa nthawi yoyamba. Mu mzinda wa Puteoli womwe unali m’mbali mwa nyanja, iye‘anapeza abale’ m’chikhulupiriro.​—Machitidwe 2:5-11; 28:11-16.

Monga mmene Yesu ndi atumwi ake analoserera, magulu ampatuko anachoka m’Chikristu choona pang’ono ndi pang’ono. Zimenezi zinachitika zaka 100 zoyambirira zisanathe. Koma mapeto a dongosolo loipali asanafike, ophunzira oona a Yesu akupititsa patsogolo ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse ngakhale ku Italy.​—Mateyu 13:36-43; Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3-8; 2 Petro 2:1-3.

Chiyambi Chosalimbikitsa

Mu 1891, Charles Taze Russell, amene anali kutsogolera ntchito yolalikira padziko lonse ya Mboni za Yehova (omwe panthawiyo ankatchedwa Ophunzira Baibulo), kwa nthawi yoyamba anapita ku mizinda ina ya ku Italy. Iye anavomera kuti ulaliki wake kumeneko sunakhale ndi zipatso zolimbikitsa, ndipo anati: “Sitinaone chilichonse chimene chikanatilimbikitsa kuyembekezera zotuta zilizonse ku Italy.” M’nyengo yachilimwe mu 1910, Mbale Russell anabwerera ku Italy ndipo anakamba nkhani ya Baibulo m’holo yochitiramo masewero yomwe inali pakati pa mzinda wa Rome. Kodi zotsatira zinali zotani? Iye anati: “Msonkhano wonsewo unali wokhumudwitsa.”

Ndipotu, kwa zaka zambiri zoyambirira, ulaliki wa uthenga wabwino ku Italy sunali kupita patsogolo kwenikweni. Izi zinali choncho chifukwa choti Mboni za Yehova zinali kuzunzidwa ndi olamulira ankhanza achifasizimu. Panthawi imeneyo, Mboni za Yehova m’dzikolo zinalipo 150 zokha. Ambiri anali aja amene anaphunzira choonadi cha Baibulo kwa achibale awo kapena anzawo omwe anali kukhala ku mayiko ena.

Kupita Patsogolo Kochititsa Chidwi

Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, amishonale ambiri anawatumiza ku Italy. Koma monga momwe makalata opezeka m’nyumba ya Boma yosungiramo zinthu zakale anasonyezera, anthu ena amaudindo aakulu ku Vatican anapempha boma kuthamangitsa amishonale. Amishonale analamulidwa kuchoka m’dzikolo, kusiyapo ochepa chabe.

Ngakhale kuti panali zopinga, anthu ambiri ku Italy anayamba kukwera ku “phiri” la kulambira kwa Yehova. (Yesaya 2:2-4) Mboni zinawonjezeka modabwitsa kwambiri. M’chaka cha 2004, chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa uthenga wabwino chinali 233,527. Zimenezi zinatanthauza kuti wofalitsa aliyense m’dzikolo anali ndi anthu 248 owalalikira. Ndipo amene anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu anali 433,242. Panali mipingo ya Mboni za Yehova yokwana 3,049 imene inali kusonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino.

Kulalikira M’zilankhulo Zambiri

Posachedwapa, magulu ena a anthu awonjezeka kwambiri. Anthu ambiri ochokera ku Africa, Asia, ndi Eastern Europe amapita ku Italy kukafuna ntchito kapena moyo wabwino. Ena nthawi zina, amathawa mavuto. Kodi anthu ambirimbiriwa angathandizidwe bwanji mwauzimu?

Mboni zambiri ku Italy zadzipereka kuti ziphunzire zilankhulo zovuta monga Chialubaniya, Chiamhariki, Chiarabu, Chibengali, Chipunjabu, Chisinhala, Chitagalogo ndi Chitchayina. Kuyambira m’chaka cha 2001, maphunziro azilankhulo anakhazikitsidwa ophunzitsa anthu ofunitsitsawa kuti azilalikira m’zilankhulo za kwina. Pa zaka zitatu zapitazi, Mboni zokwana 3,711 zinachita nawo maphunziro 79 omwe anachitika m’zilankhulo 17 zosiyanasiyana. Zimenezi zathandiza kukhazikitsa ndi kulimbikitsa mipingo yokwanira 146 ndi timagulu 274 m’zilankhulo 25 zosiyanasiyana. Chotero, anthu ambiri amaganizo abwino amva uthenga wabwino ndipo ayamba kuphunzira Baibulo. Nthawi zambiri zotsatira zimakhala zodabwitsa.

Mtumiki wa Mboni za Yehova analankhula za Baibulo ndi George, amene amalankhula Chimalayalamu ndipo kwawo ndi ku India. Ngakhale kuti George anali ndi mavuto ku ntchito, iye mosangalala anavomereza kuphunzira Baibulo. Patapita masiku ochepa, Gil mnzake wa George, amene chilankhulo chake ndi Chipunjabi ndipo kwawo ndi ku India, anapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Gil, yemwe chilankhulo chake ndi Chitelugu ndipo kwawo ndi ku India, anabweretsa David kwa Mboni. Sipanapite nthawi yaitali, David anayamba kuphunzira Baibulo. Amuna ena awiri a ku India, Sonny ndi Shubash, anali kukhala m’nyumba imodzi ndi David. Onse awiri anayamba kuphunzira Baibulo.

Patapita milungu ingapo, Mbonizo zinalandira foni kuchokera kwa Dalip, yemwe chilankhulo chake ndi Chimarathi. Iye anati: “Ndine mnzake wa George. Kodi n’kutheka kuti mungandiphunzitse Baibulo?” Ndiyeno, Sumit yemwe chilankhulo chake ndi Chitamil nayenso anafuna kuphunzira Baibulo. Panthawi inanso, mnzake wina wa George anayimba foni, kupempha phunziro la Baibulo. Ndiyeno, George anabweretsa mwamuna wina wachinyamata dzina lake, Max, ku Nyumba ya Ufumu. Iyenso anafuna kuphunzira Baibulo. Panopo, anthu okwana sikisi akuphunzira Baibulo ndipo akukonza zoti ena anayi ayambe kuphunzira. Maphunziro amenewa amachitika m’Chingelezi, ngakhale kuti zofalitsa za m’Chihindi, Chimalayam, Chimarathi, Chipunjabi, Chitamil, Chitelugu, ndi Chiurdu zimagwiritsidwanso ntchito.

Ogontha “Amva” Uthenga Wabwino

Ku Italy kuli anthu ogontha oposa 90,000. Pakati pa ma 1970, Mboni zinayamba kuganizira zophunzitsa Baibulo anthu amenewa. Poyamba, Mboni zina zogontha zinali kuphunzitsa chilankhulo chamanja cha ku Italy kwa atumiki anzawo amene anali ofunitsitsa kuthandiza m’gawo limenelo. Ndiyeno anthu ogontha ambiri anayamba kuchita chidwi ndi Baibulo. Lero, anthu oposa 1400 omwe amagwiritsa ntchito chilankhulo chamanja cha ku Italy akufika pamisonkhano yachikristu. Mipingo yokwana 15 ndi timagulu 52 amachita misonkhano m’chilankhulo chamanja cha ku Italy.

Poyamba, kulalikira anthu ogontha kunadalira kwambiri njira imene Mboni iliyonse payokha inagwiritsa ntchito. Koma mu 1978, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Italy inayamba kulinganiza misonkhano yaikulu ya ogontha. M’mwezi wa May chaka chimenecho, analengeza kuti pamsonkhano wa mayiko wotsatira ku Milan, padzakhala zigawo za ogontha. Msonkhano wadera woyamba wa ogontha unachitikira pa Nyumba ya Msonkhano ku Milan mu February chaka cha 1979.

Kuyambira nthawi imeneyo, ofesi yanthambi yaonetsetsa kuti izigawira chakudya chauzimu kwa anthu ogontha. Yachita zimenezo mwa kulimbikitsa alaliki ambiri kupititsa patsogolo luso lawo la chilankhulo chimenechi. Kuyambira chaka cha 1995, apainiya apadera (alaliki anthawi zonse) anawatumiza ku timagulu tina kuti akaphunzitse Mboni zogontha utumiki ndiponso kulinganiza misonkhano yachikristu. Nyumba za Misonkhano zitatu zili ndi makina avidiyo amphamvu kwambiri kuti azionetsa bwino mapulogalamu. Ndiponso makaseti a vidiyo alipo kuti anthu ogontha akhale ndi chakudya chauzimu.

Anthu ena aona kuti Mboni zimasamalira bwino kwambiri zosowa zauzimu za anthu ogontha. Magazini ya anthu ogontha, (P@role & Segni), yofalitsidwa ndi bungwe la anthu ogontha ku Italy, inagwira mawu kalata yomwe inatumizidwa ndi wansembe wamkulu wa Katolika. Ndipo inati: “Kukhala wogontha n’kovuta kwambiri chifukwa choti nthawi zonse munthu wogontha amafunika kum’samalira. Mwachitsanzo, amafika ku tchalitchi yekha popanda vuto, koma afunika wom’thandiza kumasulira kuti athe kutsatira zonse zimene zikuwerengedwa, kukambidwa, kapena nyimbo zoyimbidwa pamsonkhanopo. Wansembeyu akuvomereza kuti n’zomvetsa chisoni kuti, tchalitchi si chokonzeka kusamalira vuto limeneli. Ananenanso kuti anthu ogontha ambiri amasamalidwa bwino kwambiri ku Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova kuposa anthu a mu tchalitchi yathu.”

Uthenga Wabwino Unalalikidwa kwa Akaidi

Kodi n’zotheka kuti munthu angakhale womasuka pamene ali m’ndende? Inde, chifukwa choti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu ‘yomasula’ aja amene amawalandira ndi kuwagwiritsa ntchito pamoyo wawo. Uthenga umene Yesu analengeza kwa “am’nsinga” unali kuwamasula ku tchimo ndi chipembedzo chonyenga. (Yohane 8:32; Luka 4:16-19) Ku Italy, ntchito yolalikira ku ndende yabweretsa mapindu abwino koposa. Pafupifupi atumiki 400 a Mboni za Yehova anavomerezedwa ndi Boma kuti azichezera akaidi n’cholinga chopereka thandizo lauzimu. Pa mabungwe omwe sali a Katolika, a Mboni za Yehova anali oyamba kupempha ndi kuvomerezedwa.

Uthenga wa Baibulo ungafalitsidwe m’njira zosayembekezeka. Akaidi amalankhula kwa akaidi anzawo za ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi, akaidi ena apempha kuti mtumiki wa Mboni aziwayendera. Kapena achibale omwe ayamba kuphunzira Baibulo amalimbikitsa akaidi amenewa kupempha wa Mboni kuwayendera. Akaidi ena omwe analamulidwa kukhala m’ndende moyo wawo wonse chifukwa chopha munthu kapena milandu ina yaikulu, alapa ndipo asintha kwambiri miyoyo yawo. Zimenezi zawathandiza kuti adzipereke kwa Yehova Mulungu ndi kubatizidwa.

M’ndende zingapo, anakonza zakuti azikamba nkhani za onse zokhudza mfundo za m’Baibulo, kuchita Chikumbutso cha imfa ya Yesu ndiponso kusonyeza mavidiyo kaseti a nkhani za Baibulo opangidwa ndi Mboni za Yehova. Nthawi zambiri akaidi ambiri amafika pamisonkhano imeneyi.

Kuti Mboni zithandize akaidi mogwira mtima, zinafalitsa kwambiri magazini okhudza nkhani zimene akaidiwo anaona kuti n’zowathandiza. Magazini imodzi yotero inali Galamukani! ya May 8, 2001, imene inafotokoza nkhani yakuti, “Kodi Akaidi Angatheke Kuwasintha?” Galamukani! ya April 8, 2003, inali ndi nkhani yakuti, “Mungatani Ngati Mwana Wanu Anayamba Mankhawala Osokoneza Bongo?” Magazini amenewa okwanira zikwi zingapo anawagawira kwa akaidi. Chifukwa cha zimenezi, akaidi mazana angapo akuphunzira Baibulo. Ndipo alonda a ndende enanso anachita chidwi ndi uthenga wa Baibulo.

Atavomerezedwa mwapadera ndi akuluakulu a ndende, mkaidi wotchedwa Costantino anabatizidwa m’Nyumba ya Ufumu ku San Remo. Mboni za kumeneko zokwana 138 zinapezekapo. Ubatizo utatha, Constantino anakhudzidwa kwambiri ndipo anati: “Ndinaona kuti anandisonyeza chikondi kwambiri.” Nyuzipepala ya kumaloko inali ndi mawu amene woyang’anira ndende ananena. Iyo inati: “Tinapereka chilolezo chimenechi . . . ndi chisangalalo chachikulu. Chilichonse chimene chingathandize akaidi kusintha kuti azitha kuyanjana bwino ndi anthu, kukhala ndi umunthu ndiponso uzimu wabwino chiyenera kuloledwa.” Mkazi wa Constantino ndi mwana wake wamkazi anasangalala kwambiri kuona mmene kudziwa Baibulo molongosoka kunakhudzira moyo wa Constantino. Iwo anati: “Tikunyadira chifukwa cha kusintha kumene apanga. Iwo akukhala mwamtendere ndipo akutidera nkhawa kwambiri. Tayambiranso kuwadalira ndiponso kuwalemekeza.” Iwonso anayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu.

Sergio, amene anapezeka ndi mlandu wakuba ndi mfuti, kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo, ndi kupha munthu analamulidwa kukhala m’ndende mpaka chaka cha 2024. Ataphunzira malemba zaka zitatu ndi kusintha kwambiri moyo wake, Sergio anasankha kubatizidwa. Iye anali munthu wa nambala 15 kubatizidwa kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova m’ndende yozunzirako ya Porto Azzurro, pachilumba cha Elba. Ubatizo wake unachitikira m’dziwe lochita kunyamula lomwe linaikidwa pa bwalo la masewero ndipo akaidi anzake angapo anapezekapo.

Leonardo yemwe analamulidwa kukhala m’ndende zaka 20, anapempha chilolezo chapadera choti akabatizidwe m’Nyumba ya Ufumu ku Parma. Leonardo atafunsidwa ndi nyuzipepala ya kumaloko, ananena kuti anafuna “kumveketsa bwino kuti anasankha kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, osati chifukwa chofuna kupeza njira yotulukira m’ndende, koma chifukwa chofuna kukhutiritsa kusowa kwake kwakulu kwauzimu.” Iye anati: “Moyo wanga unali ndi zophophonya zambiri, koma umenewu ndausiya. Ndasintha, ngakhale kuti zimenezi sizinachitike mwadzidzidzi. Ndifunika kupitiriza kukhala wolungama.”

Salvatore, yemwe anapezeka ndi mlandu wa kupha munthu, ali m’ndende ya Spoleto yokhala ndi chitetezo chokhwima. Ubatizo wake umene unachitikira m’ndende unasangalatsa anthu ambiri. Woyang’anira ndende kumeneko anati: “Chosankha chimene chili chothandiza kwa anthu komanso chothandiza munthuyo kusintha khalidwe lake kwa ena tiyenera kuchilimbikitsa. Ubwino wa kusintha kumeneku umakhudza akaidi anzake ndi anthu ena onse amene sali m’ndende.” Chifukwa cha kusintha kumene Salvatore anapanga, mkazi wake ndi mwana wake wamkazi tsopano akupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Mkaidi amene Salvatore anam’lalikira anabatizidwa kukhala mtumiki wa Yehova wodzipereka.

Kupita patsogolo ndi kuwonjezeka kwina kwa Chikristu choyambirira kunachitikira ku Italy. (Machitidwe 2:10; Aroma 1:7) M’nthawi ino yotuta, kupita patsogolo ndi kuwonjezeka kwauzimu kukupitiriza m’madera amodzimodzi amene Paulo ndi Akristu anzake analimbikira kulalikira uthenga wabwino.​—Machitidwe 23:11; 28:14-16.

[Mapu patsamba 13]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ITALY

Rome

[Zithunzi patsamba 15]

Nyumba ya Misonkhano ya Bitonto ndiponso mpingo wa chilankhulo chamanja cha ku Italy ku Rome.

[Chithunzi patsamba 16]

Akaidi ‘akumasulidwa’ ndi choonadi cha Baibulo

[Zithunzi patsamba 17]

Kupita patsogolo kwauzimu kukupitirizabe ku dziko limene kale Chikristu chinali kuyenda bwino