Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akudzipereka ndi Mtima Wonse

Akudzipereka ndi Mtima Wonse

Akudzipereka ndi Mtima Wonse

“ANTHU anu adzadzipereka eni ake.” (Salmo 110:3) Mawu amenewa ali ndi tanthauzo lapadera kwa ophunzira 46 a m’kalasi la nambala 118 la Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Kodi iwo anachitanji pokonzekera kukalowa nawo sukulu imeneyi, yomwe imaphunzitsa anthu oyembekezera kukhala amishonale kukatumikira anthu m’mayiko ena mwa kukawapatsa zinthu zofunika zauzimu? Mike ndi Stacie, omwe anali ophunzira m’kalasi limeneli la nambala 118 anafotokoza kuti: “Tinasankha kukhala moyo wosafuna zambiri, ndipo zimenezi zatithandiza kuchepetsa zododometsa ndi kuona zinthu zauzimu kukhala zofunika m’moyo wathu. Tinatsimikiza mtima kusalola ntchito imene inali kutiyendera bwino kutichotsera zolinga zathu zauzimu.” Mofanana ndi Mike ndi Stacie, ophunzira ena onse m’kalasi limeneli, anadzipereka ndi mtima wonse ndipo tsopano akupita kukatumikira monga olengeza Ufumu m’makontinenti anayi.

Loweruka pa March 12, 2005, zinali zoonekeratu kuti anthu 6,843 amene anali kumvetsera pulogalamu ya mwambo womaliza maphunzirowu anali osangalala. Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani. Mbale Jaracz atalandira ndi manja awiri alendo ochokera m’mayiko 28 omwe anafika pa mwambowu, anayamba kufotokoza phindu la maphunziro a Baibulo. Pogwira mawu William Lyon Phelps, mphunzitsi wa ku America, mbale Jaracz anati: “Aliyense amene akulidziwa bwino Baibulo tinganenedi kuti anaphunzira.” Ngakhale kuti maphunziro a kusukulu ngwofunika, maphunziro a Baibulo ngwofunika koposa. Amathandiza anthu kum’dziwa Mulungu, ndipo zimenezi zingawathandize kudzapeza moyo wosatha. (Yohane 17:3) Mbale Jaracz anayamikira omaliza maphunzirowo chifukwa chodzipereka kutenga nawo mbali yaikulu pa ntchito ya padziko lonse yophunzitsa Baibulo imene ikuchitika m’mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 98,000 padziko lonse lapansi.

Chilimbikitso cha Panthawi Yake kwa Omaliza Maphunzirowo

Tcheyamani atamaliza malonje, William Samuelson anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Mmene Mungakhalire Ngati Mtengo Wauwisi wa Azitona M’nyumba ya Mulungu,” kuchokera pa lemba la Salmo 52:8. Iye ananena kuti m’Baibulo, mtengo wa azitona umagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa kuimira kubala zipatso, kukongola, ndi kulemekezeka. (Yeremiya 11:16) Poyerekezera ophunzirawo ndi mitengo ya azitona, wokamba nkhaniyu anati: “Mukamagwira ntchito yanu yolalikira za Ufumu mokhulupirika m’magawo anu aumishonale, mudzakhala okongola ndi olemekezeka kwa Yehova.” Mtengo wa azitona umafunika mizu yamphamvu kuti usafe nthawi yachilala. Mofananamo, ophunzirawo afunika kulimbitsa mizu yawo yauzimu kuti akathe kupirira akakakumana ndi anthu opanda chidwi, chitsutso, kapena ziyeso zina mu utumiki wawo m’dziko lachilendo.​—Mateyu 13:21; Akolose 2:6, 7.

John E. Barr, mmodzi mwa abale atatu a m’Bungwe Lolamulira omwe anali ndi mbali mu pulogalamuyi, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Inu Ndinu Mchere wa Dziko Lapansi.” (Mateyu 5:13) Iye ananena kuti mofanana ndi mchere womwe umateteza chakudya kuti chisavunde, kulalikira Ufumu wa Mulungu kumene amishonalewo azikachita, kudzatha kupulumutsa miyoyo ya amene akamvetsera, mwa kuwateteza kuti asavunde mwa makhalidwe komanso mwauzimu. Kenako, ndi mawu achikondi, mbale Barr analimbikitsa omaliza maphunzirowo, kuti ‘akakhale ndi mtendere’ wina ndi mnzake. (Marko 9:50) “Kulitsani chipatso cha mzimu, ndipo samalani kuti makhalidwe anu ndi mawu anu azikhala achisomo ndi olimbikitsa nthawi zonse,” analangiza motero mbale Barr.

“Yendetsani Sitima Yanu pa Madzi Akuya.” Umenewu unali mutu wa nkhani imene anakamba Wallace Liverance, mmodzi wa alangizi a Gileadi. Sitima imene ikuyenda pa madzi akuya ingakafike kumene ikupita. Mofananamo, kumvetsa “zakuya za Mulungu,” zomwe ndi choonadi chokhudza chifuno cha Mulungu ndi mmene adzachikwaniritsire, kungathandize munthu kupita patsogolo mwauzimu. (1 Akorinto 2:10) Kuyenda m’madzi auzimu osazama mwa kungokhutira ndi “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu” sikungatithandize kupita patsogolo, ndipo zingachititse ‘chikhulupiriro chathu kutayika,’ kapena kuti kusweka ngati ngalawa. (Ahebri 5:12, 13; 1 Timoteo 1:19) Pomaliza, mbale Liverance anati: “Lolani ‘kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu’ zikutsogolereni mu utumiki wanu wa umishonale.”​—Aroma 11:33.

Mark Noumair, mlangizi wina wa Gileadi, anakamba nkhani yakuti “Kodi Mudzachita Zinthu Mogwirizana ndi Cholowa Chanu?” Kwa zaka zoposa 60, Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo yakhala yodalirika komanso ya mbiri yabwino chifukwa cha ‘umboni wabwino wochuluka’ umene omaliza maphunziro ku sukulu imeneyi apereka. (Genesis 31:48) Cholowa cha Gileadi chimenechi chaperekedwanso kwa ophunzira a kalasi la nambala 118. Mbale Noumair analimbikitsa ophunzirawo kutsanzira Atekoa a m’nthawi ya Nehemiya, mwa kukagwirizana modzichepetsa ndi mipingo ya kumene akukatumikira komanso ndi amishonale anzawo. Anawalangiza kupewa mtima wonyada wa anthu “omveka” otchulidwa ndi Nehemiya, ndipo mmalo mwake akakhale ofunitsitsa kugwira ntchito mwakachetechete osati modzionetsera.​—Nehemiya 3:5.

Zokumana Nazo Komanso Zimene Ena Ananena Zinali Zopindulitsa

Nkhani yotsatira pa pulogalamuyi inali yamutu wakuti “Mawu a Mulungu Anakula.” (Machitidwe 6:7) Potsatira malangizo a Lawrence Bowen, mlangizi wa Gileadi, ophunzirawo anachita zitsanzo za zokumana nazo mu utumiki zomwe zinawasangalatsa panthawi imene anali kusukuluko. Zokumana nazo zimenezo zinasonyeza kuti ophunzirawo anali kulalikira Mawu a Mulungu mwachangu ndiponso kuti Yehova anawadalitsa kwambiri chifukwa cha khama lawo.

Richard Ashe anafunsa mafunso abale a m’banja la Beteli amene ntchito yawo imakhudzana kwambiri ndi sukuluyi. Ndemanga zawo zinathandiza kuona mmene banja la Beteli limathandizira ophunzira a Gileadi kuti apindule kwambiri ndi maphunziro awo. Kenako, Geoffrey Jackson analankhula ndi ena amene anamaliza maphunziro ku Gileadi zaka za m’mbuyomu. Iwowa anatchula mipata yambiri yotamandira ndi kulemekezera Yehova imene imabwera kwa amishonale. Wina anati: “Anthu amaona chilichonse chimene mukuchita monga amishonale. Amamvetsera, amaona, ndiponso amakumbukira.” Choncho, ophunzirawo analimbikitsidwa kukhala osamala mwa kusonyeza chitsanzo chabwino nthawi zonse. Mosakayikira, amishonale atsopanowa akapindula ndi malangizo othandizawa mtsogolo muno.

Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yomaliza yamutu wakuti, “Pitani Mukagawe ‘Madzi Amoyo.’” (Yohane 7:38) Iye anati kwa miyezi isanu, ophunzirawo anapindula kwambiri chifukwa anamwa choonadi chochuluka cha Mawu a Mulungu. Koma kodi amishonale atsopanowo akachita chiyani ndi zomwe aphunzirazo? Mbale Lett analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti akagawane ndi ena madzi auzimu amenewa mosaumira, kuti enawo akakhalenso ndi “kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:14) Wokamba nkhaniyu anawonjezera kuti: “Musakaiwale kupereka ulemu ndi ulemerero woyenera kwa Yehova, ‘kasupe wa madzi amoyo.’ Mukakhale oleza mtima pophunzitsa anthu omwe atuluka mu Babulo Wamkulu mmene muli chilala chosaneneka.” (Yeremiya 2:13) Pomaliza, mbale Lett analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti ndi mtima wonse, atsanzire mzimu ndi mkwatibwi ndi kupitiriza kulengeza kuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 22:17.

Mbale Jaracz anamaliza mwambowu mwa kupereka moni wochokera m’mayiko osiyanasiyana. Pambuyo pake, mmodzi wa omaliza maphunzirowo anawerenga kalata yosonyeza kuyamikira kwawo.

Kodi ndinu wokonzeka kudzipereka kukatumikira kumene ofalitsa akufunika kwambiri? Ngati ndi choncho, yesetsani kukwaniritsa zolinga zauzimu, monga momwe omaliza maphunzirowa achitira. Pezani chimwemwe ndi kukhala wokhutira. Zimenezi zimabwera ngati mofunitsitsa munthu wadzipereka kutumikira Mulungu, kaya monga mmishonale m’dziko lakutali, kapena ngati mtumiki pafupi ndi kwawo.

[Bokosi patsamba 13]

ZIWERENGERO ZA KALASI

Chiwerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 8

Chiwerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 19

Chiwerengero cha ophunzira: 46

Avereji ya zaka zakubadwa: 33.0

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 16.5

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 12.9

[Chithunzi patsamba 15]

Kalasi la Nambala 118 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Brockmeyer, A.; Moloney, S.; Symonds, N.; Lopez, Y.; Howard, C. (2) Jastrzebski, T.; Brown, D.; Hernandez, H.; Malagón, I.; Jones, A.; Connell, L. (3) Howard, J.; Lareau, E.; Shams, B.; Hayes, S.; Brown, O. (4) Burrell, J.; Hammer, M.; Mayer, A.; Kim, K.; Stanley, R.; Rainey, R. (5) Jastrzebski, P.; Zilavetz, K.; Ferris, S.; Torres, B.; Torres, F. (6) Connell, J.; Hernandez, R.; Moloney, M.; Malagón, J.; Shams, R.; Hayes, J. (7) Ferris, A.; Hammer, J.; Stanley, G.; Kim, C.; Symonds, S.; Lopez, D.; Burrell, D. (8) Brockmeyer, D.; Mayer, J.; Rainey, S.; Zilavetz, S.; Jones, R.; Lareau, J.