Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”

Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”

Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”

“Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene . . . adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”​—YESAYA 52:7.

1, 2. (a) Ndi zinthu zoopsa zotani zimene zikuchitika tsiku lililonse? (b) Kodi anthu ambiri zimawakhudza bwanji akamamva nkhani zoipa nthawi zonse?

ANTHU pa dziko lonse lapansi masiku ano, atopa ndi kumangomva nkhani zoipa zokhazokha. Akatsegula wailesi, zomwe akumva ndi nkhani zochititsa mantha za matenda oopsa amene akusowetsa anthu mtendere padziko lonse. Akamamvetsera nkhani pa wailesi yakanema akungoona zithunzi zosachoka m’maganizo za ana ovutika ndi njala omwe akupempha thandizo. Akafuna kuwerenga nyuzipepala akumva za kuphulika kwa mabomba amene amagwetsa nyumba ndi kupha anthu ambirimbiri osalakwa.

2 Inde, tsiku lililonse kukuchitika zinthu zoopsa. Kunena zoona, zinthu zikuipiraipira chifukwa maonekedwe adzikoli akusintha. (1 Akorinto 7:31) Magazini ina ya kummawa kwa Ulaya inanena kuti nthawi zina zimaoneka ngati dziko lonseli “lili pafupi kuwonongeka kotheratu.” N’zosadabwitsa kuti anthu ovutika m’maganizo akuchulukirachulukira. Mosakayikira, munthu wina amene anagwidwa mawu pa kafukufuku wa nkhani za pa wailesi yakanema ku United States anafotokoza maganizo ofanana ndi omwe anthu mamiliyoni ambiri ali nawo. Iye anati: ‘Ndikatha kuonerera nkhani pa TV, nkhawa imandigwira. Nkhani zonse zimakhala zoipa zokhazokha ndi zothetsa nzeru.’

Nkhani Imene Aliyense Afunikira Kumva

3. (a) Kodi Baibulo likufalitsa uthenga wabwino wotani? (b) N’chifukwa chiyani mumaona uthenga wabwino wa Ufumu kukhala wofunika?

3 Kodi nkhani yabwino ingapezeke m’dziko lodzaza ndi mavutoli? Inde ingapezeke. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Baibulo likufalitsa uthenga wabwino. Umenewu ndi uthenga wakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa matenda, njala, uchigawenga, nkhondo, ndi kuponderezana kwa mtundu uliwonse. (Salmo 46:9; 72:12) Kodi imeneyi si nkhani imene aliyense akufunikira kumva? Mboni za Yehova zikuganiza choncho. Chotero, zikudziwika kulikonse chifukwa zikuyesetsa mosaleka kuuza anthu a mitundu yonse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 24:14.

4. Kodi m’nkhani ino tikambirana mbali ziti za utumiki wathu, nanga m’nkhani yotsatira tidzakambirana mbali iti?

4 Koma kodi tingatani kuti tipitirize kulalikira uthenga wabwinowu mogwira mtima komanso mokhutiritsa, ngakhale m’madera omwe anthu salabadira kwenikweni? (Luka 8:15) Mosakayikira, kupenda mwachidule mbali zitatu zofunika za ntchito yathu yolalikira kutithandiza. Tipenda (1) zolinga zathu, kapena kuti chifukwa chake timalalikira; (2) uthenga wathu, kapena kuti zimene timalalikira; ndiponso (3) njira zathu, kapena kuti mmene timalalikirira. Zolinga zathu zikakhala zabwino, uthenga wathu ukakhala womveka bwino, ndipo njira zathu zolalikirira zikakhala zogwira mtima, tidzapatsa anthu ochuluka mwayi wakumva nkhani yosangalatsa koposa, yomwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. *

Chifukwa Chimene Timalalikirira Uthenga Wabwino

5. (a) Kuposa china chilichonse, n’chiyani chimene chimatilimbikitsa kutenga nawo mbali mu utumiki? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti timasonyeza chikondi kwa Mulungu mwa kumvera lamulo la m’Baibulo lakuti tizilalikira?

5 Tiyeni tikambirane mbali yoyamba, zolinga zathu. N’chifukwa chiyani timalalikira uthenga wabwino? Chifukwa chake n’chofanana ndi cha Yesu. Iye anati: “Ndikonda Atate.” (Yohane 14:31; Salmo 40:8) Kuposa china chilichonse, chikondi chathu pa Mulungu ndi chimene chimatilimbikitsa kulalikira. (Mateyu 22:37, 38) Baibulo limagwirizanitsa kukonda Mulungu ndi utumiki, pamene limati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.” (1 Yohane 5:3; Yohane 14:21) Kodi malamulo a Mulungu amenewa akuphatikizapo lamulo lakuti “mukani, phunzitsani anthu”? (Mateyu 28:19) Inde. N’zoona kuti mawu amenewa ananena ndi Yesu, koma kwenikweni anachokera kwa Yehova. Chifukwa chiyani tikutero? Yesu anafotokoza kuti: “Sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 8:28; Mateyu 17:5) Chotero, mwa kumvera lamulo lakuti tizilalikira, timam’sonyeza Yehova kuti timam’konda.

6. Kodi kukonda Mulungu kumatilimbikitsa motani kulalikira?

6 Kuwonjezera pamenepo, chikondi chathu pa Yehova chimatilimbikitsa kulalikira chifukwa chakuti tikufuna kutsutsa mabodza amene Satana akunenera Mulungu. (2 Akorinto 4:4) Satana anayambitsa kukayikira zoti ulamuliro wa Mulungu ndi wolungama. (Genesis 3:1-5) Monga Mboni za Yehova, ndife ofunitsitsa kutenga nawo mbali povumbula mabodza a Satana ndi kuyeretsa dzina la Mulungu pamaso pa anthu onse. (Yesaya 43:10-12) Komanso, timalalikira chifukwa chakuti tadziwa makhalidwe ndi njira za Yehova. Tikuona kuti tayandikana naye ndipo ndife ofunitsitsa kwambiri kuuzako ena za Mulungu wathu. Ndipotu, ubwino wa Yehova ndi njira zake zolungama zimatipatsa chimwemwe mwakuti sitingaleke kulankhula za iye. (Salmo 145:7-12) Timakakamizika kumutamanda ndi kulankhula za “zoposazo za Iye” kwa amene angamvetsere.​—1 Petro 2:9; Yesaya 43:21.

7. Kuwonjezera pa kukonda Mulungu, kodi timalalikira pa chifukwa china chofunika chiti?

7 Pali chifukwa china chofunika chopitirizira kutenga nawo mbali mu utumiki: Timafunitsitsa kulimbikitsa anthu amene atopa ndi kumangomva nkhani zoipa zokhazokha, komanso anthu amene akuvutika pa zifukwa zina. Pantchito imeneyi, timayesetsa kutsanzira Yesu. Mwachitsanzo, onani zimene zikufotokozedwa pa Marko chaputala 6.

8. Kodi nkhani ya pa Marko chaputala 6 ikusonyeza kuti Yesu anali kuwaona motani anthu?

8 Atumwi atafika kuchokera kuulaliki anauza Yesu zonse zimene anachita ndi kuphunzitsa. Yesu anaona kuti atumwiwo atopa, ndipo anawauza kuti amutsatire kuti ‘akapumule kamphindi.’ Choncho anakwera ngalawa ndi kunyamuka kupita kumalo abata. Anthu anawalondola, anawathamangira m’mphepete mwa nyanja, ndipo posakhalitsa anawapeza. Kodi Yesu anachitanji? Nkhaniyi imati: ‘Anaona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ (Marko 6:31-34) Chifukwa cha chifundo chake, Yesu anapitiriza kulengeza uthenga wabwino ngakhale kuti anali wotopa. Mwachionekere, Yesu anawamvera chisoni kwambiri anthu amenewa.

9. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhani ya pa Marko chaputala 6 ponena za cholinga chabwino cholalikirira?

9 Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhani imeneyi? Monga Akristu tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. Timazindikira udindo umene tili nawowu wolengeza uthenga wabwino, chifukwa chifuniro cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke.” (1 Timoteo 2:4) Komabe, sikuti timachita utumiki wathu pongofuna kukwaniritsa chabe ntchito imene tapatsidwa, koma timauchita chifukwa cha chifundo. Ngati timachitira chifundo anthu monga momwe Yesu anachitira, mtima wathu udzatilimbikitsa kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tipitirizebe kuwauza uthenga wabwino. (Mateyu 22:39) Utumiki wathu tikamauchita ndi zolinga zabwino zoterezi, zidzatilimbikitsa kulalikira uthenga wabwino mosaleka.

Tikulengeza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu

10, 11. (a) Kodi Yesaya anaufotokoza motani uthenga umene timalalikira? (b) Kodi Yesu anadza motani ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, nanga atumiki amakono a Mulungu atengera motani chitsanzo cha Yesu?

10 Bwanji za uthenga wathu, yomwe ndi mbali yachiwiri ya utumiki wathu? Kodi timalalikira chiyani? Mneneri Yesaya anafotokoza momveka bwino uthenga umene tikufalitsa, anati: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.”​—Yesaya 52:7.

11 Mawu ofunika kwambiri pa lemba limeneli akuti, “Mulungu wako ndi mfumu,” akutikumbutsa uthenga umene tikuyenera kulengeza, womwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Marko 13:10) Onaninso kuti vesi limeneli likusonyeza ubwino wa uthenga wathu. Yesaya anatchula mawu ngati “chipulumutso,” “uthenga wabwino,” “mtendere,” ndi “zinthu zabwino.” Patapita zaka zambiri kuchokera m’nthawi ya Yesaya, m’zaka 100 zoyambirira, Yesu Kristu anakwaniritsa ulosi umenewu mwapadera kwambiri mwa kutiikira chitsanzo polalikira mwachangu uthenga wa zinthu zabwino, Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo. (Luka 4:43) M’nthawi yathu ino, makamaka kuyambira 1919, Mboni za Yehova zatengera chitsanzo cha Yesu mwa kulengeza mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwawo ndi madalitso amene udzadzetsa.

12. Kodi anthu amene amalabadira uthenga wabwino wa Ufumu umawakhudza motani?

12 Kodi uthenga wabwino wa Ufumu umawakhudza motani anthu amene amaulandira? Lerolino, monga momwe zinalili m’masiku a Yesu, uthenga wabwino umapatsa anthu chiyembekezo ndiponso kuwalimbikitsa. (Aroma 12:12; 15:4) Umapereka chiyembekezo kwa anthu oona mtima chifukwa chakuti amaphunzira kuti pali zifukwa zamphamvu zokhulupirira kuti kutsogoloku kuli zabwino. (Mateyu 6:9, 10; 2 Petro 3:13) Chiyembekezo choterechi chimathandiza kwambiri anthu oopa Mulungu kukhala osatekeseka akamaganizira za m’tsogolo. Wamasalmo ananena kuti anthu oterewa “sadzaopa mbiri yoipa.”​—Salmo 112:1, 7.

Uthenga Womwe ‘Umamanga Osweka Mtima’

13. Kodi mneneri Yesaya anafotokoza motani madalitso amene anthu omwe akulabadira uthenga wabwino akupeza panopa?

13 Chinanso, amene amamvetsera uthenga wabwino amalimbikitsidwa ndi kupeza madalitso panopa. Motani? Yesaya mneneri anatchula ena mwa madalitso amenewa pamene analosera kuti: “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.”​—Yesaya 61:1, 2; Luka 4:16-21.

14. (a) Kodi mawu akuti “ndikamange osweka mtima” akusonyeza chiyani za uthenga wa Ufumu? (b) Kodi timasonyeza bwanji mmene Yehova amamvera akaona anthu osweka mtima?

14 Malinga ndi ulosi umenewu, Yesu ‘anamanga osweka mtima’ mwa kulalikira uthenga wabwino. Apatu Yesaya anagwiritsa ntchito fanizo lofotokoza zinthu momveka bwino. Malinga ndi dikishonale ina ya Baibulo, mawu a Chihebri omwe anawamasulira kuti ‘kumanga’ “kawirikawiri amagwiritsidwa ntchito kunena za ‘kumanga’ bandeji, ndipo malinga ndi zimenezi akunena za kupereka mankhwala ndi kuchiritsa munthu wovulala.” Nesi wachifundo angakulunge bandeji, mbali yovulala ya thupi pofuna kuziziritsa malo opwetekawo. Mofananamo, mwa kulalikira uthenga wa Ufumu, ofalitsa achifundo amalimbikitsa onse omvetsera uthenga wawo amene akuvutika m’njira iliyonse. Ndipo pothandiza anthu amene akufunikiradi thandizo, amasonyeza mmene Yehova akuwadera nkhawa. (Ezekieli 34:15, 16) Ponena za Mulungu, wamasalmo anati: “Achiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.”​—Salmo 147:3.

Mmene Uthenga wa Ufumu Umathandizira Anthu

15, 16. Ndi zitsanzo za zochitika zenizeni ziti zomwe zikusonyeza mmene uthenga wa Ufumu umathandizira ndi kulimbikitsira anthu?

15 Zitsanzo zambiri za zochitika zenizeni m’moyo zimasonyeza mmene uthenga wa Ufumu umachirikizira ndi kulimbikitsira anthu a mitima yosweka. Ganizirani za a Oreanna, mayi wachikulire wa ku South America, amene chilakolako chokhalabe ndi moyo chinam’thera. Mayi wina wa Mboni za Yehova anayamba kucheza ndi a Oreanna ndi kumawawerengera Baibulo ndi buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Poyamba, mayi wovutika maganizoyu anali kumvetsera kuwerengako ali chigonere pabedi komanso atatseka maso, ndipo nthawi zonse anali kuusa moyo. Koma posakhalitsa, anayamba kuyesetsa kukhala tsonga pabedi pawo pomwepo ndi kumamvetsera kuwerengako. Patapita nthawi, anayamba kukhala pa mpando m’chipinda chochezera, ndi kumayembekezera mphunzitsi wawo wa Baibulo uja kuti abwere. Kenako, mayiwo anayamba kufika ku misonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu. Atalimbikitsidwa ndi zimene anaphunzira pa misonkhano imeneyo, anayamba kugawira mabuku ofotokoza Baibulo kwa aliyense wodutsa pafupi ndi nyumba yawo. Kenako, a Oreanna anabatizidwa monga Mboni ya Yehova, ali ndi zaka 93. Uthenga wa Ufumu unasintha maganizo awo osafuna moyo aja ndi kuyamba kuona moyo mwa njira ina.​—Miyambo 15:30; 16:24.

16 Uthenga wa Ufumu umalimbikitsanso kwambiri anthu amene akudziwa kuti moyo wawo uli pafupi kutha chifukwa cha matenda. Mwachitsanzo, ganizirani za Maria wa kumadzulo kwa Ulaya. Iye anali kudwala matenda osachiritsika ndipo anatayiratu mtima. Pamene Mboni za Yehova zimakumana naye, n’kuti ali wovutika maganizo kwambiri. Komabe, ataphunzira za zifuno za Mulungu, moyo wake unasintha n’kukhalanso watanthauzo. Anabatizidwa ndipo anali wachangu pantchito yolalikira. M’zaka ziwiri zomaliza za moyo wake, nkhope yake inkaoneka yowala chifukwa cha chiyembekezo ndi chimwemwe chimene anali nacho. Maria anamwalira ali ndi chiyembekezo cholimba chakuti akufa adzauka.​—Aroma 8:38, 39.

17. (a) Kodi uthenga wa Ufumu ukuthandiza motani anthu amene akuulandira? (b) Kodi inuyo mwadzionera nokha m’njira zotani mmene Yehova ‘akuwongolera onse owerama’?

17 Nkhani zoterezi zikuchitira umboni kuti uthenga wa Ufumu umathandizadi pa moyo wa anthu amene akufuna kudziwa choonadi cha m’Baibulo. Anthu omwe akulirira wokondedwa wawo amene wamwalira amapezanso mphamvu akaphunzira za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. (1 Atesalonika 4:13) Anthu omwe ali paumphawi ndipo akuchita kuvutikira kuti adyetse mabanja awo, samadziona monga opanda pake ndipo amalimba mtima akaphunzira kuti Yehova sadzawasiya ngati akhalabe okhulupirika kwa iye. (Salmo 37:28) Ndi thandizo la Yehova, ambiri amene anatheratu mphamvu chifukwa chovutika maganizo, pang’ono ndi pang’ono akupezanso mphamvu yofunika kuti athe kupirira vuto lawolo, ndipo nthawi zina vuto limeneli limathetsedwa. (Salmo 40:1, 2) Inde, kudzera m’mphamvu yopezeka m’Mawu ake, panopa Yehova ‘akuwongola onse owerama.’ (Salmo 145:14) Tikamaona mmene uthenga wabwino wa Ufumu ukulimbikitsira osweka mtima m’gawo lathu ndi mu mpingo wachikristu, nthawi zonse zimatikumbutsa kuti uthenga umene tili nawo masiku ano ndiwo uthenga wabwino koposa.​Salmo 51:17.

“Pemphero Langa Limene Ndiwapempherera kwa Mulungu”

18. Kodi Paulo anamva bwanji Ayuda atakana uthenga wabwino, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Ngakhale kuti uthenga wathu ndi uthenga wabwino koposa, ambiri amaukana. Kodi zimenezi zingatikhudze motani? Zingatikhudze mofanana ndi mmene zinakhudzira mtumwi Paulo. Kawirikawiri ankalalikira Ayuda, koma ambiri a iwo anakana uthenga wa chipulumutso. Paulo anakhudzika kwambiri ndi kukana kwawoko. Iye anavomereza kuti: “Ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.” (Aroma 9:2) Paulo anamvera chifundo Ayuda omwe anali kuwalalikirawo. Ndipo atakana uthenga wabwinowo iye anamva chisoni.

19. (a) N’chifukwa chiyani zili zomveka kuti nthawi zina tingagwe mphwayi? (b) N’chiyani chinathandiza Paulo kupitirizabe ntchito yake yolalikira?

19 Nafenso timalalikira uthenga wabwino kwa anthu chifukwa tikuwamvera chifundo. Choncho m’pomveka kuti tingagwe mphwayi ngati anthu ambiri akukana uthenga wa Ufumu. Zimenezi zimasonyeza kuti timaderadi nkhawa moyo wauzimu wa anthu amene timawalalikirawo. Komabe, tiyenera kukumbukira chitsanzo cha mtumwi Paulo. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupitiriza ntchito yake yolalikira? Ngakhale kuti zinamuwawa ndi kumumvetsa chisoni Ayuda atakana uthenga wabwino, Paulo sanasiyiretu kulalikira Ayuda onse, poganiza kuti ndi anthu osatheka kuwathandiza. Anali ndi chiyembekezo kuti ena a iwo adzalandira Kristu. Chotero ponena za mmene anali kuonera Myuda aliyense payekha, Paulo analemba kuti: “Kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.”​—Aroma 10:1.

20, 21. (a) Ponena za utumiki wathu, kodi tingam’tsanzire motani Paulo? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana mbali iti ya utumiki wathu?

20 Onani zinthu ziwiri zimene Paulo anatchula. Mtima wake unali wofunitsitsa kuti ena akapeze chipulumutso, ndipo anapempha kwa Mulungu kuti zimenezi zitheke. Masiku ano, timatsanzira chitsanzo chimenechi cha Paulo. Nthawi zonse ndife ofunitsitsa kupeza aliyense amene akufunadi kumva uthenga wabwino. Timapemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti atithandize kupeza anthu oterowo kuti tiwathandize kuyenda m’njira yomwe ingawathandize kukapeza chipulumutso.​—Miyambo 11:30; Ezekieli 33:11; Yohane 6:44.

21 Komano, kuti tifikire anthu ambiri mmene tingathere ndi uthenga wa Ufumu, sitikufunikira kungoika maganizo athu pa chifukwa chimene timalalikirira ndi zimene timalalikira, komanso pa mmene timalalikirira. Tidzakambirana mfundo imeneyi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 M’nkhani ino tikambirana mbali ziwiri zoyambirirazo. Ndipo m’nkhani yotsatira tidzakambirana mbali yachitatuyo.

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi timachita utumiki pa zifukwa ziti?

• Kodi uthenga waukulu umene timalalikira ndi uti?

• Kodi amene amalandira uthenga wa Ufumu amapeza madalitso otani?

• N’chiyani chomwe chingatithandize kupitiriza utumiki wathu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Uthenga wa Ufumu umalimbikitsa osweka mtima

[Zithunzi patsamba 20]

Pemphero limatithandiza kupirira mu utumiki wathu