Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Mtendere wa Mumtima

Kufunafuna Mtendere wa Mumtima

Kufunafuna Mtendere wa Mumtima

ALBERT anali ndi banja lachimwemwe, ndipo anali ndi ana awiri osangalatsa. Komabe, ankaona kuti chinachake chikusowa m’moyo wake. Panthawi imene anali kufufuza ntchito, anayamba ndale ndipo anali kutsatira mfundo zokhwima za sosholizimu zofuna kuti aliyense azipindula ndi chuma cha dzikolo. Iye anakhala wokangalika kwambiri m’chipani cha chikomyunizimu cha kwawoko.

Koma posakhalitsa, Albert anakhumudwa chifukwa chikomyunizimu chinam’gwiritsa fuwa la moto. Anasiya kuchita zandale ndipo anaika maganizo ake onse pa kusamalira banja lake. Cholinga chake m’moyo tsopano chinali kuonetsetsa kuti onse m’banja lake ndi achimwemwe. Komabe, Albert ankadzimva kuti kenakake kakusowa ndithu m’moyo wake. Samatha kumvetsa mmene akanapezera mtendere weniweni wa mumtima.

Zomwe zinachitikira Albert si zachilendo ayi. Pofuna kupeza cholinga chenicheni cha moyo, anthu mamiliyoni ambiri ayesa kutsatira zikhulupiriro, nzeru za anthu, ndi zipembedzo zosiyanasiyana. M’zaka za m’ma 1960, ku mayiko a kumadzulo kunali gulu la anthu osafuna kutsatira chikhalidwe chawo. Kwenikweni amene anali m’gulu limeneli anali achinyamata. Iwowa ankafunitsitsa kupeza chimwemwe ndi tanthauzo la moyo. Choncho ankamwa mankhwala osokoneza bongo ndi kutsatira nzeru za anthu omwe anali monga aphunzitsi ndi akulu a nsembe a gulu lawolo. Komabe, gulu limeneli linalephera kuwapatsa chimwemwe chenicheni. M’malo mwake, linalimbikitsa anthu kukonda kwambiri mankhwala osokoneza bongo, ndiponso linaphunzitsa achinyamata makhalidwe oipa. Zimenezi zinapangitsa kuti makhalidwe a anthu aipe mofulumira.

Kwa zaka zambiri, anthu ochuluka ayesa kudzikundikira chuma, mphamvu za ulamuliro, kapena kuphunzira kwambiri pofuna kupeza chimwemwe. Koma zimenezi pamapeto pake akhumudwa nazo. Yesu anati: “Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) M’malo mwake, munthu amene akuyesetsa kuti akhale wolemera, kawirikawiri sapeza chimwemwe. Baibulo limati: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba . . . [a]nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

Koma tsopano kodi munthu angakhale bwanji pamtendere mumtima ndi kudziwa cholinga cha moyo? Kodi afunikira kungoyesa njira iliyonse mwachisawawa ngati kuti zingachitike mwa mwayi? Ayi ndithu. Monga momwe tionere m’nkhani yotsatira, yankho lake lagona pa kukhutiritsa chosowa chofunika kwambiri komanso chapadera kwa anthu.

[Chithunzi patsamba 3]

Kodi chuma, mphamvu, kapena maphunziro zingakupatseni mtendere wa mumtima?