Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Lemba la Deuteronomo 14:21 limati: “Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha.” Kodi zimenezi zikutsutsana ndi lemba la Levitiko 11:40, lomwe limanena kuti: “Iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo”?

Mavesi awiri amenewa sakutsutsana. Lemba loyambalo likungobwereza lamulo loletsa kudya nyama yomwe yapezeka itafa, mwinamwake imene yaphedwa ndi zilombo zakuthengo. (Eksodo 22:31; Levitiko 22:8) Lemba lachiwirili likufotokoza zimene Mwisrayeli akanachita ngati mwinamwake mwangozi waswa lamulo limeneli.

Ngakhale kuti Chilamulo chinali kuletsa kuchita zinthu zina, nthawi zina anthu anali kunyalanyaza malamulowo. Mwachitsanzo, panali malamulo oletsa kuba, kupha, kupereka umboni wonama, ndi ena otero. Panthawi imodzimodziyo, anatchulanso zilango zimene woswa malamulo operekedwa ndi Mulungu amenewa anafunika kulandira. Zilango zimenezo zinapatsa mphamvu malamulowo ndi kusonyeza kuwopsa kwake.

Munthu akaswa lamulo loletsa kudya nyama yofa yokha anali wodetsedwa pamaso pa Yehova ndipo anafunikira kutsatira njira yoyenera ya kudziyeretsa. Koma akalephera kudziyeretsa moyenerera, anali ‘kusenza mphulupulu yake.’​—Levitiko 17:15, 16.