Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndine Wosangalala Kuti Ndagwira Nawo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

Ndine Wosangalala Kuti Ndagwira Nawo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

Mbiri ya Moyo Wanga

Ndine Wosangalala Kuti Ndagwira Nawo Ntchito ya Padziko Lonse Yophunzitsa Baibulo

YOSIMBIDWA NDI ANNA MATHEAKIS

Sitima inali kuyaka. Ngati sitima imeneyi ya mamita 171 ikanamira, moyo wanga ukanathera pamenepo. Mwamsanga ndinasambira, kwinaku ndikulimbana ndi mafunde amphamvu. Ndinagwira chovala cha mayi wina chothandiza munthu kuti asamire. Imeneyi inali njira yokhayo yomwe inandithandiza kuti ndisamire. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andipatse mphamvu ndi kundilimbitsa mtima. Sindikanachita zoposa pamenepa.

IZI zinachitika m’chaka cha 1971, pamene ndinali paulendo wobwerera ku gawo langa lachitatu la umishonale ku Italy. Pa ngozi ya sitima imeneyo, katundu wanga yense anatayika. Koma pali zinthu zina zofunika kwambiri zomwe sizinatayike, monga moyo wanga, ubale wachikondi wa Akristu, ndi mwayi wotumikira Yehova. Utumiki umenewu unali utandiyendetsa kale m’makontinenti atatu, ndipo ngozi ya sitimayi ndi chimodzi mwa zinthu zambiri zomwe zandichitikira m’moyo wanga.

Ine ndinabadwa mu 1922. Makolo anga anali kukhala ku Rām Allāh, pafupifupi makilomita 16 kumpoto kwa Yerusalemu. Makolo anga onse anali ochokera ku chilumba cha Kirete, koma bambo anga anakulira ku Nazareti. M’banja mwathu tinalipo ana asanu, anyamata atatu ndi atsikana awiri, ndipo ine ndinali womaliza pa onsewo. Banja lathu linali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya mchimwene wathu wachiwiri, amene anamwalira atamira mu mtsinje wa Yordano pa ulendo wa sukulu wokaona malo osiyanasiyana. Itachitika ngozi imeneyi, amayi anga anakaniratu kukhala ku Rām Allāh, choncho ine ndili ndi zaka zitatu, tinasamukira ku Atene, m’dziko la Girisi.

Choonadi cha M’Baibulo Chifika M’banja Mwathu

Titangofika ku Girisi, mchimwene wanga wamkulu Nikos, amene panthawiyo anali ndi zaka 22 za kubadwa, anakumana ndi Ophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinkadziwika nalo panthawiyo. Kuphunzira choonadi cha m’Baibulo kunam’patsa chimwemwe chochuluka ndi changu chosaneneka mu utumiki wachikristu. Bambo anga anakwiya nazo kwambiri zimenezi ndipo anam’pitikitsa Nikos panyumbapo. Komabe, bambo akachoka kupita ku Palestina, amayi anga, mchemwali wanga, ndi ine tinali kutsagana ndi Nikos ku misonkhano yachikristu. Ndikukumbukira bwino kuti amayi anga anali kunyadira pofotokoza zimene amva pa misonkhano imeneyo. Komano posakhalitsa, anadwala khansa ndipo anamwalira ali ndi zaka 42. Panthawi yovuta imeneyo, mwachikondi mchemwali wanga Ariadne anatenga udindo wosamalira banja lathu. Ngakhale kuti anali wamng’ono, anakhala ngati mayi wanga kwa zaka zambiri.

Pamene ndinali ndi bambo anga ku Atene, nthawi zonse ankapita nane ku tchalitchi cha Orthodox, ndipo atamwalira, ndinapitiriza kupitabe kutchalitchi koma mwa kamodzikamodzi. Pambuyo pake, ndinasiya kupitako nditaona kuti anthu omwe amapezeka kutchalitchiko sanali odzipereka kwa Mulungu.

Pambuyo pa imfa ya bambo anga, ndinalowa ntchito m’boma mu unduna wa zachuma. Koma mchimwene wanga uja, anadzipereka ndi moyo wake wonse pa ntchito yolalikira za Ufumu, ndipo anatumikira m’dziko la Girisi kwa zaka zambiri. M’chaka cha 1934 anasamukira ku Cyprus. Panthawiyo, pa chilumbachi panalibe Mboni yobatizidwa ya Yehova, choncho anali ndi mwayi wopititsa patsogolo ntchito yolalikira kumeneko. Atakwatira, mkazi wake Galatia, anayambanso utumiki wa nthawi zonse, ndipo anachita utumiki umenewu kwa zaka zambiri. * Nthawi ndi nthawi Nikos anali kutitumizira mabuku ndi magazini ofotokoza Baibulo koma sitinkakonda kuwawerenga. Nikos anakhalabe ku Cyprus kufikira pamene anamwalira.

Kutenga Choonadi cha M’Baibulo Kukhala Changachanga

M’chaka cha 1940, George Douras, Mboni yachangu ya ku Atene komanso bwenzi la Nikos, anafika kwathu ndi kutipempha kuti tipite kwawo kukaphunzira Baibulo limodzi ndi kagulu kakang’ono ka ophunzira ena. Tinavomera pempho limeneli monyadira. Posakhalitsa tinayamba kuuza ena zomwe tinali kuphunzirazo. Zimene tinaphunzira m’Baibulo zinalimbikitsa ine ndi mchemwali wanga kupereka miyoyo yathu kwa Yehova. Ariadne anabatizidwa mu 1942, ndipo ine ndinabatizidwa mu 1943.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, Nikos anatiitana kuti tipite ku Cyprus, choncho mu 1945 tinasamukira ku Nicosia. Mosiyana ndi ku Girisi, ntchito yolalikira ku Cyprus sinali yoletsedwa. Tinatenga nawo mbali pa utumiki wa kunyumba ndi nyumba komanso ulaliki wa mumsewu.

Patapita zaka ziwiri, Ariadne anabwerera ku Girisi. Kumeneko anapeza mbale wopembedza Yehova woti adzakwatirane naye m’tsogolo, choncho Ariadne anaganiza zokhazikika ku Atene. Posakhalitsa mlamu wanga ndi mchemwali wangayo anandilimbikitsa kuti ndibwerere ku Girisi ndi kukayamba utumiki wa nthawi zonse mu likulu la dzikoli. Popeza kuti nthawi zonse cholinga changa chinali kuchita upainiya, ndinabwerera ku Atene kumene ofalitsa anali kufunika kwambiri.

Makomo Atsopano a Utumiki Atseguka

Pa November 1, 1947, ndinayamba kuchita upainiya. Ndinkalalikira kwa maola 150 mwezi uliwonse. Mpingo wathu unali ndi gawo lalikulu, ndipo ndinafunika kuyenda maulendo ataliatali. Komabe, madalitso amene ndinasangalala nawo anali ochuluka. Kawirikawiri apolisi anali kumanga Mboni iliyonse yopezeka ikulalikira kapena kuchita misonkhano yachikristu, choncho posakhalitsa anandimanga.

Anali kundiimba mlandu wotembenuza anthu, womwe unali mlandu woopsa panthawiyo. Ndipo anandiweruza kuti ndikakhale m’ndende ya azimayi ya Averof mu Atene kwa miyezi iwiri. M’ndendemo munali kale mayi wina wa Mboni, chotero awirife tinali kusangalala ndi kulimbikitsana ndi macheza anthu achikristu ngakhale kuti tinali m’ndende. Nthawi imene anandilamula kugwira ukaidiwo itatha, ndinatuluka ndi kukapitiriza upainiya mwachimwemwe. Ambiri mwa anthu omwe ndinaphunzira nawo Baibulo panthawiyo akutumikirabe Yehova mokhulupirika, ndipo zimenezi zimandipatsa chimwemwe chochuluka.

Mu 1949, ndinalandira kalata yondiitana kuti ndikakhale nawo m’kalasi la 16 la Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo ku United States, kumene atumiki anthawi zonse amakaphunzira ntchito ya umishonale. Ine ndi achibale anga tinasangalala kwambiri. Ndinakonza zokakhala nawo pa msonkhano wa mayiko ku New York City m’chilimwe cha 1950, kuti pambuyo pake ndikapezeke ku Gileadi.

Nditafika ku United States, ndinali ndi mwayi wapadera wotumikira kwa miyezi ingapo ngati woyeretsa zipinda zogona pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku New York City. Malo amenewa anali aukhondo, osangalatsa, komanso olimbikitsa, ndipo abale ndi alongo onse anali achimwemwe. Monyadira sindidzaiwala konse miyezi isanu ndi umodzi imene ndinakhala kumeneko. Tsopano nthawi yoyamba Sukulu ya Gileadi inakwana, ndipo miyezi isanu ya maphunziro ndi malangizo akuya inadutsa mofulumira kwabasi. Ophunzira tonse tinazindikira mmene maphunziro a m’Malemba alili amtengo wapatali ndi osangalatsa, ndipo zimenezi zinawonjezera chimwemwe chathu ndi kufunitsitsa kwathu kugawana ndi ena maphunziro opatsa moyo amenewo a choonadi.

Gawo Langa Loyamba la Umishonale

Ku Sukulu ya Gileadi, anatilola kusankha mnzathu amene tikufuna kukatumikira naye limodzi asanatiuze kumene tikatumikire monga amishonale. Ine, mnzanga anali Ruth Hemmig (yemwe tsopano ndi Ruth Bosshard), mlongo wabwino kwambiri. Ine ndi Ruth tinasangalala kwambiri atatiuza kuti tikatumikira ku Istanbul, m’dziko la Turkey, m’malire mwa Asia ndi Ulaya. Tinkadziwa kuti m’dzikomo anali asanavomereze mwa lamulo ntchito yolalikira, koma sitinali kukayikira kuti Yehova akatithandiza.

Istanbul ndi mzinda wokongola womwe uli ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Mu mzinda umenewu tinapezamo anthu ambiri amalonda, njira zosiyanasiyana zophikira chakudya zochokera m’mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi, nyumba zosangalatsa zosungiramo zinthu zochititsa chidwi, malo okongola, ndi m’mbali mwa nyanja momwe nthawi zonse munali mosangalatsa. Koposa zonse, tinapezamo anthu oona mtima ofunitsitsa kuphunzira za Mulungu. Kagulu kakang’ono ka Mboni zomwe zinali mu Istanbul kanali ka abale a ku Armenia, ku Girisi, komanso achiyuda. Komabe, kunali anthu ambiri amitundu inanso, chotero kuphunzira zinenero zosiyanasiyana, kuphatikizapo Chiteki, kunali kothandiza kwambiri. Zinkatisangalatsa kwambiri kukumana ndi anthu aludzu la choonadi ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Ambiri a iwo akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika.

Mwachisoni, Ruth anam’kaniza chilolezo kuti apitirize kukhala m’dzikomo mwakuti anakakamizika kuchoka. Panopa akupitiriza utumiki wa nthawi zonse ku Switzerland. Pambuyo pa zaka zonsezi, ndikum’sowabe chifukwa anali kundisangalatsa ndi kundilimbikitsa.

Kusamukira ku Mbali Ina ya Dziko Lapansi

Mu 1963 boma la Turkey silinandilole kupitiriza kukhala m’dzikomo. Zinali zopweteka kusiya Akristu anzanga omwe ndinawaona akupita patsogolo mwauzimu, kwinaku akuyesetsa kuthana ndi mavuto ambiri. Pofuna kundilimbikitsa, mokoma mtima achibale anga anandilipirira ulendo wopita ku New York City kuti ndikapezeke pa msonkhano wachigawo kumeneko. Panthawiyi n’kuti asanandipatse gawo lina loti ndikatumikire.

Msonkhano wachigawo utatha, anandiuza kuti ndikatumikira ku Lima, m’dziko la Peru. Ine pamodzi ndi mlongo wina wachitsikana amene anali mnzanga woti ndizikatumikira naye limodzi, tinanyamuka ku New York ndi kupita ku gawo langa latsopanolo. Ndinaphunzira Chisipanya ndipo ndinali kukhala m’nyumba ya amishonale yomwe inali kumtunda kwa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Zinali zosangalatsa kulalikira kumeneko ndi kudziwana ndi abale ndi alongo akomweko.

Gawo Lina, Chinenero China

Patapita nthawi, achibale anga ku Girisi anayamba kuvutika chifukwa cha ukalamba ndi kufooka kwa matupi awo. Koma iwo sanandikakamize kusiya utumiki wa nthawi zonse ndi kumakhala moyo umene ena amati ndiwo moyo weniweni n’cholinga choti ndiziwathandiza. Komabe, nditaganiza mofatsa ndi kupemphera, ndinaona kuti zingakhale bwino ngati nditapita kukatumikira kufupi ndi achibale angawo. Mwachikondi, abale a ku nthambi anavomereza ndipo ananditumiza ku Italy kuti ndizikatumikira kumeneko, ndipo achibale anga anadzipereka kuti andithandiza kulipirira ulendo umenewu. Ndipotu ku Italy, ofalitsa anali kufunikanso kwambiri.

Apanso ndinafunikira kuphunzira chinenero chatsopano cha Chitaliyana. Gawo langa loyamba linali mu mzinda wa Foggia. Pambuyo pake, anandisintha ndi kunditumiza ku Naples, kumene ofalitsa anali kufunika kwambiri. Kumeneko gawo langa linali Posilipo, limodzi mwa madera okongola kwambiri ku Naples. Gawo langa linali lalikulu, ndipo kunali wolengeza Ufumu mmodzi yekha. Ndinasangalala kwambiri kugwira ntchito m’gawo limeneli, ndipo Yehova anandithandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri. Patapita nthawi, m’dera limeneli munakhala mpingo waukulu.

Ena mwa anthu oyambirira a komweko omwe ndinaphunzira nawo Baibulo anali mayi ndi ana ake anayi. Mayiyu ndi ana ake aakazi awiri akutumikirabe monga Mboni za Yehova. Ndinaphunziranso ndi banja lina limene linali ndi mwana wamng’ono wamkazi. Banja lonse linapita patsogolo m’choonadi ndipo linasonyeza kudzipereka kwawo mwa ubatizo wa m’madzi. Panopa mwana wawo wamkaziyo anakwatiwa ndi mtumiki wokhulupirika wa Yehova, ndipo onse awiri akutumikira Mulungu mwachangu. Pamene ndinali kuphunzira Baibulo ndi banja lina lalikulu, ndinachita chidwi ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu. Titawerenga malemba angapo osonyeza kuti Mulungu savomereza kumulambira pogwiritsa ntchito mafano, mayi a m’nyumbamo sanayembekeze kuti phunziro lithe. Nthawi yomweyo, anachotsa mafano onse m’nyumba mwawo ndi kuwataya.

Ngozi Panyanja

M’maulendo anga onse apakati pa Italy ndi Girisi, nthawi zonse ndinkayenda pa sitima ya pamadzi. Nthawi zambiri maulendo amenewa anali osangalatsa kwambiri. Koma zinthu zinasintha pa ulendo umodzi, m’chilimwe mu 1971. Ndinali paulendo wobwerera ku Italy pa sitima ya pamadzi yotchedwa Heleanna. M’mawa kwambiri pa August 28, m’khitchini ya sitimayi munabuka moto. Moto umenewu unakula ndipo m’sitimayi munali chipwirikiti pakati pa anthu apaulendofe. Azimayi anali kukomoka, ana anali kulira, ndipo azibambo anali kukalipa mwaphamvu ndi kuopseza. Anthu anali kuthamangira mbali imodzi ya sitimayo kumene kunali maboti opulumutsa anthu pangozi. Komabe, zovala zothandiza anthu kuti asamire zinali zochepa, ndipo zingwe zotsitsira maboti opulumutsira anthu sizinkagwira ntchito bwinobwino. Ine ndinalibe chovala chondithandiza kuti ndisamire, koma malawi a moto anali kukulirakulira, choncho chinthu chokha cha nzeru chinali kulumphira m’nyanjamo.

Nditangolumphira m’nyanjamo, ndinaona mayi wina amene anali ndi chovala chomuthandiza kuti asamire akuyandama pafupi ndi ine. Ankaoneka kuti sadziwa kusambira, choncho ndinam’gwira dzanja ndi kumukokera kutali ndi sitima imene inali kumirayo. Mafunde anakula panyanjapo, ndipo ndinatopa kwambiri chifukwa choyesetsa kuti ndisamire. Ngozi imeneyi inali yotayitsa mtima, koma ndinali kupempha Yehova mosaleka kuti andilimbitse mtima, ndipo zimenezi zinandipatsa mphamvu. Ngozi imeneyi inandikumbutsa zimene zinamuonekera mtumwi Paulo chombo chimene anakwera chitasweka.​—Machitidwe, chaputala 27.

Ndinayesetsa kulimbana ndi mafunde kwa maola anayi, nditam’gwirabe mnzanga uja. Ndikapeza mphamvu ndinali kusambira ndipo ndinali kuitana Yehova kuti atithandize. Kenako, ndinaona boti laling’ono likutiyandikira. Ine ndinapulumutsidwa, koma mnzangayo anali atamwalira kale. Titafika m’tauni ya Bari, ku Italy, ananditengera ku chipatala kumene anandipatsa thandizo. Ndinakhala m’chipatalamo kwa masiku angapo, ndipo Mboni zambiri zinali kudzandiona. Mokoma mtima anali kundipatsa zonse zimene ndinali kufuna. Ena amene ndinali nawo m’chipinda chimodzi m’chipatalamo, anachita chidwi ndi chikondi chachikristu chimene abalewo anali kundisonyeza. *

Nditachila bwinobwino, ananditumiza kukatumikira ku Rome. Anandipempha kuti ndizilalikira m’gawo la malonda m’katikati mwa mzindawo, ndipo ndi thandizo la Yehova ndinachitadi zimenezi kwa zaka zisanu. Ndinasangalala kutumikira m’dziko la Italy kwa zaka 20, ndipo anthu achitaliyana ndinali kuwakonda kwambiri.

Kubwerera Kumene Ndinayambira

M’kupita kwa nthawi, zinthu zinayamba kuipa m’moyo wa Ariadne ndi mwamuna wake chifukwa cha kufooka kwa matupi awo. Ndinaona kuti ngati nditakhala nawo pafupi, pamlingo winawake ndidzatha kuwabwezera zimene iwo anandichitira mwachikondi. Kunena zoona, zinandiwawa kwambiri kuchoka ku Italy. Komabe, abale amene anali kuyang’anira utumiki wanga anandilola, ndipo kuyambira m’chilimwe cha 1985, ndakhala ndikuchita upainiya mu Atene, kumene ndinayambira utumiki wa nthawi zonse kalelo mu 1947.

Ndinali kulalikira m’gawo la mpingo wathu, ndipo ndinapempha abale kuofesi ya nthambi kuti ndizilalikiranso m’gawo la malonda m’katikati mwa mzindawo. Ndinachita zimenezi kwa zaka zitatu limodzi ndi mlongo wina amenenso anali mpainiya. Tinachitira umboni mokwanira kwa anthu amene kawirikawiri sapezeka panyumba.

Pamene zaka zikudutsa, chilakolako changa chotumikira chikukulirakulira, koma mphamvu zikundithera. Panopa mlamu wanga uja anamwalira. Ariadne, amene anali ngati mayi wanga tsopano sakuthanso kuona. Kunena za ine, ndinali ndi mphamvu m’zaka zimene ndinali kuchita utumiki wa nthawi zonse. Koma posachedwapa, ndinagwa pa masitepe oterera ndipo dzanja langa lamanja linathyoka. Pambuyo pake ndinagwanso ndi kuthyoka fupa la mmunsi mwa chiuno. Anandichita opaleshoni ndipo ndinakhala ndili chigonere kwa nthawi yaitali. Panopa sindikuthanso kuyenda bwinobwino. Ndimagwiritsa ntchito ndodo koma sindingathe kutuluka panja pokhapokha wina atanditulutsa. Ngakhale zili choncho, ndimachita zonse zimene ndingathe, ndi chikhulupiriro chakuti ndidzapeza bwino. Ndikupitiriza kupeza chimwemwe ndipo ndine wokhutira potenga mbali pa ntchito yophunzitsa Baibulo, ngakhale kuti panopa ndikuchita zochepa.

Ndikakumbukira zaka zosangalatsa zomwe ndathera mu utumiki wa nthawi zonse, ndimayamikira Yehova kwambiri kuchokera pansi pa mtima. Iye komanso mbali ya padziko lapansi ya gulu lake andipatsa malangizo odalirika nthawi zonse ndiponso thandizo la mtengo wapatali. Zimenezi zandithandiza kugwiritsa ntchito luso langa mokwanira pa nthawi yonse ya moyo wanga imene ndakhala ndikum’tumikira. Chimene ndikufunitsitsa ndi mtima wonse n’chakuti Yehova andilimbikitse kuti ndipitirize kumutumikira. Ndine wachimwemwe chifukwa cha mbali yochepa imene ndachita pa ntchito ya padziko lonse yophunzitsa Baibulo imene Mulungu akuitsogolera.​—Malaki 3:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onani Yearbook ya Mboni za Yehova ya 1995 masamba 73-89.

^ ndime 34 Kuti mumve zambiri, onani Galamukani! yachingelezi ya February 8, 1972, masamba 12-16.

[Chithunzi patsamba 9]

Ine ndi mchemwali wanga Ariadne, limodzi ndi mwamuna wake Michalis, pamene ndinali kupita ku Gileadi

[Chithunzi patsamba 10]

Ine ndi Ruth Hemmig anatitumiza kukatumikira ku Istanbul, m’dziko la Turkey

[Chithunzi patsamba 11]

Ku Italy, kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1970

[Chithunzi patsamba 12]

Masiku ano, ine ndi mchemwali wanga, Ariadne