Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse

Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse

Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse

“Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.”​—MACHITIDWE 1:8.

1. Monga aphunzitsi a Baibulo, kodi timasamala za chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

APHUNZITSI aluso samangosamala chabe zokhazo zimene akuuza ophunzira awo koma amasamalanso mmene akuzinenera. Monga aphunzitsi a choonadi cha m’Baibulo, nafenso timachita chimodzimodzi. Timasamala za uthenga umene tikulalikira komanso njira zimene tikugwiritsa ntchito. Uthenga wathu, womwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu susintha, koma ifeyo timasinthasintha njira zolalikirira. Chifukwa chiyani? Kuti tifikire anthu ambiri mmene tingathere.

2. Kodi tikamasinthasintha njira zathu zolalikirira, timakhala tikutsanzira ndani?

2 Mwa kusinthasintha njira zathu zolalikirira, timatsanzira atumiki a Mulungu akale. Mwachitsanzo, ganizirani za mtumwi Paulo. Iye anati: “Kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda . . . kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, . . . Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti pali ponse ndikapulumutse ena.” (1 Akorinto 9:19-23) Paulo akasintha njira zake zophunzitsira, zotsatira za utumiki wake zinali zokhutiritsa. Ifenso tikamasintha ulaliki wathu mokoma mtima, kuti ugwirizane ndi zosowa za anthu amene tikulankhula nawo, utumiki wathu udzakhala wogwira mtima.

‘Kumalekezero Onse a Dziko’

3. (a) Kodi tikukumana ndi vuto lotani pa ntchito yathu yolalikira? (b) Kodi mawu a pa Yesaya 45:22 akukwaniritsidwa motani lerolino?

3 Vuto lalikulu limene olalikira uthenga wabwino ali nalo ndilo kukula kwa gawo, chifukwa afunika kulalikira “padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) M’zaka 100 zapitazi, atumiki ambiri a Yehova anayesetsa mwakhama kufika m’mayiko ena kukafalitsa uthenga wabwino kumeneko. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Gawo lathu lolalikira linawonjezeka modabwitsa padziko lonse lapansi. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, ntchito yolalikira inali kuchitika m’mayiko ochepa chabe. Koma lerolino Mboni za Yehova zikulalikira mwachangu m’mayiko 235. Inde, uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa mpaka ‘kumalekezero onse a dziko.’​—Yesaya 45:22.

4, 5. (a) Ndani amene achita mbali yofunika kwambiri pantchito yofalitsa uthenga wabwino? (b) Kodi maofesi ena a nthambi anena zotani zokhudza anthu ochokera m’mayiko ena omwe akutumikira m’gawo la nthambi zawo?

4 N’chiyani chathandiza kuti zinthu ziyende bwino chomwechi? Pali zinthu zambiri. Amishonale ophunzitsidwa bwino ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo, komanso posachedwapa, omaliza maphunziro ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki oposa 20,000 athandiza kwambiri. Ena amene athandizanso ndi Mboni zambirimbiri zomwe mwa kugwiritsa ntchito chuma chawo, zasamukira m’mayiko ena kumene kukufunika ofalitsa Ufumu ochuluka. Akristu odzipereka amenewa, akuphatikizapo amuna ndi akazi, ana ndi achikulire, okwatira ndi osakwatira. Iwowa akuchita mbali yofunika kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi. (Salmo 110:3; Aroma 10:18) Tikuwayamikira kwambiri. Onani zimene maofesi ena anthambi alemba zokhudza anthu ochokera m’mayiko ena kudzatumikira kumene kukufunika thandizo m’gawo la nthambi zawo.

5 “Mboni zokondedwa zimenezi zikutsogolera pa ntchito yolalikira m’madera akutali, zikuthandiza kukhazikitsa mipingo yatsopano, ndiponso zikuthandiza abale ndi alongo a m’dziko lathu lino kukula mwauzimu.” (Ecuador) “Ngati anthu ambirimbiri ochokera m’mayiko ena omwe ali m’dziko lathu lino atabwerera kwawo, mipingo yathu ingabwerere mmbuyo. Ndi dalitso lalikulu kukhala nawo.” (Dominican Republic) “M’mipingo yathu yambiri, achulukamo ndi alongo moti nthawi zina mu mpingo wa anthu 100, mumapezeka alongo 70. (Salmo 68:11) Ambiri mwa alongo amenewa ndi atsopano m’choonadi. Koma alongo osakwatiwa omwe ndi apainiya ochokera m’mayiko ena, akupereka thandizo lamtengo wapatali mwa kuphunzitsa atsopanowa. Alongo ochokera m’mayiko ena amenewa ndi mphatso yapadera kwa ife.” (Dziko lina la kum’mawa kwa Ulaya) Kodi munayamba mwaganizapo zokatumikira m’dziko lina? *​—Machitidwe 16:9, 10.

‘Amuna Khumi, Ndiwo a Manenedwe Onse’

6. Kodi lemba la Zekariya 8:23 likusonyeza motani vuto lina lokhudza chinenero pa ntchito yathu yolalikira?

6 Vuto lina lalikulu ndi kuchuluka kwa zinenero zimene anthu amalankhula padziko lapansi. Mawu a Mulungu ananeneratu kuti: “Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Pa kukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi umenewu, amuna khumiwo akuimira khamu lalikulu, loloseredwa pa Chivumbulutso 7:9. Komabe, onani kuti malinga ndi ulosi wa Zekariya, ‘amuna khumiwo’ sakungochokera m’mitundu yonse komanso ‘m’manenedwe onse a amitundu.’ Kodi taona kukwaniritsidwa kwa mbali yofunikayi ya ulosi umenewu? Inde, takuona.

7. Ndi ziwerengero ziti zomwe zikusonyeza kuti anthu “a manenedwe onse” akufikiridwa ndi uthenga wabwino?

7 Taganizirani ziwerengero zotsatirazi. Zaka 50 zapitazo mabuku athu anali kufalitsidwa m’zinenero 90. Koma lerolino chiwerengero chimenecho chakwera kufika pa zinenero zoposa 400. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wachita zonse zotheka kuti mabuku azipezeka ngakhale m’zinenero zolankhulidwa ndi anthu ochepa chabe. (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, mabuku ofotokoza Baibulo tsopano akupezeka m’chinenero cha Chigirinilandi (cholankhulidwa ndi anthu 47,000), Chipalawana (cholankhulidwa ndi anthu 15,000), ndi Chiyapese (cholankhulidwa ndi athu osakwana 7,000).

“Khomo Lalikulu” Lolowera M’magawo Atsopano

8, 9. N’chiyani chatitsegulira “khomo lalikulu,” nanga Mboni zikwizikwi zachita chiyani?

8 Koma masiku ano, sitifunikira kuchita kupita kudziko lina kuti tikalalikire uthenga wabwino kwa anthu a zinenero zosiyanasiyana. M’zaka zaposachedwapa, anthu mamiliyoni ambiri kuphatikizapo othawa kwawo asamukira m’mayiko olemera. Zimenezi zachititsa kuti m’mayiko amenewa mupezeke anthu ochuluka olankhula zinenero zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ku Paris, m’dziko la France, anthu amalankhula zinenero zosiyanasiyana pafupifupi 100. Ku Toronto, m’dziko la Canada, kuli zinenero zokwana 125; ndipo ku London, m’dziko la England anthu amalankhula zinenero za kumayiko ena zoposa 300. Kupezeka kwa anthu ochokera m’mayiko ena amenewa m’madera a mipingo yambiri, kwatsegula “khomo lalikulu” lolowera m’magawo atsopano komwe tingagawane uthenga wabwino ndi anthu a mitundu yonse.​—1 Akorinto 16:9.

9 Mboni zikwizikwi zikuchitapo kanthu pofuna kuthandiza pantchito imeneyi yolengeza uthenga wabwino kwa anthu amitundu yonse mwa kuphunzira chinenero chatsopano. Kwa ambiri a iwo, si zinthu zophweka. Komabe khama lawo n’lopindulitsa kwabasi, chifukwa akupeza chimwemwe pothandiza alendo obwera m’dziko lawo komanso anthu othawa kwawo, kuphunzira choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. M’chaka chaposachedwapa, pafupifupi 40 mwa anthu 100 aliwonse omwe anabatizidwa m’misonkhano yachigawo m’dziko lina kumadzulo kwa Ulaya anali ochokera m’mayiko ena.

10. Kodi kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse mwakagwiritsa ntchito motani? (Onani bokosi lakuti “Mbali Zosangalatsa za kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse,” pa tsamba 26.)

10 N’zoona kuti chifukwa cha zovuta zina, ambiri a ife sitingathe kuphunzira chinenero china. Komabe, tingathandize nawo anthu ochokera m’mayiko ena mwa kugwiritsa ntchito bwino kabuku komwe katulutsidwa kumene kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse! * Kabuku kameneka kali ndi uthenga wogwira mtima wa m’Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana. (Yohane 4:37) Kodi mukugwiritsa ntchito kabuku kamene mu utumiki?

Ngati Anthu Sakulabadira

11. Kodi ndi vuto lina liti limene abale akukumana nalo m’madera ena?

11 Pamene Satana akupitiriza kusonkhezera anthu padziko lapansi, mobwerezabwereza tikukumana ndi vuto lina. M’madera ena anthu salabadira kwenikweni uthenga wabwino. Komatu zimenezi sizikutidabwitsa kwenikweni, chifukwa Yesu ananeneratu kuti zoterezi zidzachitika. Ponena za masiku athu ano, iye anati: “Chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.” (Mateyu 24:12) Inde, anthu ambiri aleka kukhulupirira Mulungu ndi kulemekeza Baibulo. (2 Petro 3:3, 4) Zotsatira zake n’zakuti m’mbali zina za dziko lapansi, anthu owerengeka chabe ndiwo akhala ophunzira atsopano a Kristu. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti ntchito ya abale ndi alongo athu okondedwa achikristu omwe akulalikira mokhulupirika m’madera a anthu osalabadirawo ikungopita padera ayi. (Ahebri 6:10) Chifukwa chiyani tikutero? Ganizirani mfundo zotsatirazi.

12. Kodi ntchito yathu yolalikira ili ndi zolinga ziwiri ziti?

12 Uthenga wabwino wa Mateyu umatsindika zolinga ziwiri zikuluzikulu za ntchito yathu yolalikira. Cholinga chimodzi ndicho ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19) Cholinga china n’chakuti uthenga wa Ufumu ukhale “mboni.” (Mateyu 24:14) Zolinga zonsezi n’zofunika, koma chomalizachi chili ndi tanthauzo lapadera. Chifukwa chiyani?

13, 14. (a) Kodi mbali yapadera ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Kristu ndi iti? (b) Kodi tizikumbukira chiyani, makamaka pamene tikulalikira m’madera amene anthu salabadira kwenikweni?

13 Wolemba Baibulo Mateyu analemba kuti atumwi anafunsa Yesu kuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu ananena kuti mbali yapadera ya chizindikiro chimenecho idzakhala ntchito yolalikira padziko lonse lapansi. Kodi iye ankanena za kupanga ophunzira? Ayi. Iye anati: ‘Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:14) Ndi mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti ntchito yolalikira za Ufumu payokha idzakhala mbali yofunika ya chizindikirocho.

14 Choncho, pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, timakumbukira kuti ngakhale kuti sitikuphula kanthu pamene tikuyesetsa kupanga ophunzira, koma ‘umboni’ wokha ndiye tikuupereka ndithu. Mulimonse mmene anthu angalabadirire, mfundo ndi yakuti akudziwa zimene tikuchita, ndipo mwa kutero tikukwaniritsa nawo ulosi wa Yesu. (Yesaya 52:7; Chivumbulutso 14:6, 7) Jordy, Mboni yachinyamata ya kumadzulo kwa Ulaya, anati: “Zimandisangalatsa kwambiri kudziwa kuti Yehova akundigwiritsa ntchito kutenga nawo mbali pa kukwaniritsa lemba la Mateyu 24:14.” (2 Akorinto 2:15-17) Sitikukayika kuti inunso mukumva chimodzimodzi.

Akamatiletsa Kulalikira Uthenga Wathu

15. (a) Kodi Yesu anachenjezeratu otsatira ake za chiyani? (b) N’chiyani chimatithandiza kuti tizilalikirabe ngakhale pamene ntchito yathu yaletsedwa?

15 Vuto lina limene limakhalapo pa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndilo kutsutsidwa kwambiri. Yesu anachenjezeratu otsatira ake kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Mofanana ndi Akristu oyambirirawo, otsatira a Yesu masiku ano amadedwa, kutsutsidwa, ndi kuzunzidwa. (Machitidwe 5:17, 18, 40; 2 Timoteo 3:12; Chivumbulutso 12:12, 17) M’mayiko ena, boma linaletsa ntchito yawo. Komabe, pomvera Mulungu, Akristu oona m’mayiko amenewo akupitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Amosi 3:8; Machitidwe 5:29; 1 Petro 2:21) N’chiyani chomwe chimawathandiza komanso kuthandiza Mboni zonse padziko lapansi kuchita zimenezi? Kudzera mwa mzimu wake woyera, Yehova amawapatsa mphamvu.​—Zekariya 4:6; Aefeso 3:16; 2 Timoteo 4:17.

16. Kodi Yesu anasonyeza motani kugwirizana pakati pa ntchito yolalikira ndi mzimu wa Mulungu?

16 Yesu anasonyeza kugwirizana kwa mzimu wa Mulungu ndi ntchito yolalikira pamene anauza otsatira ake kuti: ‘Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:8; Chivumbulutso 22:17) Ndondomeko ya zochitika m’lemba limeneli ili ndi tanthauzo lapadera. Choyamba, ophunzirawo analandira mzimu woyera, ndipo kenako anayamba ntchito yolalikira ya padziko lonse. Mzimu woyera wa Mulungu wokha ndi umene unawapatsa mphamvu kuti athe kupirira pa ntchito yawo yochitira ‘umboni kwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:13, 14; Yesaya 61:1, 2) Chotero moyenerera, Yesu anatcha mzimu woyera kuti “Nkhoswe” kapena kuti mthandizi. (Yohane 15:26) Iye ananena kuti mzimu woyera wa Mulungu udzaphunzitsa ndi kutsogolera ophunzira akewo.​—Yohane 14:16, 26; 16:13.

17. Kodi mzimu woyera umatithandiza motani pamene tikutsutsidwa kwambiri?

17 Kodi mzimu wa Mulungu umatithandiza motani masiku ano pamene akutiletsa mwamphamvu ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino? Mzimu wa Mulungu umatilimbikitsa, ndipo umatsutsana ndi omwe akutizunzawo. Mwachitsanzo, ganizirani zomwe zinachitika m’moyo wa Mfumu Sauli.

Kutsutsidwa ndi Mzimu wa Mulungu

18. (a) Kodi ndi kusintha koipa kotani kumene Sauli anachita? (b) Kodi Sauli anagwiritsa ntchito njira zotani pozunza Davide?

18 Chiyambi cha Sauli, monga mfumu yoyamba ya Israyeli chinali chabwino, koma pambuyo pake sanamvere Yehova. (1 Samueli 10:1, 24; 11:14, 15; 15:17-23) Zotsatira zake zinali zakuti mzimu wa Mulungu sunalinso kuthandiza mfumuyi. Sauli anakwiyira Davide ndipo anam’chitira zachiwawa. Koma Davide anali atadzozedwa monga wolowa ufumuwo ndipo panthawiyi mzimu wa Mulungu unali kumuthandiza. (1 Samueli 16:1, 13, 14) Davide ankaoneka ngati wosavuta kumugonjetsa. Ndiponso iye analibe chida chilichonse koma zeze yekha, pamene Sauli anali ndi mkondo. Choncho tsiku lina Davide akuimba zeze, “Sauli anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kum’phatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake.” (1 Samueli 18:10, 11) Pambuyo pake, Sauli anamvera mwana wake Jonatani, yemwe anali bwenzi la Davide, ndipo analumbira kuti: “Pali Yehova, sadzaphedwa iye [Davide].” Koma kenako, Sauli anayambanso kufuna “kupyoza Davide kum’phatikiza kukhoma ndi mkondowo.” Komabe, Davide “anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma.” Davide anathawa, koma Sauli anamulondola. Panthawi yovuta imeneyi, mzimu wa Mulungu unali kutsutsana ndi Sauli. Motani?​—1 Samueli 19:6, 10.

19. Kodi mzimu wa Mulungu unateteza motani Davide?

19 Davide anathawira kwa mneneri Samueli, koma Sauli anatumiza anyamata ake kuti akagwire Davide. Ndipo atafika komwe Davide anali kubisala, “mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Sauli, ninenera iyonso.” Mzimu wa Mulungu unawagwera mwamphamvu mwakuti anaiwaliratu cholinga cha ulendo wawo. Sauli anatumiza anyamata ake kuti akagwire Davide maulendo enanso awiri, ndipo maulendo onsewa panachitika zofananazo. Pamapeto pake, Mfumu Sauli inapita yokha kwa Davide, koma Sauli nayenso sanathe kulimbana ndi mzimu wa Mulungu. Ndipotu, mzimu woyerawo unamulepheretsa kuyenda “usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse,” mwakuti Davide anali ndi mpata wokwanira wothawa.​—1 Samueli 19:20-24.

20. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhani ya Sauli pamene anali kuzunza Davide?

20 Nkhani imeneyi ya Sauli ndi Davide ikutipatsa phunziro lolimbikitsa lakuti: Ozunza atumiki a Mulungu sangapambane mzimu wa Mulungu ukamawatsutsa. (Salmo 46:11; 125:2) Yehova ankafuna kuti Davide adzakhale mfumu ya Israyeli. Palibe amene akanasintha zimenezo. M’masiku athu ano, Yehova akufuna kuti ‘uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe.’ Palibe amene angaletse kuti zimenezi zisachitike.​—Machitidwe 5:40, 42.

21. (a) Kodi otsutsa ena masiku ano amatani? (b) Kodi ndife otsimikiza mtima za chiyani?

21 Atsogoleri ena azipembedzo ndi andale amagwiritsa ntchito mabodza ngakhalenso chiwawa poyesa kulepheretsa ntchito yathu. Komabe, monga momwe Yehova anatetezera Davide mwauzimu, akutetezanso anthu ake mofananamo lerolino. (Malaki 3:6) Choncho, monga Davide, tikunena ndi chidaliro kuti: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa; Munthu adzandichitanji?” (Salmo 56:11; 121:1-8; Aroma 8:31) Ndi thandizo la Yehova, tipitirizetu kupirira mavuto onse pamene tikugwira ntchito imene Mulungu watipatsa yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu a mitundu yonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani bokosi lakuti “Akukhutira Kwambiri ndi Utumiki Wawo,” pa tsamba 22.

^ ndime 10 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani timasinthasintha njira zolalikirira?

• Kodi “khomo lalikulu” limene latseguka ndi lolowera ku magawo atsopano ati?

• Kodi ntchito yathu yolalikira ikukwaniritsa chiyani, ngakhale m’madera omwe anthu salabadira kwenikweni?

• N’chifukwa chiyani otsutsa sangaletse ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 22]

Akukhutira Kwambiri ndi Utumiki Wawo

“Ndi achimwemwe ndipo akusangalala kutumikira Yehova mogwirizana.” Mawu amenewa akunena za banja linalake limene linasamuka ku Spain, kupita ku Bolivia. Mwana wamwamuna wa m’banja limeneli anapita kumeneko kukathandiza gulu lakutali. Makolo ake anachita chidwi ndi chimwemwe chimene anali nacho, mwakuti posakhalitsa, banja lonse kuphatikizapo anyamata anayi azaka zakubadwa zoyambira 14 mpaka 25, anapita kukatumikira kumeneko. Tikunena pano, atatu mwa anyamata amenewa akuchita upainiya, ndipo amene anatsogolera uja, posachedwapa anali ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki.

Angelica wa zaka 30 wochokera ku Canada, koma akutumikira kummawa kwa Ulaya, anati: “Ndimakumana ndi mavuto ambiri, koma ndikamathandiza anthu mu utumiki ndimakhala wokhutira. Ndimakhudzikanso mtima kumva mawu ambiri oyamikira kuchokera kwa Mboni za komwe kuno zomwe nthawi zonse zimandithokoza chifukwa chobwera kuno kudzawathandiza.”

Atsikana awiri apachibale a zaka pafupifupi 30, a ku United States, omwe akutumikira ku Dominican Republic, anati: “Tinafunika kuzolowera miyambo yosiyanasiyana. Komabe, tinapitiriza utumiki wathu, ndipo tsopano Ophunzira Baibulo athu asanu ndi awiri amafika pa misonkhano.” Atsikana awiri apachibale amenewa anathandiza kwambiri kugwirizanitsa gulu la ofalitsa Ufumu m’tauni ina kumene kulibe mpingo.

Laura, mlongo wa zaka pafupifupi 30, watumikira m’dziko lina kwa zaka zoposa zinayi. Iye akuti: “Mwa kufuna kwanga, ndimakhala moyo wosafuna zambiri. Zimenezi zathandiza ofalitsa kuona kuti munthu angakhale moyo wosalira zambiri, osati chifukwa cha umphawi, koma chifukwa cha kufuna kwake komanso chifukwa chakuti anaganizira bwino. Kuthandiza ena, makamaka achinyamata, kwandipatsa chimwemwe chimene chafafaniza mavuto omwe ndakumana nawo potumikira m’dziko lina. Utumiki umene ndikuchita kuno sindingausinthanitse ndi moyo uliwonse, ndipo Yehova akalola ndipitirizabe kutumikira kuno.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 26]

Mbali Zosangalatsa za Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse

Kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse, kali ndi uthenga wokwana tsamba limodzi umene uli m’zinenero zosiyanasiyana zokwana 29. Uthengawo walembedwa ngati kuti ndinu amene mukulankhula. Choncho mwininyumba akawerenga uthengawo, adzamva ngati kuti inuyo mukulankhula kwa iye.

M’kati mwake mwa chikuto muli mapu a dziko lonse. Gwiritsani ntchito mapu amenewa monga poyambira kukambirana ndi mwininyumba. Mwina mungaloze dziko limene mukukhala ndi kum’sonyeza kuti mukufuna kudziwa kumene iye anachokera. Mwa kutero, mungam’limbikitse kulankhula ndipo pangakhale ubwenzi komanso kumasukirana.

Mawu oyamba a kabukuka akutchula njira zosiyanasiyana za mmene tingathandizire mogwira mtima anthu olankhula chinenero chimene ife sitimva. Chonde werengani njira zimenezi bwinobwino, ndipo zitsatireni mosamala.

Pa Za M’katimu pali zinenero komanso chizindikiro cha chinenero chilichonse. Mbali imeneyi idzakuthandizani kudziwa zizindikiro za zinenero zimene zimasindikizidwa m’mathirakiti athu ndi m’zofalitsa zina m’zinenero zosiyanasiyana.

[Chithunzi]

Kodi kabuku kameneka mukukagwiritsa ntchito mu utumiki?

[Zithunzi patsamba 23]

Zofalitsa zathu zofotokoza Baibulo tsopano zikupezeka m’zinenero zoposa 400

GHANA

LAPLAND (SWEDEN)

PHILIPPINES

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Kodi mungakatumikire kumene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri?

ECUADOR

DOMINICAN REPUBLIC