Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Vuto Lija Latha Tsopano”

“Vuto Lija Latha Tsopano”

“Vuto Lija Latha Tsopano”

M’CHAKA cha 2002, Mboni za Yehova zinachita msonkhano wachigawo mu mzinda wa Mbandaka, kumpoto cha kumadzulo m’dziko la Democratic Republic of Congo. Atatulutsa Baibulo la New World Translation la Malemba Achigiriki Achikristu m’chinenero cha Chilingala pa msonkhanowo, anthu anadumpha posangalalira Baibuloli, ndipo ena anagwetsa misozi. Pambuyo pake, anthu anathamangira ku pulatifomu kuti akalionetsetse Baibulo latsopanoli, ndipo anali kufuula kuti: “Basuki, Basambwe,” kutanthauza kuti: “Vuto lija latha tsopano. Achita manyazi.”

N’chifukwa chiyani anthuwa anasangalala chomwechi, nanga mawu amene anali kunenawo ankatanthauzanji? M’madera ena mumzinda wa Mbandaka, Mboni za Yehova zinkalephera kupeza mabaibulo m’chinenero cha Chilingala. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti matchalitchi ankakana kugulitsa mabaibulo kwa Mboni za Yehova. Moti Mboni zikafuna mabaibulo, zinkachita kutuma anthu ena omwe si Mboni kuti akawagulire. Tsopano anali osangalala kwambiri chifukwa chakuti matchalitchi sadzathanso kuwalepheretsa kupeza mabaibulo.

Baibulo latsopanoli lidzapindulitsa anthu ambiri, osati Mboni za Yehova zokha. Mwamuna wina amene anali kumvetsera pulogalamu ya msonkhanowo ali panyumba pake, kudzera m’zokuzira mawu za pa malo amsonkhanowo, analembera ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kuti: “Ndasangalala kwambiri ndi kutulutsidwa kwa Baibulo limeneli. Lidzatithandiza kumvetsa zinthu zambiri. Ine si wa Mboni za Yehova, koma ndikuyembekezera mwachidwi Baibulo limene mwatulutsali.”

Baibulo lonse lathunthu la New World Translation of the Holy Scriptures tsopano likupezeka m’zinenero 33, ndipo la Malemba Achigiriki Achikristu likupezeka m’zinenero zinanso 19, kuphatikizapo Chilingala. Bwanji osafunsa wa Mboni za Yehova mmene mungapezere Baibulo lapamwambali?