Kodi Ziphunzitso Zoona Mungazipeze Kuti?
Kodi Ziphunzitso Zoona Mungazipeze Kuti?
MWAMUNA wina ku Tibet, akuzunguza kawilo kamene analembapo mapemphero. Pamene akuchita zimenezi akukhulupirira kuti mapemphero akewo akubwerezedwa nthawi iliyonse akazunguza kawiloko. Ku India, m’nyumba ina yaikulu muli kachipinda kapadera kochitiramo mapemphero ochedwa puja. Pa mapempherowa amatha kupereka nsembe zofukiza, za maluwa, ndi zinthu zina kwa mafano a milungu yosiyanasiyana, yaimuna ndi yaikazi. Ku Italy, kutali kwambiri ndi ku India, mayi wina m’tchalitchi china chokongola kwambiri akugwadira fano la Mariya, mayi wake wa Yesu, n’kumapemphera atagwira korona.
Mwina inuyo mwadzioneranso nokha kuti chipembedzo chakhudza kwambiri miyoyo ya anthu. Buku lakuti The World’s Religions—Understanding the Living Faith limati, “Kuyambira kale, chipembedzo . . . chakhala mbali yofunika kwambiri kwa anthu padziko lonse.” Nalonso buku lakuti God—A Brief History, lolembedwa ndi John Bowker limati: “Sikunakhalepo mtundu wa anthu umene Mulungu sanali mbali yaikulu ya moyo wawo, makamaka mbali yoyendetsa zinthu ndi ya kulenga. Izi zili choncho ngakhale kwa anthu amene amati alibe chipembedzo.”
Zoonadi, chipembedzo chimakhudza miyoyo ya anthu ambirimbiri. Kodi uwu si umboni wamphamvu wakuti anthufe timafunika zinthu zauzimu ndiponso timazilakalaka kwambiri? Dokotala wina wotchuka wa zamaganizo, Dr. Carl G. Jung, m’buku lake lakuti The Undiscovered Self ananena za mtima umene anthufe tili nawo, wofuna kupembedza wina wake wamphamvu kwambiri kuti, “mtima umenewu umaonekera m’mbiri yonse ya anthu.”
Komabe anthu ambiri amati sakhulupirira Mulungu ndipo zachipembedzo alibe nazo ntchito.
Ambiri amene amakayikira kapena kutsutsa zoti kuli Mulungu amatero makamaka chifukwa chakuti zipembedzo zimene amazidziwa bwino zalephera kukwaniritsa zosowa zawo zauzimu. Dikishonale ina imati mawu akuti chipembedzo amatanthauza “kudzipereka pa mfundo zinazake, kukhulupirika kwambiri, kuchita zinthu mosanyalanyaza chikumbumtima chako, ndi kufuna kukhala wabwino kwambiri.” Malinga ndi tanthauzo limeneli, pafupifupi aliyense ali ndi mtundu winawake wachipembedzo pa moyo wake. Izi zikuphatikizapo ngakhale anthu amene amati kulibe Mulungu.Pa zaka masauzande angapo zimene anthu akhala padziko pano, akhala akuyesayesa kukwaniritsa zosowa zawo zauzimu mwa njira zosiyanasiyana. Zotsatira zake n’zakuti padziko lapansili tsopano pali mfundo zosiyanasiyana zachipembedzo. Mwachitsanzo, ngakhale kuti pafupifupi zipembedzo zonse zimalimbikitsa anthu kukhulupirira kuti pali winawake wamphamvu kwambiri, zimasiyana maganizo pankhani yakuti kodi iyeyo ndani kapena ndi chiyani? Komanso, zipembedzo zambiri zimalimbikira kuphunzitsa za chipulumutso kapena kuwomboledwa. Koma ziphunzitso zawo zimasiyana pa tanthauzo la chipulumutso ndi mmene anthu angadzapulumukire. Pa zikhulupiriro zambirimbiri chotere, kodi tingadziwe bwanji ziphunzitso zoona zimene zimakondweretsa Mulungu?