Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sanasiye Chikhulupiriro Chawo”

“Sanasiye Chikhulupiriro Chawo”

“Sanasiye Chikhulupiriro Chawo”

YESU Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.” (Mateyu 5:11) Potsatira chiphunzitso cha Kristu ndi chitsanzo chake, Mboni za Yehova masiku ano ndi zosangalala kwambiri chifukwa sizili mbali ya dziko, ndiponso sizilowerera m’zandale ngakhale pang’ono. Izo ndi zokhulupirika kwa Mulungu zivute zitani.​—Yohane 17:14; Mateyu 4:8-10.

M’dziko limene kale linali Soviet Union ndiponso m’dziko la Estonia, Mboni za Yehova zinali zolimba kwambiri pa chikhulupiriro chawo. Katswiri wina wa maphunziro apamwamba a zaumulungu wa tchalitchi cha Lutheran, yemwenso anamasulirapo Baibulo dzina lake Toomas Paul, analemba nkhani yokhudza kukhulupirika kwawoko m’buku lake lakuti Kirik keset küla (Tchalitchi cha Pakati pa Mudzi) kuti: “Ndi anthu ochepa chabe amene anamvapo zimene zinachitika m’mawa pa April 1, 1951. Boma linakonza zothamangitsa Mboni za Yehova ndi anthu onse ogwirizana nazo. Choncho, anthu okwana 279 anagwidwa ndi kutumizidwa ku Siberia . . . Anthuwa anapatsidwa mwayi wosaina chikalata chosiya chikhulupiriro chawo poopa kuthamangitsidwa kapena kumangidwa. . . . Onse pamodzi ndi ena amene anali atamangidwa kale, analipo 353 kuphatikizaponso 171 amene anali kungosonkhana nawo chabe m’mipingo ya Mboni. Koma iwo sanasiye chikhulupiriro chawo ngakhale ku Siberia komwe anawathamangitsirako. . . . Ndi anthu ochepa chabe a Tchalitchi [cha Lutheran cha ku Estonia] amene anali ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Mboni za Yehova.”

Mboni za Yehova padziko lonse zimadalira Mulungu kuti azithandiza kukhalabe zokhulupirika kwa iyeyo ndi zomvera ngakhale pamene zikuzunzidwa. Zimasangalala podziwa kuti mphoto ya kukhulupirika kwawo ndi yaikulu.​—Mateyu 5:12.