Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu

Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu

Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu

KUTI anthufe padziko pano tidziwe ziphunzitso zimene zili zoona ndiponso zokondweretsa Mulungu, iye ayenera kutiuza maganizo ake. Ayeneranso kukonza njira yakuti anthu tonse tithe kudziwa maganizo akewo. Kodi tingadwiwe bwanji kapembedzedwe ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo popanda iyeyo kutiuza? Kodi Mulungu watipatsa maganizo akewo? Ngati ndi choncho, kodi wachita zimenezi motani?

Kodi n’zotheka kuti munthu amene amakhala moyo zaka makumi ochepa chabe akhale njira ya Mulungu youzira anthu onse padziko lapansi zimene iye amafuna? Ayi. Koma maganizo a Mulunguwo atalembedwa ndiye zingatheke kuti afike kwa anthu onse. Choncho, kodi si koyenera kuti maganizo a Mulungu alembedwe m’buku? Buku limodzi lakale kwambiri limene limanena lokha kuti linalembedwa mouziridwa ndi Mulungu ndilo Baibulo. Wina amene analemba nawo bukuli anati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Tiyeni tiliunike bwino Baibulo kuti tione ngati lilidi maziko a ziphunzitso zoona.

Kodi Linalembedwa Liti?

Pa mabuku onse akuluakulu a zipembedzo, Baibulo ndi limodzi mwa mabuku akale kwambiri. Mbali zoyambirira za bukuli zinalembedwa zaka 3,500 zapitazo. Bukuli linamalizidwa mu 98 C.E. * Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa ndi amuna 40 pa zaka 1,600, nkhani zake ndi zogwirizana. Izi zili choncho chifukwa Mlembi wake weniweni ndi Mulungu.

Baibulo ndi buku lofala kwambiri ndipo lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse. Chaka chilichonse, mabaibulo 60 miliyoni kapena zigawo zake amagawidwa kwa anthu. Baibulo lathunthu kapena zigawo zake zamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 2,300. Anthu oposa 90 mwa anthu 100 aliwonse padziko lapansi pano akhoza kupeza Baibulo, kapena chigawo chake m’chilankhulo chawo. Malire a mayiko, kusiyana kwa mitundu ndi mafuko sizinalepheretse bukuli kufala.

Kodi Linakonzedwa Motani?

Ngati muli ndi Baibulo, litseguleni muone mmene analikonzera. Choyamba tsegulani patsamba losonyeza zimene zili m’katimo. Mabaibulo ambiri ali ndi tsamba limeneli kumayambiriro kwake. Patsambali pali mayina a mabuku onse ndiponso tsamba limene payambira bukulo. Mungaone kuti kwenikweni Baibulo linapangidwa ndi mabuku osiyanasiyana, ndipo buku lililonse lili ndi dzina lake. Buku loyamba ndi Genesis ndipo lomaliza ndi Chivumbulutso. Mabukuwa ali m’zigawo ziwiri. Mabuku 39 oyambirira amatchedwa Malemba Achihebri chifukwa chakuti ambiri analembedwa m’chinenero cha Chihebri. Mabuku 27 otsalawo analembedwa m’Chigiriki ndipo amatchedwa Malemba Achigiriki. Anthu ena amatcha zigawo ziwirizi kuti Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano.

Mabuku a m’Baibulo ali ndi machaputala ndiponso mavesi kuti tisamavutike kupeza pamene tikufuna. M’magazini ino, malemba a m’Baibulo amalembedwa motere: Timayamba ndi dzina la buku la m’Baibulo, kenako nambala imene imaimira chaputala cha bukulo, ndipo nambala yachiwiri imaimira vesi lake. Mwachitsanzo tikalemba kuti “2 Timoteo 3:16,” tikutanthauza buku la Timoteo Wachiwiri, chaputala 3, vesi 16. Tayesani kupeza vesi limeneli m’Baibulo.

Kuti mulidziwe bwino Baibulo, njira yabwino kwambiri ndiyo kuliwerenga nthawi zonse. Ena aona kuti ndi bwino kuyamba ndi kuwerenga Malemba Achigiriki, kuyambira buku la Mateyu. Mutati muziwerenga machaputala atatu mpaka asanu patsiku, mungathe kuwerenga Baibulo lonse chaka chimodzi. Koma kodi mungatsimikize bwanji kuti zimene mumawerenga m’Baibulo zinalembedwa mouziridwadi ndi Mulungu?

Kodi Mungalikhulupirire Baibulo?

Kodi buku la anthu onse louziridwa ndi Mulungu siliyenera kukhala ndi malangizo ogwira ntchito kwa anthu a mibadwo yonse ofotokoza mmene tingakhalire ndi moyo? Baibulo limasonyeza kuti mlembi wake amamvetsetsa chikhalidwe cha anthu a mibadwo yonse. Mfundo zake zimagwirabe ntchito masiku ano monga mmene zinkagwirira ntchito poyamba. Mfundo imeneyi imaonekera bwino mu ulaliki wotchuka wa munthu amene anayambitsa Chikristu, Yesu Kristu. Ulaliki umenewu unalembedwa m’machaputala 5 mpaka 7 a buku la Mateyu. Ulalikiwu umatchedwa ulaliki wa paphiri. Umatiuza mmene tingapezere chimwemwe chenicheni, mmene tingathetsere mikangano, mmene tingapempherere, ndiponso umatipatsa maganizo abwino a mmene tiyenera kuonera zofunika pamoyo ndi zina zambiri. Mu ulaliki umenewu ndi m’mbali zina zonse, Baibulo limatiuza momveka bwino zimene tiyenera kuchita ndi zimene sitiyenera kuchita kuti tikondweretse Mulungu ndi kuti tikhale ndi moyo wabwino.

Chifukwa china chimene mungakhulupirire Baibulo n’chakuti buku la makedzana limeneli limanena zoona zokhazokha pankhani za sayansi. Mwachitsanzo, panthawi imene anthu ambiri ankakhulupirira kuti dziko lapansi ndi lafulati, Baibulo linanena za “malekezero [kapena mbulunga] a dziko lapansi.” * (Yesaya 40:22) Komanso, zaka zoposa 3,000 wasayansi wotchuka Sir Isaac Newton asanafotokoze kuti mapulaneti anangokhala m’malere chifukwa cha mphamvu yokoka, Baibulo linali litanena kale mwa ndakatulo kuti ‘dziko linalenjekeka pachabe.’ (Yobu 26:7) Taganiziraninso mmene Baibulo linalongosolera kusintha kwa madzi kuchoka padziko n’kukapanga mitambo ndi kudzagwa monga mvula. Zimenezi zinalembedwa mwa ndakatulo zaka 3,000 zapitazo kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” (Mlaliki 1:7) Inde, Mlengi wa zakuthambo ndiyenso Mlembi wa Baibulo.

Mfundo ina yotsimikizira kuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu ndi yakuti limanena zoona zokhazokha za mbiri yakale. Zochitika zolembedwa m’Baibulo si nthano chabe. Zimakhudza masiku enieni, anthu enieni ndiponso malo enieni. Mwachitsanzo, lemba la Luka 3:1 limanena zenizeni potchula “chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya.”

Anthu ambiri olemba mbiri yakale nthawi zambiri ankangolemba za kupambana kwa mafumu awo ndiponso zabwino zimene anachita. Koma olemba Baibulo anali oona mtima, ndipo anavomereza poyera ngakhale zolakwa zawo. Mwachitsanzo, Mfumu Davide ya Israyeli inavomereza kulakwa kwake kuti: “Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; . . . ndinachita kopusa ndithu.” Mawu amenewa analembedwa moona mtima m’Baibulo. (2 Samueli 24:10) Mose, amene analemba nawo Baibulo analembanso nkhani inayake yosonyeza kuti iyeyo pa nthawi ina sanadalire Mulungu woona.​—Numeri 20:12.

Palinso umboni wina wotsimikizira kuti Baibulo linalembedwa mouziridwa ndi Mulungu. Umboni wake ndi wakuti, maulosi kapena kuti zinthu zimene zinalembedwa zisanachitike, zimakwaniritsidwa. Ena mwa maulosi amenewa ndi onena za Yesu Kristu. Mwachitsanzo, zaka zoposa 700 Yesu asanabadwe, Malemba Achihebri ananeneratu molondola kuti Wolonjezedwa Ameneyu adzabadwira “m’Betelehemu wa Yudeya.”​—Mateyu 2:1-6; Mika 5:2.

Taonani chitsanzo china. Pa 2 Timoteo 3:1-5, Baibulo limati: “Masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” Kodi mawuwa sakufotokoza bwino mmene anthu ambiri alili masiku ano? Mawu amenewa analembedwa m’chaka cha 65 C.E., zaka zoposa 1,900 zapitazo.

Kodi Baibulo Limatiphunzitsa Chiyani?

Powerenga Baibulo, mudzaona kuti ndi chitsime cha nzeru zapamwamba. Limapereka mayankho okhutiritsa pa mafunso monga akuti: Kodi Mulungu ndani? Kodi Mdyerekezi ndi weniweni? Kodi Yesu Kristu ndani? N’chifukwa chiyani timavutika? Ndiponso, kodi chimatichitikira n’chiyani tikamwalira? Anthu ena angayankhe mafunsowa mosiyanasiyana malinga ndi zikhulupiriro ndiponso miyambo yawo. Koma Baibulo limanena choonadi pankhani zimenezi ndi pankhani zinanso zambiri. Kuwonjezera apo, Baibulo lili ndi malangizo abwino kwambiri a mmene tiyenera kukhalira ndi anzathu ndi mmene tiyenera kuonera olamulira. *

Kodi Baibulo limati Mulungu ali ndi cholinga chotani kwa anthu ndi dziko lapansi? Limalonjeza kuti: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) “Mulungu yekha adzakhala [ndi anthu], Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29.

Baibulo linaneneratunso kuti nkhondo, umbanda, ziwawa, ndi zoipa zonse zidzatha posachedwapa. Matenda, ukalamba, ndi imfa sizidzakhalakonso. Moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso udzakhala wotheka. Kodi chimenechi si chiyembekezo chosangalatsa? Zonsezitu zikutsimikizira chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa anthu.

Kodi Muchita Chiyani Tsopano?

Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu. Kodi muyenera kutani nalo bukuli? Munthu wina wa Chihindu amakhulupirira kuti uthenga wochokera kwa Mulungu umene anaupereka kalekale anthu atangoyamba kukhala padziko lapansi ndi umene ungakhale wopindulitsa kwa anthu onse. Atadziwa kuti mbali zina za Baibulo n’zakale kwambiri kuposa malemba akale a Chihindu otchedwa Vedas, anaganiza zoliwerenga Baibulo ndi kuunika zimene limanena. * Mphunzitsi wina wa ku yunivesite ku United States anaonanso kuti ndi bwino kuliwerenga buku lofalitsidwa kwambiri limeneli mmalo mongokhala ndi maganizo akeake pa za bukuli.

Mukamawerenga Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zimene limaphunzitsa, mudzapeza madalitso ambiri. Baibulo limati: “Wodala munthuyo . . . [amene] m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” * (Salmo 1:1-3) Kuwerenga Baibulo ndi kuganizira mofatsa zimene limanena kudzakupatsani chimwemwe chifukwa mwa kutero mudzakhutira mwauzimu. (Mateyu 5:3) Baibulo lidzakuphunzitsani mmene mungakhalire ndi moyo wopindulitsa ndiponso mmene mungapiririre mavuto. Inde, ‘m’kusunga [malamulo a Mulungu olembedwa m’Baibulo] muli mphotho yaikulu.’ (Salmo 19:11) Kuwonjezera apo, mukamakhulupirira malonjezo a Mulungu mudzapeza madalitso panopo ndiponso mudzakhala ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo.

Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Lirani monga makanda alero mkaka woyenera [wa mawu], wopanda chinyengo.” (1 Petro 2:2) Khanda limadalira kudyetsedwa ndipo limachita kulilira. Ifenso timadalira nzeru zochokera kwa Mulungu. Chotero, ‘lilirani,’ kapena kuti khalani ndi chilakolako champhamvu cha Mawu ake. Baibulo ndi buku limene lili ndi ziphunzitso zoonadi zochokera kwa Mulungu. Khalani ndi cholinga choliwerenga nthawi zonse. Mboni za Yehova za kwanuko ndi zokonzeka kukuthandizani kuti mupindule kwambiri pophunzira Baibulo. Tikukulimbikitsani kulankhaula nazo, kapena mungalembere kalata ofalitsa a magazini ino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 C.E. amatanthauza “Yesu atabwera.” Kawirikawiri amatchedwa A.D., chidule cha Anno Domini, kutanthauza kuti “m’chaka cha Ambuye wathu.” B.C.E. amatanthauza “Yesu asanabwere.”

^ ndime 13 M’chinenero choyambirira, mawu amene anawamasulira kuti “malekezero” pa Yesaya 40:22 angatembenuzidwenso kuti “mbulunga.” Mabaibulo ena amati, “mbulunga ya dziko lapansi” (Douay Version) komanso “dziko lapansi lobulungira.”​—Moffatt.

^ ndime 19 Nkhani zimenezi zafotokozedwa m’buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

^ ndime 23 Anthu amakhulupirira kuti nyimbo zina zakale kwambiri za mu Vedas zinalembedwa pafupifupi zaka 3,000 zapitazo ndipo anthuwo ankangouzana mwapakamwa kuchokera m’badwo wina kufika m’badwo wina. Koma “Buku la Vedas linalembedwa m’ma 1300 A.D.,” anatero P. K. Saratkumar m’buku lake lakuti A History of India.

^ ndime 24 Yehova ndi dzina la Mulungu wotchulidwa m’Baibulo. M’mabaibulo ambiri dzinali limapezeka pa Salmo 83:18.

[Chithunzi patsamba 7]

Khalani ndi chilakolako cha Mawu a Mulungu. Phunzirani Baibulo nthawi zonse

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

NASA photo