Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Wosangalala

Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Wosangalala

Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Wosangalala

NGAKHALE kuti Baibulo si buku lofotokoza za mankhwala, limalongosola za mmene maganizo abwino kapenanso oipa, amakhudzira thanzi la munthu. Limati: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” Ndiye limapitiriza kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 17:22; 24:10) Maganizo olefula angatifooketse kwambiri, motero tingafike posathanso kudziteteza ndiponso tingasiye kuyesetsa kuthetsa vuto lathu kapena kufuna thandizo.

Kufooka m’njira imeneyi kungathenso kusokoneza munthu mwauzimu. Anthu amene amadziona ngati opanda ntchito nthawi zambiri amaona kuti sangakhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu ndiponso kuti iye sangawadalitse. Simone, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo ija, ankakayikira kuti anali “munthu woti Mulungu angam’konde.” Komabe, tikaona zimene amanena Mawu a Mulungu, Baibulo, timaona kuti anthu amene amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu, iye amawakonda.

Mulungu Amakuganizirani

Baibulo limatiuza kuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” Mulungu sanyoza “mtima wosweka ndi wolapa,” koma amalonjeza “kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.”​—Salmo 34:18; 51:17; Yesaya 57:15.

Panthawi ina Mwana wa Mulungu, Yesu, anaona kuti akufunika kuuza ophunzira ake kuti Mulungu amaona zabwino zimene atumiki Ake amachita. Popereka chitsanzo, iye analongosola kuti Mulungu amaona mpheta imodzi imene yagwa pansi. Koma iyitu si nkhani yaikulu kwa anthu ambiri. Iye anagogomezeranso kuti Mulungu amadziwa zinthu zing’onozing’ono zokhudza anthu, ngakhale kuchuluka kwa tsitsi la m’mutu mwawo. Yesu anamaliza fanizo lakeli ponena kuti: “Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) * Yesu anasonyeza kuti ngakhale munthu atamamva kuti n’ngosafunika, Mulungu amaona kuti anthu onse okhala ndi chikhulupiriro n’ngofunika. Ndipotu mtumwi Petro anatikumbutsa kuti “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Onani Zinthu Moyenerera

Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tizidziona m’njira yoyenerera. Mtumwi Paulo analemba mouziridwa kuti: “Ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.”​—Aroma 12:3.

Indedi, sitiyenera kuganiza kuti ndife ofunika kwambiri mpaka kuyamba kunyada; komanso tisachite kudzitsitsa monyanyira n’kufika pomadziona ngati ndife opanda ntchito. Cholinga chathu chiyenera kukhala chomadziona m’njira yoyenerera moganizira zinthu zimene tingachite ndiponso zimene sitingathe kuchita. Mkristu wina wamkazi ananena mfundo imeneyi motere: “Ndimadziwa kuti sindine munthu woipitsitsa kuposa wina aliyense; koma panthawi yomweyomweyo ndimadziwanso kuti sindine munthu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense. Ndili ndi makhalidwe abwino komanso ndili ndi makhalidwe ena oipa, ndipotu umu ndi mmene aliyense alili.”

Inde, n’zovuta kuona zinthu m’njira yoyenerera yotereyi. Pangafunike khama lalikulu zedi kuti tisiye maganizo omadziona ngati opanda ntchito omwe mwina takhala nawo kwa zaka zambiri. Komabe, mothandizidwa ndi Mulungu tingathe kusintha umunthu wathu ndiponso mmene timaonera zinthu. Kwenikweni, zimenezi n’zimene Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kumachita. Amatiuza kuti: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma . . . mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.”​—Aefeso 4:22-24.

Poyesetsa kusintha “mzimu wa mtima wanu,” kapena kuti, zimene timakonda kuganiza, tingathe kusintha umunthu wathu kusiya kudziona ngati wopanda ntchito n’kuyamba kudziona ngati munthu wofunika. Lena, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo ija, anafika pozindikira kuti akapanda kusiya kuganiza kuti palibe munthu amene angam’konde kapena kum’thandiza, palibe china chilichonse chimene chingam’thandize kusiya kudziona ngati wopanda ntchito. Kodi ndi malangizo abwino ati a m’Baibulo amene anathandiza Lena, Simone, ndi anthu enanso kusintha maganizo awo?

Mfundo za M’Baibulo Zothandiza Kukhala Wosangalala

“Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakugwiriziza.” (Salmo 55:22) Chinthu choyamba ndiponso chofunikira kwambiri chotithandiza kukhaladi osangalala ndicho pemphero. Simone anati: “Nthawi iliyonse ndikalefuka, ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Nthawi zonse ndikamavutika m’njira imeneyi Yehova wakhala akundipatsa mphamvu ndiponso kunditsogolera.” Potilimbikitsa kum’senza Yehova nkhawa zathu, kwenikweni wamasalmo akutikumbutsa kuti Yehova si kuti amangotiganizira chabe, komanso ifeyo patokhapatokha amationa kuti ndife oyenerera kuthandizidwa ndi iyeyo. Pa tsiku la Paskha, usiku, m’chaka cha 33 C.E., ophunzira a Yesu anali achisoni kwambiri chifukwa cha zimene Yesu anawauza kuti posakhalitsa iye asiyana nawo. Yesu anawalimbikitsa kupemphera kwa Atate, ndipo anawonjezera kunena kuti: “Pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.”​—Yohane 16:23, 24.

“Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Monga mmene Yesu anaphunzitsira, kupatsa ndiko njira yokhalira munthu wosangalala m’moyo. Pogwiritsira ntchito mfundo ya m’Baibulo imeneyi, timaganizira kwambiri zofuna za ena osati kumangoganizira zolephera zathu ayi. Tikamathandiza anzathu kenaka n’kuona mmene akuyamikirira thandizolo, timadziona kuti ndife anthu ofunika. Lena sakayikira ngakhale pang’ono kuti kuuza ena uthenga wabwino wa m’Baibulo nthawi zonse, kumam’thandiza m’njira ziwiri. Iye anati: “Njira yoyamba n’njakuti kumandipatsa chimwemwe chimene Yesu anatchula. Yachiwiri n’njakuti anthu ena amayamikira ntchito yangayi, ndipo zimenezi zimandithandiza kukhala wachimwemwe.” Mwa kudzipereka kuti tithandize ena, timaona kuti mawu a pa Miyambo 11:25, n’ngoona. Mawu ake n’ngakuti: “Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”

“Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.” (Miyambo 15:15) Tonsefe timasankha tokha mmene tikufuna kudzionera ndiponso mmene tikufuna kuonera moyo wathu. Tingathe kukhala munthu womangoona zoipa zokhazokha n’kumanyong’onyeka nazo, kapena tingasankhe kumaona mbali yabwino ya zinthu, kukhala “wokondwera mtima,” n’kumasangalala ngati kuti tili pa phwando. Simone anati: “Ndimayesetsa kuti nthawi zonse ndiziona mbali yabwino ya zinthu. Ndimakhala wotanganidwa ndi zinthu monga kuphunzira Baibulo pandekha ndiponso kulowa muutumiki, ndipo ndimalimbikira kupemphera. Ndimayesetsanso kumacheza ndi anthu achimwemwe ndiponso kuthandiza anthu ena.” Mtima woterewu umathandiza munthu kukhaladi wosangalala zenizeni, monga mmene Baibulo limatilimbikitsira kuti: “Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu owongoka mtima.”​—Salmo 32:11.

Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Kuuza mnzathu kapena mlangizi amene timamukhulupirira za vuto lathu kungatithandize kuthetsa maganizo omadziona ngati ndife opanda ntchito moti maganizowa sangachite kufika potifooleratu. Kukambirana ndi anzathu kungatithandize kuona zinthu mosatengeka maganizo, komanso moona mbali yabwino ya zinthu. Simone anavomereza kuti: “Ndimamva bwino kwambiri ndikauzako ena mmene ndikumvera. Pamafunika kuuzako munthu wina mmene mukumvera. Nthawi zambiri kuchita zimenezi n’kumene kumathandiza kwambiri.” Pochita zimenezi mungaone kuti mawu a mwambi wotsatirawu n’ngoona: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.”​—Miyambo 12:25.

Zimene Mungachite

Taonapo mfundo za m’Baibulo zingapo chabe zomwe zili zabwino ndiponso zotithandiza kuti tisamadzione ngati wopanda ntchito ndiponso kuti tikhaledi osangalala. Ngati muli m’gulu la anthu amene akuvutika chifukwa chodziona ngati achabechabe, tikukulimbikitsani kuti muphunzire bwinobwino Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Phunzirani kudziona mmene mulili, kudziona m’njira yoyenerera ndiponso kuona ubwenzi wanu ndi Mulungu m’njira yoyenerera. Tikukhulupirira kuti mukatsatira Mawu a Mulungu, mukhaladi wosangalala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mbali ya Malemba imeneyi tailongosola mwatsatanetsatane pa tsamba 22 ndi tsamba 23.

[Chithunzi patsamba 7]

Kutsatira mfundo za m’Baibulo kumathandiza munthu kuti akhale wachimwemwe