Kodi Mumadziona Ngati Munthu Wopanda Ntchito?
Kodi Mumadziona Ngati Munthu Wopanda Ntchito?
MBALI yaikulu ya moyo wake, Lena wakhala akudziona ngati munthu wosafunika kwenikweni. Iye anati: “Ndinagwiriridwa kwa zaka zambiri ndili mwana motero sindinkadzionanso ngati munthu waulemu wake. Ndinkangodziona ngati munthu wotha ntchito.” Simone nayenso amakumbukira zimene zinkamuchitikira ali mwana ndipo anati: “Mumtima mwanga ndinkangoona kuti ndine wachabechabe ndiponso kuti ndilibe ntchito kwenikweni.” Chifukwa cha maganizo oterewa zikuoneka kuti masiku ano anthu ambiri sakhala osangalala ngakhale pang’ono. Bungwe lina lolangiza achinyamata patelefoni, linanena kuti pafupifupi theka la achinyamata amene amaimba telefoni ku bungweli, amanena kuti “maganizo akuti iwowo ndi munthu wopanda ntchito sawachokera ayi.”
Akatswiri ena anati munthu amayamba kudziona kuti ndi wopanda ntchito chifukwa cha zinthu zomupeputsa zimene anthu ena amam’chitira. Munthu angakhale ndi maganizo oterewa chifukwa chomangokhalira kunenedwa, kunyozedwa, kapenanso kutukwanidwa.
Zifukwa zimenezi kapena zinanso zingafooketse munthuyo mwinanso kum’pweteketsa kumene. Atafufuza a zachipatala posachedwapa anapeza kuti anthu amene sadziona ngati kanthu nthawi zambiri sadzikhulupirira ndiponso sakhulupirira ena, motero amalephera kugwirizana bwinobwino ndi abale awo kapenanso anzawo, ngakhale kuti sichikhala cholinga chawo kutero. Lipotilo linati, “Tingati, kwenikweni anthuwa ‘amayambitsa’ okha mavutowa omwenso ali mavuto amene amawaopa kwambiri.”Anthu amene amamva choncho mumtima mwawo nthawi zambiri amakhala kuti akuvutika ndi zimene Baibulo limati “nkhawa” zawo. (Salmo 94:19 [93:19, Malembo Oyera]) Amadziona kuti n’ngosakwanira pa china chilichonse. Zinazake zikalakwika, amangothamangira kuganiza kuti zalakwika chifukwa cha iwowo. Ngakhale anzawo awayamikire pa zimene achita, iwo mu mtima mwawo amadziona ngati munthu wachinyengo ndipo kuti tsiku lina adzaululika. Chifukwa chokhulupirira kuti si oyenera kukhala osangalala, ambiri amalowa m’mavuto aakulu owapweteketsa amene amalephera kuchokamo. Lena, amene tam’tchula poyamba uja anayamba kudwala matenda ovutika kudya chifukwa chodziona ngati munthu wachabechabe, ndipo anavomereza kuti: “Ndinkaona kuti palibe chimene ndingachitepo pa matendawa.”
Kodi anthu amene amavutika ndi “nkhawa” zimenezi sangadzakhalenso bwinobwino mpakana kalekale? Kodi pali chilichonse chimene iwowo angachite kuti alimbane ndi maganizo oterewa? Baibulo limatchula mfundo ndiponso malangizo amene athandiza anthu ambiri okhala ndi vutoli. Kodi zina mwa mfundo zimenezi n’ziti, ndipo kodi zathandiza bwanji anthuwa kukhala osangalala m’moyo wawo? Nkhani yotsatirayi ilongosola zimenezi.