Ulendo Wautali Wopindulitsa
Ulendo Wautali Wopindulitsa
KU Democratic Republic of Congo, mlongo wina ndi mng’ono wake anaganiza zoyenda ulendo wautali m’dera lankhondo kuti akakhale nawo pa Msonkhano Wachigawo wa “Patsani Mulungu Ulemerero” womwe unachitikira ku Lisala. Iwowa anapita kumsonkhanowu kuti akamve nawo malangizo auzimu, akacheze ndi Akristu anzawo, komanso kuti akakumaneko ndi abale oimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yomwe ili ku Kinshasa. Chifukwa cha nkhondo ya pachiweniweni m’dzikolo, kwa zaka zambiri, alongowa anali asanakumanepo ndi munthu aliyense wa kunthambi, motero anaganiza zotengerapo mwayi pamsonkhanowu.
Alongo awiriwa anayenda pa bwato m’mitsinje iwiri kudutsa m’nkhalango kuchokera kwawo ku Basankusu kukafika ku Lisala. Uwu ndi ulendo wautali makilomita 300, ndipo anauyenda kwa milungu itatu. Alongowa akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse, mmodziyo kwa zaka zitatu ndipo winayo kwa zaka 19, motero anatengerapo mwayi pa ulendowu kuti afalitse uthenga wabwino wa Ufumu. Anatha maola okwana 110 akulalikira kwa anthu amene anakumana nawo m’njira, ndipo anagawira mathirakiti 200 ndi magazini 30.
Mumtsinjewo, iwo anayenera kuyenda mosamala chifukwa m’derali mumakonda kupezeka mvuu ndi ng’ona. Sakanatha kuyenda mumtsinjewo usiku, chifukwa zinali zosatheka. Komanso anadutsa malo ambiri okhala ndi asilikali ofufuza anthu amene ali paulendo.
Ngakhale kuti ulendowu unali wautali ndiponso wotopetsa, alongowa anasangalala chifukwa cha khama lawoli. Onse awiri anali oyamikira kwambiri kuti anakapezeka kumsonkhanowo ku Lisala. Anali ofunitsitsa zedi kuti akamve choonadi, ndipo anatsitsimulidwa posonkhana limodzi ndi abale ndiponso alongo 7,000 amene anali pamsonkhanopo. Msonkhanowo utatha, anakumana ndi mavuto omwewo pobwerera kunyumba. Atafika anakapeza kuti achibale awo onse anatsala bwino.