Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amadalitsa Kwambiri Amene Amasunga Njira Yake

Yehova Amadalitsa Kwambiri Amene Amasunga Njira Yake

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Amadalitsa Kwambiri Amene Amasunga Njira Yake

YOSIMBIDWA NDI ROMUALD STAWSKI

Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itayamba mu September 1939, kumpoto kwa dziko la Poland kunali kumenyana kwadzaoneni. Apa n’kuti ine ndili ndi zaka nayini ndipo chifukwa cha chibwana, ndinapita kudera lina lapafupi lomwe ankamenyerako nkhondo kuti ndikadzionere ndekha. Zimene ndinaona kumeneko zinali zosowetsa tulo. Mitembo inangoti mbwee ndipo dera lonselo linali utsi wochita kubanikitsa. Ndili kumeneko ndinkadzifunsa kuti ndibwerera bwanji kunyumba, koma ndinayambanso kudzifunsa mafunso ena monga akuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu akulola zinthu zosautsa ngati zimenezi? Kodi Mulunguyo ali mbali iti pankhondoyi?”

NKHONDOYI itatsala pang’ono kutha, boma la dziko la Germany linayamba kukakamiza ntchito achinyamata. Aliyense woyerekeza kukana ankam’pachika pamtengo kapena pa mlatho n’kumuika chizindikiro pachifuwa pake atalembapo kuti “woukira” kapena “wosokoneza.” Tauni yakwathu, yotchedwa Gdynia, inali pakatikati pa magulu awiri ankhondo amene anali kumenyanawo. Tikatuluka m’tauniyi kuti tikatunge madzi kwina, zipolopolo zinkachita kutiphuluza m’mutu, ndipo tsiku lina mng’ono wanga Henryk chipolopolo chinamuwomba, n’kufa. Chifukwa cha kuipa kwa zinthuku, mayi anga anatisamutsa ana anayi tonsefe kuti tizikagona m’chipinda cha pansi pa nyumba yathu kuti tikhale otetezeka. Mng’ono wanga wa zaka ziwiri, dzina lake Eugeniusz, anafa tikukhala mmenemu chifukwa cha matenda amene ankam’chititsa kuti azibanika.

Apanso ndinadzifunsa kuti: “Kodi Mulunguyo ali kuti? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthu tizivutika chonchi?” Ngakhale kuti ndinali Mkatolika wolimbikira kwambiri ndiponso ndinkapita kopemphera nthawi zonse, sindinayankhidwe mafunso angawa.

Ndinaphunzira Choonadi cha M’Baibulo

Mafunso anga anandiyankha ndi anthu amene sindinkayembekezera n’komwe kuti angandiyankhe. Nkhondo ija inatha mu 1945, ndipo kumayambiriro kwa 1947, munthu wina wa Mboni za Yehova anafika kunyumba kwathu ku Gdynia. Mayi anga anayankhula ndi wa Mboniyo, ndipo ndinamvako zina zimene iyeyo amanena. Zinkaoneka kuti n’zomveka ndithu, motero tinavomera atatiitanira ku misonkhano yachikristu. Patangotha mwezi umodzi wokha, ngakhale kuti ndinali ndisanamvetse bwinobwino choonadi cha m’Baibulo, ndinagwirizana ndi gulu lakwathu la Mboni n’kuyamba kulalikira zakuti kukubwera dziko labwino koposa, lopanda nkhondo ndiponso lopanda zosautsa. Ntchito imeneyi inandithandiza kukhala wosangalala kwambiri.

Mu September 1947, ndinabatizidwa pa msonkhano wadera ku Sopot. Chaka chotsatira m’mwezi wa May, ndinayamba utumiki wa upainiya wokhazikika, kutanthauza kuti nthawi yambiri ndinkalalikira uthenga wa m’Baibulo. Atsogoleri achipembedzo a m’dera lakwathu ankalimbana nafe pantchito yathuyi ndipo anachititsa kuti anthu atiukire n’kumatichitira zachiwawa. Nthawi ina chigulu cha anthu olusa chinatiponya miyala, n’kutimenya zolimba. Panthawi ina, asisitere ndiponso azibusa ena a dera lakwathu anapsepsezera gulu lina la anthu kuti litikhaulitse. Tinathawira ku polisi, koma gululi linazungulira polisiyo, n’kumanena kuti litionetsa zakuda. Mapeto ake panabwera apolisi ena owonjezera, ndipo tinachita kuperekezedwa ndi apolisi ambirimbiri.

Panthawiyi, m’dera lathu munalibe mpingo uliwonse. Nthawi zina tinkakhala usiku wonse tili m’tchire. Tinkasangalala kuti tinkachitabe ntchito yolalikira ngakhale kuti zinthu sizinali bwino. Panopo m’dera limeneli muli mipingo yamphamvu kwambiri.

Kutumikira pa Beteli Kenako Kumangidwa

M’chaka cha 1949, ndinaitanidwa kupita ku Nyumba ya Beteli ku Łódź. Chinali chimwayi chachikulu kwambiri kutumikira pa malo amenewa. Koma tsoka ilo, sindinakhalitsepo. Mu June 1950, patangotsala mwezi umodzi kuti ntchito yathu iletsedwe ndi boma, ineyo ndinamangidwa pamodzi ndi abale ena a pa Beteli. Anandipititsa kundende, ndipo kumeneko anakandifunsa mafunso m’njira yozunza kwambiri.

Pakuti bambo anga ankagwira ntchito m’sitima inayake ya pamadzi imene nthawi zambiri inkapita ku New York, apolisi amene ankafufuza mlandu wangawo anayesa kundikakamiza kuvomereza bodza lakuti bambo anga analembedwa ntchito ya ukazitape ndi dziko la United States. Anandizunza kwadzaoneni pofufuza mlanduwo. Kuphatikizanso apo, apolisi anayi anandipanikiza nthawi imodzi kuti ndinene zinthu zopachikitsa Mbale Wilhelm Scheider, amene panthawiyi anali kuyang’anira ntchito yathu ku Poland. Anandimenya m’zidendene ndi ndodo zazikulu. Ndinagona pansi kwalaa, magazi ali chuchuchu, ndipo ndinkangoti basi kwanga kwatha lero, motero ndinafuula kuti, “Yehova, ndithandizeni chonde!” Asilikali ankandizunzawo anadabwa nazo ndipo anasiya kundimenya. Patangotha mphindi zochepa chabe, onse anagona tulo. Mtima unakhala pansi ndipo mphamvu zinabwereramo. Pamenepa m’pamene ndinadziwira kuti ndithu, Yehova mwachikondi chake amathandiza atumiki ake odzipereka akafuula kwa iye. Zimenezi zinandilimbitsa chikhulupiriro ndipo zinandiphunzitsa kukhulupirira Mulungu mwa mtima wanga wonse.

Pa lipoti lotsiriza lokhudza mlandu wanga analembapo umboni wabodza umene ananama kuti ndinapereka ndine. Nditatsutsa za umboniwo, wapolisi wina anandiuza kuti, “Zimenezo ukanenera kukhoti!” Mkaidi mnzanga wina amene ankamasuka nane anandiuza kuti ndisadandaule, chifukwa chakuti lipoti lotsiriza amayenera kulitsimikizira kaye msilikali wozenga milandu, ndipo pamenepa ineyo ndidzakhala ndi mwayi wotsutsa umboniwo. Izi n’zimene zinachitikadi.

Kuyang’anira Dera ndi Kumangidwanso

Ndinamasulidwa mu January 1951. Patangotha mwezi, ndinakhala woyang’anira woyendayenda. Ngakhale kuti ntchito yathu inali yoletsedwa, ineyo pamodzi ndi abale ena tinalimbikitsa mipingo ndi kuthandiza a Mboni anzathu amene anabalalitsidwa chifukwa cha apolisi. Tinalimbikitsa abale kuti apitirize kuchita utumiki. M’zaka za patsogolo pake, abale amenewa analimba mtima pothandiza oyang’anira oyendayenda ndipo anachita mobisa ntchito yosindikiza ndi kufalitsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo.

Tsiku lina mu April 1951, nditapita ku msonkhano wachikristu, apolisi ena omwe anali kuyang’anitsitsa zochita zanga anandimanga ndikuyenda mumsewu. Chifukwa choti ndinakana kuyankha mafunso awo, anandipititsa kundende ina ku Bydgoszcz n’kuyamba kundipanikiza ndi mafunso usiku omwewo. Anandiuza kuti ndiimirire motsamira khoma kwa masiku asanu ndi limodzi, masana ndi usiku womwe, ndipo sanandipatse chakudya kapena chakumwa chilichonse komanso m’chipinda chonsecho munali utsi thoo! chifukwa cha fodya amene apolisiwo ankasuta. Ankandimenya ndi chibonga ndiponso ankanditentha ndi ndudu za fodya. Ndikakomoka, ankandithira madzi mpaka nditsitsimuke kenaka n’kuyamba kundipanikiza ndi mafunso. Ndinapemphera kwa Yehova kuti ndilimbe nazo, ndipo anandilimbitsadi.

Kukhala m’ndende ya Bydgoszcz kunali m’pabwino pake. Ku ndendeyi ndinauzako choonadi cha m’Baibulo anthu amene sizikanatheka kukumana nawo m’njira zina. Ndipotu kunena zoona, ndinali ndi mipata yambiri yolalikira. Chifukwa choti akaidiwo ankakhala movutika ndiponso mopanda chiyembekezo chilichonse, iwo ankamvetsera uthenga wabwino moona mtima.

Moyo Wanga Unasintha M’njira Ziwiri Zikuluzikulu

Nditangomasulidwa mu 1952, ndinakumana ndi Nela, mlongo wakhama kwambiri yemwe anali mpainiya. Iyeyu anakhala akuchita upainiya kummwera kwa dziko la Poland. Kenaka anagwira ntchito mu malo amene tinkawatcha kuti malo ophikira buledi, amene kwenikweni anali malo achinsinsi amene tinkasindikizirako mabuku athu. Imeneyi inali ntchito yovuta kwambiri, yofunika munthu wochangamuka ndiponso wololera kuvutikira ena. Tinakwatirana mu 1954, ndipo tinapitiriza utumiki wa nthawi zonse mpaka pamene mwana wathu Lidia, anabadwa. Kenaka ine ndi mkazi wanga tinaganiza zoti mkazi wangayo asiye utumiki wa nthawi zonse n’kubwerera kumudzi, kukasamalira mwana wathu. Cholinga chathu chinali chakuti ineyo ndithe kupitiriza ntchito yoyendayenda.

Chaka chomwecho, tinafunikanso kuganiza zochita pa nkhani ina yaikulu. Ndinapemphedwa kuti ndikakhale woyang’anira chigawo m’dera lina lalikulu kwambiri la dziko la Poland. Tinapemphera kwa Yehova za nkhani imeneyi. Ineyo ndinkadziwa kuti zinali zofunika kwambiri kulimbikitsa abale athu m’nthawi yoletsedwayi. Abale ambiri anamangidwa, motero abale anafunika kulimbikitsidwa kwambiri mwauzimu. Mogwirizana ndi mkazi wanga Nela, ndinavomera ntchitoyi. Yehova anandithandiza kutumikira m’njira imeneyi kwa zaka 38.

Kuyang’anira Nyumba Zophikira Buledi Zija

Masiku amenewo, oyang’anira zigawo ankayang’anira nyumba zophikira buledi zija. Nthawi zonse apolisi ankatilondalonda pofuna kupeza ndi kutseka malo a ntchito yathu yosindikiza mabuku. Nthawi zina ankakwanitsa kutero, komabe sitinafike pochita kusowa chakudya chauzimu. Zinali zoonekeratu kuti Yehova ankatisamalira.

Kuti munthu aitanidwe kukachita ntchito yolimba ndiponso yoopsa yosindikiza mabuku, anayenera kukhala wokhulupirika, wochangamuka, wololera kuvutikira ena, ndiponso womvera. Makhalidwe amenewa ndi amene ankatheketsa kuti nyumba zophikirako buledizo zipitirire kugwira ntchito bwinobwino. Kupeza malo abwino osindikizirako mabuku mobisa kunalinso kovuta. Panali malo ena amene ankaoneka kuti n’ngabwino, koma abale a kumeneko sanali kuchita zinthu mosamala kwambiri. M’malo ena, abale ankakhala osamala komano malowo sanali abwino. Abale ankalolera kuchita zinthu zimene anthu ambiri sangalolere kuchita. Kunena zoona, ndinawayamikira kuchokera pansi pa mtima abale ndi alongo onse amene ndinali ndi mwayi wogwira nawo ntchito.

Kumenyera Nkhondo Uthenga Wabwino

M’zaka zovuta zimenezo, nthawi zonse ankatipititsa ku khoti kukatizenga mlandu wakuti ati timachita zinthu zofuna kugwetsa boma. Limeneli linali vuto chifukwa choti tinalibe maloya otiimira pa milandu yathu. Maloya ena ankatimvetsa koma ambiri ankaopa kuti adzatchuka kuti akutithandiza ndipo sankafuna kuchita zinthu zokwiyitsa aboma. Komabe, Yehova ankadziwa zimene tikufunikira, ndipo patapita nthawi iye anachititsa kuti zinthu zitiyendere.

Alojzy Prostak, woyang’anira woyendayenda wina wa ku Kraków, anamuzunza kwambiri panthawi imene ankamufunsa mafunso ofufuza mlandu wake moti anafika pomutengera kuchipatala cha pa ndendeyo. Iyeyu analimba nazo ngakhale kuti anamuchita zinthu zomusokoneza maganizo ndiponso zomuvulaza kwambiri, moti akaidi anzake m’chipatalamo ankam’patsa ulemu. Mmodzi wa akaidiwo anali loya, dzina lake Witold Lis-Olszewski. Iyeyu anagoma nako kulimba mtima kwa Mbale Prostak. Motero anacheza naye kwa nthawi zingapo n’kumulonjeza kuti: “Akangonditulutsa n’kundilola kuyambiranso kuchita ntchito yanga, ndidzalola kumenyera nkhondo Mboni za Yehova.” Ankanenadi zoona.

A Olszewski anali ndi kagulu kawo ka maloya, kamene kanatsimikizadi mtima kutithandiza, zivute zitani. Panthawi imene tinali kuvutitsidwa kwambiri, kaguluka kankateteza abale pa milandu pafupifupi 30 pamwezi, kapena kuti tsiku lililonse mlandu umodzi! Popeza kuti a Olszewski ankafunika kudziwa bwino za milandu yonseyo, ineyo ndinapatsidwa ntchito yomalankhula nawo. Ndinagwira nawo ntchito kwa zaka seveni m’ma 1960 ndi m’ma 1970.

Panthawiyi ndinaphunzira zinthu zambiri zokhudza malamulo. Nthawi zambiri ndinkamvetsera akamazenga milandu, ndipo ndinkamvetsera mwachidwi zonena za maloya, zabwino ndi zoipa zomwe, njira zosiyanasiyana zodzitetezera mwalamulo, ndiponso umboni wa abale amene ankaimbidwa mlandu. Zonsezi zinandithandiza kwambiri pothandiza abale, makamaka amene ankaitanidwa monga mboni, kudziwa zoyenera kunena ndiponso kudziwa nthawi yoyenera kusanena chilichonse m’khotimo.

Mlandu ukakhala m’kati, a Olszewski nthawi zambiri ankagona m’nyumba za a Mboni za Yehova. Sikuti ankatero chifukwa choti sakanakwanitsa kugona m’hotela, koma chifukwa chake chinali chimene iwo panthawi ina ananena kuti, “Tisanapite kozenga mlandu, ndimafuna kuti nanenso ndizipumako mzimu wanu.” Chifukwa cha chithandizo cha bamboyu, milandu yambiri inatikomera. Ineyo anandithandiza pa milandu yanga ingapo, ndipo ankakana kuti ineyo ndimulipire ndalama ina iliyonse. Panthawi ina, anakana kulipidwa pa milandu 30. Kodi ankakana chifukwa chiyani? Iye anati: “Ndikufuna kuti ndithandizeko ntchito yanuyi, ngakhale pang’ono chabe.” Koma kunena zoona ndalama zimene anakana pa milanduyi sizinali zochepa ayi. Aboma anaona zimene gulu la maloya la bambo Olszewski linali kuchita, koma zimenezi sizinafooketse bamboyu kutithandiza.

M’povuta kufotokoza mwa mawu chabe mmene abale anachitira umboni mwamphamvu pozengedwa milandu yawoyo. Ambiri ankabwera kukhoti kudzaonerera milanduyo ndi kudzalimbikitsa abale ozengedwa milandu. Nditawerengetsera abale ndi alongo obwera kukhoti kudzaonerera milandu panthawi imene tinali ndi milandu yambiri, ndinapeza kuti chaka china anakwana 30,000. Ilitu linali khamu lalikuludi la Mboni!

Kupatsidwa Ntchito Ina

Pofika chaka cha 1989 ntchito yathu anali ataivomereza mwalamulo. Patatha zaka zitatu tinamanga ofesi ya nthambi yatsopano ndipo tinaipereka kwa Yehova. Ndinaitanidwa kukagwira ntchito kumeneku mu Dipatimenti Yopereka Chidziwitso cha Zachipatala, ndipo ndinavomera ntchito imeneyi mosangalala. Tinalipo abale atatu, ndipo tinagwira ntchito yothandiza abale athu pankhani ya magazi. Tinawathandiza kumenyera nkhondo chikhulupiriro chawo pankhaniyi malingana ndi chikumbumtima chawo chachikristu.​—Machitidwe 15:29.

Ine ndi mkazi wanga tasangalala kwambiri ndi mwayi wotumikira Yehova polalikira anthu. Mkazi wanga Nela nthawi zonse wakhala akundithandiza ndiponso kundilimbikitsa. Sindiiwala mtima wake wosakonda kudandaula panthawi imene ineyo ndatanganidwa ndi ntchito zokhudza kutumikira Mulungu kapena pamene ndatsekeredwa m’ndende. Pa mavuto, iye ankalimbikitsa ena m’malo momadzimvera chisoni.

Mwachitsanzo, mu 1974, ndinamangidwa pamodzi ndi oyang’anira oyendayenda ena. Abale ena amene anadziwa nkhaniyi anafuna kuti mkazi wanga amubenthulire nkhaniyi mwapang’onopang’ono. Atapezana naye anam’funsa kuti: “Mlongo Nela, pepani zinthu sizili bwino, tabwera ndi nkhani yovuta.” Iye atangomva zimenezi anachita kakasi, chifukwa ankaganiza kuti ndamwalira. Ndiyeno atam’longosolera zimene zinachitika, anayankha moupeza mtima kuti: “Si mwati ali moyo. Akatu si koyamba iwo aja kumangidwa.” Pambuyo pake abalewo anandiuza kuti anagoma nako kulimba mtima kwake.

Ngakhale kuti tinakumana ndi zosautsa zosiyanasiyana m’mbuyomo, nthawi zonse Yehova wakhala akutidalitsa chifukwa chosunga njira yake. Ndife osangalala kwambiri kuti mwana wathu, Lidia, ndiponso mwamuna wake, Alfred DeRusha, ndi anthu achitsanzo chabwino kwambiri cha banja lachikristu. Ana awo, Christopher ndi Jonathan, awalera bwino moti ndi atumiki odzipereka a Mulungu ndipo zimenezi zimatisangalatsa kwambiri. Mng’ono wanga Ryszard, ndi mlongo wanga wamng’ono Urszula, nawonso akhala Akristu okhulupirika kwa zaka zambiri.

Yehova sanatisiyepo ayi, ndipo tikufuna kupitiriza kum’tumikira ndi mtima wonse. Ifeyo patokha tinaona kuti lemba la Salmo 37:34 n’loona. Lembali limati: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.” Tikuyembekezera nthawi imeneyo mwa mtima wonse.

[Chithunzi patsamba 17]

Pamsonkhano womwe unachitikira m’munda wa mbale ku Kraków mu 1964

[Chithunzi patsamba 18]

Ndili ndi mkazi wanga, Nela, ndi mwana wathu, Lidia, mu 1968

[Chithunzi patsamba 20]

Tili ndi mwana wina wa Mboni akukamuchita opaleshoni ya mtima popanda kumuika magazi

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili ndi Dr. Wites, mkulu woona za opaleshoni ya mtima ya ana yosaika magazi, ku chipatala cha ku Katowice

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili ndi mkazi wanga Nela, mu 2002