Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Akanamasulidwa Mosavuta”

“Akanamasulidwa Mosavuta”

“Akanamasulidwa Mosavuta”

GENEVIÈVE DE GAULLE anali mwana wamkazi wa mkulu wake wa Charles de Gaulle, pulezidenti wakale wa dziko la France. Mayiyu anadziwira Mboni za Yehova kundende yokhaulitsira anthu ya Ravensbrück, kumpoto kwa Germany. Iye analemba mawu ali pamwambawa m’kalata imene anailemba mu August 1945.

Akaidi a m’ndende yokhaulitsira anthu ya Auschwitz, ku Poland, anamasulidwa pa January 27, 1945. Mu 1996, tsiku limeneli linakhazikitsidwa ku Germany kukhala lokumbukira anthu amene anaphedwa m’nthawi ya ulamuliro wa Hitler.

Pokambapo pa mwambo wa chikumbutsochi pa January 27, 2003, mkulu wa nyumba ya malamulo ya ku Baden-Württemberg, dzina lake Peter Straub anati: “Onse amene anazunzidwa chifukwa cha chipembedzo kapena nkhani za ndale, amenenso analola kufa m’malo mogonja, tiyenera kuwapatsa ulemu waukulu zedi. Mboni za Yehova zinali gulu lokhalo lachipembedzo limene linakaniratu kugonja ku zofuna za boma la Hitler. Iwo sananyamule dzanja lawo kuti apangire sawacha Hitler. Anakana kulumbirira kuti adzakhala okhulupirika kwa ‘Mfumu ndi Boma,’ ngati mmene anakaniranso kumenya nkhondo kapena kugwira ntchito zina zachibalo. Ndipo ana awo sanalowe nawo m’gulu la Achinyamata a Hitler.”

Ponena za otsatira ake Yesu Kristu anati: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Chotero, chimene Mboni za Yehova zinakanira kuchita zinthuzo si china ayi, koma inali nkhani ya chipembedzo basi. Straub anapitiriza kuti: “A Mboni za Yehova, amene anali ndi chizindikiro chaukaidi chamtundu wapepo pa malaya awo, anali okhawo amene anali ndi ufulu wosankha kuphedwa kapena kumasulidwa. Anangofunikira kusaina pepala lokanira chikhulupiriro chawo basi.”

Mboni zochuluka sizikanayerekeza m’pang’onong’ono pomwe kukana chikhulupiriro chawo. Choncho, 1,200 zinafa m’nthawi ya ulamuliro wa Nazi. Zokwanira 270 zinachita kunyongedwa pokana kusiya chikhulupiriro chawo. Kwa Mbonizo, sanali nkhambakamwa chabe mawu akuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Mboni za Yehovazo zinali anthu ngati wina aliyense, monga ananenera Ulrich Schmidt, mkulu wa nyumba ya malamulo ya ku North Rhine-Westphalia. Ponena za mawu ake, kabuku kotchedwa Landtag Intern kanafotokoza kuti ndi “anthu ngati wina aliyense amene, potsatira chikumbumtima chawo, sanasunthike pa chikhulupiriro chawo. Anasonyeza kukhala nzika zolimba mtima, ndipo anatsutsa boma la Nazi chifukwa cha Chikristu chawo.” Tili otsimikiza kuti Yehova Mulungu amasangalala poona anthu amene amakhala okhulupirikabe kwa iye pamene ali m’mayesero ovuta kwambiri. Pa Miyambo 27:11, timawerenga kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Courtesy of United States Holocaust Memorial Museum