Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akristu Amawalitsa Ulemelero wa Yehova

Akristu Amawalitsa Ulemelero wa Yehova

Akristu Amawalitsa Ulemelero wa Yehova

“Maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.”​—MATEYU 13:16.

1. Kodi tikukhala ndi funso lotani tikaona mmene Aisrayeli anachitira kwa Mose pa phiri la Sinai?

PAMENE Aisrayeli anasonkhana pa phiri la Sinai, anali ndi chifukwa chabwino choyandikirira Yehova. Ndi iko komwe, anali atawalanditsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu. Iye anasamaliranso zosowa zawo, powagawira chakudya ndi madzi m’chipululu. Kenako, anawathandiza kugonjetsa gulu lankhondo la Amaleki limene linawaukira. (Eksodo 14:26-31; 16:2–17:13) Pamene anamanga msasa m’chipululu m’munsi mwa phiri la Sinai, anthuwo ananjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha mabingu ndi mphezi. Pambuyo pake, anaona Mose akutsika m’phiri la Sinai, nkhope yake ikunyezimira ndi ulemerero wa Yehova. Komabe, m’malo mochita chidwi ndi kuyamikira, iwo anachita mantha. ‘Anaopa kumuyandikira [Mose].’ (Eksodo 19:10-19; 34:30) Kodi n’chifukwa chiyani iwo anaopa kuyang’ana kuwala kwa ulemerero wa Yehova, amene anawachitira zabwino zambiri choncho?

2. Kodi chifukwa chimene Aisrayeli anachitira mantha poona nkhope ya Mose ikuwalitsa ulemerero wa Mulungu chingakhale chinali chiyani?

2 Mwachionekere, Aisrayeliwo anachita mantha panthawiyi makamaka chifukwa cha zimene zinachitika m’mbuyomo. Pamene analakwira Yehova mwadala mwa kupanga mwana wa ng’ombe wagolide, anawalanga. (Eksodo 32:4, 35) Kodi iwo anaphunzirapo kanthu pa chilango cha Yehova ndi kuchiyamikira? Ayi, ochuluka sanatero. Chakumapeto kwa moyo wake, Mose anakumbukira chochitika cha mwana wa ng’ombe wagolide, limodzi ndi zochitika zina pamene Aisrayeli sanamvere Yehova. Iye anati kwa anthuwo: “Munapikisana nawo mawu a Yehova Mulungu wanu, osam’khulupirira, kapena kumvera mawu ake. Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani.”​—Deuteronomo 9:15-24.

3. Kodi Mose anachita motani ponena za kuphimba nkhope yake?

3 Taganizirani mmene Mose anachitira ataona kuti Aisrayeliwo akuchita mantha. Nkhaniyo imanena kuti: “Mose atatha kulankhula nawo, anaika chophimba pankhope pake. Koma pakulowa Mose [m’chihemacho] pamaso pa Yehova kunena ndi iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israyeli chimene adamuuza. Ndipo ana a Israyeli anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose naikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi [Yehova].” (Eksodo 34:33-35) Kodi n’chifukwa chiyani Mose anaphimba nkhope yake nthawi zina? Tingaphunzirepo chiyani pamenepa? Mayankho pa mafunso amenewa akhoza kutithandiza kupenda ubale wathu ndi Yehova.

Anaphonya Mwayi

4. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza kuti kuphimba nkhope kwa Mose kunatanthauza chiyani?

4 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti kuphimba nkhope kwa Mose kunali kokhudzana ndi maganizo ndi mitima ya Aisrayeli. Paulo analemba kuti: “Ana a Israyeli sanathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake . . . Mitima yawo inaumitsidwa.” (2 Akorinto 3:7, 14) Zomvetsa chisoni kwambiri! Aisrayeliwo anali anthu osankhika a Yehova, ndipo iye anafuna kuti awayandikire. (Eksodo 19:4-6) Koma iwo sanafune kuti ayang’ane ulemerero wa Mulungu ndi kuuona bwinobwino. M’malo motembenuzira mitima ndi maganizo awo kwa Yehova mwa kudzipereka mwachikondi, iwo anamufulatira.

5, 6. (a) Kodi n’chiyani chimene Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira anachita mofanana ndi Aisrayeli a m’masiku a Mose? (b) Kodi panali kusiyana kotani pakati pa anthu amene anamvetsera kwa Yesu ndi amene sanamvetsere?

5 Zimenezo zinachitikanso m’zaka 100 zoyambirira. Panthawi imene Paulo anatembenuka kukhala Mkristu, pangano la Chilamulo linali litalowedwa m’malo ndi pangano latsopano, limene nkhoswe yake anali Yesu Kristu, Mose Wamkulu. Yesu anawalitsa bwino lomwe ulemerero wa Yehova m’mawu ndi m’zochita zomwe. Polemba za Yesu woukitsidwayo, Paulo anati: “Ali chinyezimiro cha ulemerero wake [wa Mulungu], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Ahebri 1:3) Ha! Ayudawo anali ndi mwayi waukulu bwanji! Anatha kumvetsera mawu opatsa moyo wosatha akutuluka pakamwa pa Mwana wa Mulungu weniweniyo! Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, ochuluka amene Yesu anawalalikira sanalabadire. Ponena za amenewo, Yesu anagwira mawu ulosi wa Yehova wodzera mwa Yesaya kuti: “Unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m’makutu awo anamva mogontha, ndipo maso awo anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wawo, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.”​—Mateyu 13:15; Yesaya 6:9, 10.

6 Panali kusiyana kwakukulu pakati pa Ayudawo ndi ophunzira a Yesu, amene Yesu anati za iwo: “Maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.” (Mateyu 13:16) Akristu oona amafunitsitsa kudziwa Yehova ndi kum’tumikira. Amasangalala kuchita chifuniro chake, chimene chimafotokozedwa m’Baibulo. Mwakutero, Akristu odzozedwa amawalitsa ulemerero wa Yehova mu utumiki wawo wa pangano latsopano, ndipo nawonso a nkhosa zina amachita chimodzimodzi.​—2 Akorinto 3:6, 18.

Mmene Uthenga Wabwino Umakhalira Wophimbika

7. N’chifukwa chiyani sitikudabwa kuti anthu ochuluka amakana uthenga wabwino?

7 Monga taonera kale, m’masiku a Yesu ndi a Mose, Aisrayeli ochuluka anakana mwayi umene unawatsegukira. N’chimodzimodzinso masiku athu ano. Anthu ochuluka amakana uthenga wabwino umene timalalikira. Koma sikuti timadabwa nazo zimenezi. Paulo analemba kuti: “Ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.” (2 Akorinto 4:3, 4) Kuwonjezera pa njira za Satana zophimbira uthenga wabwino, anthu ambiri amaphimba okha nkhope zawo chifukwa sakufuna kuti aone.

8. Kodi anthu ambiri ali mu umbuli wotani wowachititsa khungu, ndipo ifeyo tingalipewe motani khungulo?

8 Ambiri, maso awo ophiphiritsa ali akhungu chifukwa sakudziwa uthenga wabwino. Baibulo limanena kuti anthu a mitundu adzakhala “odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo.” (Aefeso 4:18) Paulo asanakhale Mkristu, ngakhale kuti anali katswiri wa Chilamulo, umbuli unam’chititsa khungu mwakuti anazunza mpingo wa Mulungu. (1 Akorinto 15:9) Komabe, Yehova anamuvumbulira choonadi. Paulo mwiniwakeyo anati: “Mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m’tsogolo kufikira moyo wosatha.” (1 Timoteo 1:16) Mofanana ndi Paulo, anthu ambiri amene kale anali otsutsa choonadi cha Mulungu, tsopano akumutumikira. Ndiye chifukwa chake tiyenera kupitiriza kuchitira umboni ngakhale kwa anthu amene amatitsutsa. Potero, mwa kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse ndi kuzindikira tanthauzo lake, timakhala otetezedwa kuti tisachite zinthu mwaumbuli ndi kukhumudwitsa Yehova.

9, 10. (a) Kodi Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira anasonyeza motani kuti anali osafuna kuphunzira, ndiponso osasinthika pamaganizo awo? (b) Kodi pali kufanana kulikonse ndi mmene zikuchitikira m’Matchalitchi Achikristu masiku ano? Fotokozani.

9 Anthu ambiri satha kupenya bwino mwauzimu chifukwa safuna kuphunzira ndipo ndi osasunthika pamaganizo awo. Ayuda ambiri anam’kana Yesu ndi zimene anali kuphunzitsa chifukwa iwo anali oumirira nganganga pa Chilamulo cha Mose. Koma analipo ena omwe sanali otero. Mwachitsanzo, Yesu ataukitsidwa, “khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” (Machitidwe 6:7) Koma ponena za Ayuda ochuluka, Paulo analemba kuti: “Kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pawo.” (2 Akorinto 3:15) Mwachionekere, Paulo anadziwa zimene Yesu ananena kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda kuti: “Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo.” (Yohane 5:39) Malemba amene anawafufuza mwakhama chotero, anayenera kuwathandiza kuzindikira kuti Yesu anali Mesiya. Komabe, Ayudawo anali ndi maganizo awoawo, moti ngakhale Mwana wa Mulungu wochita zozizwitsayo sanathe kuwasintha maganizo kuti alandire choonadi.

10 Ndi mmenenso anthu ambiri alili m’Matchalitchi Achikristu masiku ano. Mofanana ndi Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira, iwo “ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.” (Aroma 10:2) Ngakhale kuti ena amaphunzira Baibulo, safuna kuti akhulupirire zimene limanena. Amakana kuvomereza kuti Yehova amaphunzitsa anthu ake kupyolera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru la Akristu odzozedwa. (Mateyu 24:45) Koma ifeyo tikudziwa kuti Yehova amaphunzitsa anthu ake. Timadziwanso kuti kamvedwe ka choonadi cha Mulungu kakhala kakumawonjezereka nthawi zonse. (Miyambo 4:18) Mwa kumulola Yehova kuti atiphunzitse, timadalitsidwa mwa kudziwa chifuniro chake ndi cholinga chake.

11. Kodi choonadi chaphimbika motani kwa anthu amene amakhulupirira zimene mtima wawo ukufuna kukhulupirira?

11 Anthu ena amachita khungu chifukwa chokhulupirira zimene mtima wawo umafuna kukhulupirira. Ulosi unaneneratu kuti ena adzatonza anthu a Mulungu ndi uthenga wawo wonena za kukhalapo kwa Yesu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, . . . aiwala dala.” Amaiwala zoti Mulungu anadzetsa chigumula pa dziko la m’masiku a Nowa. (2 Petro 3:3-6) Mofananamo, ambiri onena kuti ndi Akristu amavomereza mosavuta kuti Yehova ndi wachifundo, wokoma mtima, komanso wokhululukira; komabe amanyalanyaza kapena kukana mfundo yakuti iye salekerera wopalamula. (Eksodo 34:6, 7) Akristu oona amayesetsa mwakhama kuti amvetsetse zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa.

12. Kodi miyambo yawachititsa khungu motani anthu?

12 Anthu ambiri opita ku tchalitchi miyambo ya anthu inawachititsa khungu. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake kuti: “Mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.” (Mateyu 15:6) Ayudawo atabwerako kuukapolo ku Babulo, analimbikitsa mwakhama kubwezeretsa kupembedza koona. Komano, ansembe enieniwo anayamba kudzitukumula ndi kudziona olungama m’maso mwa iwo eni. Madyerero achipembedzo anali kungochitika mwamwambo, opanda ulemu weniweni kwa Mulungu. (Malaki 1:6-8) Podzafika m’nthawi ya Yesu, alembi ndi Afarisi anali atawonjezera miyambo ya anthu yambirimbiri ku Chilamulo cha Mose. Yesu anavumbula poyera anthu amenewo kuti anali onyenga chifukwa sanali kuzindikiranso mfundo zolungama zimene Chilamulocho chinazikidwapo. (Mateyu 23:23, 24) Akristu oona ayenera kusamala kuti asalole miyambo ya anthu yachipembedzo kuwapatutsa pa kupembedza koyera.

“Kuona Wosaonekayo”

13. Kodi Mose anaona ulemerero wa Mulungu m’njira ziwiri ziti?

13 Mose anapempha kuti aone ulemerero wa Mulungu pamene anali m’phiri, ndipo anaonadi kuwala kotsalira m’mbuyo kwa ulemerero wa Yehova. Mose polowa m’chihema, sanali kuphimba nkhope yake. Iye anali munthu wa chikhulupiriro chozama, ndipo anali wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu. Ngakhale kuti anadalitsidwa mwa kuonako mbali ina ya ulemerero wa Yehova m’masomphenya, kwenikweni iye anali atamuona kale Mulungu ndi maso a chikhulupiriro. Ponena za Mose, Baibulo limanena kuti “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27; Eksodo 34:5-7) Ndipo iye anawalitsa ulemerero wa Mulungu. Sanatero ndi kunyezimira kokha kwa nkhope yake kwakanthawi, komanso mwa kulimbikira kuthandiza Aisrayeli kuti adziwe Yehova ndi kumutumikira.

14. Kodi Yesu anaona ulemerero wa Mulungu motani, ndipo anali kusangalala kuchita chiyani?

14 Pamene Yesu anali kumwamba, anaona mwachindunji ulemerero wa Mulungu kwa zaka zosawerengeka, kuchokera ngakhale chilengedwe chisanakhalepo. (Miyambo 8:22, 30) Panthawi yonseyo, iwo anakhala paubale wa chikondi chenicheni chozama. Yehova Mulungu anasonyeza chikondi chenicheni kwa mwana wake woyamba wa chilengedwe chonse. Yesu nayenso anachitapo kanthu posonyeza chikondi chake chozama kwa Mulungu, amene anam’patsa moyo. (Yohane 14:31; 17:24) Chawo chinali chikondi chenicheni cha Bambo ndi Mwana wake. Mofanana ndi Mose, Yesu anasangalala ndi kuwalitsa ulemerero wa Yehova m’zinthu zimene anaphunzitsa.

15. Kodi Akristu amayang’ana ndi kusinkhasinkha motani ulemerero wa Mulungu?

15 Mofanana ndi Mose ndiponso Yesu, Mboni za Mulungu za masiku ano padziko lapansi zimafunitsitsa kuyang’ana ndi kusinkhasinkha ulemerero wa Yehova. Izo sizifulatira uthenga wabwino waulemerero. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene akatembenukira kwa Mulungu [ndiko kuchita chifuniro chake], chophimbacho chichotsedwa.” (2 Akorinto 3:16) Timaphunzira Malemba chifukwa timafuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Timasirira ulemerero umene umanyezimira pankhope pa Mwana wa Yehova yemwenso ali Mfumu yodzozedwa, Yesu Kristu. Ndiponso timatengera chitsanzo chake. Mofanananso ndi Mose komanso Yesu, ifeyo tadalitsidwa popatsidwa utumiki wophunzitsa anthu za Mulungu waulemerero amene timam’pembedza.

16. N’chifukwa chiyani tili odalitsika podziwa choonadi?

16 Yesu anapemphera kuti: “Ndivomerezana ndi Inu, Atate, . . . kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda.” (Mateyu 11:25) Anthu amene ali oona mtima ndi a mtima wodzichepetsa, Yehova amawathandiza kumvetsa zolinga zake ndi khalidwe lake. (1 Akorinto 1:26-28) Iye watifungatira m’chitetezo chake, ndipo amatiphunzitsa kupindula​—kuti tipeze zabwino koposa pa moyo wathu. Tiyenitu tigwiritse ntchito mpata uliwonse kuti timuyandikire Yehova, poyamikira zonse zimene amatikonzera kuti timudziwe bwino lomwe.

17. Kodi tiyenera kuchitanji kuti makhalidwe a Yehova tiwadziwe bwino lomwe?

17 Paulo analembera Akristu odzozedwa kuti: “Ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kumka kuulemerero.” (2 Akorinto 3:18) Kaya chiyembekezo chathu n’chopita kumwamba kapena n’chokhala padziko lapansi, pamene tim’dziwa Yehova mokulirakulira​—kudziwa makhalidwe ake ofotokozedwa m’Baibulo​—timafanana naye mokulirakuliranso. Ngati moyamikira tisinkhasinkha moyo wa Yesu Kristu, utumiki wake, ndi zimene anaphunzitsa, tidzasonyeza makhalidwe a Yehova bwino lomwe. N’zosangalatsa bwanji, kudziwa kuti mwakutero timatamanda ndi kulemekeza Mulungu wathu, amene tikuyesetsa kusonyeza chithunzi chake!

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Aisrayeli anachita mantha kuyang’ana ulemerero wa Mulungu umene unanyezimira pa nkhope ya Mose?

• Kodi uthenga wabwino unali ‘kuphimbika’ motani m’zaka 100 zoyambirira? nanga masiku ano?

• Kodi timawalitsa motani ulemerero wa Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 19]

Aisrayeli anachita mantha kuyang’ana nkhope ya Mose

[Zithunzi patsamba 21]

Mofanana ndi Paulo, anthu ambiri amene kale anali otsutsa choonadi cha Mulungu tsopano akum’tumikira

[Zithunzi patsamba 23]

Atumiki a Yehova amasangalala kuwalitsa ulemerero wa Mulungu