Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anawayamikira Chifukwa cha Chidwi Chawo pa Baibulo

Anawayamikira Chifukwa cha Chidwi Chawo pa Baibulo

Anawayamikira Chifukwa cha Chidwi Chawo pa Baibulo

MARIANNA, mtsikana amene ndi Mboni ya Yehova amakhala kum’mwera kwa Italy. Iye ali ndi zaka 18 ndipo akumaliza sukulu yake yasekondale. Pa sukuluyo palinso achinyamata ena amene ndi Mboni zinzake.

Marianna analemba kuti: “Kwa zaka zingapo tsopano, enafe takhala tikukambirana lemba la tsiku la m’Baibulo panthawi yopuma kuchokera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Malo okha amene tikutha kukambiranapo lemba la tsiku ndi m’khonde pafupi ndi chipinda chopumira cha aphunzitsi. Pakhondepo si pabata kwenikweni. Aphunzitsi ambiri akhala akutiona akamadutsa, ndipo ena amaima kuti aone zimene tikuchita. Zimenezi zatipatsa mwayi woyankha mafunso awo. Patsiku lililonse mpaka mphunzitsi mmodzi amaimapo. Aphunzitsi angapo afikapo ndi kumvetsera ndithu makambirano athu a lemba la m’Baibulo, ndipo ayamikira chidwi chimene Mbonife tili nacho pa zinthu zauzimu. Tsiku lina, wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu anatipempha kuti tikakambirane m’chipinda chopumira cha aphunzitsi.

“Poona mmene m’chipindamo munalili, mphunzitsi wanga anapempha mphunzitsi wamkulu kuti tikakambirane lembalo m’kalasi, mmene munalibe phokoso kwambiri. Mphunzitsi wamkuluyo analola, pambuyo pake mphunzitsi wanga anatiyamikira pamaso pa kalasi yonse chifukwa cha chitsanzo chathu chabwino. Tonse tili osangalala kwambiri chifukwa cha mwayi waukulu umene Yehova watipatsa.”