Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Imfayo Yamezedwa M’chigonjetso”

“Imfayo Yamezedwa M’chigonjetso”

“Imfayo Yamezedwa M’chigonjetso”

TAYEREKEZANI kuti mutu wa nkhani uli pamwambawu ndi umene mwawerenga m’nyuzipepala, m’malo mwa nkhani ija ya mtsikana wamng’ono amene anadzipha. N’zoona kuti palibe nyuzipepala iliyonse imene inatulutsapo nkhani ngati imeneyi. Koma mawu amene ali pamwambapa amapezeka m’buku limene lakhalapo zaka masauzande angapo​—bukulo ndi Baibulo.

Malemba amafotokoza za imfa momvekera bwino. Ndiponso, Baibulo silimangofotokoza chifukwa chimene timafera, koma limalongosolanso za mmene akufa alili, komanso limapereka chiyembekezo chokhudza okondedwa athu amene anamwalira. Limanenanso za nthawi yosangalatsa kwambiri pamene kudzakhala kotheka kulengeza kuti: “Imfayo yamezedwa m’chigonjetso.”​—1 Akorinto 15:54.

Baibulo limafotokoza imfa ndi mawu omveka bwino lomwe, osati mawu osamvetsetseka. Mwachitsanzo, mobwerezabwereza limayerekeza kufa ndi ‘kugona tulo,’ ndipo limati anthu akufa “akugona.” (Salmo 13:3; 1 Atesalonika 4:13; Yohane 11:11-14) Imfa imatchedwanso “mdani.” (1 Akorinto 15:26) Koma chofunika koposa n’chakuti, Baibulo limatithandiza kumvetsa chifukwa chake imfa ili ngati tulo, chifukwa chake imagwera anthu, ndi mmene mdani ameneyu adzam’gonjetsere potsirizira pake.

Kodi N’chifukwa Chiyani Timafa?

Buku loyamba la m’Baibulo limafotokoza mmene Mulungu anapangira munthu woyamba, Adamu, ndi kumuika m’mudzi wake wa paradaiso. (Genesis 2:7, 15) Adamu atalengedwa, anapatsidwa ntchito yoti azigwira, koma analetsedwa chinthu chimodzi. Ponena za mtengo winawake wa m’munda wa Edene, Mulungu anamuuza kuti: “Usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” * (Genesis 2:17) Choncho, Adamu anadziwa kuti imfa inali yopeweka. Kusamvera lamulo la Mulungu n’kumene kukanadzetsa imfa.

Mwa tsoka ilo, Adamu ndi mkazi wake Hava, sanamvere Mulungu. Ananyalanyaza dala chifuniro cha Mlengi wawo, choncho anakolola zotsatira zake. Powafotokozera zotsatira za tchimo lawo, Mulungu anawauza kuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Iwo anakhala ndi chilema choopsa​—ndicho kupanda ungwiro. Kupanda ungwiro kwawo, kapena kuti kuchimwa kwawo, kunali kowatengera ku imfa.

Chilema chimenechi​—tchimolo​—linawolokeranso kwa ana a Adamu ndi Hava, kutanthauza mtundu wonse wa anthu. Kunena kwina, tingati uchimowo unali ngati matenda otengera kwa makolo. Adamu sanangotaya mwayi wokhala ndi moyo wosafa, koma anapatsiranso ana ake kupanda ungwiro. Banja lonse la anthu linakhala akapolo a imfa. Baibulo limanena kuti: “Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

“Uchimo Unalowa m’Dziko Lapansi”

Chilema chotengera kwa makolo chimenechi, kapena kuti uchimo, si chinthu chooneka ndi maso. “Tchimo” ndi chofooka m’makhalidwe ndi moyo wauzimu chimene tinatengera kwa makolo athu oyambirira. Ndipo chofookacho chili ndi zotsatira zake. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anakonza njira yotiwombolera. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) M’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, Paulo anawonjezeranso chitsimikiziro chothandiza kwambiri. Iye anati: “Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.”​—1 Akorinto 15:22.

Mwachionekere, Yesu Kristu akuchita mbali yofunika kwambiri pothandiza kuchotsa uchimo ndi imfa. Iye anati anabwera padziko lapansi ‘kudzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Zili ngati pamene zigawenga zagwira munthu, ndipo zikufuna dipo kuti munthuyo amasulidwe. Koma m’nkhaniyi, moyo waumunthu wangwiro wa Yesu ndiwo unakhala dipo lotimasulira ku uchimo ndi imfa. *​—Machitidwe 10:39-43.

Pofuna kupereka dipolo, Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake nsembe. “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye . . . akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Asanafe imfa yopereka nsembe, Yesu ‘anachitira umboni za choonadi.’ (Yohane 18:37) Ndipo panthawi ya utumiki wake, anatengera mwayi zochitika zina kuti asonyeze zenizeni zokhudza imfa.

“Kabuthuko . . . Kali M’tulo”

Imfa sinali nkhani yachilendo kwa Yesu pamene anali padziko lapansi. Anali kumva chisoni pa imfa za anthu amene anali kuwadziwa, ndipo anali kudziwanso bwino lomwe kuti tsiku lina iye adzafa asanakalambe. (Mateyu 17:22, 23) Pakali miyezi ingapo Yesu asanaphedwe, bwenzi lake lapamtima Lazaro anamwalira. Chochitika chimenecho chimatithandiza kuzindikira mmene Yesu anaonera imfa.

Atangomva za imfa ya Lazaro, Yesu anati: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” Ophunzira ake anaganiza kuti ngati Lazaro anali kungopuma, apeza bwino. Choncho Yesu mosabisa mawu anati: “Lazaro wamwalira.” (Yohane 11:11-14) Mwachidziwikire, Yesu anaona imfa kukhala ngati tulo. Ngakhale kuti imfa sitingaimvetse kwenikweni, kugona tulo timakumvetsa. Tikagona tulo tofa nato usiku, sitizindikira mmene nthawi ikudutsira kapenanso zimene zikuchitika zotizungulira. Timakhala ngati takomoka. Ndi mmene Baibulo limafotokozera akufa. Lemba la Mlaliki 9:5 limanena kuti: “Akufa sadziwa kanthu bi.”

Chinanso chimene Yesu anayerekezera imfa ndi tulo n’chakuti anthu amatha kudzutsidwa ku imfa, mwa mphamvu ya Mulungu. Panthawi ina, Yesu anapita kunyumba ya banja lina limene linali pachisoni chachikulu chifukwa mwana wawo wamtsikana anali atangomwalira kumene. Yesu anati: “Kabuthuko sikanafa koma kali m’tulo.” Kenako Yesu anayandikira mtsikana wakufayo nagwira dzanja lake, ndipo “kabuthuko kadauka.”​—Mateyu 9:24, 25.

Ndi mmenenso Yesu anaukitsira bwenzi lake Lazaro. Koma asanachite chozizwitsa chimenecho, anayamba kaye watonthoza Marita, mlongo wake wa Lazaro, kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anayankha mwachidaliro kuti: “Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:23, 24) Mwachionekere, Marita anali ndi chiyembekezo chakuti atumiki a Mulungu onse adzaukitsidwa panthawi ina m’tsogolo.

Kodi kuuka kwa akufa kumatanthauzanji kwenikweni? Liwu lachigiriki lomasuliridwa kuti “kuuka kwa akufa” (a·naʹsta·sis) kwenikweni limatanthauza “kunyamuka.” Limatanthauza kudzuka kuchokera kwa akufa. Zimenezi zingamveke zodabwitsa kwa ena. Koma Yesu atanena kuti akufa adzamva mawu ake, anati: “Musazizwe ndi ichi.” (Yohane 5:28) Kuukitsa anthu kumene Yesu anachita ali padziko lapansi kumatithandiza kudalira lonjezo la m’Baibulo lakuti, akufa omwe ali m’chikumbumtima cha Mulungu, adzadzuka ku “tulo” timene akhala akugona kwa nthawi yaitali. Lemba la Chivumbulutso 20:13 limalosera kuti: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade [manda a anthu onse] zinapereka akufawo anali m’menemo.”

Kodi akufa amenewa akadzaukitsidwa, adzakalamba ndi kufanso, ngati mmene anaferanso Lazaro? Cholinga cha Mulungu si chimenecho. Baibulo limatitsimikizira kuti nthawi idzafika pamene “sipadzakhalanso imfa,” ndipo palibe amene adzakalamba ndi kufa.​—Chivumbulutso 21:4.

Imfa ndi mdani. Anthu alinso ndi adani ena ofanana ndi ameneyu. Adaniwo ndiwo matenda ndi ukalamba, ndipo nawonso amabweretsanso mavuto ambiri. Mulungu analonjeza kuti adzagonjetsa adani onsewo, ndipo potsirizira pake adzathana ndi mdani wamkulu wa anthu. “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.”​—1 Akorinto 15:26.

Lonjezo limenelo likadzakwaniritsidwa, anthu adzasangalala ndi moyo wangwiro, wopanda uchimo ndi imfa. Pakali pano, tiyenera kukhazika mitima yathu pansi podziwa kuti okondedwa athu amene anamwalira akupuma. Ndipo ngati ali m’chikumbumtima cha Mulungu, adzaukitsidwa panthawi yake yoikika.

Munthu Akaimvetsa Imfa Moyo Umakhala Watanthauzo

Ngati tiimvetsa bwino imfa ndi kudziwa za chiyembekezo chokhudza akufa, zingatithandize kuona moyo kukhala watanthauzo. Ian, amene tam’tchula m’nkhani yapitayo, anali wa zaka za m’ma 20 pamene anaphunzira zimene Baibulo limafotokoza za imfa. Iye anati: “Ndinali kukhulupirira koma mokayikabe kuti bambo anga amene anamwalira anali ndi moyo kwinakwake. Choncho nditaphunzira kuti anali chigonere mu imfa, poyamba ndinali wokhumudwa.” Komabe, Ian atawerenga lonjezo la Mulungu la kuuka kwa akufa, anasangalala kwambiri podziwa kuti bambo ake adzawaonanso. Iye anati: “Kwa nthawi yoyamba pamoyo wanga, ndinakhala ndi mtendere mumtima mwanga.” Inde, kuimvetsa bwino imfa kunam’patsa mtendere wa maganizo ndi kukhazikitsa mtima wake pansi.

Clive ndi Brenda anataya mwana wawo wamwamuna, Steven, wa zaka 21, pangozi ya galimoto imene tatchula m’nkhani yapitayo. Ngakhale kuti anali kudziwa zimene Baibulo limanena za imfa, mitima yawo inasweka ndi imfa yadzidzidzi imeneyo. Pajatu imfa ndi mdani, ndipo mbola yake imapweteka zedi. Popeza kuti anali kudziwa zimene Malemba amanena za mmene akufa alili, pang’ono ndi pang’ono chisoni chawo chinayamba kuchepa. Brenda anati: “Kumvetsa kwathu imfa kwatithandiza kulimbikitsanso mitima yathu ndi kupitiriza ndi moyo. Komabe, tsiku silingadutse popanda kuganizira za nthawi pamene Steven adzagalamuke ku tulo take ta imfa.”

“Imfawe, Mbola Yako Ili Kuti?”

Mwachionekere, kumvetsa mmene akufa alili kungatithandize kuona moyo moyenerera. Imfa sifunika kukhala chinthu chosamvetsetseka. Titha kusangalala ndi moyo popanda kuchita mantha ndi mdani ameneyu amene akutiwenda. Ndipo podziwa kuti imfa singawononge moyo wathu kosatha, sitilakalaka m’pang’ono pomwe kumangochita zotisangalatsa basi, ati chifukwa chakuti “moyo ndi waufupi kwambiri.” Pamene tikudziwa kuti okondedwa athu amene anamwalira, omwe ali m’chikumbumtima cha Mulungu akugona mu imfa, ndipo akuyembekezera kuukitsidwa, timakhala ndi mtendere wa maganizo. Zimatilimbikitsanso kungopitiriza ndi moyo wathu.

Inde, tikhale ndi chidaliro chonse cha za m’tsogolo pamene Yehova Mulungu, Mpatsi wa moyo, adzakwirira imfa kwamuyaya. Zidzakhala zosangalatsa bwanji! Inde, panthawiyo tidzatha kufunsa kuti: “Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?”​—1 Akorinto 15:55.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Awa ndiwo malo oyamba m’Baibulo pamene imfa ikutchulidwa.

^ ndime 11 Moyo wangwiro waumunthu ndi umene unaperekedwa ngati dipo chifukwa ndi umene Adamu anataya. Uchimo unaipitsa anthu onse, chotero palibe munthu wopanda ungwiro amene akanatha kukhala dipo. Ndiye chifukwa chake Mulungu anatumiza Mwana wake kuchokera kumwamba kudzapereka dipolo. (Salmo 49:7-9) Kuti mudziwe zambiri pankhani imeneyi, onani mutu 7 wa m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 5]

Kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunabweretsa imfa

[Chithunzi patsamba 6]

Yesu anagwira dzanja la mtsikana wakufayo, ndipo anadzuka

[Chithunzi patsamba 7]

Ambiri akuyembekezera nthawi pamene okondedwa awo amene anamwalira adzagalamuka ku tulo ta imfa, monga zinakhalira kwa Lazaro