Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Imfa Imakhudzira Anthu

Mmene Imfa Imakhudzira Anthu

Mmene Imfa Imakhudzira Anthu

“MWANA WA ZAKA SIKISI ANADZIPHA.” Nkhani yodabwitsa kwambiri imeneyi inatuluka m’nyuzipepala, ndipo inali kunena za imfa yomvetsa chisoni ya mtsikana wina dzina lake Jackie. Mayi ake anali atamwalira posachedwa ndi matenda amene sakanachira nawo. Jackie anali atauza ana anzake a m’banja mwawo kuti anafuna ‘kukhala mngelo kuti akakhale ndi mayi ake.’ Atatero anakalowa panjanje sitima ikubwera.

Pamene Ian anali ndi zaka 18, anachonderera wansembe wawo kuti am’fotokozere chifukwa chake bambo ake anafa ndi matenda a kansa. Wansembeyo anati popeza bambo a Ian anali munthu wabwino, Mulungu anawafuna kumwamba. Ian atamva zimenezi, anakhala ndi maganizo osafunanso kupembedza Mulungu wankhanza chotero. Ndipo popeza kuti anaona moyo kukhala wopanda tanthauzo, Ian anaganiza zongokhala ndi moyo wochita zomusangalatsa basi. Atatero, analowerera uchidakwa, mankhwala osokoneza bongo, ndi chiwerewere. Moyo wake unali kupita ku ngozi.

“Amoyo Adziwa Kuti Tidzafa”

Nkhani ziwiri zomvetsa chisoni zimenezi zikusonyeza mmene imfa ingakhudzire moipa miyoyo ya anthu, makamaka ikawagwera modzidzimutsa. Inde, anthu onse amadziwa mfundo yotchulidwa m’Baibulo yakuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa.” (Mlaliki 9:5) Komabe, anthu ambiri amakonda kunyalanyaza dala tsoka losapeweka limeneli. Bwanji inuyo? Moyo uli ndi zinthu zambiri zotitagwanitsa mwakuti tingaiwale zakuti kuli imfa.

“Anthu ambiri amaopa imfa ndipo amayesa kusaiganizira n’komwe,” limatero buku lakuti The World Book Encyclopedia. Komabe mwadzidzidzi, ngozi yoopsa kapena matenda akayakaya akhoza kutipangitsa kuyang’anizana ndi imfa. Kapenanso maliro a mnzathu ngakhale mbale wathu angatikumbutse mwa njira yopweteka kwambiri za kumene anthufe timathera.

Ngakhale zili choncho, anthu ambiri pamaliro amakonda kunena kuti, “Pepani, izi zimachitika.” Ndipo zimachitikadi. Ndipotu, zaka zimaoneka ngati zimadutsa mofulumira moti posatenga nthawi timapezeka kuti tikulimbana ndi mavuto a ukalamba. Zikafika pamenepo, imfa siionekanso ngati ili kutali. Zimawapweteka kwambiri okalamba pamene amapita ku maliro ambiri a okalamba anzawo, ndipo amakhala achisoni chachikulu chifukwa chotaya mabwenzi awo ambiri omwe anakula nawo. Funso lomvetsa chisoni limene limakhala m’maganizo mwa achikulire ambiri n’lakuti “Kaya langa tsiku lifika liti?”

Nkhani Imene Imasiya Anthu ndi Mafunso Ambiri

Palibe munthu amene amakana zakuti imfa ilipo, koma chimene chimachitika pambuyo pa imfa ndiyo nkhani imene imasiya anthu ndi mafunso ambiri. Poona zikhulupiriro zambiri zosiyansiyana zimene zilipo, munthu wokayikira angaone nkhani imeneyi ngati kungokangana zopanda pake pa zinthu zosadziwika. Kwa munthu amene amavomereza imfa ikachitika, amaganiza kuti “moyo ndi wokhawo umene munthuwe uli nawo,” ndi bwino kusangalaliratu mmene ungathere ndi zinthu zabwino koposa.

Koma pali ena amene sakhulupirira kuti zonse zimathera pa imfa. Chikhalirecho, iwo sadziwa kwenikweni kuti chimachitika pambuyo pa imfa n’chiyani. Ena amaganiza kuti moyo umakapitiriza ku malo a mtendere wosatha, pamene ena amaganiza kuti adzakhalanso ndi moyo panthawi ina m’tsogolo, mwina monga munthu wina.

Kawirikawiri ofedwa amafunsa kuti, “Kodi akufa amapita kuti?” Zaka zingapo m’mbuyomu, mamembala a kalabu ya masewera a mpira wa miyendo anali paulendo wopita kumene timu yawo imakamenya mpira. Mwadzidzidzi lole yaikulu inagunda minibasi yawo, ndipo basiyo inachoka pamsewu ndi kuyamba kugubuduzika. Mamembala asanu anafera pomwepo. Mayi wina moyo wake unasinthiratu chimwalirireni mwana wake pangozi imeneyo. Iye amavutika maganizo posamvetsa kuti mwana wake kwenikweni ali kuti. Nthawi ndi nthawi amapita pamanda ake kukalankhula naye kwa maola ndithu. Amadandaula kuti: “Sindikutha kukhulupirira kuti moyo umatheratu pa imfa. Koma mwina umatheratu.”

Ndithudi, mmene imfa timaionera zikhoza kukhudza moyo wathu panopo. Pali mafunso ambiri okhudza mmene anthu amachitira pakagwa tsoka la imfa. Sinkhasinkhani mmene mungawayankhire. Kodi tiyenera kungoiwala za imfa, kuti tizingosamalira za moyo umene tili nawo basi? Kodi tiyenera kulola nkhawa yoopa imfa kutilepheretsa kusangalala ndi moyo? Kodi anamfedwa ayenera kungokhala choncho osadziwa kumene wokondedwa wawo wapita akamwalira? Kodi imfa iyenera kukhala chinthu chosamvetsetseka?