Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amenoni Afunafuna Choonadi cha M’Baibulo

Amenoni Afunafuna Choonadi cha M’Baibulo

Amenoni Afunafuna Choonadi cha M’Baibulo

TSIKU lina m’mawa mu November 2000, amishonale ena a Mboni za Yehova ku Bolivia anasuzumira pawindo la nyumba yawo n’kuona gulu la amuna ndi akazi ooneka amantha ali pa geti. Amishonalewo atatsegula getilo, mawu oyamba a alendowo anali akuti, “Tikufuna kudziwa choonadi kuchokera m’Baibulo.” Alendowo anali Amenoni. Amuna anavala maovololo pamene akazi anavala maepuloni akuda, ndipo ankalankhulana m’Chijeremani. Maso awo anali kuoneka kuti anali kuopa zinazake. Ankangoti chewuchewu kuti aone ngati winawake anali kuwatsatira. Koma ngakhale kuti anali ndi mantha, pokwera masitepe olowera m’nyumba ya amishonalewo mnyamata wina anati, “Ndikufuna n’tadziwa anthu amene amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu.”

Ali m’nyumbamo, alendowo anayamba kumasuka atapatsidwa chakudya. Iwo anachokera ku midzi ya alimi yakutali, kwayokhayokha. Kumeneko anakhala akulandira magazini a Nsanja ya Olonda kudzera papositi kwa zaka sikisi. Iwo anafunsa kuti: “Tinawerenga kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Kodi n’zoona?” Mbonizo zinawasonyeza yankho lake m’Baibulo. (Yesaya 11:9; Luka 23:43; 2 Petro 3:7, 13; Chivumbulutso 21:3, 4) “Mwamvatu,” anatero mlimi wina kwa anzakewo. “Ndi zoona. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso.” Ena anali kunena kuti: “Choonadi tachipeza basi.”

Kodi Amenoni ndani? Kodi amakhulupirira zotani? Tiyeni tibwerere m’mbuyo tifike m’zaka za m’ma 1500 kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa.

Kodi Amenoni Ndani?

M’zaka za m’ma 1500, kuchuluka kwa Mabaibulo amene anali kumasuliridwa ndi kusindikizidwa m’zinenero za anthu wamba ku Ulaya kunachititsa kuti anthu ambiri kumeneko akhalenso ndi chidwi chophunzira Baibulo. Martin Luther ndi anzake ena omwe anali kufuna kukonza zinthu m’Tchalitchi cha Katolika anatsutsa ziphunzitso zambiri za tchalitchicho. Ngakhale zinali choncho, matchalitchi a Chipolotesitanti omwe anali atangopangidwa kumene anapitiriza kuchita zinthu zambiri zosagwirizana ndi Baibulo. Mwachitsanzo, ambiri anali kufuna kuti khanda lililonse lizibatizidwa kuti lizionedwa kuti n’la m’tchalitchi chawocho. Koma anthu ena omwe anali kuphunzira Baibulo n’cholinga chopeza choonadi anazindikira kuti munthu amakhala membala wa mpingo wachikristu pokhapokha akaphunzira bwinobwino n’kudzisankhira zochita asanabatizidwe. (Mateyu 28:19, 20) Alaliki achangu omwe ankakhulupirira zimenezi anayamba kuyendayenda m’matauni ndi m’midzi kuphunzitsa Baibulo ndi kubatiza anthu akuluakulu. Motero, anthu ankatcha alaliki amenewa Anabaptists, kutanthauza “obatiza kachiwiri.”

Mmodzi wa anthu amene ankakhulupirira kuti Anabaptists am’thandiza kupeza choonadi anali Menno Simons. Menno anali wansembe wachikatolika m’mudzi wa Witmarsum kumpoto kwa dziko la Netherlands. Pofika m’chaka cha 1536 iye anali atasiyiratu kugwirizana ndi Tchalitchi cha Katolika ndipo akuluakulu a tchalitchichi anali kum’sakasaka kwambiri. Mu 1542, Mfumu Charles Yachisanu ya Ufumu Wopatulika wa Roma inalonjeza kupereka ndalama zokwana magiluda 100 kwa amene angagwire Menno. Ngakhale zinali choncho, Menno anasonkhanitsa Anabaptists ena n’kupanga mipingo. Posapita nthawi, iye ndi anthu omwe anali kum’tsatira anayamba kutchedwa Amenoni.

Mmene Alili Amenoni Masiku Ano

M’kupita kwa nthawi, Amenoni ambiri anasamuka kumadzulo kwa Ulaya kupita ku North America pothawa kuzunzidwa. Kumeneko anali ndi mwayi wopitiriza kuphunzira kuti adziwe choonadi ndiponso wofalitsa uthenga wawo kwa anthu ambiri. Koma chidwi chachikulu chomwe makolo awo anali nacho chofuna kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi kulalikira chinali chitazirala. Ambiri ankakhulupirirabe ziphunzitso zina ndi zina zimene sizili m’Baibulo. Zina mwa ziphunzitsozi ndi Utatu, chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mzimu wosafa, ndiponso moto wa helo. (Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4; Marko 12:29) Masiku ano, ntchito za amishonale achimenoni kwenikweni zimakhudza zaumoyo ndiponso zoyesayesa kutukula miyoyo ya anthu osati kulalikira zachikristu.

Akuti tsopano pali Amenoni okwana pafupifupi 1,300,000 m’mayiko 65. Komatu, Amenoni a masiku ano amadandaula kuti alibe umodzi pakati pawo, monganso mmene Menno Simons anadandaulira zaka zambiri zapitazo. Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, kusiyana maganizo pankhani ya nkhondo za dziko kunawagawanitsa kwambiri. Amenoni ambiri a ku North America anakana ntchito zausilikali potsatira za m’Baibulo. Koma buku lina lofotokoza mbiri yawo, lakuti An Introduction to Mennonite History, limati: “Pofika m’chaka cha 1914, nkhani yokana ntchito zausilikali m’matchalitchi a Amenoni a kumadzulo kwa Ulaya inali mbiri chabe.” Masiku ano, magulu ena a Amenoni atengera kwambiri moyo wamakono pamene ena sanautengere kwambiri. Ena, m’malo mogwiritsa ntchito mabatani amakono kubophera zovala, adakagwiritsabe ntchito zinthu zachikale zongokoletsa, ndipo amakhulupirira kuti amuna sayenera kumeta ndevu.

Magulu ena a Amenoni, pofunitsitsa kuti asatengere zochitika m’dzikoli masiku ano, asamutsa midzi yawo n’kukakhala m’madera amene maboma a m’mayikowo amawalola kuti azikhala popanda kusokonezedwa. Mwachitsanzo, ku Bolivia akuti kuli Amenoni pafupifupi 38,000 amene ali m’midzi yambirimbiri ya kwayokhayokha, ndipo mudzi uliwonse uli ndi malamulo osiyana ndi a mudzi wina. M’midzi ina salola kuti mudutse galimoto, amangolola ngolo za akavalo basi. M’midzi ina salola wailesi, TV ndiponso nyimbo. Ndiye pali midzi ina imene salola munthu kuphunzira chinenero cha dziko limene akukhalalo. “Pofuna kuti azingotilamulirabe, alaliki salola kuti tiphunzire Chisipanya,” anatero mwamuna wina wa m’mudzi wina wa Amenoni. Ambiri amaona kuti akukhala moponderezedwa ndipo nthawi zonse amaopa kuthamangitsidwa m’midzi mwawo. Izitu zingakhale zoopsa kwambiri kwa munthu amene moyo wake wonse wakhala akukhala m’mudzi wa Amenoni.

Mmene Mbewu za Choonadi Zinafesedwera

Umu ndi mmene zinthu zinalili pamene mlimi wina wachimenoni dzina lake Johann anaona magazini ya Nsanja ya Olonda m’nyumba mwa mnzake wina m’mudzi mwawo. Banja la Johann linachoka ku Canada kusamukira ku Mexico ndipo kenako linapita ku Bolivia. Koma Johann nthawi zonse ankalakalaka thandizo pofunafuna choonadi cha m’Baibulo moti anapempha kuti am’bwereke magaziniyo.

Patapita nthawi, ali m’tauni kukagulitsa zinthu za pafamu yake, Johann analankhula ndi mayi wa Mboni amene anali kugawira magazini a Nsanja ya Olonda mumsikawo. Mayiyo anauza Johann kuti apite kwa mmishonale wina wolankhula Chijeremani, ndipo pasanathe nthawi yaitali Johann anayamba kulandira magazini a Chijeremani a Nsanja ya Olonda kudzera papositi. Magazini iliyonse inkaphunziridwa mwachifatse ndipo mabanja a m’mudzi mwawo ankailandizana mpaka kufika pokhala nsanza. Nthawi zina mabanjawo ankasonkhana n’kuphunzira magazini ya Nsanja ya Olonda mpaka pakati pa usiku. Pophunzirapo anali kuwerenga m’Baibulo malemba a m’magaziniyo amene sanawagwire mawu. Johann anafika potsimikiza kuti Mboni za Yehova ndizo zikuchita chifuniro cha Mulungu mogwirizana padziko lonse. Asanamwalire, Johann anauza mkazi ndi ana ake kuti: “Muziwerenga magazini a Nsanja ya Olonda nthawi zonse. Adzakuthandizani kumvetsa Baibulo.”

Ena mwa achibale a Johann anayamba kufotokozera anthu a m’mudzi mwawo zinthu zimene anali kuphunzira m’Baibulo. Iwo ankati: “Dziko lapansili silidzawonongedwa. Koma Mulungu adzalikonza kukhala paradaiso. Ndipo Mulungu sazunza anthu mu helo.” Sipanapite nthawi yaitali, nkhaniyi inafika kwa alaliki a tchalitchi chawo, ndipo anaopseza banja la Johann kuti alichotsa m’tchalitchimo ngati silisiya. Nthawi ina, banjali likukambirana za mmene akuluakulu a tchalitchiwo ankawaopsezera, mnyamata wina anati: “Sindikudziwa chifukwa chimene tikudandaulira ndi akuluakulu a tchalitchi chathu. Tonse tikudziwa kuti chipembedzo choona ndi chiti, koma mpaka pano sitinachitepo chilichonse.” Mawu amenewa anakhudza mtima abambo ake a mnyamatayu. Posapita nthawi, anthu khumi a m’banjali anauyamba ulendo wobisa womka nafunafuna Mboni za Yehova, ndipo umu ndi mmene anafikira panyumba ya amishonale ija, monga momwe tafotokozera poyamba paja.

Tsiku lotsatira, amishonalewo anapita kukachezera mabwenzi awo atsopanowo kumudzi kwawo. Msewu wonse, galimoto inali ya amishonalewo basi. Akamadutsana ndi ngolo za akavalo, anthu a m’deralo ankachita nawo chidwi kwambiri amishonalewo. Nawonso, amishonalewo ankachita chimodzimodzi. Posakhalitsa anakhala patebulo ndi Amenoni khumi amene anali kuimira mabanja awiri.

Tsiku limenelo, panatenga maola anayi kuti amalize kuphunzira mutu woyamba m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Pandime iliyonse, alimiwo anapezerapo mavesi owonjezera a m’Baibulo ndipo ankafuna kudziwa ngati akugwiritsa ntchito mavesiwo molondola. Ankati akafunsa funso pankapita mphindi zingapo lisanayankhidwe chifukwa ankayamba akambirana kaye m’Chijeremani kenako wina wolankhulira gululo ankayankha m’Chisipanya. Ilitu linali tsiku losaiwalika, koma chizunzo chinali pafupi. Anali atatsala pang’ono kukumana ndi mayesero, monga mmene zinalili ndi Menno Simons pamene anayamba kufunafuna choonadi cha m’Baibulo zaka pafupifupi 500 zapitazo.

Kukumana ndi Mayesero Chifukwa cha Choonadi

Patangotha masiku ochepa, akuluakulu a tchalitchi anafika kunyumba kwa Johann n’kudzaopseza aja amene anali kuchita chidwi ndi choonadi, kuti: “Tamva kuti Mboni za Yehova zinabwera kuno. Muwaletse asabwerenso, ndipo mutipatse titenthe mabuku amene akupatsani, ngati simutipatsa tikuchotsani m’tchalitchi.” Apatu n’kuti atangophunzira kamodzi kokha Baibulo ndi Mboni, moti awa anali mayesero aakulu kwambiri.

Mmodzi wa mitu ya mabanjawo anayankha kuti: “Sitingachite zimene mwatiuzazi. Anthu amenewa anabwera kudzatiphunzitsa Baibulo.” Ndiyeno akuluakulu a tchalitchiwo anatani? Anawachotsa m’tchalitchi chawo chifukwa chophunzira Baibulo. Izi zinali nkhanza zoopsa. Ngolo ya kampani yopanga tchizi yomwe inkabwera kudzatenga mkaka m’makomo mwa anthu m’mudziwo inangodutsa osatenga mkaka wa banja lina, zomwe zinaika banjalo m’mavuto a zachuma, poti njira yopezera ndalama inali yokhayi. Mwamuna wina yemwe anali mutu wa pabanja anachotsedwa ntchito. Winanso anam’letsa kugula zinthu m’sitolo ya m’mudzimo, ndipo mwana wake wamkazi wa zaka khumi anachotsedwa sukulu. Anthu ena a m’mudzimo anazinga nyumba ina kudzatenga mkazi wa mnyamata wina, ati chifukwa choti sangakhale pabanja ndi mwamuna wochotsedwa mumpingo. Ngakhale kuti zinthu zinafika pamenepa, mabanja omwe anaphunzira Baibulowo sanasiye kufunafuna choonadi.

Amishonale aja anapitiriza kuyenda mlungu uliwonse maulendo aatali okachititsa phunziro la Baibulo. Mabanjawo analimbikitsidwa kwambiri ndi maphunzirowo. Pofuna kudzakhala nawo pa maphunzirowa, ena a m’mabanjawa ankayenda kwa maola awiri pangolo za akavalo. Zinali zokhudza mtima kwambiri pamene mabanjawo anapempha kwanthawi yoyamba mmodzi wa amishonalewo kuti apemphere. M’midziyi, Amenoni sapemphera mokweza, motero anali asanamvepo munthu akuwapempherera, moti anakhetsa misozi. Anachitanso chidwi kwambiri kuona wailesi ya kaseti yomwe amishonalewo anabweretsa. M’mudzi mwawomu sankalola nyimbo. Anasangalala kwambiri ndi Nyimbo Zamalimba zokoma kwambiri moti anaganiza zoti aziimba nyimbo za Ufumu akatha phunziro lililonse. Komabe, nkhawa inali idakalipo, Kodi moyo wawo ukhala wotani tsopano malinga n’zimene zinawachitikirazi?

Kupeza Abale Achikondi

Popeza tsopano anali anthu osalidwa m’midzi mwawo, mabanjawa anayamba kudzipangira okha tchizi. Amishonale aja anawathandiza kupeza anthu odzagula katundu wawoyu. Mboni ina yakale kwambiri ya ku North America imene inakulira m’mudzi wina wa Amenoni ku South America inamva za mavuto awo. Mboniyi inali ndi mtima wofunitsitsa kuwathandiza. Pasanathe mlungu umodzi, Mboniyi inapita pandege ku Bolivia kuti ikaonane nawo. Inawalimbikitsa kwambiri mwauzimu, ndiponso inawathandiza kugula galimoto yawoyawo kuti aziyendera popita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu ndiponso kuti azinyamulira zinthu za m’mafamu awo kupita nazo kumsika.

Mayi wina anati: “Zinthu sizinali bwino pamene anayamba kutisala. Tinkapita ku Nyumba ya Ufumu tili achisoni, koma tinkabwerako tili achimwemwe.” Inde, Mboni za m’dzikolo zinathandizaponso pa mavutowo. Ena anaphunzira chinenero cha Chijeremani, ndiponso Mboni zingapo zolankhula Chijeremani zinafika ku Bolivia kuchokera ku Ulaya n’cholinga chodzathandiza kuchita misonkhano m’Chijeremani. Posapita nthawi, anthu 14 ochokera m’midzi ya Amenoni anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.

Pa October 12, 2001, pasanathe n’komwe chaka kuchokera pamene anapita koyamba kunyumba ya amishonale ija, anthu 11 mwa anthu amene anali Anabaptists amenewa anabatizidwanso, ndipo ulendo uno anali kusonyeza kuti adzipereka kwa Yehova. Kuchokera nthawi imeneyo anthu ambiri abatizidwa. Nthawi ina mwamuna wina anati: “Popeza taphunzira choonadi cha m’Baibulo, timamva ngati akapolo omwe amasulidwa.” Winanso anati: “Amenoni ambiri amadandaula kuti alibe chikondi pakati pawo. Koma Mboni za Yehova zimakondana. Ndimakhala wotetezeka ndikakhala pakati pawo.” Nanunso mungakumane ndi mavuto ngati mukufunafuna kumvetsa choonadi cha m’Baibulo. Koma ngati mufunafuna thandizo la Yehova, kusonyeza chikhulupiriro ndiponso kukhala wolimba mtima ngati mmene mabanjawa anachitira, nanunso zinthu zidzakuyenderani ndipo mudzakhala wachimwemwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 25]

Kusangalala chifukwa cholandira mabuku a Chijeremani ofotokoza za m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 26]

Ngakhale kuti m’mbuyo monsemo sankalola nyimbo, pano amaimba akatha phunziro lililonse la Baibulo