Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lakale la Chijeremani Lili Ndi Dzina la Mulungu

Baibulo Lakale la Chijeremani Lili Ndi Dzina la Mulungu

Baibulo Lakale la Chijeremani Lili Ndi Dzina la Mulungu

DZINA lenileni la Mulungu, lakuti Yehova, limapezeka nthawi masauzande angapo m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, lomwe linafalitsidwa m’chinenero cha Chijeremani m’chaka cha 1971. * Komabe, Baibulo limeneli silinali Baibulo loyamba la Chijeremani kukhala ndi dzina la Mulungu. Zikuoneka kuti Baibulo loyamba la Chijeremani limene linali ndi dzina lakuti Yehova linafalitsidwa zaka pafupifupi 500 zapitazo ndi Johann Eck, yemwe anali wotchuka ndi maphunziro apamwamba a zaumulungu mu Roma Katolika.

Johann Eck anabadwira kummwera kwa dziko la Germany m’chaka cha 1486. Pamene amakwanitsa zaka 24 n’kuti ali pulofesa wa maphunziro apamwamba a zaumulungu pa yunivesite ya Ingolstadt. Anakhala pa udindo umenewu mpaka imfa yake m’chaka cha 1543. Eck anali ndi moyo m’nthawi ya Martin Luther, ndipo panthawi ina anthu awiriwa anali kugwirizana. Komabe, Luther kenako anakhala mtsogoleri wa gulu lomwe linafuna kukonzanso zinthu m’Tchalitchi cha Katolika, pamene Eck anali kuikira kumbuyo Tchalitchi cha Katolika.

Mfumu ya Bavaria inauza Eck kuti amasulire Baibulo m’chinenero cha Chijeremani. Baibulo limene anamasuliralo linafalitsidwa m’chaka cha 1537. Malinga n’kunena kwa buku lotchedwa Kirchliches Handlexikon, Baibulo lakelo linatsatira kwambiri malemba oyambirira ndipo “n’loyenera kuti anthu aziligwiritsa ntchito kwambiri kuposa mmene akhala akuligwiritsira ntchito kufikira panopa.” Mu Baibulo la Eck, lemba la Eksodo 6:3 limati: “Ine ndine Ambuye, amene ndinaonekera kwa Abramu, Isake, ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse: koma dzina langa lakuti Adonai, sindinawauze iwo.” Eck analemba pambali pa vesili ndemanga yakuti: “Dzina lakuti Adonai Jehoua.” Akatswiri ambiri a Baibulo amakhulupirira kuti imeneyi ndiyo inali nthawi yoyamba kuti dzina lenileni la Mulungu lilembedwe mu Baibulo la Chijeremani.

Komabe, dzina lenileni la Mulungu lakhala likudziwika ndiponso kugwiritsidwa ntchito kwa zaka masauzande angapo. Mabuku amasonyeza kuti poyambirira penipeni linagwiritsidwa ntchito m’chinenero cha Chihebri. Ahebri anali kugwiritsa ntchito dzina lakuti “Yehova” potchula Mulungu woona yekha. (Deuteronomo 6:4) Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, mawu a Yesu onena kuti anadziwitsa anthu dzina la Mulungu analembedwa m’chinenero cha Chigiriki. (Yohane 17:6) Kuchokera panthawi imeneyo, dzinali lakhala likulembedwa m’zinenero zosawerengeka, ndipo posachedwapa, pokwaniritsa lemba la Salmo 83:18, onse adzadziwa kuti uyo amene dzina lake ndi Yehova ndiye Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Linafalitsidwa choyamba m’Chingelezi mu 1961, ndipo tsopano, lonse lathunthu kapena mbali yake ina, likupezeka m’zinenero zoposa 50.

[Chithunzi patsamba 32]

Baibulo la Eck losindikizidwa m’chaka cha 1558, ndi ndemanga yonena za dzina lakuti Yehova pambali pa Eksodo 6:3