Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Monga Msilikali wa Kristu

Kupirira Monga Msilikali wa Kristu

Mbiri ya Moyo Wanga

Kupirira Monga Msilikali wa Kristu

YOSIMBIDWA NDI YURII KAPTOLA

“Tsopano ndatsimikiza kuti ulidi ndi chikhulupiriro.” Mawu amenewa ananena ndi munthu yemwe sindinamuyembekezere n’komwe kuti angawanene. Iye anali msilikali wa gulu la nkhondo la ku Soviet. Mawu akewo anandipatsa nyonga panthawi imene ndinkafunika kulimbikitsidwa. Ndinali nditatsala pang’ono kulandira chilango chokakhala m’ndende kwa nthawi yaitali, ndipo ndinapemphera ndi mtima wonse kuti Yehova andithandize. Panali zambiri zoti ndilimbane nazo kwa nthawi yaitali zimene zinafuna kupirira komanso kukhala wotsimikiza mtima kusasintha maganizo anga.

NDINABADWA pa October 19, 1962, ndipo ndinakulira kumadzulo kwa dziko la Ukraine. M’chaka chomwecho, bambo anga, omwenso dzina lawo linali Yurii, anakumana ndi Mboni za Yehova. Sipanapite nthawi, iwo anakhala munthu woyamba kukhala wopembedza Yehova m’mudzi mwathu. Ndipo zimene iwo anali kuchita zinadziwika kwa akuluakulu a boma amene sanali kugwirizana ndi zochita za Mboni za Yehova.

Komabe, anthu ambiri a m’mudzi mwathumo anali kuwapatsa ulemu makolo anga chifukwa cha makhalidwe awo achikristu ndi kudera nkhawa anzawo. Makolo anga anali kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene anapeza kuti, ineyo ndi azilongo anga atatu, atiphunzitse kukonda Mulungu kuchokera tili ana. Zimenezi zinandithandiza kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana amene ndinakumana nawo ku sukulu. Limodzi mwa mavuto amene ndinakumana nawo linali loti mwana wa sukulu aliyense anafunikira kumavala baji yosonyeza kuti ndi membala wa gulu la Lenin’s October Children. Chifukwa chakuti monga Mkristu sindinali kuchita nawo zandale, sindinkavala bajiyo, choncho ndinali kuoneka wosiyana ndi ana ena.​—Yohane 6:15; 17:16.

Kenako, nditafika kalasi yachitatu, ana a sukulu onse ankafunika kulowa gulu la achinyamata la Chikomyunizimu lotchedwa Young Pioneers [Anyamata Apainiya]. Tsiku lina kalasi yathu inauzidwa kupita ku bwalo la pa sukulupo kumene kunali mwambo wolowa m’gululi. Ndinachita mantha kwambiri, ndinkaganiza kuti ndikanyozedwa ndi kukalipiridwa. Aliyense, kupatulapo ineyo, pochoka kwawo anatenga nsalu yofiira yatsopano ya gulu la Apainiya yoti azivala m’khosi. Tinaima pa mzere wautali pamaso pa mphunzitsi wamkulu wa pa sukulupo, aphunzitsi ena, ndi ana a sukulu a makalasi akutsogolo. Ana a makalasi akutsogolowo atauzidwa kuti atimange nsaluzo m’khosi, ndinazyolika n’kumayang’ana pansi, ndinkangolakalaka kuti wina asandione.

Kutumizidwa ku Ndende za Kutali

Ndili ndi zaka 18, ndinaweruzidwa kuti ndikhale m’ndende zaka zitatu chifukwa chakuti monga Mkristu sindinafune kuchita nawo zausilikali. (Yesaya 2:4) Chaka choyamba ndinagwirira ukaidiwo m’tauni ya Trudovoye, m’boma la Vinnitskaya ku Ukraine. Kumeneko ndinakumana ndi Mboni zina za Yehova pafupifupi 30. Chifukwa chakuti akuluakulu a kundendeko amafuna kuti tisamacheze, anali kutigawa awiriawiri kukagwira ntchito m’malo osiyanasiyana.

Mu August 1982, ine ndi Eduard, yemwenso anali wa Mboni, limodzi ndi akaidi ena anatitumiza kumpoto kumapiri a Ural pa sitima m’mabogi a ndende. Kwa masiku eyiti tinakhaula ndi kutentha kosaneneka ndiponso kukhala mopanikizana kwambiri mpaka tinafika ku ndende ya Solikamsk, m’boma la Permskaya. Anandiika m’selo yosiyana ndi ya Eduard. Patapita milungu iwiri, ananditumiza kumpoto kwambiri ku mudzi wa Vels, m’chigawo cha Krasnovishersky.

Galimoto imene tinakwera inafika pakati pausiku, ndipo kunali mdima wandiweyani. Ngakhale kuti kunali mdima choncho, msilikali anatilamula kuti tiwoloke mtsinje pa bwato. Komatu mtsinjewo ngakhalenso bwatolo sizinali kuoneka n’komwe! Komabe, tinapapasapapasa mpaka mwamwayi bwatolo tinalipeza ndipo, ngakhale kuti tinali ndi mantha, tinawoloka mtsinjewo. Titawoloka, tinalunjika kumene kunali kuoneka moto pa kaphiri kenakake kamene kanali pafupi ndipo kumeneko tinapezako matenti angapo. Umenewu ndiwo unali mudzi wathu tsopano. Ndinkakhala mu tenti yaikulu ndithu limodzi ndi akaidi ena pafupifupi 30. M’nthawi yozizira, tinali kukhaula ndi chisanu chifukwa nthawi zina kunkazizira kwambiri mpaka kufika pa –40 digiri Seshasi, ndipo ukakhala m’tentimo umangokhala ngati uli panja pomwe. Ntchito yaikulu imene akaidi anzanga anali kugwira inali yodula mitengo, koma ine ndinali kumanga tinyumba ta akaidi.

Chakudya Chauzimu Chifika ku Msasa Wathu Wakutali, Kwawokhawokha

Mu msasawu ndinalimo ndekha wa Mboni; komatu Yehova sananditaye. Tsiku lina amayi anga omwe anali kukhalabe kumadzulo kwa Ukraine ananditumizira phukusi. Chinthu choyamba chimene mlonda anaona atamasula phukusilo chinali kabaibulo kakang’ono. Anatenga kabaibuloko n’kuyamba kuona m’kati mwake. Ndinayesa kuganizira chonena kuti ndipulumutse chuma chauzimu chimenechi. Mosayembekezeka, mlondayo anafunsa kuti: “Ichi n’chiyani?” Ndisanaganize chomuyankha, woyang’anira asilikali wina yemwe anali pomwepo anayankha kuti: “Ndi buku la matanthauzo a mawu limenelo.” Basi ine ndinangoti chete. (Mlaliki 3:7) Woyang’anirayo anasanthula zinthu zina zonse zimene zinali m’phukusimo kenako n’kundipatsa limodzi ndi Baibulo la mtengo wapatalilo. Ndinali wokondwa kwambiri moti ndinamutapirako mtedza umene unali m’phukusimo. Nditalandira phukusili ndinadziwa kuti Yehova sanandiiwale. Mwa kukoma mtima kwake anandithandiza ndi kundisamalira pa zosowa zanga zauzimu.​—Ahebri 13:5.

Sindinasiye Kulalikira

Patapita miyezi ingapo, ndinadzidzimuka kulandira kalata yochokera kwa Mkristu mzanga wina amene anali ku ndende ina makilomita pafupifupi 400 kuchokera kumene ine ndinali. Anandipempha kuti ndifunefune munthu wina amene anaonetsa chidwi. Anali kuganiza kuti munthuyo tsopano ali m’ndende imene ine ndinali. Kunali kupanda nzeru kulemba kalata yosabisa mawu yoteroyo, chifukwa makalata athu ankayamba awawerenga kaye asanatipatse. Choncho sizinali zodabwitsa kuti msilikali wina anandiitanira ku ofesi yake ndi kundichenjeza mwamphamvu kuti ndisamalalikire. Ndiyeno anandilamula kuti ndisaine pepala linalake lonena kuti ndisiya kuuza ena zimene ndimakhulupirira. Ndinayankha kuti sindikumvetsa kuti n’chifukwa chiyani ndiyenera kusaina pepala limenelo, chifukwa aliyense akudziwa kale kuti ndine wa Mboni za Yehova. Ndinamuuza kuti akaidi ena amafuna kudziwa chimene ndinamangidwira. Ndiye ndiziwayankha kuti chiyani? (Machitidwe 4:20) Msilikaliyo anaona kuti sangandiopseze, motero anangoganiza zondichotsapo. Choncho ananditumiza kundende ina.

Ananditumiza ku mudzi wa Vaya, womwe unali pa mtunda wa makilomita 200 kuchokera kumene ndinaliko. Oyang’anira a kumeneko anali kulemekeza maganizo anga monga Mkristu ndipo anandipatsa ntchito zosakhudzana ndi usilikali. Choyamba ndinagwira ntchito ya ukalipentala, kenako ya zamagetsi. Komabe ntchitozi zinali ndi mavuto ake nazo. Mwachitsanzo, tsiku lina anandiuza kuti nditenge zida zanga ndipite ku nyumba yochitiramo zachisangalalo ya m’mudzimo. Nditafika kumeneko asilikali omwe anali m’nyumbayo anasangalala kundiona. Anali kuvutika kukonza magetsi ounikira ndi kukongoletsera zizindikiro zosiyanasiyana za nkhondo. Anafuna kuti ndiwathandize kukonza magetsiwo chifukwa anali kukonzekera chikondwerero cha tsiku la asilikali chimene anali kuchita chaka ndi chaka. Nditapemphera n’kuganizira chochita, ndinawauza kuti sindingagwire ntchito yoteroyo. Ndinawapatsa zida zanga ine n’kuchokapo. Iwo anakandinenera kwa wachiwiri kwa mkulu wa pamalopo. Chinandidabwitsa n’chakuti iye anamvetsera madandaulo a asilikaliwo n’kuyankha kuti: “Ndamutayira kamtengo. Ndi munthu amene amatsatira mfundo zomwe anamanga.”

Ndinalimbikitsidwa ndi Munthu Wosamuyembekezera N’komwe

Ndinamasulidwa pa June 8, 1984, patatha ndendende zaka zitatu ndili m’ndende. Nditabwerera ku Ukraine, ndinafunika kukalembetsa kwa asilikali kuti ndinali mkaidi. Akuluakulu a kumeneko anandiuza kuti ndikaonekeranso m’khoti pakatha miyezi sikisi ndiye zingakhale bwino ngati nditangosamuka m’deralo. Motero ndinachoka ku Ukraine, ndipo m’kupita kwa nthawi ndinapeza ntchito ku Latvia. Kwa kanthawi ndithu ndinali kulalikira ndi kusonkhana ndi kagulu ka Mboni za mu mzinda wa Riga ndi madera ozungulira mzindawu, womwe ndi likulu la dzikolo. Komabe panangopita chaka chimodzi chokha anandiitananso ku usilikali. Ndinauza msilikali ku ofesi yolembetsera ntchitoyi kuti m’mbuyomu ndinakana kugwira ntchito ya usilikali. Iye anandiyankha mozaza kuti: “Koma ukudziwa zimene ukuchita? Tiye kwa msilikali wamkulu tikaone zimene ukanene.”

Anapita nane m’mwamba m’chipinda china popeza nyumbayi inali yosanja. M’chipindacho ndi mmene munali msilikali wamkuluyo, ndipo munali tebulo lalikulu. Iye anamvetsera mwatcheru pamene ndinali kulongosola maganizo anga ndiyeno n’kundiuza kuti nthawi idakalipo yoti ndikhoza kuganiziranso nkhaniyo ndisanaonane ndi komiti yolemba anthu ntchitoyi. Tikutuluka mu ofesi ya msilikali wamkuluyo, msilikali amene anandikalipira poyamba uja anati: “Tsopano ndatsimikiza kuti ulidi ndi chikhulupiriro.” Nditaonekera kwa komiti yoona za asilikali, ndinawafotokozeranso kuti sindilowerera m’zandale kaya zankhondo. Panthawiyi anandisiya.

Tsiku lina madzulo ndinamva kugogoda pa chitseko cha chipinda chimene ndinali kukhala. Ndinatsegula n’kupeza kuti paima mwamuna wina yemwe anavala suti ndipo ananyamula chikwama. Atandiuza dzina lake, anati: “Ndine wapolisi wa KGB. Ndikudziwa kuti ukuvutika ndiponso kuti uzengedwa mlandu m’khoti.” “Inde n’zoona,” ndinayankha motero. Munthuyo anapitiriza kuti: “Tikhoza kukuthandiza ngati utavomera kugwira nafe ntchito.” “Zimenezo n’zosatheka. Sindingasiye kutsatira zimene ndimakhulupirira monga Mkristu,” ndinanena choncho. Anangochoka osayesanso kundinyengerera.

Kubwereranso ku Ndende, N’kumakalalikiranso

Pa August 26, 1986, ndinaweruzidwa ndi Khoti Lalikulu la Riga kuti ndikagwire ukaidi zaka zinayi. Ananditumiza ku ndende ya Riga Central Prison. Kumeneko anandiika mu selo yaikulu momwe munalinso akaidi ena 40. Ndinayesa kulalikira kwa mkaidi aliyense mu selo imeneyo. Ena mwa akaidiwo ankati amakhulupirira Mulungu, pamene ena ankangoseka. Ndinkaona kuti anthuwa anali kukhala m’magulumagulu, ndipo patatha milungu iwiri atsogoleri a magulu amenewo anandiuza kuti sindinali wololedwa kumalalikira chifukwa sindinali kutsatira malamulo awo omwe sanalembedwe pena paliponse. Ndinawafotokozera kuti ndinamangidwa pachifukwa chomwecho chosatsatira malamulo oterowo. Ine ndimatsatira malamulo ena.

Ndinapitiriza kulalikira mochenjera, ndipo nditapeza ena okonda zinthu zauzimu, ndinali ndi mwayi wophunzira Baibulo ndi anthu anayi. Pophunzirapo iwo anali kulemba m’buku ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo zimene tinali kukambirana. Patatha miyezi ingapo, ananditumiza ku ndende ya chitetezo chokhwima ku Valmiera, kumene ndinali kugwira ntchito ya zamagetsi. Kumeneko ndinali kuphunzira Baibulo ndi munthu wina amenenso anali kuchita zamagetsi ndipo patapita zaka zinayi anakhala wa Mboni za Yehova.

Pa March 24, 1988, anandisamutsa ku ndende ya chitetezo chokhwimayo n’kundipititsa ku msasa wa akaidi. Umenewu unali mwayi waukulu chifukwa tsopano ndinali kukhala mwaufulu kwambiri. Ndinagwira ntchito m’malo osiyanasiyana amene anali kumangamo, ndipo nthawi zonse ndinali kufunafuna mipata yoti ndizilalikira. Nthawi zambiri ndimapezeka kuti ndachoka ku msasawo ndikulalikira kwinakwake mpaka kamdima, koma palibe tsiku limene zinandivutapo nditabwerera ku msasako.

Yehova anadalitsa zimene ndinali kuchita. M’dera limene munali msasa wa akaidiwo munali Mboni zingapo ndithu, koma m’mudzi weniweniwo umene munali msasawo munali Mboni imodzi yokha, mlongo wachikulire dzina lake Vilma Krūmin̗a. Ine ndi Mlongo Krūmin̗a tinayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi achinyamata ambiri. Nthawi ndi nthawi, abale ndi alongo a ku Riga anali kubwera kudzachita utumiki, ndipo apainiya okhazikika ena anali kuchokera ngakhale ku Leningrad (mzinda umene tsopano umatchedwa St. Petersburg). Tinayambitsa maphunziro a Baibulo ochuluka ndi thandizo la Yehova, ndipo sipanapite nthawi kuti ine ndilembetse utumiki waupainiya. Ndinali kuthera maola 90 pamwezi ndikulalikira.

Pa April 7, 1990, Khoti la Anthu Onse ku Valmiera linaunikanso mlandu wanga. Mlandu utayamba kuzengedwa, munthu yemwe anali kundiimba mlanduwo ndinamuzindikira. Anali mnyamata winawake amene panthawi ina ndinakambirana naye za Baibulo. Iyenso anandizindikira ndipo anamwetulira koma sananene chilichonse. Ndimakumbukirabe zimene woweruza anandiuza pa mlanduwo tsiku limenelo. Iye anati: “Yurii, chigamulo chimene unapatsidwa zaka zinayi zapitazo chakuti umangidwe chinali chosemphana ndi malamulo. Unalibe mlandu.” Basitu, kumasuka kunali komweko!

Msilikali wa Kristu

Mu June 1990, ndinafunika kukalembetsanso ku ofesi yomwe ija imene anandiitana kuti akandilembe usilikali, koma ulendo uwu n’cholinga choti andipatse chilolezo chokhalira mu Riga. Ndinalowa mu ofesi ya tebulo lalikulu lija momwe zaka zinayi m’mbuyomo ndinauza msilikali wamkulu kuti sindingapite ku usilikali. Pa ulendo uno iye anaimirira kuti andipatse moni, ndipo titagwirana chanza iye anati: “N’zochititsa manyazi kuti mpakana unavutika chomwechi. Pepa kuti zinafika pamenepa.”

Ndinayankha kuti: “Ndine msilikali wa Kristu, ndiye ndiyenera kukwaniritsa ntchito yanga. Inunso Baibulo lingakuthandizeni kupeza zimene Kristu walonjeza otsatira ake, zomwe ndi kukhala ndi moyo wosangalala ndipo m’tsogolo, moyo wosatha.” (2 Timoteo 2:3, 4) Msilikaliyo anati: “Ndinagulatu Baibulo posachedwapa, moti tsopano ndimaliwerenga.” Ndinali ndi buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Ndinatsegula pa mutu umene ukunena za chizindikiro cha masiku otsiriza ndi kumusonyeza mmene ulosi wa m’Baibulo ukugwirizanirana ndi zochitika za m’masiku athu ano. Msilikaliyo anayamikira kwambiri ndipo titagwirananso chanza anandifunira mafuno abwino pa ntchito yanga.

Pofika nthawiyi, ku Latvia m’munda munalidi mutayera mofunika kukolola. (Yohane 4:35) Mu 1991 ndinaikidwa kukhala mkulu pa mpingo. Ndipotu m’dziko lonselo munali akulu awiri okha. Patatha chaka, mpingo umodzi wokhawo womwe unali m’dziko la Latvia unagawidwa kukhala mipingo iwiri, wina wa chinenero cha Chilativia ndi wina wa Chirasha. Ine ndinali mu mpingo wa Chirasha. Anthu ochuluka kwambiri anali kuphunzira choonadi moti chaka chotsatira mpingo wathu unagawidwa kukhala mipingo itatu! Tsopano ndikaona zimene zinali kuchitika nthawi imeneyo, n’zoonekeratu kuti Yehova mwiniyo ndiye anali kutsogolera nkhosa zake ku gulu lake.

Mu 1998, ndinaikidwa kukhala mpainiya wapadera m’tauni ya Jelgava, yomwe ili pa mtunda wa makilomita 40 kulowera kummwera chakumadzulo kwa mzinda wa Riga. M’chaka chomwecho, ndinali mmodzi wa abale oyambirira a ku Latvia omwe anaitanidwa kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ya chinenero cha Chirasha yomwe inachitikira m’tauni ya Solnechnoye, kufupi ndi mzinda wa St. Petersburg, ku Russia. Ndili ku sukuluko, ndinazindikira kuti kukonda anthu n’kofunika kwambiri kuti utumiki uzikuyendera bwino munthu. Chimene chinandichititsa chidwi kwambiri kuposa zimene tinali kuphunzira m’kalasi chinali chikondi ndiponso chidwi chimene banja la Beteli ndi aphunzitsi athu anatisonyeza.

Chinthu chinanso chachikulu pa moyo wanga chinachitika m’chaka cha 2001. M’chakachi ndinakwatira Karina, mkazi wabwino wachikristu. Titachita ukwati, Karina naye anayamba utumiki wa nthawi zonse wapadera, ndipo zimandilimbikitsa tsiku lililonse kuona mkazi wanga akuchokera mu utumiki wa kumunda ali wosangalala. Ndithudi, kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri. Zovuta zimene ndinakumana nazo mu ulamuliro wa Chikomyunizimu zinandiphunzitsa kukhala wodalira Yehova m’zonse. Zonse zimene munthu angataye pofuna kukhalabe paubwenzi ndi Yehova ndi kuima kumbali ya ulamuliro wake, n’zoyenereradi. Moyo wanga uli n’cholinga chifukwa chothandiza ena kuphunzira za Yehova. Ndi ulemu wosaneneka kwa ine kutumikira Yehova “monga msilikali wabwino wa Kristu.”​—2 Timoteo 2:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 29 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 10]

Ndinaweruzidwa kuti ndikagwire ukaidi kwa zaka zinayi ku ndende ya Riga Central Prison

[Chithunzi patsamba 12]

Ndili ndi Karina mu utumiki