Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yendani ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti Ino

Yendani ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti Ino

Yendani ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti Ino

“Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamutenga.”​—GENESIS 5:24.

1. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe zikuchititsa masiku athu ano kukhala osautsa?

NTHAWI ya chipwirikiti! Mawu amenewa akufotokoza bwino zaka za chisokonezo ndi chiwawa zimene anthu akhalamo kuyambira pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa mu 1914. Kwa zaka zonsezo anthu akhala ali ‘m’masiku otsiriza.’ Masoka monga ngati njala, miliri, zivomezi, ndi nkhondo, avutitsa anthu kwambiri kusiyana ndi kalelonse. (2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 6:1-8) Anthu amene amapembedza Yehova nawonso akhala akukumana ndi masokawa. Mwa njira inayake, tonse tiyenera kulimbana ndi mavuto ndiponso kusadalirika kwa zinthu masiku ano. Mavuto azachuma, kusakhazikika kwa ndale, upandu, ndiponso matenda, ndi zina mwa zinthu zimene zimachititsa moyo kukhala wovuta kwambiri.

2. Kodi atumiki a Yehova akumana ndi mavuto otani?

2 Komanso, atumiki a Yehova ambiri apirira mazunzo ambirimbiri obwera chifukwa chakuti Satana akuchitabe nkhondo ndi anthu ‘amene akusunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.’ (Chivumbulutso 12:17) Ndipo ngakhale kuti si tonse amene tazunzidwapo mwachindunji, Akristu onse oona ayenera kulimbana ndi Satana Mdyerekezi ndiponso mzimu umene iye amalimbikitsa mwa anthu. (Aefeso 2:2; 6:12) Timafunika kukhala maso nthawi zonse kuti mzimu umenewo usatilowerere, chifukwa timapezana nawo kuntchito, kusukulu, ndi m’malo ena alionse amene timacheza ndi anthu omwe alibe chidwi ndi kupembedza koyera.

Yendani ndi Mulungu Osati ndi Amitundu

3, 4. Kodi Akristu ndi osiyana motani ndi dzikoli?

3 Kalelo m’nthawi ya atumwi, Akristu anayesetsanso kulimbana ndi mzimu wa dzikoli, ndipo zimenezi zinawachititsa kukhala osiyana kwambiri ndi anthu amene sanali mu mpingo wachikristu. Paulo anafotokoza kusiyana kumene kunalipo kuti: “Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.”​—Aefeso 4:17-19.

4 Mawu amenewa akufotokoza bwino kwambiri mmene dzikoli lilili mu mdima wadzaoneni mwauzimu komanso pa nkhani ya makhalidwe. Zinali choncho m’masiku a Paulo ndipo ndi mmenenso zilili masiku athu ano. Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, Akristu masiku ano ‘sayendanso monga amitundu amayendera.’ M’malo mwake iwo ali ndi mwayi wosaneneka woyenda ndi Mulungu. N’zoona kuti anthu ena angakayikire ngati m’pomveka kunena kuti anthu omwe ndi opanda ungwiro amayenda ndi Yehova. Komatu Baibulo limasonyeza kuti zimenezi n’zotheka. Ndiponso n’zimene Yehovayo amayembekezera. M’zaka za m’ma 700 B.C.E., mneneri Mika analemba mawu ouziridwa awa: ‘Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?’​Mika 6:8.

Kodi Tingayende Bwanji ndi Mulungu, Ndipo N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutero?

5. Kodi zingatheke bwanji kuti munthu wopanda ungwiro ayende ndi Mulungu?

5 Kodi Mulungu wamphamvuyonse ndiponso wosaoneka tingayende naye bwanji? N’zachidziwikire kuti sitingayende naye monga mmene timayendera ndi anthu anzathu. M’Baibulo, mawu akuti “kuyenda” angatanthauze “kuchita zinthu motsatira ndondomeko inayake.” * Ndi mfundo imeneyi, tikuona kuti munthu amene amayenda ndi Mulungu amatsatira moyo umene Mulunguyo amafuna ndiponso umene amakondwera nawo. Kukhala ndi moyo woterowo kumatichititsa kukhala osiyana ndi anthu ambiri amene timakhala nawo. Komatu palibe chinthu china chabwino chimene Mkristu angasankhe choposa kukhala ndi moyo woterewu. N’chifukwa chiyani tikutero? Zifukwa zake n’zambiri.

6, 7. N’chifukwa chiyani kuyenda ndi Mulungu ndicho chinthu chabwino koposa?

6 Choyamba, Yehova ndiye Mlengi wathu. Ndiye Chitsime cha moyo wathu ndipo ndiye amatipatsa zonse zimene timafunikira kuti tikhale ndi moyo. (Chivumbulutso 4:11) Motero, ndiye yekha amene ali ndi ufulu wotiuza mmene tiyenera kuyendera. Ndiponso, kuyenda ndi Mulungu ndiko njira yothandiza koposa. Kwa amene amayenda ndi Yehova, iye wawakonzera zoti machimo awo akhululukidwe, ndipo amawapatsa chiyembekezo chodalirika chokhala ndi moyo wosatha. Atate wathu wakumwamba amene amatikonda kwambiriyu amaperekanso malangizo anzeru omwe amathandiza anthu amene amayenda naye kuti azipindula ndi moyo wawo panopa, ngakhale kuti iwo ndi opanda ungwiro ndiponso akukhala m’dziko lomwe likugona mwa Satana. (Yohane 3:16; 2 Timoteo 3:15, 16; 1 Yohane 1:8; 2:25; 5:19) Chifukwa chinanso choyendera ndi Mulungu n’chakuti tikakhala ofunitsitsa kuyenda naye timathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendere ndi umodzi.​—Akolose 3:15, 16.

7 Chomalizira, ndiponso chofunika kwambiri pa zonse, n’chakuti tikamayenda ndi Mulungu timasonyeza mbali imene tili pankhani yofunika koposa yomwe inabuka kalelo m’munda wa Edene, yomwe ndi nkhani ya ulamuliro. (Genesis 3:1-6) Mmene tikukhalira moyo wathu zimasonyeza kuti taima mosasunthika kumbali ya Yehova, ndipo timalengeza mosaopa kuti iye yekha ndiye Wolamulira Wamkulu woyenerera. (Salmo 83:18) Motero timachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lathu lakuti dzina la Mulungu liyeretsedwe ndipo chifuniro chake chichitike. (Mateyu 6:9, 10) Ndithudi, amene amasankha kuyenda ndi Mulungu amasankha mwanzeru kwambiri. Iwo angakhale otsimikiza kuti moyo wawo ukulowera koyenera, chifukwa Yehova ndi yekhayo “wanzeru.” Palibe chimene amalakwitsa.​—Aroma 16:27.

8. Kodi nthawi zimene anali kukhalamo Enoke ndi Nowa zinali zofanana bwanji ndi nthawi yathu ino?

8 Koma kodi n’zotheka bwanji kukhala ndi moyo umene Akristu amayenera kukhala nawo pomwe tili m’nthawi ya chipwirikiti ndiponso anthu ambiri alibe chidwi chotumikira Yehova? Yankho la funsoli tingalipeze poganizira za anthu okhulupirika akale amene anakhalabe okhulupirika m’nthawi zovuta kwambiri. Awiri chabe mwa anthu amenewa ndi Enoke ndi Nowa. Onse awiri anali kukhala m’nthawi zofanana kwambiri ndi imene tilimoyi. Kuipa kunali ponseponse. M’masiku a Nowa dziko lapansi linadzaza ndi chiwawa ndiponso chiwerewere. Ngakhale zinali choncho, Enoke ndi Nowa anakana mzimu wa dziko limene anali kukhalamo ndipo anayenda ndi Yehova. Kodi iwo anatha bwanji kuchita zimenezi? Kuti tiyankhe funso limeneli, m’nkhani ino tikambirana za Enoke. M’nkhani yotsatira tidzakambirana za Nowa.

Enoke Anayenda ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti

9. Kodi tikudziwapo zotani za Enoke?

9 Enoke ndiye munthu woyamba m’Malemba kutchulidwa kuti anayenda ndi Mulungu. Nkhani ya m’Baibulo imanena kuti: “Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela.” (Genesis 5:22) Ndiyeno nkhaniyi imafotokoza zaka zimene Enoke anakhala ndi moyo, zomwe, ngakhale kuti zinali zambiri poyerekeza ndi moyo wathu, zinali zochepa malinga ndi mmene anthu anali kukhalira masiku amenewo. Kenako imati: “Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamutenga.” (Genesis 5:24) Mosakayikira, Yehova anasamutsa Enoke m’dziko la anthu amoyo n’kumugonetsa mu imfa zinthu zisanafike poti anthu amene anali kumutsutsa amuchitire choipa chilichonse. (Ahebri 11:5, 13) Kupatulapo mavesi achidule amenewa, m’Baibulo muli malo ochepa amene amanena za Enoke. Ngakhale ndi choncho, tikaona mfundo zimene zilipozi limodzinso ndi maumboni ena, m’pomveka kunena kuti Enoke anali kukhala m’nthawi ya chipwirikiti.

10, 11. (a) Kodi kuipa kunafalikira motani Adamu ndi Hava atapanduka? (b) Kodi ndi uthenga waulosi wotani umene Enoke analalikira, ndipo mwachionekere anthu anatani ataumva?

10 Mwachitsanzo, Adamu atachimwa sipanapite nthawi kuti anthu akhale oipa. Taonani mmene kuipaku kunachitikira mofulumira. Baibulo limati mwana woyamba kubadwa wa Adamu, Kaini, anali munthu woyamba kupha munthu mnzake. Iye anapha mchimwene wake Abele. (Genesis 4:8-10) Abele ataphedwa mwankhanza, Adamu ndi Hava anabalanso mwana wina wamwamuna ndipo anamutcha dzina lake Seti. Za iye timawerenga kuti: “Kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.” (Genesis 4:25, 26) N’zomvetsa chisoni kuti “kutchula dzina la Yehova” kumeneko kunali chifukwa cha mpatuko. * Patapita zaka zambiri Enosi atabadwa, mbadwa ina ya Kaini, dzina lake Lameke, inapeka nyimbo imene inaimbira akazi ake awiri. M’nyimboyo inali kunena kuti inapha mnyamata wina amene anaipweteka. Munalinso chenjezo ili m’nyimboyo: “Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri, koma Lameke makumi asanu ndi awiri.”​—Genesis 4:10, 19, 23, 24.

11 Mfundo zachidule ngati zimene zatchulidwazi zimasonyeza kuti sipanatenge nthawi kuti kuipa kumene anayambitsa Satana m’munda wa Edene kuchititse ana a Adamu kukhala oipa. Tsono Enoke anali mneneri wa Yehova pakati pa anthu oterowo, ndipo mawu ake amphamvu ouziridwawo akugwirabe ntchito ngakhale masiku ano. Yuda ananena kuti Enoke analosera kuti: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.” (Yuda 14, 15) Mawu amenewa adzakwaniritsidwa onse bwinobwino pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Komabe n’zosakayikitsa kuti ngakhale m’masiku a Enoke “ochimwa osapembedza” ambiri ananyansidwa pomva ulosi wa Enoke. Choncho tingaone kuti Yehova anasonyeza chikondi kwambiri posamutsa mneneriyo kuti anthuwo asamuchitire choipa.

Kodi N’chiyani Chimene Chinalimbikitsa Enoke Kuti Ayende ndi Mulungu?

12. Kodi n’chiyani chinasiyanitsa Enoke ndi anthu a m’masiku ake?

12 M’munda wa Edene muja, Adamu ndi Hava anamvera Satana, ndipo Adamu anapandukira Yehova. (Genesis 3:1-6) Mwana wawo Abele anachita zosiyana ndi zimene iwo anachitazo, ndipo Yehova anasangalala naye. (Genesis 4:3, 4) Zachisoni n’zakuti ana ambiri a Adamu sanakhale ngati Abele. Komabe Enoke, yemwe anabadwa patapita zaka mahandiredi angapo, anakhala ngati Abele. Kodi Enoke anasiyana bwanji ndi mbadwa zina zambirimbiri za Adamu? Mtumwi Paulo anayankha funso limeneli mwa kunena kuti: “Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamutenga: pakuti asanamutenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.” (Ahebri 11:5) Enoke anali mmodzi wa ‘mtambo waukulu wa mboni’ za m’nthawi zakale Chikristu chisanayambe zomwe zinali zitsanzo zabwino kwambiri za anthu a chikhulupiriro. (Ahebri 12:1) Chikhulupiriro ndicho chinathandiza Enoke kuti akhalebe ndi khalidwe labwino kwa moyo wake wonse wa zaka zoposa 300, zomwe tikaziyerekezera ndi zaka zomwe ambirife masiku ano timakhala ndi moyo, ndi zochuluka kuposa maulendo atatu.

13. Kodi Enoke anali ndi chikhulupiriro chotani?

13 Paulo anafotokoza chikhulupiriro chimene Enoke anali nacho limodzinso ndi mboni zina pamene analemba kuti: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Inde, chikhulupiriro ndicho kuyembekezera zinthu mosakayikira konse, chifukwa cha zomwe wina watitsimikizira, kuti zimene tikuyembekezerazo zidzachitikadi. Chimatipangitsa kuyembekezera zinthu ndi mtima wonse ndipo chimakhudza mmene timaonera zinthu zofunika kwambiri pamoyo wathu. N’chikhulupiriro choterocho chimene chinathandiza Enoke kuyenda ndi Mulungu ngakhale kuti anthu amene anali kukhala nawo sanayende Naye.

14. Kodi Enoke ayenera kuti anali ndi chikhulupiriro chifukwa chodziwa molondola zinthu ziti?

14 Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chenicheni ngati akudziwa zinthu molondola. Kodi Enoke anali kudziwa zinthu zotani? (Aroma 10:14, 17; 1 Timoteo 2:4) Ndithudi iye ayenera kuti anali kudziwa zimene zinachitika mu Edene. N’kuthekanso kuti anamvapo za mmene moyo unalili m’munda wa Edene, munda womwe n’kutheka kuti unali udakalipo panthawiyo ngakhale kuti anthu anali ataletsedwa kufikako. (Genesis 3:23, 24) Ndiponso iye anali kudziwa cholinga cha Mulungu chakuti ana a Adamu adzaze dziko lapansi ndi kupanga dziko lonselo kukhala lofanana ndi Paradaiso woyambirirayo. (Genesis 1:28) Komanso, n’zosakayikitsa kuti Enoke anali kuona lonjezo la Yehova lotulutsa Mbewu imene idzaphwanya mutu wa Satana ndi kuthetsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha chinyengo cha Satana kukhala lofunika kwambiri. (Genesis 3:15) Inde, ulosi wouziridwa wa Enoke mwiniwakeyo, womwe ukupezeka m’buku la Yuda, unanena za kuwonongedwa kwa mbewu ya Satana. Ndiye popeza kuti Enoke anali ndi chikhulupiriro, tikudziwa kuti iye anapembedza Yehova monga yemwe amakhala “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Choncho, ngakhale kuti Enoke sanadziwe zinthu zonse zimene ifeyo tikuzidziwa, anali kudziwa zinthu zokwanira kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Pokhala ndi chikhulupiriro choterocho, iye anakhalabe wokhulupirika m’nthawi ya chipwirikiti.

Tengerani Chitsanzo cha Enoke

15, 16. Kodi tingatengere motani moyo umene Enoke anali nawo?

15 Popeza kuti, mofanana ndi Enoke, tikufuna kusangalatsa Yehova m’nthawi ya chipwirikiti imene tilimo masiku ano, ndi bwino kuti titengere chitsanzo cha Enokeyo. Tifunika kumudziwa bwino Yehova ndi cholinga chake, ndipo tizisunge zimenezo. Komano si zokhazo. Tiyenera kulola kuti zinthu zimene tazidziwa molondolazo zizitsogolera moyo wathu. (Salmo 119:101; 2 Petro 1:19) Tifunika kutsogoleredwa ndi kaganizidwe ka Mulungu, ndipo nthawi zonse tiziyesetsa kumusangalatsa ndi chilichonse chimene tikuganiza ndi kuchita.

16 Palibe winanso amene analembedwa kuti anali kutumikira Yehova m’masiku a Enoke, koma n’zachidziwikire kuti mwina Enoke analipo yekha kapena panali kagulu kochepa chabe. Ifenso tilipo ochepa kwambiri m’dzikoli, komatu zimenezi sizitigwetsa ulesi. Yehova adzatithandiza mosasamala kanthu kuti ndi ndani amene akutitsutsa. (Aroma 8:31) Enoke anachenjeza molimba mtima kuti anthu osapembedza adzawonongedwa. Ifenso timalalikira molimba mtima “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” ngakhale kuti ena amatiseka, kutitsutsa, ndi kutizunza. (Mateyu 24:14) Enoke sanakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali ngati mmene anthu ambiri a m’masiku ake ankakhalira. Ngakhale ndi choncho, iye sanayembekezere zinthu za dziko limenelo. Anaika maso ake pa chinthu chofunika kwambiri. (Ahebri 11:10, 35, 36) Ifenso taika maso athu pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Yehova. Motero sitigwiritsa ntchito kwambiri dzikoli. (1 Akorinto 7:31) M’malo mwake, timagwiritsa ntchito mphamvu zathu ndi chuma chathu makamaka potumikira Yehova.

17. Kodi ife tikudziwa zotani zimene Enoke sanazidziwe, choncho tiyenera kuchitanji?

17 Enoke anali kukhulupirira kuti Mbewu imene Mulungu analonjeza idzaonekera m’nthawi yoikika ya Yehova. Tsopano patha zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene Mbewuyo, yomwe ndi Yesu Kristu, inaoneka, kupereka dipo, ndi kutsegula njira yakuti ife, ndiponso mboni zakale zokhulupirika monga Enoke, tikalandire moyo wosatha. Mbewu imeneyo, yomwe tsopano inaikidwa pa mpando wachifumu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, inachotsa Satana kumwamba ndi kumuponyera ku dziko lino lapansi, ndipo paliponse tikuona mavuto amene abwera chifukwa cha zimenezi. (Chivumbulutso 12:12) Ndithudi, pali zambiri zimene ife tingadziwe kusiyana ndi zimene Enoke akanadziwa. Ndiyetu tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro cholimba monga chimene iye anali nacho. Ndipotu, kutsimikiza mtima kwathu kwakuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa kuzilamulira zonse zimene timachita. Mofanana ndi Enoke, tiyeni tiziyenda ndi Mulungu ngakhale kuti tikukhala m’nthawi ya chipwirikiti.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani ndime 6, patsamba 220, mu Voliyumu 1 ya buku la Insight on the Scriptures, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 10 Enosi asanabadwe, Yehova analankhula ndi Adamu. Ndipo Abele anapereka nsembe kwa Yehova yomwe Yehovayo anailandira. Komanso Mulungu analankhula ndi Kaini asanaphe mbale wake pokwiya ndi nsanje. Motero, kuyamba “kutchula dzina la Yehova” kumeneku kuyenera kuti kunali mwa njira yachilendo, osati pa kupembedza koyera.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kuyenda ndi Mulungu kumatanthauzanji?

• N’chifukwa chiyani kuyenda ndi Mulungu kuli kofunika koposa?

• N’chiyani chimene chinathandiza Enoke kuyenda ndi Mulungu ngakhale kuti anali kukhala m’nthawi ya chipwirikiti?

• Kodi Enoke tingamutengere bwanji?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Pokhala ndi chikhulupiriro, “Enoke anayendabe ndi Mulungu”

[Chithunzi patsamba 17]

Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Woman, far right: FAO photo/​B. Imevbore; collapsing building: San Hong R-C Picture Company