Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ochuluka Ayamba Kupembedza Yehova

Anthu Ochuluka Ayamba Kupembedza Yehova

“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”

Anthu Ochuluka Ayamba Kupembedza Yehova

MAULOSI a m’Baibulo onena za masiku ano anati makamu a anthu ochokera m’mitundu yonse adzakhamukira kwa Yehova n’kuyamba kumupembedza m’njira yokwezeka. Mwachitsanzo, Yehova Mulungu ananena mawu otsatirawa, kudzera mwa mneneri Hagai: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” (Hagai 2:7) Yesaya ndi Mika analosera kuti m’nthawi yathu ya “masiku otsiriza” ino, mitundu ya anthu idzapembedza Yehova m’njira yoyenerera.​—Yesaya 2:2-4; Mika 4:1-4.

Kodi maulosi amenewa akukwaniritsidwadi masiku ano? Tiyeni tione tokha mmene zinthu zikuyendera. Pa zaka 10 zapitazi, anthu atsopano opitirira 3,110,000 adzipereka kwa Yehova m’mayiko opitirira 230. Inde, padziko lonse anthu a Mboni za Yehova 6 pa 10 aliwonse amene akutumikira Yehova anabatizidwa m’zaka 10 zapitazi. M’chaka cha 2004, pafupifupi mphindi ziwiri zilizonse munthu mmodzi ankabatizidwa n’kukhala Mboni ya Yehova. *

Monga mmene zinalili Chikristu chitangoyamba kumene, masiku ano ‘unyinji wakhulupirira ndipo watembenukira kwa Ambuye.’ Ngakhale kuti kuchuluka kwa anthu pakokha sikutsimikizira kuti pali madalitso a Mulungu, kumapereka umboni wakuti “dzanja la Ambuye” lili ndi anthu ake. (Machitidwe 11:21) Kodi n’chiyani chimakopa anthu mamiliyoni onsewa kuti ayambe kupembedza Yehova? Ndipo kodi zimenezi zimakukhudzani bwanji inuyo panokha?

Anthu Amtima Wabwino Amakopeka

Yesu ananena mosapita m’mbali kuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Motero, Yehova ndiye kwenikweni amakoka anthu “ofuna moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48, NW) Mzimu wa Mulungu ungathe kugalamutsa anthu kuti ayambe kufunafuna zinthu zauzimu. (Mateyu 5:3) Anthu ena angayambe kufunafuna Mulungu n’kudziwa cholinga chake chomwe analengera anthu, pa zifukwa monga kupwetekedwa chikumbumtima, kutaya mtima, kapena vuto linalake lalikulu.​—Marko 7:26-30; Luka 19:2-10.

Anthu ambiri amakopeka n’kuyamba kulambira Yehova chifukwa choti ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova imawathandiza kumvetsa zinthu zimene sazimvetsa bwino.

Davide wa ku Italy, yemwe ankagulitsa mankhwala osokoneza bongo, ankavutika ndi funso lakuti, “Ngati Mulungu alipodi, n’chifukwa chiyani anthu akuvutikabe ndi kusoweka kwa chilungamo?” Iyeyo analibe nazo ntchito kwenikweni zachipembedzo, motero anafunsa zimenezi pofuna kungoyambitsa mkangano basi. Iye anati: “Sindinkaganiza kuti angandiyankhe zomveka ndiponso zogwira mtima. Koma wa Mboni amene ankalankhula nane analeza mtima kwambiri ndipo zonse zimene ankanena ankazitsimikizira ndi malemba a m’Baibulo. Zimene tinakambiranazo zinandikhudza kwambiri.” Tikunena pano, Davide anasiya kuchita zinthu zosalongosoka ndipo akutumikira Yehova.

Anthu ena amabwera m’gulu la Yehova lapadziko lapansi pano chifukwa chofuna kuti moyo wawo ukhale n’cholinga. Mayi wina yemwe ndi dokotala wa matenda a maganizo mumzinda wa Zagreb ku Croatia, anapita kwa dokotala wina wotchuka wa maganizo kuti akafune thandizo popeza kuti iyemwini analinso ndi vuto la maganizo. Iyeyu anadabwa dokotalayo atamupatsa nambala ya telefoni ya ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Zagreb, komanso dzina la wa Mboni wina amene dokotalayo ankam’dziwa. Ndiye anamulangiza kuti: “Sindikukayika kuti anthu awa akakuthandizani. Sindikufuna kukulangizani zopita ku matchalitchi ena, chifukwa choti kumeneko mukangopezako ziboliboli basi, simukamvako chilichonse ndipo simukapindulako chilichonse. Ndikudziwa kuti sakakuthandizani kumeneko. Ndalangizapo kale odwala ena kuti akaonane ndi a Mboni za Yehova, ndipo ndikuona kuti inunso angakuthandizeni kwambiri.” A Mboniwo anasangalala kwambiri kumuyendera mayiyu ndipo posakhalitsa anayamba kuphunzira naye Baibulo. Patatha milungu yochepa chabe, mayi uja ananena mosangalala kuti kudziwa cholinga cha Mulungu kwam’thandiza kuti tsopano moyo wake aziumva kukoma chifukwa chokhala ndi cholinga chenicheni pamoyo.​—Mlaliki 12:13.

Anthu ambiri aona kuti akakhala pa vuto linalake, choonadi cha m’Baibulo chokha ndicho chimawalimbikitsadi. Ku Greece, kamnyamata kena ka zaka seveni kanagwa kuchokera padenga la kusukulu ndipo kanamwalira. Patatha miyezi ingapo, anthu awiri a Mboni anakumana ndi mayi a mwanayu n’kuyesa kuwalimbikitsa pokambirana nawo za chiyembekezo cha chiukiriro. ( Yohane 5:28, 29) Atatero mayiyo anayamba kulira. Ndiyeno alongo awiriwo anamufunsa kuti: “Kodi tingathe kubwera nthawi ina imene mungakonde kuti tidzakambirane bwinobwino zinthu zina zokhudza Baibulo?” Koma, mayiyo anawayankha kuti: “Mundiuze pompano.” Mayiyo anawatengera kunyumba kwake, ndipo anayamba kumuphunzitsa Baibulo. Tikunena pano banja lake lonse likutumikira Yehova.

Kodi Mukugwira Nawo Ntchitoyi?

Nkhani ngati zimenezi zikusonyeza zimene zikuchitika padziko lonse. Yehova akusonkhanitsa ndi kuphunzitsa khamu lalikulu la olambira oona kuchokera m’mitundu yosiyanasiyana. Gulu la padziko lonse limeneli lili ndi chiyembekezo chosangalatsa chodzapulumuka posachedwapa pa chimaliziro cha dongosolo loipa la zinthuli, n’kudzakhala m’dziko latsopano lachilungamo.​—2 Petro 3:13.

Chifukwa cha madalitso a Yehova, ntchito yosonkhanitsa anthuyi, yomwe siinachitikepo moteremu n’kale lonse, ikupitirizabe kuyenda bwino kwambiri mpakana pamene idzathere. (Yesaya 55:10, 11; Mateyu 24:3, 14) Kodi inuyo mukuchita nawo mwakhama ntchito yolalikira za Ufumuyi? Ngati mukutero, musakayike ngakhale pang’ono kuti Mulungu akuthandizani ndipo nanunso munganene mawu a wamasalmo akuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, pa mwezi wa September ndi October.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” ​—YOHANE 6:44

[Bokosi patsamba 8]

KODI NDANI AKUBWERETSA ANTHU ONSEWA?

“Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.”​—Salmo 127:1.

“Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.”​—1 Akorinto 3:6, 7.