Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Kristu Ndani?

Kodi Yesu Kristu Ndani?

Kodi Yesu Kristu Ndani?

TAGANIZIRANI mmene Andreya anamvera pamene anamva kwa nthawi yoyamba mawu a Yesu wa ku Nazarete. Andreya anali Myuda wachinyamata ndipo Baibulo limati iye atamva mawu a Yesuwo anathamanga kupita kwa mchimwene wake n’kumuuza kuti: “Tapeza ife Mesiya [kapena kuti Kristu].” (Yohane 1:41) M’Chihebri ndi m’Chigiriki mawu amene kawirikawiri amawamasulira kuti “Mesiya” ndiponso kuti “Kristu” amatanthauza “Wodzozedwa.” Yesu anali Wodzozedwa, kapena kuti Wosankhidwa wa Mulungu, komanso anali Mtsogoleri yemwe anthu analonjezedwa. (Yesaya 55:4) Malemba anali ndi maulosi okhudza iyeyo, ndipo Ayuda panthawiyi ankayembekezera kudza kwake.​—Luka 3:15.

Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu analidi Wosankhidwa wa Mulungu? Taganizirani zimene zinachitika m’chaka cha 29 C.E. pamene Yesu anali ndi zaka 30. Iye anapita kwa Yohane Mbatizi kuti akabatizidwe mu mtsinje wa Yorodano. Baibulo limati: “Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inam’tsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Atamva mawu amenewo, kodi Yohane akanakayikira m’pang’ono pomwe kuti Yesu anali Wosankhidwa wa Mulungu? Pomutsanulira Yesu mzimu Wake woyera, Yehova Mulungu anam’dzoza Yesuyo, kapena kuti kumuika kukhala Mfumu ya Ufumu Wake womwe ukubwera. Motero, Yesu anakhala Yesu Kristu, kapena kuti Yesu Wodzozedwa. Komano kodi Yesu anali Mwana wa Mulungu m’njira yotani? Kodi anachokera kuti?

Ndi “Wakale Lomwe”

Moyo wa Yesu tingaugawe mbali zitatu. Mbali yoyamba inayamba kale kwambiri asanabadwe padziko lapansi monga munthu. Lemba la Mika 5:2 limati “matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.” Yesu mwini ananena kuti: “Ndine wochokera Kumwamba.” (Yohane 8:23) Ali kumwambako iye anali munthu wauzimu wamphamvu.

Popeza kuti zolengedwa zonse zili ndi chiyambi, panali nthawi ina pamene Mulungu anali yekhayekha. Komabe, Mulungu anayamba kulenga zinthu zaka zosawerengeka zapitazo. Kodi anayambira kulenga chiyani? Buku lomaliza la m’Baibulo limanena kuti Yesu ndiye anali “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu ndi “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” Izi zili chonchi “pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo.” (Akolose 1:15, 16) Inde, Yesu ndi yekhayo amene analengedwa ndi Mulungu mwini. Motero, amatchedwa “Mwana wake wobadwa yekha” wa Mulungu. (Yohane 3:16) Mwana woyamba kubadwayu amatchedwanso “Mawu.” (Yohane 1:14) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti asanabadwe monga munthu, iyeyo ndiye ankalankhulira Mulungu kumwamba.

“Mawu” ameneyu anali ndi Yehova Mulungu “pachiyambi,” pamene “kumwamba ndi dziko lapansi” zimalengedwa. Iyeyu ndiye amene Mulungu anali kumulankhulitsa pamene ananena kuti: “Tipange munthu m’chifanizo chathu.” (Yohane 1:1; Genesis 1:1, 26) Mwana wobadwa yekha wa Yehovayu anali pambali pa Atate wake, kugwira nawo ntchito limodzi. Mophiphiritsira, lemba la Miyambo 8:22-31, limanena za Mwanayu akufotokoza kuti: “Ndinali pa mbali [pa Mlengi] ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse.”

Yehova Mulungu ndi Mwana wake wobadwa yekha ayenera kuti anadziwana bwino zedi pogwirira ntchito limodzi chonchi. Kukhalira limodzi ndi Yehova kwa zaka zosawerengeka kunam’khudza kwambiri zedi Mwana wa Mulungu. Mwana womverayu anafika powatengera ndendende Atate wake, Yehova. N’chifukwa chake lemba la Akolose 1:15 limamutcha Yesu kuti ndi “fanizo la Mulungu wosaonekayo.” Ichi n’chimodzi mwa zifukwa zimene kudziwa Yesu kuli kofunika kuti tikhale osangalala mwauzimu ndiponso kuti tim’dziwe Mulungu, mogwirizana ndi chikhumbo chathu chachibadwa. Chilichonse chimene Yesu anachita ali padziko pano n’chimene Yehova anafuna kuti achite. Motero, kudziwa bwino Yesu kumatithandizanso kudziwa bwino Yehova. (Yohane 8:28; 14:8-10) Koma kodi Yesu anafika bwanji padziko lapansi?

Atakhala Munthu Padziko Lapansi

Mbali yachiwiri ya moyo wa Yesu inayamba Mulungu atatumiza Mwana wakeyu padziko lapansi. Yehova anachita zimenezi potumiza modabwitsa, moyo wa Yesu kuchokera kumwamba n’kuulowetsa m’mimba mwa namwali wokhulupirika wachiyuda, dzina lake Mariya. Yesu sanatengere kupanda ungwiro kulikonse chifukwa choti atate wake sanali munthu. Mzimu woyera wa Yehova, kapena kuti mphamvu Yake yogwira ntchito inam’fikira Mariya ndipo mphamvu ya Yehova ‘inamuphimba’ Mariyayo n’kumuchititsa kukhala ndi pakati m’njira yozizwitsa. (Luka 1:34, 35) Motero mwana amene Mariya anabereka anali wangwiro. Bambo amene analera mwanayo anali Yosefe, yemwe anali kalipentala, choncho mwanayo anakulira m’banja losauka ndipo anali woyamba pa ana angapo a m’banjalo.​—Yesaya 7:14; Mateyu 1:22, 23; Marko 6:3.

Pali zinthu zochepa zimene zikudziwika zokhudza ubwana wa Yesu, koma pali chinthu chimodzi chimene chili chofunika kwambiri. Yesu ali ndi zaka 12, makolo ake anapita naye ku Yerusalemu kukachita Paskha, monga ankachitira chaka n’chaka. Ali kumeneko, iye anakhala kwa nthawi yaitali ndithu pa kachisi, “pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.” Komanso “onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.” Inde, Yesu ali wamng’ono chonchi ankatha kufunsa mafunso anzeru kwambiri okhudza zinthu zauzimu komanso kupereka mayankho anzeru amene anadabwitsa anthu. (Luka 2:41-50) Akukula mumzinda wa Nazarete, anaphunzira ukalipentala, ndipo n’zosakayikitsa kuti anaphunzira ntchitoyi kwa bambo ake om’lera aja, a Yosefe.​—Mateyu 13:55.

Yesu ankakhala ku Nazarete mpaka pamene anakwanitsa zaka 30. Kenaka anapita kwa Yohane kukabatizidwa. Pambuyo pobatizidwa, Yesu anayamba ntchito yaikulu yautumiki. Kwa zaka zitatu ndi theka, iye anayenda m’chigawo chonse cha kwawo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Anapereka umboni woti anatumizidwa ndi Mulungu. Anatero motani? Anatero pochita zozizwitsa zambirimbiri zomwe sizingachitike mwa mphamvu ya munthu.​—Mateyu 4:17; Luka 19:37, 38.

Yesu analinso munthu wachifundo ndiponso wachikondi zedi. Chifundo chake chinkaonekera kwambiri chifukwa cha mmene ankaonera anthu ndiponso mmene ankachitira nawo zinthu. Anthu ankamukonda Yesu chifukwa anali wochezeka ndiponso wokoma mtima. Ngakhale ana ankakhala omasuka akakhala ndi Yesu. (Marko 10:13-16) Yesu ankalemekeza akazi, ngakhale kuti anthu ena panthawi ya Yesu ankanyoza akazi. (Yohane 4:9, 27) Iye anathandiza anthu osauka ndi oponderezedwa kuti ‘apeze mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mateyu 11:28-30) Ankaphunzitsa m’njira yotsatirika bwino, yosavuta kumvetsa, ndiponso yothandizadi. Ndipo zimene ankaphunzitsa zinali kusonyeza kuti ankafunitsitsa kuti omvetserawo am’dziwe bwino Mulungu woona, Yehova.​—Yohane 17:6-8.

Mwa chifundo chake, Yesu anachiritsa anthu odwala ndi ovutika ndipo anatero mwa mzimu woyera wa Mulungu. (Mateyu 15:30, 31) Mwachitsanzo, munthu wakhate anapita kwa iye n’kunena kuti: “Ngati mufuna mungathe kundikonza.” Kodi Yesu anatani? Iye anakhudza munthuyo potambasula dzanja lake n’kumuuza kuti: “Ndifuna; takonzedwa.” Ndipo munthu wodwalayo anachira.​—Mateyu 8:2-4.

Taganiziraninso nthawi ina pamene gulu la anthu limene linatsata Yesu linakhala naye masiku atatu popanda chakudya. Yesu anawamvera chisoni anthuwa ndipo mozizwitsa iye anadyetsa “amuna zikwi zinayi kuwaleka [kapena kuti osawerengera] akazi ndi ana.” (Mateyu 15:32-38) Panthawi ina, Yesu anatontholetsa namondwe amene akanatha kumiza anzake. (Marko 4:37-39) Iye anaukitsanso anthu akufa. * (Luka 7:22; Yohane 11:43, 44) Yesu anapereka ngakhale moyo wake wangwiro kuti anthu opanda ungwirofe tikhale ndi chiyembekezo cha m’tsogolo. Izitu zikusonyezeratu kuti Yesu ankakonda anthu kwambiri.

Kodi Yesu Ali Kuti Panopo?

Yesu anafa pa mtengo wozunzirapo ali ndi zaka 33 ndi theka. * Koma imfa imeneyi siinali mapeto a moyo wake. Mbali yachitatu ya moyo wake inayamba patatha masiku atatu atamwalira, pamene Yehova Mulungu anaukitsa Mwana wakeyu kukhala munthu wauzimu. Ataukitsidwa, Yesu anaonekera kwa anthu ambirimbiri amene analipo panthawi imeneyi. (1 Akorinto 15:3-8) Kenaka, iye “anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu,” kudikirira nthawi yodzalandira mphamvu za ufumu. (Ahebri 10:12, 13) Nthawiyi itakwana, Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu. Motero, kodi Yesu tizimuona motani masiku ano? Kodi tikamaganiza za Yesu tiziganizira za munthu amene akuzunzidwa pophedwa? Kapena kodi tizimuona ngati munthu woyenera kulambiridwa? Panopo Yesu si munthu ngati ifeyo ndiponso si Mulungu Wamphamvuyonse. Koma ndi munthu wauzimu wamphamvu amene akulamulira monga Mfumu. Posachedwapa, iye ayamba kulamulira dziko lathu lamavutoli.

Lemba la Chivumbulutso 19:11-16 limafotokoza mophiphiritsa za Yesu Kristu ali mfumu, atakwera pa kavalo woyera ndipo akubwera kudzaweruza ndi kudzachita nkhondo yachilungamo. Lembali limati iye ali ndi “lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu.” Inde, Yesu adzawononga anthu oipa ndi mphamvu zazikulu zimene iye ali nazo. Nanga kodi anthu amene amayesetsa kutsatira chitsanzo chimene Yesu anapereka ali padziko lapansi chidzawachitikire n’chiyani? (1 Petro 2:21) Yesu ndi Atate wake adzawapulumutsa anthuwa pa nkhondo yomwe ichitike posachedwa imene kawirikawiri imatchedwa kuti Armagedo, yomwe ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Adzatero kuti anthuwa akhale kosatha padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu wa kumwamba wa Mulungu.​—Chivumbulutso 7:9, 14; 16:14, 16; 21:3, 4.

Mu ulamuliro wake wamtenderewu, Yesu adzachita zozizwitsa zosasimbika pothandiza anthu onse. (Yesaya 9:6, 7; 11:1-10) Iye adzachiritsa matenda onse n’kuthetsanso imfa. Yehova adzatuma Yesu kuukitsa anthu mabiliyoni amene anafa, n’kuwapatsa mwayi woti athe kukhala padziko lapansi kosatha. (Yohane 5:28, 29) Zoonadi, mu ulamuliro wa Ufumuwu moyo tidzaumva kukoma kwabasi. Motero m’pofunikadi kupitiriza kuphunzira zimene Baibulo limanena ndi kum’dziwa bwino Yesu Kristu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Zozizwitsa zimene Yesu anachita zinali zodziwika kwa aliyense. Ngakhale anthu amene ankadana ndi Yesu anavomereza kuti iye ‘ankachita zizindikiro zambiri.’​—Yohane 11:47, 48.

^ ndime 17 Kuti mumve tsatanetsatane wa nkhani yakuti kodi Kristu anafera pa mtengo kapena pa mtanda, onani masamba 302 mpaka 304 a buku la Kukambitsirana za m’Malemba, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 7]

KODI YESU NDI MULUNGU WAMPHAMVUYONSE?

Anthu ambiri opembedza amanena kuti Yesu ndi Mulungu. Ena amati Mulungu ndi Utatu. Malingana ndi chiphunzitso cha Utatu, “Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu, ndiponso Mzimu Woyera ndi Mulungu, koma sikuti pali Milungu itatu koma Mulungu mmodzi.” Chiphunzitsochi chimatinso atatuwa ndi “amuyaya ndiponso ofanana m’zonse.” (Limatero buku la The Catholic Encyclopedia) Kodi maganizo oterewa n’ngolondola?

Yehova Mulungu ndiye Mlengi. (Chivumbulutso 4:11) Iye alibe chiyambi ndiponso malekezero, ndipo ndi wamphamvuyonse. (Salmo 90:2) Komano Yesu anali n’chiyambi. (Akolose 1:15, 16) Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndiye Atate wake ndipo anati: “Atate ali wamkulu ndi Ine.” (Yohane 14:28) Yesu analongosolanso kuti panali zinthu zina zimene ngakhale iyeyo ndi angelo sankadziwa, koma Atate wake wokha basi.​—Marko 13:32.

Komanso, Yesu anapemphera kwa Atate wake kuti: “Si kufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Kodi Yesu ankapemphera kwa ndani ngati palibe wina wom’posa? Kuphatikizanso apo, Mulungu ndiye anaukitsa Yesu kwa akufa. Yesu sanadziukitse yekha ayi. (Machitidwe 2:32) N’zoonekeratu kuti Atate ndi Mwana sanali ofanana m’zonse, Yesu asanabwere padziko lapansi kapenanso pamene anali kuchita utumiki wake padziko lapansi. Nanga bwanji pambuyo poti Yesu waukitsidwa kupita kumwamba? Lemba la 1 Akorinto 11:3 limati: “Mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Ndipotu Kristuyu adzakhala pansi pa Mulungu kwamuyaya. (1 Akorinto 15:28) Motero Malemba amasonyeza kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse ayi, koma ndi Mwana wa Mulungu.

Chinanso, amene amati ndi munthu wachitatu pa chiphunzitso cha Utatu, yemwe ndi mzimu woyera, si munthu ayi. Wamasalmo ananena mawu otsatirawa popemphera kwa Mulungu: “Potumizira mzimu wanu, zilengedwa.” (Salmo 104:30) Mzimu umenewu si Mulungu yemweyo ayi. Ndi mphamvu yogwira ntchito imene Mulungu amatumiza kapena kuchitira china chilichonse chimene akufuna. Mphamvu imeneyi ndi imene Mulungu analengera kumwamba timakuonaku, dziko lapansi, ndiponso zamoyo zonse. (Genesis 1:2; Yobu 33:4) Mulungu anagwiritsira ntchito mzimu woyera kuuzira amuna amene analemba Baibulo. (2 Petro 1:20, 21) Motero, chiphunzitso cha Utatu, si chiphunzitso cha m’Malemba ayi. * Baibulo limati “Yehova ndiye mmodzi.”​—Deuteronomo 6:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 28 Kuti mudziwe zambiri za nkhaniyi onani kabuku kakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 5]

Pa ubatizo wake, Yesu anakhala Wodzozedwa wa Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu anathera mphamvu zake kuchita ntchito imene Mulungu anam’tuma

[Chithunzi patsamba 7]

Panopo Yesu ndi Mfumu yamphamvu